Kodi Tiyembekezere Kuti Mulungu Adzachitapo Kanthu Motani?
Kodi Tiyembekezere Kuti Mulungu Adzachitapo Kanthu Motani?
M’ZAKA za m’ma 700 B.C.E., Mfumu Hezekiya ya Yuda, yemwe anali ndi zaka 39, anazindikira kuti anali kudwala matenda osachiritsika. Atakhumudwa kwambiri ndi nkhani imeneyi, Hezekiya anapemphera kwa Mulungu kuti am’chiritse. Mulungu anayankha kudzera mwa mneneri Yesaya 38:1-5.
wake kuti: “Ndamva kupemphera kwako, ndaona misozi yako; taona, ndidzawonjezera pa masiku ako zaka khumi ndi zisanu.”—Kodi n’chifukwa chiyani Mulungu anachitapo kanthu pa nthaŵi imeneyo? Zaka mazana angapo m’mbuyomo, Mulungu anali atalonjeza Mfumu yolungama Davide kuti: “Nyumba yako ndi ufumu wako zidzakhazikikadi ku nthaŵi zonse pamaso pako; mpando wachifumu wako udzakhazikika ku nthaŵi zonse.” Mulungu ananenanso kuti Mesiya adzabadwira mu mzera wa banja la Davide. (2 Samueli 7:16; Salmo 89:20, 26-29; Yesaya 11:1) Panthaŵi imene Hezekiya anadwala, analibe mwana wamwamuna. Choncho, mzera wachifumu wa banja la Davide ukanatha ngati Hezekiya akanamwalira. Kuloŵerera kwa Mulungu pa nkhani ya Hezekiya kunathandiza kuti mzera wa anthu umene Mesiya anadzabadwiramo usaduke.
Pofuna kukwaniritsa malonjezo ake, Yehova anayesetsa kuchitapo kanthu kuthandiza anthu ake pa nthaŵi zosiyanasiyana Chikristu chisanayambe. Ponena za kumasulidwa kwa Aisrayeli kuchoka ku ukapolo ku Igupto, Mose anati: “Koma Yehova anakutulutsani ndi dzanja lamphamvu, . . . chifukwa Yehova akukondani, ndi chifukwa cha kusunga lumbiro lija analumbirira makolo anu.”—Deuteronomo 7:8.
M’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino, kuloŵererapo kwa Mulungu kunachititsanso kuti chifuno chake chichitike. Mwachitsanzo, Myuda wotchedwa Saulo anaona masomphenya odabwitsa pa njira yopita ku Damasiko omwe cholinga chake chinali chom’letsa kuti asazunze ophunzira a Kristu. Kutembenuka mtima kwa munthu ameneyu, amene anadzakhala mtumwi Paulo, kunathandiza kwambiri kuti uthenga wabwino ufalikire kwa anthu amitundu.—Machitidwe 9:1-16; Aroma 11:13.
Kodi Ankachitapo Kanthu Nthaŵi Zonse?
Kodi Mulungu ankachitapo kanthu nthaŵi zonse kapena nthaŵi zapadera zokha? Malemba amasonyeza momveka bwino kuti sankachitapo kanthu nthaŵi zonse. Ngakhale kuti Mulungu anapulumutsa Ahebri achinyamata atatu kuti asafe mu ng’anjo ya moto ndiponso anapulumutsa mneneri Danieli m’dzenje la mikango, Iye sanapulumutse aneneri ena ku imfa. (2 Mbiri 24:20, 21; Danieli 3:21-27; 6:16-22; Ahebri 11:37) Petro anapulumutsidwa modabwitsa m’ndende imene Herode Agripa woyamba anam’tsekera. Koma mfumu yomweyi inapha mtumwi Yakobo, ndipo Mulungu sanachitepo kanthu koletsa zimenezi. (Machitidwe 12:1-11) Ngakhale kuti Mulungu anapatsa atumwi mphamvu zotha kuchiritsa odwala ndipo ngakhale kuukitsa akufa, sanalole kuti achotse “munga m’thupi” mwa Paulo, umene mwina unali matenda enaake.—2 Akorinto 12:7-9; Machitidwe 9:32-41; 1 Akorinto 12:28.
Mulungu sanachitepo kanthu kuletsa chizunzo chadzidzidzi chomwe Mfumu ya Aroma, Nero, anavutitsa nacho ophunzira a Kristu. Akristu anazunzidwa, kuotchedwa akadali a moyo, ndi kuponyedwa ku zinyama zolusa. Komabe, chizunzo chimenechi sichinadabwitse Akristu oyambirirawo, ndipo sichinafooketse chikhulupiriro chawo chakuti Mulungu alipo. Ophunzirawo sanadabwe chifukwa Yesu anali atawachenjezeratu kuti adzawatengera ku mabwalo a milandu ndipo ayenera kukhala okonzeka kuvutika, ngakhale kufa kumene, chifukwa cha chikhulupiriro chawo.—Mateyu 10:17-22.
Monga mmene anachitira kale, masiku anonso Mulungu angathe kupulumutsa atumiki ake ku mavuto oopsa, ndipo anthu amene amaona kuti Mulungu anawapulumutsako penapake sitiyenera kuwatsutsa. Komabe, n’zovuta kunena mwatchutchutchu kuti Mulungu anawapulumutsadi kapena ayi ku mavuto amenewo. Atumiki angapo okhulupirika kwa Yehova anavulala pamene fakitale yamankhwala inaphulika ku Toulouse, ndipo zikwi za Akristu okhulupirika zinafa ku misasa ya Nazi ndi ya maboma a Chikomyunizimu, kapena m’njira zina zomvetsa chisoni zosiyanasiyana popanda Mulungu kuchitapo kanthu koletsa zimenezi. Kodi n’chifukwa chiyani Mulungu sachitapo kanthu nthaŵi zonse kuthandiza anthu amene amamumvera?—Danieli 3:17, 18.
“Nthaŵi ndi Zochitika Zosayembekezeka”
Pakachitika ngozi, aliyense akhoza kukhudzidwa, ndipo sizitengera kuti munthuyo amakhulupirira Mulungu kapena ayi. Panthaŵi imene fakitale yamankhwala inaphulika ku Toulouse, Alain ndi Liliane anapulumuka, koma anthu 30 anafa ndipo anthu mazana angapo anavulala, ngakhale kuti sanalakwe chilichonse. Nkhani yaikulu kuposa pamenepa ndi yakuti anthu zikwi zambiri amakhala pa mavuto chifukwa cha upandu, kuyendetsa galimoto mosasamala kwa anthu ena, kapena nkhondo, ndipo sitinganene kuti ndi Mulungu amene amachititsa zinthu zoipa zimenezi. Baibulo limatikumbutsa kuti “nthaŵi ndi zochitika zosayembekezeka zimagwera” aliyense.—Mlaliki 9:11, NW.
Kuonjezera apo, anthu amadwala, amakalamba, ndipo amafa. Ngakhale anthu ena amene anaganizapo kuti Mulungu anawapulumutsa modabwitsa kapena kuwachiritsa matenda awo mosayembekezeka pamapeto pake anafa. Kuchotsa matenda ndi imfa ndi ‘kupukuta misozi yonse’ m’maso mwa anthu kudzachitika m’tsogolo.—Chivumbulutso 21:1-4.
Kuti zimenezo zidzachitike, pakufunika pachitike chinachake chachikulu komanso champhamvu, osati kungochitapo kanthu pa nthaŵi zapadera zokha. Baibulo limafotokoza za nthaŵi yotchedwa “tsiku la Yehova.” (Zefaniya 1:14) Pa nthaŵi imene Mulungu adzachite zinthu zazikulu imeneyi, adzachotsa kuipa konse. Anthu adzapatsidwa mwayi wokhala ndi moyo wosatha komanso zinthu zidzakhala zabwino zokhazokha, ndipo panthaŵi imeneyo “zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kulowa mumtima.” (Yesaya 65:17) Ngakhale akufa adzakhalanso ndi moyo, ndipo kumeneku kudzakhala kuchotseratu chinthu choipa kwambiri kuposa zonse chimene chimapweteka anthu. (Yohane 5:28, 29) Mulungu adzatero chifukwa cha chikondi ndi ubwino wake wosatha, ndipo adzathetseratu mavuto onse a anthu mpaka kalekale.
Zimene Mulungu Akuchitapo Masiku Ano
Komabe, zimenezi sizikutanthauza kuti pakadali pano Mulungu amangoyang’ana osachitapo kanthu pamene chilengedwe chake chikuzunzika. Masiku ano, Mulungu akupereka mwayi kwa anthu onse woti amudziŵe ndiponso kuti akhale mabwenzi ake, mosaganizira za fuko kapena moyo wawo. (1 Timoteo 2:3, 4) Yesu anafotokoza zimene Mulungu akuchitazi m’mawu aŵa: “Kulibe mmodzi akhoza kudza kwa Ine koma ngati Atate wondituma Ine am’koka iye.” (Yohane 6:44) Mulungu amakokera anthu oona mtima kwa iye pogwiritsa ntchito uthenga wa Ufumu umene atumiki ake akulalikira padziko lonse lapansi.
Kuonjezera apo, Mulungu amatsogolera mwachindunji moyo wa anthu amene akufuna kumutsatira. Mwa kugwiritsa ntchito mzimu wake woyera, Mulungu ‘akutsegula mitima yawo’ kuti amvetsetse cholinga chake ndiponso kuti azichita zimene iye amafuna. (Machitidwe 16:14) Inde, mwa kupereka mwayi kwa anthu woti amudziŵe, adziŵe Mawu ake, komanso zolinga zake, Mulungu akupereka umboni woti amakonda ndipo amaganizira aliyense wa ife.—Yohane 17:3.
Pomaliza, Mulungu amathandiza atumiki ake masiku ano, osati mwa kuwapulumutsa modabwitsa, koma mwa kuwapatsa mzimu wake woyera ndi “ukulu woposa wamphamvu” kuti athe kulimbana ndi vuto lililonse limene angakumane nalo. (2 Akorinto 4:7) Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ndikhoza zonse mwa Iye [Yehova Mulungu] wondipatsa mphamvuyo.”—Afilipi 4:13.
Choncho, tili ndi zifukwa zabwino zokhalira oyamikira kwa Mulungu tsiku lililonse chifukwa cha moyo umene tili nawo ndi chiyembekezo chimene akutipatsa chodzakhala ndi moyo kosatha m’dziko lopanda mavuto alionse. “Ndidzabwezera Yehova chiyani chifukwa cha zokoma zake zonse anandichitira?” anafunsa motero wamasalmo. “Ndidzanyamula chikho cha chipulumutso, ndipo ndidzaitanira dzina la Yehova.” (Salmo 116:12, 13) Kuŵerenga magazini ano nthaŵi zonse kudzakuthandizani kumvetsetsa zimene Mulungu wachita kale, zimene akuchita, ndi zimene adzachite m’tsogolo. Kudziŵa zimenezi kungakupatseni chimwemwe pakadali pano ndi chiyembekezo cholimba cha m’tsogolo.—1 Timoteo 4:8.
[Mawu Otsindika patsamba 6]
“Zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kulowa mumtima.”—Yesaya 65:17
[Zithunzi patsamba 5]
M’nthaŵi za m’Baibulo, Yehova sanaletse kuponyedwa miyala kwa Zekariya . . .
kapena kuphedwa kwa anthu osalakwa ndi Herode
[Chithunzi patsamba 7]
Nthaŵi imene sikudzakhalanso mavuto alionse yatsala pang’ono kukwana; ngakhale akufa adzakhalanso ndi moyo