Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kupirira Poyesedwa Kumalemekeza Yehova

Kupirira Poyesedwa Kumalemekeza Yehova

Kupirira Poyesedwa Kumalemekeza Yehova

“Ngati pochita zabwino, ndi kumvako zowawa mumapirira, kumeneko ndiko chisomo pa Mulungu.”​—1 PETRO 2:20.

1. Popeza kuti Akristu oona amafunitsitsa kukwaniritsa kudzipatulira kwawo, kodi ndi funso liti limene tiyenera kukambirana?

AKRISTU anadzipatulira kwa Yehova ndipo amafuna kuchita zimene iye amafuna. Kuti akwaniritse kudzipatulira kwawo, amayesetsa kutsatira mapazi a Yesu Kristu, Chitsanzo chawo, ndiponso kuchitira umboni choonadi. (Mateyu 16:24; Yohane 18:37; 1 Petro 2:21) Komabe, chifukwa cha chikhulupiriro chawo, Yesu ndi anthu ena okhulupirika anapereka miyoyo yawo nsembe ndi kufa monga ofera chikhulupiriro. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Akristu onse angayembekezere kufera chikhulupiriro chawo?

2. Kodi Akristu amaziona bwanji ziyeso ndi mavuto?

2 Ife monga Akristu, tikulimbikitsidwa kukhala okhulupirika mpaka imfa, osati kutanthauza kuti nthaŵi zonse tiyenera kufera chikhulupiriro chathu. (2 Timoteo 4:7; Chivumbulutso 2:10) Ngakhale kuti ndife okonzeka kuvutika ndipo ngati n’koyenera kufa chifukwa cha chikhulupiriro chathu, sizikutanthauza kuti timalakalaka zimenezi zitatichitikira. Sitisangalala tikamazunzidwa ndiponso tikamamva kuwawa kapena kuchititsidwa manyazi. Komabe, tingayembekezere ziyeso ndi chizunzo, choncho tiyenera kuganizira mofatsa zimene tingachite ngati zoterozo zitatichitikira.

Kukhulupirika Poyesedwa

3. Kodi ndi zitsanzo ziti za m’Baibulo zolimbana ndi chizunzo zimene mungafotokoze? (Onani bokosi lakuti, “Zimene Anachita Pozunzidwa,” patsamba lotsatira.)

3 M’Baibulo timapezamo nkhani zosiyanasiyana zosonyeza zimene atumiki a Mulungu akale anachita atakumana ndi mavuto amene anaika moyo wawo pangozi. Njira zosiyanasiyana zimene anatsatira n’zothandiza kwa Akristu masiku ano ngati atakumana ndi mavuto ofananawo. Taonani nkhani zimene zili m’bokosi lakuti “Zimene Anachita Pozunzidwa,” ndipo onani zimene mukuphunzirapo.

4. Kodi tinganene chiyani za mmene Yesu ndi atumiki ena okhulupirika anachitira pamene anali kuyesedwa?

4 Ngakhale kuti Yesu ndi atumiki ena okhulupirika a Mulungu anachita zinthu zosiyanasiyana atakumana ndi chizunzo mogwirizana ndi mmene zinthu zinalili panthaŵiyo, n’zachidziŵikire kuti sanaike dala pangozi miyoyo yawo. Akakhala kuti ali pangozi, ankachita zinthu molimba mtima koma mochenjera. (Mateyu 10:16, 23) Cholinga chawo chinali kupititsa patsogolo ntchito yolalikira ndi kukhalabe okhulupirika kwa Yehova. Zimene anachita panthaŵi zosiyanasiyana zimapereka chitsanzo kwa Akristu amene akukumana ndi ziyeso ndi chizunzo masiku ano.

5. Kodi ndi chizunzo chotani chimene chinabuka m’Malawi cha m’ma 1960, ndipo kodi Mboni zinachita chiyani?

5 Masiku anonso, anthu a Yehova akukumana ndi zinthu zovuta kwambiri ndiponso akusowa zinthu zina chifukwa cha nkhondo, ziletso, kapena chizunzo. Mwachitsanzo, m’zaka za m’ma 1960, Mboni za Yehova ku Malawi zinazunzidwa mwankhanza kwambiri. Nyumba za Ufumu zawo, nyumba zawo, chakudya, mabizinesi awo,​—pafupifupi chilichonse chimene anali nacho​—zinawonongedwa. Anamenyedwa ndiponso anawachitira zinthu zina zoopsa. Kodi abaleŵa anachita chiyani? Anthu mazana ambiri anathaŵa m’midzi yawo. Ambiri anathaŵira kuthengo, pamene ena anathaŵira ku dziko loyandikana nalo la Mozambique. Ngakhale kuti anthu ambiri okhulupirika anafa, ena anasankha kuthaŵa pamalo angozi, zimene zinali zothandiza malinga ndi mmene zinalilimo. Mwakuchita zimenezo, abalewo anatsatira chitsanzo cha Yesu ndi Paulo.

6. Ngakhale kuti Mboni za ku Malawi zinakumana ndi chizunzo choopsa, kodi sizinasiye kuchita chiyani?

6 Ngakhale kuti abale a ku Malawi anafunika kusamuka kapena kukabisala, anafufuza malangizo a gulu la Mulungu n’kuwatsatira ndipo anapitiriza ntchito zawo zachikristu mwakabisira monga momwe akanathera. Kodi n’chiyani chinachitika chifukwa cha zimenezo? Chiŵerengero cha ofalitsa Ufumu chinakwera kufika anthu 18,519 chiletso chisanayambe mu 1967. Ngakhale kuti chiletso chinalipobe ndipo anthu ambiri anali atathaŵira ku Mozambique, pofika chaka cha 1972 anachitira lipoti chiŵerengero chapamwamba cha ofalitsa chokwana 23,398. Pa avareji aliyense anathera maola opitirira 16 mu utumiki mwezi uliwonse. Mosakayikira, ntchito yawo inalemekezetsa Yehova, ndipo Yehova anadalitsa abale okhulupirika ameneŵa pa nthaŵi yamavuto imeneyo. *

7, 8. N’chifukwa chiyani ena sasamuka, ngakhale kuti akuvutika chifukwa cha chizunzo?

7 Komabe, m’mayiko amene chitsutso chikuyambitsa mavuto, abale ena angasankhe kusasamuka, ngakhale kuti angathe kusamuka. Kusamuka kungachepetseko mavuto ena, koma mosakayikira kungayambitsenso mavuto ena. Mwachitsanzo, kodi akasamuka angakapitirizebe kusonkhana ndi abale Achikristu kuti asadzipatule mwauzimu? Kodi angakathe kupitiriza kuchita zinthu zauzimu pamene akuyesetsa kuti akhazikike, mwina m’dziko lotukuka kapena m’dziko limene anthu angapeze zinthu zambiri zakuthupi?​—1 Timoteo 6:9.

8 Ena sasamuka chifukwa chodera nkhaŵa za moyo wauzimu wa abale awo. Amasankha kukhala ndi kulimbana ndi chizunzocho kuti apitirizebe kulalikira m’dera lawo ndiponso kuti alimbikitse olambira anzawo. (Afilipi 1:14) Mwakuchita zimenezi, ena mpaka athandiza kuwina milandu m’dziko lawo. *

9. Kodi ndi zinthu ziti zimene munthu ayenera kuziganizira ngati akufuna kukhala kapena kusamuka pa nthaŵi ya chizunzo?

9 Munthu amasankha yekha kukhala kapena kusamuka. Tiyenera kusankha titapemphera kwa Yehova kuti atitsogolere. Komabe, kaya tingasankhe kukhala kapena kusamuka, tiyenera kukumbukira mawu a mtumwi Paulo akuti: “Munthu aliyense wa ife adzadziŵerengera mlandu wake kwa Mulungu.” (Aroma 14:12) Monga taonera koyambirira, zimene Yehova akufuna n’zakuti mtumiki wake aliyense akhalebe wokhulupirika nthaŵi zonse. Ena mwa atumiki ake akukumana ndi ziyeso ndi chizunzo lerolino; ena angakumane nazo mtsogolo. Onse adzayesedwa m’njira zosiyanasiyana, ndipo wina asaganize kuti sangakumane ndi ziyeso ndi chizunzo. (Yohane 15:19, 20) Chifukwa chakuti ndife atumiki a Yehova odzipatulira, sitingapeŵe nkhani yayikulu yokhudza kuyeretsedwa kwa dzina la Yehova ndiponso nkhani yoti iye ndiye woyenera kulamulira.​—Ezekieli 38:23; Mateyu 6:9, 10.

“Musabwezere Munthu Aliyense Choipa Chosinthana ndi Choipa”

10. Kodi Yesu ndi atumwi anapereka chitsanzo chabwino chiti choti titsatire polimbana ndi mavuto ndi chitsutso?

10 Mfundo ina imene tingaphunzire pa zimene Yesu ndi atumwi anachita ali pamavuto ndi kusabwezera anthu amene akutizunza. Palibe pena paliponse m’Baibulo pamene pamasonyeza kuti Yesu kapena otsatira ake anapanga kagulu kolimbana ndi boma kapena kuchita zachiwawa kuti alimbane ndi amene amawazunza. Mosiyana ndi zimenezo, mtumwi Paulo analangiza Akristu kuti: “Musabwezere munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa. Musabwezere choipa, okondedwa, koma patukani pamkwiyo; pakuti kwalembedwa, kubwezera kuli kwanga, Ine ndidzabwezera, ati Ambuye.” Ndiponso, “musagonje kwa choipa, koma ndi chabwino gonjetsani choipa.”​—Aroma 12:17-21; Salmo 37:1-4; Miyambo 20:22.

11. Kodi wolemba mbiri wina anati Akristu oyambirira ankachita motani ndi boma?

11 Akristu oyambirira anatsatira malangizo ameneŵa. M’buku lake lakuti The Early Church and the World, wolemba mbiri yakale Cecil J. Cadoux anafotokoza mmene Akristu ankachitira ndi boma m’zaka za m’ma 30 mpaka m’ma 70 C.E. Iye analemba kuti: “Tilibe umboni wotsimikizika kuti Akristu panthaŵi imeneyi ankafuna kuthetsa chizunzo pochita ziwawa. Zimene ankachita kunali kungodzudzula olamulira awo mwamphamvu kapena kungothaŵa. Komabe zimene Akristu ankachita polimbana ndi chizunzo sizinkapitirira pa kukana mwamphamvu malamulo a boma amene amawaona kuti akusemphana ndi kumvera Kristu.”

12. N’chifukwa chiyani kupirira mavuto n’kwabwino kusiyana n’kubwezera?

12 Kodi kulolera kuzunzidwa mwanjira yoteroyo kumathandizadi? Kodi zimenezi sizingachititse anthu amene akufuna kuwapulula kuwadyera masuku pamutu? Kodi sikungakhale kwanzeru kudziteteza? Malinga n’kuona kwa anthu, zingakhaledi choncho. Komabe, chifukwa chakuti ndife atumiki a Yehova, timakhulupirira kuti kutsatira malangizo a Yehova pankhani iliyonse ndiyo njira yabwino. Timakumbukira mawu a Petro akuti: “Ngati pochita zabwino, ndi kumvako zowawa mumapirira, kumeneko ndiko chisomo pa Mulungu.” (1 Petro 2:20) Tili ndi chikhulupiriro kuti Yehova akudziŵa bwino lomwe vutolo ndipo sadzalola kuti lipitirire mpaka kalekale. Kodi tingatsimikizire bwanji zimenezo? Kwa anthu ake amene anali pa ukapolo ku Babulo, Yehova anawauza kuti: “Iye wokhudza inu, akhudza mwana wa m’diso [langa, NW].” (Zekariya 2:8) Kodi ndani amene angalolere kuti mwana wa m’diso lake akhudzidwe kwa nthaŵi yaitali? Yehova adzathandiza panthaŵi yoyenera. Zimenezo n’zosakayikitsa m’pang’onong’ono pomwe.​—2 Atesalonika 1:5-8.

13. N’chifukwa chiyani Yesu analolera kuti adani amugwire?

13 Pankhani imeneyi, Yesu ndiye chitsanzo chathu. Pamene analolera kuti adani ake amugwire m’munda wa Getsemane, sikuti sakanatha kudziteteza. Iye anauza wophunzira wake kuti: “Uganiza kuti sindingathe kupemphera Atate wanga, ndipo iye adzanditumizira tsopano lino mabungwe a angelo oposa khumi ndi aŵiri? Koma pakutero, malembo adzakwaniridwa bwanji, pakuti kuyenera chomwecho?” (Mateyu 26:53, 54) Yesu anali wofunitsitsa kukwaniritsa chifuno cha Yehova, moti anali wokonzeka kuvutika. Anadalira kwambiri mawu a mu salmo la ulosi la Davide akuti: “Simudzasiya moyo wanga kumanda. Simudzalola wokondedwa wanu avunde.” (Salmo 16:10) Patapita zaka, mtumwi Paulo pofotokoza za Yesu anati: “Chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira mtanda, nanyoza manyazi, nakhala pa dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.”​—Ahebri 12:2.

Chimwemwe Chobwera Chifukwa Choyeretsa Dzina la Yehova

14. Kodi n’chimwemwe chotani chimene chinalimbikitsa Yesu nthaŵi yonse imene amayesedwa?

14 Kodi n’chimwemwe chotani chimene Yesu amayembekezera chimene chinamulimbikitsa panthaŵi yonse ya chiyeso chake chosayerekezekacho? Mwa atumiki onse a Yehova, Yesu, Mwana wokondedwa wa Mulungu, ndiye anali mdani wamkulu wa Satana. Choncho, kukhulupirika kwa Yesu pamene anali kuyesedwa kukanapereka yankho lamphamvu koposa onse kwa Yehova lotsutsa chitonzo cha Satana. (Miyambo 27:11) Kodi mungayerekezere chimwemwe chimene Yesu anali nacho ataukitsidwa? Ayenera kuti anali wachimwemwe kwambiri atazindikira kuti wakwaniritsa udindo umene anapatsidwa monga munthu wangwiro potsimikizira kuti Yehova ndiye woyenera kulamulira ndiponso kuyeretsa dzina Lake. Kuwonjezera apo, kukhala ‘pa dzanja lamanja la Mulungu’ ndi ulemu wapadera kwambiri ndiponso ndi chinthu chimene chimabweretsa chimwemwe chachikulu kwa Yesuyo kuposa china chilichonse.​—Salmo 110:1, 2; 1 Timoteo 6:15, 16.

15, 16. Kodi ndi chizunzo chankhanza chotani chimene Mboni zinapirira ku msasa wa Sachsenhausen, ndipo chinawalimbitsa n’chiyani kuti apirire?

15 Akristunso amapeza chimwemwe akamagwira nawo ntchito yoyeretsa dzina la Yehova mwa kupirira ziyeso ndi chizunzo, pamene akutsatira chitsanzo cha Yesu. Chitsanzo chabwino kwambiri ndi cha Mboni zimene zinavutika koopsa mu msasa wa chibalo wankhanza kwambiri wa Sachsenhausen. Mbonizo zinapulumuka pa ulendo wopita kokaphedwa kumapeto kwa nkhondo yachiŵiri yapadziko lonse. Paulendowo, akaidi mazana ambiri anafa chifukwa cha nyengo yoipa, matenda, ndi njala kapena anaphedwa mwankhanza munsewu momwemo ndi asilikali a SS. Mboni zonse zokwana 230 zinapulumuka chifukwa zinkakhala pafupi wina ndi mzake n’kumathandizana ngakhale kuti zimenezi zinaika miyoyo yawo pangozi.

16 Kodi n’chiyani chinalimbitsa Mboni zimenezi kuti zipirire chizunzo choopsa chimenecho? Mbonizo zitangofika malo otetezeka, zinafotokoza chimwemwe chawo ndi kuthokoza Yehova m’chikalata chamutu wakuti “Maganizo a Mboni za Yehova 230 zochokera mayiko asanu ndi limodzi, zimene zinasonkhana m’nkhalango ina pafupi ndi Schwerin ku Mecklenburg.” M’chikalata chimenechi Mbonizo zinalemba kuti: “Nthaŵi yaitali yovuta ya mayesero yatha tsopano ndipo amene apulumuka, akukhala ngati achita kuchotsedwa m’ng’anjo yamoto, koma sakumveka n’komwe fungo la motowo. (Onani Danieli 3:27.) Ngakhale kuti akumana ndi mavuto otere, alimbikitsidwa ndi Yehova ndipo akuyembekezera mwachidwi malamulo atsopano ochokera kwa Mfumu kuti apititse patsogolo zolinga za Mulungu.” *

17. Kodi anthu a Mulungu akukumana ndi ziyeso zotani masiku ano?

17 Mofanana ndi Mboni 230 zokhulupirika zimenezo, ifenso chikhulupiriro chathu chingakhale chitayesedwa, ngakhale kuti ‘sitinakane kufikira mwazi.’ (Ahebri 12:4) Ndipo chiyeso chingabwere m’njira zosiyanasiyana. Kungakhale kusekedwa ndi anzanu a m’kalasi, kapena anzanu angakulimbikitseni kuti muchite chiwerewere ndi zinthu zina zoipa. Kuonjezera apo, nkhani monga kukana kuthiridwa magazi, kukwatira mwa Ambuye, kapena kulera ana kuti akhale okhulupirira m’banja losiyana zikhulupiriro nthaŵi zina kungabweretse mavuto aakulu ndi ziyeso.​—Machitidwe 15:29; 1 Akorinto 7:39; Aefeso 6:4; 1 Petro 3:1, 2.

18. Kodi tikutsimikiza bwanji kuti tikhoza kupirira ngakhale pa chiyeso chovuta kwambiri?

18 Komabe, kaya tikumane ndi chiyeso chotani, timadziŵa kuti timavutika chifukwa timaika Yehova ndi Ufumu wake patsogolo, ndipo timauona kukhala mwayi ndiponso timapeza chimwemwe pochita zimenezo. Timalimbikitsidwa ndi mawu a Petro akuti: “Mukatonzedwa pa dzina la Kristu, odala inu; pakuti Mzimu wa ulemerero, ndi Mzimu wa Mulungu apuma pa inu.” (1 Petro 4:14) Mphamvu ya mzimu wa Yehova imatipatsa nyonga kuti tipirire ngakhale pamavuto aakulu, zimene zimachititsa kuti Yehovayo alemekezedwe ndi kutamandidwa.​—2 Akorinto 4:7; Aefeso 3:16; Afilipi 4:13.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Zimene zinachitika m’ma 1960 zinali chiyambi chabe cha chizunzo ndi kuphedwa mwankhanza kumene Mboni za m’Malawi zinafunika kupirira kwa zaka pafupifupi makumi atatu. Kuti mumve nkhani yonse, onani bulosha lakuti Mboni za Yehova m’Malaŵi​—Nkhani ya Kukhulupirika Kwawo, kapena 1999 Yearbook of Jehovah’s Witnesses, masamba 171 mpaka 212.

^ ndime 8 Onani nkhani yakuti, “Khoti Lalikulu Lagamula Kuti Kulambira Koona Kupitirire ‘M’dziko la ku Ararati’” mu Nsanja ya Olonda ya April 1, 2003, masamba 11 mpaka 14.

^ ndime 16 Kuti muone chikalata chonse, onani buku la 1974 Yearbook of Jehovah’s Witnesses, masamba 208 mpaka 209. Nkhani ya munthu amene anapulumuka nawo pa ulendo umenewu mungaipeze mu Nsanja ya Olonda ya January 1, 1998, masamba 25 mpaka 29.

Kodi Mungafotokoze?

• Kodi Akristu amaona bwanji kuvutika ndi chizunzo?

• Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene Yesu ndi anthu ena okhulupirika anachita pa nthaŵi ya ziyeso?

• N’chifukwa chiyani n’kwanzeru kusabwezera pamene tikuzunzidwa?

• Kodi n’chimwemwe chotani chimene Yesu ankayembekezera chimene chinamulimbikitsa pa nthaŵi ya ziyeso, ndipo tikuphunzirapo chiyani pa zimenezi?

[Mafunso]

[Bokosi/​Zithunzi patsamba 15]

Zimene Anachita Pozunzidwa

• Mngelo anauza Yosefe ndi Mariya kuti atenge Yesu ali kamwana ndi kuthaŵira ku Igupto, asilikali a Herode asanafike ku Betelehemu kudzapha ana onse aamuna a zaka ziŵiri kapena kucheperapo.​—Mateyu 2:13-16.

• Nthaŵi zambiri pamene Yesu ankachita utumiki wake, adani ake ankafuna kumupha chifukwa ankachita umboni mwamphamvu. Nthaŵi zonsezo Yesu anawapeŵa.​—Mateyu 21:45, 46; Luka 4:28-30; Yohane 8:57-59.

• Asilikali ndi akuluakulu ena atabwera m’munda wa Getsemane kuti adzagwire Yesu, anadzizindikiritsa yekha, ndipo kaŵiri konse anawauza kuti: “Ndine.” Analetsa ngakhale omutsatira ake kuti alimbane nawo ndipo odzamugwirawo anamutenga.​—Yohane 18:3-12.

• Ku Yerusalemu, Petro ndi ena anamangidwa, kumenyedwa, ndi kulamulidwa kuti asiye kulankhula za Yesu. Koma atangowamasula, “anapita . . . , ndipo masiku onse, m’Kachisi ndi m’nyumba, sanaleka kuphunzitsa ndi kulalikira Kristu Yesu.”​—Machitidwe 5:40-42.

• Saulo, amene anadzakhala mtumwi Paulo, atadziŵa zimene Ayuda ku Damasiko anali atakonza zoti amuphe, abale anamuika mu mtanga ndi kum’tulutsira palinga usiku, ndipo anathaŵa.​—Machitidwe 9:22-25.

• Patapita zaka, Paulo anasankha kuchita apilo kwa Kaisara, ngakhale kuti Kazembe Festo ndi Mfumu Agripa anapeza kuti “sanachita kanthu koyenera imfa, kapena nsinga.”​—Machitidwe 25:10-12, 24-27; 26:30-32.

[Zithunzi pamasamba 16, 17]

Mboni zokhulupirika mazana ambiri za ku Malawi zinapitiriza kugwira ntchito ya Ufumu mwachimwemwe ngakhale kuti zinakakamizika kuthaŵa m’dziko lawo chifukwa cha chizunzo

[Zithunzi patsamba 17]

Chimwemwe chobwera chifukwa choyeretsa dzina la Yehova chinalimbikitsa anthu okhulupirika aŵa paulendo wopita kokaphedwa ndi m’misasa yachibalo, nthaŵi ya chizunzo cha Nazi

[Mawu a Chithunzi]

Ulendo wopita kokaphedwa: KZ-Gedenkstätte Dachau, courtesy of the USHMM Photo Archives

[Zithunzi patsamba 18]

Ziyeso ndi mavuto zingabwere m’njira zosiyanasiyana