Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kumvetsa Cholinga cha Kulanga

Kumvetsa Cholinga cha Kulanga

Kumvetsa Cholinga cha Kulanga

KODI mumaganiza chiyani mukamva mawu akuti “kulanga”? Buku lina lotanthauzira mawu limati kulanga ndiko ‘kupereka malango pa makhalidwe ndi kupereka chilango kwa munthu wolakwa.’ Anthu ambiri masiku ano amaipidwa akamva mawu akuti kulanga.

Koma kulanga kumene Baibulo limafotokoza n’kosiyana ndi mmene anthuwo amaganizira. Mfumu ya nzeru Solomo inalemba kuti: “Mwananga, usapeputse mwambo wa Yehova.” (Miyambo 3:11) Mawu ameneŵa sakunena za mwambo, kapena kuti kulanga, kwawamba koma akunena za “mwambo wa Yehova,” kutanthauza kuti ndi kulanga kotsatira mfundo zapamwamba za Mulungu. Kulanga koteroko n’kumene kumapindulitsa mwauzimu, ndipo munthu angafune kulangidwa motero. Mosiyana ndi zimenezi, kulanga motsatira maganizo a anthu kumene kumatsutsana ndi mfundo zapamwamba za Yehova n’kolakwika ndipo kumapweteka ena. Zimenezi n’zimene zachititsa kuti anthu aziipidwa ndi kulanga.

N’chifukwa chiyani timalimbikitsidwa kumvera kulanga kwa Yehova? Malemba amafotokoza kuti kulanga kwa Mulungu kumasonyeza kuti amakonda anthu amene anawalenga. Motero, Solomo anapitiriza kuti: “Yehova adzudzula omwe awakonda; monga atate mwana amene akondwera naye.”​—Miyambo 3:12.

Kodi Kulanga ndi Kukhaulitsa N’zosiyana Bwanji?

Kulanga kumene Baibulo limafotokoza kuli ndi mbali zosiyanasiyana monga kutsogolera, kulangiza, kuphunzitsa, kudzudzula, kuwongolera, ngakhalenso chilango. Komabe, m’mbali zonsezo, chikondi n’chimene chimamulimbikitsa Yehova kuti alange munthu, ndipo cholinga chake chimakhala choti munthu wolangidwayo apindule. Yehova akamalanga munthu kuti amuwongolere sakhala n’cholinga chongokhaulitsa.

Komabe, cholinga cha chilango cha Mulungu sikuti nthaŵi zonse chimakhala chakuti awongolere kapena aphunzitse munthuyo. Mwachitsanzo, kuyambira tsiku limene Adamu ndi Hava anachimwa, anayamba kuvutika chifukwa cha kusamvera kwawo. Yehova anawathamangitsa m’munda wa Edene wa paradaiso, ndipo anakumana ndi mavuto chifukwa cha kupanda ungwiro, matenda, ndi ukalamba. Patatha zaka mazana angapo akuvutika, anamwalira moti sadzaukanso. Chimenechi chinali chilango cha Mulungu, koma sikunali kulanga kofuna kuwongolera. Adamu ndi Hava, amene anachimwa mwadala ndiponso sanafune kulapa, sakanatheka kuwawongolera.

Nthaŵi zinanso zimene Yehova anapereka chilango kwa anthu ndi panthaŵi monga ya Chigumula cha m’masiku a Nowa, kuwonongedwa kwa Sodomu ndi Gomora, ndi kuwonongedwa kwa ankhondo a Aigupto pa Nyanja Yofiira. Zimene Yehova anachita pa nthaŵi zimenezi, cholinga chake sichinali choti atsogolere, alangize, kapena choti aphunzitse anthuwo. Pofotokoza za chilango cha Mulungu choterocho, mtumwi Petro analemba kuti: “Sanalekerera dziko lapansi lakale, koma anasunga Nowa mlaliki wa chilungamo, ndi anzake asanu ndi aŵiri pakulitengera dziko la osapembedza chigumula; ndipo pakuisandutsa makala midzi ya Sodomu ndi Gomora anaitsutsa poigwetsa, ataiika chitsanzo cha kwa iwo akakhala osapembedza.”​—2 Petro 2:5, 6.

Kodi chilango choterocho ‘chinaika chitsanzo cha kwa iwo akakhala osapembedza’ motani? Paulo, m’kalata imene analembera Atesalonika, ananena kuti nthaŵi imene tikukhala ino ndi nthaŵi imene Mulungu, kudzera mwa Yesu Kristu, ‘adzabwezera chilango kwa iwo osam’dziŵa Mulungu, ndi iwo osamvera Uthenga Wabwino.’ Ndiyeno anapitiriza kuti: “Amene[ŵa] adzamva chilango, ndicho chiwonongeko chosatha.” (2 Atesalonika 1:8, 9) Mwachionekere, cholinga cha chilango choterocho si choti aphunzitse kapena awongolere anthu amene akuwapatsa chilangowo. Koma Yehova akamapempha anthu amene amamulambira kuti amvere kulanga kwake, satanthauza kuti awakhaulitsa monga mmene amachitira kwa anthu osalapa.

N’zochititsa chidwi kuti Baibulo silifotokoza kuti khalidwe lalikulu la Yehova ndilo kupereka chilango. M’malo mwake, nthaŵi zambiri limati iye ndi mphunzitsi wachikondi ndiponso woleza mtima. (Yobu 36:22; Salmo 71:17; Yesaya 54:13) Inde, Mulungu akamalanga munthu n’cholinga chofuna kumuwongolera, nthaŵi zonse amatero mwachikondi ndiponso moleza mtima. Mwakumvetsa cholinga cha chilango, Akristu adzatha kuvomera kulangidwa ndi ena ndiponso adzatha kulanga ena ndi mtima wabwino.

Kulanga kwa Makolo Achikondi

N’zofunika kwambiri kuti anthu onse, m’banja ndiponso mumpingo wachikristu, azimvetsa cholinga cha kulanga. Zimenezi ziyenera kukhala choncho makamaka kwa anthu amene ali ndi ulamuliro, monga makolo. Lemba la Miyambo 13:24 limati: “Wolekerera mwanake osam’menya amuda; koma wom’konda am’yambize kum’langa.”

Kodi makolo ayenera kulanga motani? Baibulo limafotokoza kuti: “Atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.” (Aefeso 6:4) Langizo limeneli analibwereza m’mawu aŵa: “Atate inu, musaputa ana anu, kuti angataye mtima.”​—Akolose 3:21.

Makolo achikristu amene amamvetsa cholinga cha kulanga sadzachita zinthu mwankhanza. Mfundo imene ili mu lemba la 2 Timoteo 2:24 ingagwiritsidwe ntchito pankhani ya mmene makolo amalangira. M’lembalo Paulo anati: “Kapolo wa Ambuye sayenera kuchita ndewu, komatu akhale woyenera, waulere pa onse, wodziŵa kuphunzitsa.” Mkwiyo wosalamulirika, kukalipa ndiponso kutukwana kapena kunyoza, sindiko kulanga kwachikondi ndipo Akristu sayenera kuchita zimenezi.​—Aefeso 4:31; Akolose 3:8.

Makolo akamawongolera ana sayenera kungowalanga msangamsanga n’cholinga chofuna kuwakhaulitsa mowaumira mtima. Ana ambiri amafuna kuwalangiza mobwerezabwereza asanayambe kuwongolera maganizo awo. Motero, makolo ayenera kukhala ndi nthaŵi yokwanira, kusonyeza kuleza mtima, ndi kuganizira mofatsa za njira imene amaperekera chilango. Ayenera kukumbukira kuti ana amafunika kuwalera “m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.” Zimenezi zimatanthauza kuphunzitsa kumene kumatenga zaka zambiri.

Akulu Achikristu Amalanga Mofatsa

Akulu achikristu afunikanso kutsatira mfundo zimenezi. Monga abusa achikondi, amayesetsa kulimbikitsa nkhosa mwa kulangiza, kutsogolera, ndi kudzudzula pakafunikira kutero. Pochita zimenezo, amakumbukira cholinga chenicheni cha kulanga. (Aefeso 4:11, 12) Akanati cholinga chawo chizingokhala kukhaulitsa, bwenzi akumangom’patsa chilango munthu wolakwayo n’kumusiya osamusamala. Kulanga kotsatira mfundo za Mulungu kumafuna zambiri. Chikondi chimalimbikitsa akuluwo kupitirizabe kumuthandiza munthu wolakwayo. Popeza amamuganizira kwambiri, nthaŵi zambiri amakonza maulendo angapo okamulimbikitsa ndi kum’phunzitsa.

Potsatira langizo limene lili pa 2 Timoteo 2:25, 26, akulu amalangiza “mofatsa” ngakhale anthu amene savomera mwamsanga kulanga kwawo. Ndiyeno lembalo limafotokoza cholinga cha kulanga kuti: “Kapena Mulungu awapatse iwo chitembenuziro, kukazindikira choonadi, ndipo akadzipulumutse ku msampha wa Mdyerekezi.”

Nthaŵi zina kumakhala koyenera kuchotsa mumpingo anthu amene akungochita zoipa osalapa. (1 Timoteo 1:18-20) Ngakhale kuchotsa munthu mumpingo n’kulanga, osati kukhaulitsa. Nthaŵi ndi nthaŵi, akulu amayesetsa kukaonana ndi anthu ochotsedwa amene sakuchita zoipa. Panthaŵi yokawaonayo, akulu amatsatira tanthauzo lenileni la kulanga mwa kumufotokozera munthuyo zimene angachite kuti abwerere mumpingo wachikristu.

Yehova Ndiye Woweruza Wangwiro

Makolo, abusa achikristu, ndi anthu ena amene ali ndi ulamuliro wa m’Malemba wolanga sayenera kuona udindowo mopepuka. Sayenera kuweruza ena mowaona ngati sangakonzeke. Motero, kulanga kwawo sikuyenera kukhala ngati akubwezera kapena akukhaulitsa mwankhanza.

N’zoona kuti Baibulo limati Yehova adzapereka chilango chachikulu ndiponso chomaliza. Ndipotu, Malemba amanena kuti “kugwa m’manja a Mulungu wamoyo n’koopsa.” (Ahebri 10:31) Koma palibe munthu amene ayenera kudziyerekezera ndi Yehova pankhani imeneyi kapena pankhani zina. Ndipo palibe amene ayenera kuona kuti kugwera m’manja mwa kholo kapena mkulu wina wake mumpingo n’koopsa.

Yehova akamalanga amatha kuona mbali zonse mwangwiro. Anthu satha kuchita zimenezo. Mulungu angadziŵe mtima wa munthu ndi kuzindikira nthaŵi imene munthuyo wafika poti sangathenso kukonzeka ndipo adzafunika kulandira chilango chachikulu ndiponso chomaliza. Koma anthu sangathe kuweruza motero. N’chifukwa chake, pakafunika kulanga, anthu amene ali ndi ulamuliro nthaŵi zonse ayenera kuchita zimenezo n’cholinga chomuwongolera munthuyo.

Kumvera Kulanga kwa Yehova

Tonsefe timafunikira kulanga kapena kuti mwambo wa Yehova. (Miyambo 8:33) Inde, tiyenera kumafuna kulangidwa ndi Mawu a Mulungu. Tikamaphunzira Mawu a Mulungu, tingamvere kulanga kwa Yehova kwachindunji kudzera m’Malemba. (2 Timoteo 3:16, 17) Koma nthaŵi zina, tingalangidwe ndi Akristu anzathu. Kuzindikira cholinga chenicheni cha kulanga koteroko kudzatithandiza kumvera ndi mtima wonse.

Mtumwi Paulo anati: “Chilango chili chonse, pakuchitika, sichimveka chokondweretsa, komatu chowawa.” Ndiyeno anawonjezera kuti: “Koma chitatha, chipereka chipatso cha mtendere, kwa iwo ozoloweretsedwa nacho, ndicho cha chilungamo.” (Ahebri 12:11) Kulanga kwa Yehova kumasonyeza kuti amatikonda kwambiri. Kaya tikulangidwa kapena tikulanga ena, tizikumbukira cholinga cha kulanga kwa Mulungu ndi kumvera langizo lanzeru la m’Baibulo lakuti: “Gwira mwambo, osauleka; uusunge; pakuti ndiwo moyo wako.”​—Miyambo 4:13.

[Zithunzi patsamba 21]

Mulungu amapereka chilango poweruza anthu ochita zolakwa osalapa, osati kuwalanga kuti awongolere

[Zithunzi patsamba 22]

Chikondi chimalimbikitsa akulu kupatula nthaŵi kufufuza m’zofalitsa ndi kuthandiza olakwa

[Zithunzi patsamba 23]

Makolo moleza mtima ndiponso mwachikondi amalanga ‘m’chilangizo cha Ambuye’