Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kupemphera Kosaleka?

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kupemphera Kosaleka?

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kupemphera Kosaleka?

“Pempherani kosaleka; m’zonse yamikani.”​—1 Atesalonika 5:17, 18.

1, 2. Kodi Danieli anasonyeza bwanji kuti anaona mwayi wopemphera kukhala wofunika kwambiri, ndipo zimenezi zinakhudza bwanji ubwenzi wake ndi Mulungu?

MNENERI Danieli anali ndi chizoloŵezi chopemphera kwa Mulungu katatu patsiku. Iye anali kupemphera atagwada pawindo la chipinda chake, lomwe linaloza ku mzinda wa Yerusalemu. (1 Mafumu 8:46-49; Danieli 6:10) Ngakhale pamene lamulo la mfumu linaletsa kupemphera kwa wina aliyense koma kwa Dariyo yekha basi, mfumu ya Amedi, Danieli sanaganizeko n’komwe zosiya kupemphera. Kaya zimenezi zinaika moyo wake pangozi kapena ayi, munthuyu wokhala ndi chizoloŵezi chopemphera anachonderera Yehova kosaleka.

2 Kodi Yehova anamuona bwanji Danieli? Pamene mngelo Gabrieli anabwera kudzayankha limodzi mwa mapemphero a Danieli, anatcha mneneriyu ‘wokondedwa kwambiri.’ (Danieli 9:20-23) Mu ulosi wa Ezekieli, Yehova anatcha Danieli munthu wolungama. (Ezekieli 14:14, 20) Kwa zaka zambiri, mapemphero a Danieli anapangitsa kuti pakhale ubwenzi wolimba ndi Mulungu wake, mfundo imene ngakhale Dariyo anadziŵa.​—Danieli 6:16.

3. Malinga ndi zimene zinachitikira mmishonale wina, kodi pemphero lingatithandize bwanji kukhala okhulupirika?

3 Kupemphera nthaŵi zonse kungatithandizenso kulimbana ndi mayesero aakulu. Mwachitsanzo, taganizirani za Harold King, mmishonale ku China, yemwe analamulidwa kukhala kundende zaka zisanu mu chipinda chayekha. Pa zimene zinamuchitikira, Mbale King anati: “Ndingapatulidwe kwa anthu anzanga, koma palibe amene angandipatule kwa Mulungu. . . . Chotero, ndinali kugwada katatu patsiku mu chipinda changacho pamalo oonekera kwa aliyense amene akanadutsa ndi kupemphera mokweza, poganizira Danieli, amene Baibulo limanena. . . . Zinaoneka kuti panthaŵi zimenezi mzimu wa Mulungu unkanditsogolera kuganizira zinthu zopindulitsa ndipo unandipangitsa kukhala wosatekeseka. Pemphero linandipatsa mphamvu ndi kundilimbitsa mwauzimu.”

4. Kodi ndi mafunso ati okhudza pemphero amene tikambirane m’nkhaniyi?

4 Baibulo limati: “Pempherani kosaleka; m’zonse yamikani.” (1 Atesalonika 5:17, 18) Poganizira malangizo ameneŵa, tiyeni tikambirane mafunso otsatiraŵa: Kodi n’chifukwa chiyani tifunika kuikira mtima pa mapemphero athu? Kodi tili ndi zifukwa zotani zopempherera kwa Yehova nthaŵi zonse? Ndipo tingachite chiyani ngati tikudziona wosayenera kupemphera kwa Mulungu chifukwa cha zolakwa zathu?

Pangani Ubwenzi Kudzera M’pemphero

5. Kodi ndi ubwenzi wapadera uti umene pemphero limatithandiza kukhala nawo?

5 Kodi mungafune kuti Yehova akuoneni monga bwenzi lake? Iye anatchula Abrahamu kholo lakale motero. (Yesaya 41:8; Yakobo 2:23) Yehova akufuna kuti tikhale naye paubwenzi wangati umenewu. Akutipempha kuti tiyandikire kwa iye. (Yakobo 4:8) Kodi pempho limeneli silingatipangitse kuganizira mosamalitsa za mwayi wapadera wopemphera? N’kovuta kwambiri kupatsidwa nthaŵi yolankhulana ndi nduna yolemekezeka ya boma, kananji kukhala bwenzi lake! Koma Mlengi wachilengedwe chonse amatilimbikitsa kupemphera kwa iye momasuka, nthaŵi iliyonse imene tingafune kutero. (Salmo 37:5) Mapemphero athu osaleka amatithandiza kukhala ndi ubwenzi wolimba ndi Yehova.

6. Kodi chitsanzo cha Yesu chikutiphunzitsa chiyani za kufunika ‘kopemphera mosaleka’?

6 Komabe, n’kosavuta m’pang’ono pomwe kunyalanyaza pemphero. Mavuto a moyo watsiku ndi tsiku amene tingakumane nawo angatidodometse kwambiri moti tingalephere kulankhula ndi Mulungu. Yesu analimbikitsa ophunzira ake “kupemphera [kosaleka, NW]” ndipo iye anachita zimenezi. (Mateyu 26:41) Ngakhale kuti nthaŵi zonse anali wotanganidwa kuchoka m’maŵa mpaka usiku, iye ankapatula nthaŵi yolankhula ndi Atate wake wakumwamba. Nthaŵi zina, Yesu anali kudzuka “usikusiku” kuti apemphere. (Marko 1:35) Pa nthaŵi zina, pamapeto a tsiku anali kupita ku malo ayekha kuti akapemphere kwa Yehova. (Mateyu 14:23) Nthaŵi zonse Yesu ankapeza nthaŵi yopemphera ndipo ifenso tiyenera kutero.​—1 Petro 2:21.

7. Kodi n’chiyani chiyenera kutichititsa kulankhula ndi Atate wathu wakumwamba tsiku ndi tsiku?

7 Tsiku lililonse timakhala ndi mipata yambiri yomwe tingapemphere patokha. Mipatayi imapezeka pamene tikumana ndi mavuto, zokopa ndiponso popanga zosankha. (Aefeso 6:18) Pamene tipempha Mulungu kutitsogolera pa zochitika zonse za moyo, mosakayika ubwenzi wathu ndi iye udzakula. Ngati mabwenzi aŵiri akumana ndi mavuto pamodzi, kodi ubwenzi wawo sumakhala wolimba? (Miyambo 17:17) Ifenso ubwenzi wathu ndi Yehova udzakhala wolimba ngati timudalira ndiponso iye akatithandiza.​—2 Mbiri 14:11.

8. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Nehemiya, Yesu ndi Hana ponena za kutali kwa mapemphero athu patokha?

8 Tingakhale osangalala kwambiri kuti Mulungu saika malire pa kutalika kwa nthaŵi kapena maulendo amene tiyenera kulankhula naye m’pemphero. Nehemiya anapemphera chamumtima asanapemphe mfumu ya Perisiya. (Nehemiya 2:4, 5) Yesunso anapemphera mwachidule pamene amapempha Yehova kum’patsa mphamvu zoukitsira Lazaro. (Yohane 11:41, 42) Mosiyanako ndi zimenezi, Hana ‘anapempherabe pamaso pa Yehova’ pomuuza zakukhosi kwake. (1 Samueli 1:12, 15, 16) Mapemphero athu angakhale aafupi kapena aatali malinga ndi zimene tikufuna ndiponso mmene zinthu zilili.

9. N’chifukwa chiyani mapemphero athu afunika kukhala otamanda ndi kuyamikira zonse zimene Yehova amatichitira?

9 Mapemphero ambiri m’Baibulo amasonyeza kuyamikira kochokera pansi pamtima malo apamwamba a Yehova ndi ntchito zake zodabwitsa. (Eksodo 15:1-19; 1 Mbiri 16:7-36; Salmo 145) Mtumwi Yohane anaona akulu 24 m’masomphenya, chiŵerengero chonse cha Akristu odzozedwa ali m’malo awo kumwamba, akutamanda Yehova kuti: “Muyenera inu, Ambuye wathu, ndi Mulungu wathu, kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu; chifukwa mudalenga zonse, ndipo mwa chifuniro chanu zinakhala, nizinalengedwa.” (Chivumbulutso 4:10, 11) Ifenso tili ndi chifukwa chotamandira Mlengi nthaŵi zonse. Makolo amasangalala kwambiri pamene mwana wawo awayamikira ndi mtima wonse chifukwa cha chinthu chinachake chimene am’chitira. Kusinkhasinkha moyamikira ubwino wa Yehova ndi kufotokoza kuuyamikira kwathu ndi mtima wonse ndi njira yabwino yowongolerera mapemphero athu.

N’chifukwa Chiyani Tiyenera ‘Kupemphera Kosaleka’?

10. Kodi pemphero limathandiza bwanji kuti chikhulupiriro chathu chilimbe?

10 Kupemphera nthaŵi zonse n’kofunika pa chikhulupiriro chathu. Yesu atasonyeza kufunika ‘kopemphera nthaŵi zonse, osafooka mtima,’ anafunsa kuti: “Mwana wa munthu pakudza Iye, adzapeza chikhulupiriro padziko lapansi kodi?” (Luka 18:1-8) Kupemphera ndi mtima wonse kumakulitsa chikhulupiriro. Pamene kholo lakale Abrahamu anali kukalamba, koma wopanda mwana, anauza Mulungu za nkhaniyo. Poyankha, Yehova choyamba anamuuza kuti ayang’ane kumwamba ndi kuŵerenga nyenyezi, ngati akanatha kutero. Ndiyeno Mulungu anatsimikizira Abrahamu kuti: “Zoterezo zidzakhala mbewu zako.” Kodi zotsatira zake zinali zotani? Abrahamu “anakhulupirira Yehova, ndipo kunayesedwa kwa iye chilungamo.” (Genesis 15:5, 6) Ngati popemphera tiuza Yehova zakukhosi kwathu, kukhulupirira malonjezo ake a m’Baibulo ndi kumvera Iye, adzalimbitsa chikhulupiriro chathu.

11. Kodi pemphero lingatithandize bwanji kuthana ndi mavuto?

11 Pemphero lingatithandizenso kuthana ndi mavuto. Kodi moyo wathu ndi wolemetsa ndipo tikukumana ndi mavuto osapiririka? Baibulo limatiuza kuti: “Um’senze Yehova nkhaŵa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza: Nthaŵi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.” (Salmo 55:22) Pamene tikumana ndi zosankha zovuta, tingatsatire chitsanzo cha Yesu. Asanasankhe atumwi ake 12, anakhala usiku wonse akupemphera. (Luka 6:12-16) Ndipo usiku woti aphedwa maŵa, Yesu anapemphera kwambiri moti “thukuta lake linakhala ngati madontho aakulu a mwazi alinkugwa pansi.” (Luka 22:44) Kodi chinatsatira n’chiyani? ‘Anamvedwa popeza anaopa Mulungu.’ (Ahebri 5:7) Mapemphero athu amtima wonse ndiponso osaleka adzatithandiza kuthana ndi zinthu zodetsa nkhaŵa komanso mayesero ovuta.

12. Kodi pemphero limasonyeza bwanji kuti Yehova amatikonda patokha?

12 Chifukwa china choyandikirira kwa Yehova kudzera m’pemphero n’chakuti, Iye adzayandikiranso kwa ife. (Yakobo 4:8) Tikamauza Yehova zakukhosi kwathu popemphera, kodi sitimaona kuti amatikonda ndipo amatisamalira mwachikondi? Timaona kuti Mulungu amatikonda patokha. Yehova sanapatse wina aliyense udindo womvetsera mapemphero amene atumiki ake amapemphera kwa Iye monga Atate wawo wakumwamba. (Salmo 66:19, 20; Luka 11:2) Ndipo akutipempha kuti ‘titaye pa Iye nkhaŵa zathu zonse pakuti Iye amatisamalira.’​—1 Petro 5:6, 7.

13, 14. Kodi tili ndi zifukwa zotani zopempherera kosaleka?

13 Pemphero lingatilimbikitse kukhala achangu kwambiri mu utumiki ndiponso lingatilimbikitse pamene tikufuna kuusiya chifukwa cha mphwayi za anthu kapena chitsutso. (Machitidwe 4:23-31) Pemphero lingatitchinjirizenso ku “machenjerero a Mdyerekezi.” (Aefeso 6:11, 17, 18) Pamene tiyesetsa kuthana ndi mayesero atsiku ndi tsiku, tingapemphe Mulungu nthaŵi zonse kuti atilimbitse. Pemphero lachitsanzo la Yesu lili ndi pempho lakuti Yehova “atipulumutse kwa woipayo,” Satana Mdyerekezi.​—Mateyu 6:13.

14 Ngati tipitirizabe kupempherera thandizo lothetsa zikhumbo zathu zochimwa, Yehova adzatithandiza. Tinalonjezedwa kuti: “Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.” (1 Akorinto 10:13) Mtumwi Paulo analimbikitsidwa ndi Yehova pa zochitika zosiyanasiyana. Iye anati: “Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.”​—Afilipi 4:13; 2 Akorinto 11:23-29.

Limbikani Kupemphera Ngakhale Muli ndi Zolakwa

15. Kodi chingachitike n’chiyani ngati khalidwe lathu silikugwirizana ndi miyezo ya Mulungu?

15 Kuti mapemphero athu amvedwe, sitiyenera kukana malangizo a Mawu a Mulungu. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Chimene chilichonse tipempha, tilandira kwa Iye chifukwa tisunga malamulo ake, ndipo tichita zom’kondweretsa pamaso pake.” (1 Yohane 3:22) Komabe, chingachitike n’chiyani ngati khalidwe lathu silikugwirizana ndi miyezo ya Mulungu? Adamu ndi Hava atachimwa m’munda wa Edene anabisala. Ifenso tingafune kudzibisa “pamaso pa Yehova” ndi kusiya kupemphera. (Genesis 3:8) Klaus, yemwe watumikira monga woyang’anira woyendayenda kwanthaŵi yaitali anati: “Ndaona kuti nthaŵi zambiri kulakwitsa koyamba kumene anthu amene amachoka kwa Yehova ndi gulu lake amachita ndiko kusiya kupemphera.” (Ahebri 2:1) Ndi mmenenso zinachitikira ndi José Ángel. Iye akuti: “Pafupifupi zaka zisanu ndi zitatu, sindinali kupemphera kaŵirikaŵiri kwa Yehova. Ndinali kudziona wosayenera kumulankhula, ngakhale ndinali kumuonabe kukhala Atate wanga wakumwamba.”

16, 17. Perekani zitsanzo za mmene kupemphera nthaŵi zonse kungatithandizire kuthetsa kufooka kwauzimu?

16 Enafe tingadzione kukhala osayenera kupemphera chifukwa cha kufooka mwauzimu kapena chifukwa chochita tchimo. Koma imeneyi ndiyo nthaŵi yeniyeni imene tifunika kupindula ndi mwayi wopemphera. Yona anathawa ntchito yake. Koma ‘Yona anaitana Yehova m’nsautso yake, ndipo anamuyankha iye; Yona anafuula ali m’mimba ya manda, ndipo Yehova anamva mawu ake.’ (Yona 2:2) Yona anapemphera, Yehova anayankha pemphero lake ndipo Yona anachira mwauzimu.

17 José Ángel nayenso anapemphera ndi mtima wonse kuti athandizidwe. Iye akuti: “Ndinanena zakukhosi kwanga ndi kupempha Mulungu kuti andikhululukire. Ndipo anandithandizadi. Sindiganiza kuti ndikanabwerera m’choonadi popanda thandizo la pemphero. Tsopano ndimapemphera nthaŵi zonse tsiku lililonse ndipo ndimalakalaka nthaŵi zimenezi.” Nthaŵi zonse tizikhala omasuka kumuuza Mulungu zolakwa zathu ndi kum’pempha modzichepetsa kuti atikhululukire. Pamene Mfumu Davide anaulula machimo ake, Yehova anam’khululukira. (Salmo 32:3-5) Yehova amafuna kutithandiza osati kutiweruza. (1 Yohane 3:19, 20) Ndiponso mapemphero a akulu mu mpingo angatithandize mwauzimu, chifukwa mapemphero otero ‘akhoza kwakukulu.’​—Yakobo 5:13-16.

18. Kodi ndi chidaliro chotani chimene atumiki a Mulungu angakhale nacho mosasamala za mmene angakhalire atalowerera?

18 Kodi ndi tate wotani angakanire mwana amene modzichepetsa apita kwa iye atalakwitsa kuti amuthandize ndi kumulangiza? Fanizo la mwana wolowerera likusonyeza kuti zilibe kanthu kuti talowerera bwanji, Atate wathu wakumwamba amasangalala tikabwerera kwa iye. (Luka 15:21, 22, 32) Yehova akuuza onse amene alakwa kuti amupemphe, “pakuti Iye adzakhululukira koposa.” (Yesaya 55:6, 7) Ngakhale kuti Davide anachita machimo angapo aakulu, anapempha Yehova, kuti: “Tcherani khutu pemphero langa, Mulungu; ndipo musadzibisa pa kupempha kwanga.” Iye anatinso: “Madzulo, m’maŵa, ndi m’sana ndidzadandaula, ndi kubuula, ndipo [Yehova] adzamva mawu anga.” (Salmo 55:1, 17) Zimenezitu ndi zolimbikitsa kwambiri!

19. N’chifukwa chiyani sitiyenera kunena kuti mapemphero amene aoneka ngati osayankhidwa ndi umboni woti Mulungu sanawayanje?

19 Bwanji ngati pemphero lathu siliyankhidwa nthaŵi yomweyo? Ndiye kuti tiyenera kuonetsetsa kuti pemphero lathu likugwirizana ndi chifuno cha Yehova ndipo liperekedwe m’dzina la Yesu. (Yohane 16:23; 1 Yohane 5:14) Wophunzira Yakobo ananena za Akristu ena omwe mapemphero awo sanayankhidwe chifukwa anali “kupempha ndi chifuno cholakwika.” (Yakobo 4:3, NW) Komabe, sitiyenera kugamula msanga kuti mapemphero amene aoneka ngati osayankhidwa ndiye kuti nthaŵi zonse ndi umboni woti Mulungu sanawayanje. Nthaŵi zina Yehova angalole atumiki okhulupirika kuti azipemphererabe za nkhani inayake kwa kanthaŵi iye asanawayankhe. Yesu anati: ‘Pemphanibe, ndipo chidzapatsidwa kwa inu.’ (Mateyu 7:7) N’chifukwa chake tifunika ‘kulimbika chilimbikire m’kupemphera.’​—Aroma 12:12.

Pempherani Nthaŵi Zonse

20, 21. (a) N’chifukwa chiyani tifunika kupemphera kosaleka “masiku otsiriza” ano? (b) Kodi tidzalandira chiyani ngati tsiku ndi tsiku tiyandikira mpando wachifumu wachisomo wa Yehova?

20 Mavuto akuwonjezeka “masiku otsiriza” ano, odziŵika ndi “nthaŵi zowawitsa.” (2 Timoteo 3:1) N’kosavuta kuti tizingoganiza za mayesero. Komabe, mapemphero athu osaleka adzatithandiza kukhalabe ndi moyo wauzimu mosasamala kanthu za mavuto, zokopa ndiponso zokumudwitsa za nthaŵi zonse. Mapemphero athu atsiku ndi tsiku kwa Yehova angatipatse thandizo limene tikufunika.

21 Yehova “wakumva pemphero” sakhala wotanganidwa kwambiri koti n’kulephera kutimvetsera. (Salmo 65:2) Tisakhale otanganidwa kwambiri moti n’kulephera kulankhula naye. Ubwenzi wathu ndi Mulungu ndi chinthu chofunika kwambiri chimene tili nacho. Tisauone mopepuka. “Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wachifumu wachisomo, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthaŵi yakusoŵa.”​—Ahebri 4:16.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi tikuphunzira chiyani kwa mneneri Danieli za kufunika kwa pemphero?

• Kodi tingalimbitse bwanji ubwenzi wathu ndi Yehova?

• N’chifukwa chiyani tifunika kupemphera kosaleka?

• N’chifukwa chiyani kudziona wosayenera kusatilepheretse kupemphera kwa Yehova?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 16]

Nehemiya anapemphera mwachidule chamumtima asanalankhule ndi mfumu

[Chithunzi patsamba 17]

Hana ‘anapempherabe pamaso pa Yehova’

[Zithunzi patsamba 18]

Yesu anapemphera usiku wonse asanasankhe atumwi ake 12

[Zithunzi patsamba 20]

Mipata yopemphera imapezeka tsiku lonse