Kuzunzika Chifukwa cha Chilungamo
Kuzunzika Chifukwa cha Chilungamo
“Odala ali akuzunzidwa chifukwa cha chilungamo.”—Mateyu 5:10.
1. N’chifukwa chiyani Yesu anakaonekera kwa Pontiyo Pilato, ndipo kodi Yesu ananena chiyani?
“NDINABADWIRA ichi Ine, ndipo ndinadzera ichi kudza ku dziko lapansi, kuti ndikachite umboni ndi choonadi.” (Yohane 18:37) Yesu analankhula mawu ameneŵa pamene anaonekera kwa Pontiyo Pilato, Kazembe wa Roma ku Yudeya. Yesu sanachite kufuna kapena kuitanidwa kuti akaonane ndi Pilato. Koma iye anapita kwa Pilato chifukwa atsogoleri achipembedzo a Ayuda anali kumuimba mlandu wabodza womwe chilango chake chinali imfa.—Yohane 18:29-31.
2. Kodi Yesu anachita zotani, ndipo kodi zotsatirapo zake zinali zotani?
2 Yesu ankadziŵa bwino kwambiri kuti Pilato anali ndi mphamvu zom’masula kapena kumupha. (Yohane 19:10) Koma zimenezo sizinam’lepheretse kulankhula molimba mtima za Ufumu kwa Pilato. Yesu anagwiritsa ntchito mpata umenewo kuchitira umboni kwa munthu wokhala ndi udindo waukulu m’boma m’deralo, ngakhale kuti moyo wake unali pangozi. Ngakhale kuti anachitira umboni chotero, Yesu anatsutsidwa ndi kuphedwa imfa yopweteka yofera chikhulupiriro pa mtengo wozunzirapo.—Mateyu 27:24-26; Marko 15:15; Luka 23:24, 25; Yohane 19:13-16.
Wochitira Umboni Kapena Wofera Chikhulupiriro?
3. Kodi mawu a Chigiriki amene amamasuliridwa kuti “kufera chikhulupiriro” ankatanthauza chiyani m’nthaŵi za Baibulo, nanga masiku ano amatanthauza chiyani?
3 Kwa anthu mbiri masiku ano, munthu wofera chikhulupiriro amamuona ngati munthu wochita zinthu monyanyira. Amene amafera chikhulupiriro chawo, makamaka chikhulupiriro cha chipembedzo, nthaŵi zambiri amawakayikira kuti ndi zigaŵenga kapena ndi anthu oopsa m’dziko. Komatu, mawu a Chigiriki amene amamasuliridwa kuti wofera chikhulupiriro (marʹtys), m’nthaŵi za Baibulo ankatanthauza “mboni,” munthu amene amapereka umboni, mwina m’khoti, pofotokoza zoona zimene iye amakhulupirira. Patapita nthaŵi m’pamene mawu ameneŵa anayamba kutanthauza “munthu amene amapereka moyo wake chifukwa chochitira umboni,” kapena kuchitira umboni popereka moyo wake.
4. Kodi Yesu anali wofera chikhulupiriro m’lingaliro liti?
4 Yesu anali wofera chikhulupiriro m’lingaliro Yohane 2:23; 8:30) Anthu ambiri, makamaka atsogoleri achipembedzo, anakwiya kwambiri. Yesu anauza abale ake osakhulupirira kuti: “Dziko lapansi silingathe kudana ndi inu; koma Ine lindida popeza Ine ndilichitira umboni, kuti ntchito zake zili zoipa.” (Yohane 7:7) Chifukwa chakuti anachitira umboni choonadi, atsogoleri a mtunduwo anakwiya ndi Yesu ndipo pomalizira pake anamupha. Kunena zoona, Yesu analidi “mboni (marʹtys) yokhulupirika ndi yoona.”—Chivumbulutso 3:14.
loyamba la mawuwa. Mogwirizana ndi zimene anauza Pilato, anabwera ‘kudzachita umboni ndi choonadi.’ Anthu ena anavomereza ulaliki wake pamene ena anaukana. Ena mwa anthu wamba anakhudzidwa kwambiri ndi zimene anamva ndi kuona ndipo anakhulupirira Yesu. (“Adzada Inu”
5. Kodi Yesu ananena chiyani za chizunzo koyambirira kwa utumiki wake?
5 Yesu sanangokumana ndi chizunzo iye mwiniyo basi, koma ananenanso kuti ophunzira ake adzakumananso ndi chizunzo. Koyambirira kwa utumiki wake, Yesu anauza omvera ake pa Ulaliki wa pa Phiri kuti: “Odala ali akuzunzidwa chifukwa cha chilungamo, chifukwa uli wawo Ufumu wa Kumwamba. Odala muli inu mmene adzanyazitsa inu, nadzazunza inu, nadzakunenerani monama zoipa zilizonse chifukwa cha Ine. Sekerani, sangalalani, chifukwa mphotho yanu ndi yaikulu m’Mwamba.”—Mateyu 5:10-12.
6. Kodi Yesu anapereka chenjezo lotani pamene ankatumiza atumwi ake khumi ndi aŵiri?
6 Kenako, potumiza atumwi ake khumi ndi aŵiri, Yesu anawauza kuti: “Koma chenjerani ndi anthu; pakuti adzakuperekani inu kwa akulu a mlandu, nadzakukwapulani inu m’masunagoge mwawo; ndiponso adzamuka nanu kwa akazembe ndi mafumu chifukwa cha Ine, kukhala mboni ya kwa iwo, ndi kwa anthu akunja.” Koma amene anazunza ophunzira a Yesu sanali akuluakulu achipembedzo okha. Yesu ananenanso kuti: “Mbale adzapereka mbale wake kuimfa, ndi atate mwana wake, ndipo ana adzatsutsa akuwabala, nadzawafetsa iwo. Ndipo adzada inu anthu Mateyu 10:17, 18, 21, 22) Mbiri ya Akristu a m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino ikusonyeza kuti zimenezo zinachitikadi.
onse chifukwa cha dzina langa; koma iye wakupirira kufikira chimaliziro, iyeyu adzapulumutsidwa.” (Nkhani ya Kupirira Mokhulupirika
7. N’chiyani chinachititsa kuti Stefano akhale wofera chikhulupiriro?
7 Patapita nthaŵi yochepa Yesu atafa, Stefano anakhala Mkristu woyamba kufa chifukwa chochitira umboni choonadi. Anali “wodzala ndi chisomo ndi mphamvu, [ndipo] anachita zozizwa ndi zizindikiro zazikulu mwa anthu.” Adani ake achipembedzo “sanathe kuilaka nzeru ndi Mzimu amene analankhula naye.” (Machitidwe 6:8, 10) Chifukwa cha nsanje, anatengera Stefano ku bwalo la Sanihedirini, khoti lalikulu la Ayuda, kumene anakakumana ndi omuimba milandu abodza ndipo anapereka umboni wamphamvu. Komabe, pomalizira pake Stefano, mboni yokhulupirika, anaphedwa ndi adani ake.—Machitidwe 7:59, 60.
8. Kodi ophunzira ku Yerusalemu anachita chiyani pamene anayamba kuzunzidwa Stefano atamwalira?
8 Stefano ataphedwa, “kunayamba kuzunza kwakukulu pa Mpingo unali m’Yerusalemu; ndipo anabalalitsidwa onse m’mayiko a Yudeya ndi Samariya, koma osati atumwi ayi.” (Machitidwe 8:1) Kodi chizunzo chinalepheretsa ntchito yolalikira ya Akristu? Ayi, chifukwa nkhaniyo imatiuza kuti: “Iwo akubalalitsidwa anapitapita nalalikira mawuwo.” (Machitidwe 8:4) Ayenera kuti anamva ngati mmene mtumwi Petro anamvera poyambirira pamene ananena kuti: “Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.” (Machitidwe 5:29) Ngakhale kuti panali chizunzo, ophunzira okhulupirika ndi olimba mtima amenewo anagwirabe ntchito yochitira umboni choonadi mwakhama, ngakhale kuti ankadziŵa kuti kuchita zimenezo kukanawabweretsera mavuto aakulu.—Machitidwe 11:19-21.
9. Kodi ndi chizunzo chotani chimene otsatira a Yesu anapitiriza kukumana nacho?
9 Kunena zoona, chizunzo chinapitirizabe. Poyamba, tikumva kuti Saulo, munthu amene anavomereza ndi kuonerera kuphedwa kwa Stefano, “wosaleka kupumira pa akuphunzira a Ambuye kuwopsa ndi kupha, anamka kwa mkulu wa ansembe, napempha kwa iye akalata akumka nawo ku Damasiko kumasunagoge, kuti akapeza ena otsata Njirayo, amuna ndi akazi, akawatenge kudza nawo omangidwa ku Yerusalemu.” (Machitidwe 9:1, 2) Kenako, pafupifupi chaka cha 44 C.E., “Herode mfumu anathira manja ena a m’Eklesia kuwachitira zoipa. Ndipo adapha ndi lupanga Yakobo mbale wa Yohane.”—Machitidwe 12:1, 2.
10. Kodi timapeza nkhani zotani za chizunzo m’buku la Machitidwe ndi la Chivumbulutso?
10 Buku lonse la Machitidwe lili ndi nkhani zosaiŵalika za ziyeso, kuikidwa m’ndende, ndi chizunzo chimene anthu okhulupirika ngati Paulo, amene kale anali wozunza asanakhale mtumwi, anapirira. Paulo ayenera kuti anaphedwa chifukwa cha chikhulupiriro chake molamulidwa ndi Nero, Mfumu ya Roma, pafupifupi chaka cha 65 C.E. (2 Akorinto 11:23-27; 2 Timoteo 4:6-8) Pomalizira pake, m’buku la Chivumbulutso, limene linalembedwa cha kumapeto kwa zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino, timaŵerenga kuti mtumwi Yohane wachikulire anakamuika pachilumba cha Patmo, kumene anali kulangirako anthu, “chifukwa cha mawu a Mulungu ndi umboni wa Yesu.” Buku la Chivumbulutso limatchulanso za “Antipa, mboni yanga, wokhulupirika wanga, amene anaphedwa” ku Pergamo.—Chivumbulutso 1:9; 2:13.
11. Kodi moyo wa Akristu oyambirira unasonyeza bwanji kuti mawu a Yesu anali oona pa nkhani ya chizunzo?
11 Zonsezi zinatsimikizira mawu a Yesu kwa atumwi ake kuti: “Ngati anandilondalonda Ine, adzakulondalondani inunso.” (Yohane 15:20) Akristu okhulupirika oyambirira anali okonzeka kukumana ndi chiyeso chachikulu kuposa zonse chomwe ndi imfa—kaya kuphedwa mwa kuzunzidwa, kuponyedwa ku nyama zolusa kapena m’njira zina—kuti achite ntchito imene analamulidwa ndi Ambuye Yesu Kristu. Iye anati: “Mudzakhala mboni zanga m’Yerusalemu, ndi m’Yudeya lonse, ndi m’Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko.”—Machitidwe 1:8.
12. N’chifukwa chiyani kuzunzidwa kwa Akristu si chinthu chomwe chinangochitika kale lokha?
12 Ngati munthu angaganize kuti chizunzo chankhanza choterocho chinachitika kwa otsatira a Yesu akale okha, ndiye kuti akulakwitsa kwambiri. Paulo, amene anapirira mavuto ambiri ngati mmene taonera, analemba kuti: “Onse akufuna kukhala opembedza m’moyo mwa Kristu Yesu, adzamva mazunzo.” (2 Timoteo 3:12) Pokambapo za chizunzo, Petro anati: “Pakuti kudzachita ichi mwaitanidwa; pakutinso Kristu anamva zowawa m’malo mwanu, nakusiyirani chitsanzo kuti mukalondole mapazi ake.” (1 Petro 2:21) Kuyambira nthaŵi imeneyo mpaka “masiku otsiriza” a dongosolo la zinthu lino, anthu a Yehova akupitiriza kudedwa ndi kuchitiridwa nkhanza. (2 Timoteo 3:1) Mboni za Yehova padziko lonse nthaŵi zina zazunzidwapo monga munthu payekha ndiponso monga gulu m’maulamuliro opondereza ndi m’maboma a demokalase.
N’chifukwa Chiyani Amadedwa ndi Kuzunzidwa?
13. Kodi n’chiyani chimene atumiki a Yehova amasiku ano ayenera kukumbukira nthaŵi zonse za chizunzo?
13 Ngakhale kuti ambirife masiku ano tili ndi ufulu wokulirapo wolalikira ndi kusonkhana mwamtendere, tizikumbukira zimene Baibulo limatikumbutsa kuti, “maonekedwe a dziko ili apita [“akusintha,” NW].” (1 Akorinto 7:31) Zinthu zikhoza kusintha mosayembekezeka moti ngati sitikonzekeretsa maganizo athu, mtima wathu, komanso kukhala okonzeka mwauzimu tikhoza kukhumudwa mosavuta. Kodi tingachite chiyani kuti tidziteteze? Njira yabwino kwambiri yodzitetezera ndi kukumbukira nthaŵi zonse chifukwa chimene Akristu okonda mtendere ndi omvera malamulo amadedwa ndi kuzunzidwa.
14. Kodi Petro ananena kuti n’chifukwa chiyani Akristu ankazunzidwa?
14 Mtumwi Petro analankhulapo pa nkhani imeneyi m’kalata yake yoyamba, imene analemba cha mu 62 mpaka 64 C.E. Panthaŵiyo Akristu mu ufumu wonse wa Roma ankakumana ndi ziyeso ndi chizunzo. Iye anati: “Okondedwa, musazizwe ndi mayesedwe amoto adakugwerani inu akhale chakukuyesani, ngati chinthu chachilendo chachitika nanu.” Pofotokoza zimene amatanthauza, Petro anapitiriza kuti: “Asamve zowawa wina wa inu ngati wambanda, kapena mbala, kapena wochita zoipa, kapena ngati wodudukira; koma akamva zowawa ngati Mkristu asachite manyazi; koma alemekeze Mulungu m’dzina ili.” Petro anafotokoza kuti anali kuvutika chifukwa chakuti anali Akristu, osati chifukwa chakuti anali atachita khalidwe linalake loipa. Akanakhala kuti ankachita nawo “kusefukira komwe kwa chitayiko” mofanana ndi anthu omwe ankakhala nawo, anthuwo akanawalandira. Koma mfundo inali yakuti, ankazunzika chifukwa anayesetsa kukwaniritsa udindo wawo monga otsatira Kristu. Zilinso chimodzimodzi ndi Akristu oona masiku ano.—1 Petro 4:4, 12, 15, 16.
15. Ngakhale kuti Mboni za Yehova ndi anthu abwino, kodi n’chiyani chimene anthu amawachitira?
15 M’madera ambiri padziko lapansi, Mboni za Yehova zimalemekezedwa chifukwa chogwirizana ndi kuchitira zinthu pamodzi kumene zimasonyeza pa misonkhano yawo yachigawo ndi pa ntchito zawo zomanga. Zimalemekezedwanso chifukwa cha kuona mtima ndi kudzipereka kwawo, chifukwa cha chitsanzo chabwino chimene zimasonyeza pa khalidwe ndi moyo wabanja, ndiponso chifukwa cha kaonekedwe ndi kavalidwe kawo kabwino. * Koma, pamene nkhani ino imalembedwa, n’kuti ntchito yawo ili yoletsedwa kapena kuponderezedwa m’mayiko osachepera 28 ndipo Mboni zambiri zikumenyedwa ndi kulandidwa katundu chifukwa cha chikhulupiriro chawo. N’chifukwa chiyani Mboni za Yehova zomwe zimadziŵika chifukwa cha khalidwe labwino zikuletsedwa ndi kuponderezedwa? Ndipo n’chifukwa chiyani Mulungu amalola zimenezi?
16. Kodi n’chifukwa chachikulu chiti chimene Mulungu amalolera anthu ake kuzunzika?
16 Poyamba, tiyeni tizikumbukira mawu opezeka pa Miyambo 27:11 omwe amati: “Mwananga, khala wanzeru, nukondweretse mtima wanga; kuti ndimuyankhe yemwe anditonza.” Zoonadi, n’chifukwa cha nkhani ya ulamuliro wachilengedwe chonse imene inayamba kalekale. Ngakhale kuti pali umboni wochuluka umene wasonyezedwa ndi anthu amene akhala okhulupirika kwa Yehova kwa zaka mazana ambiri, Satana sanasiyebe kutonza Yehova ngati mmene anachitira m’masiku a munthu wolungama Yobu. (Yobu 1:9-11; 2:4, 5) Tsopano pamene Ufumu wa Mulungu wakhazikitsidwa, umene uli ndi nzika zokhulupirika ndi owuimira padziko lonse lapansi, mosakayikira Satana ali pakalikiliki kuyesetsa komaliza kufuna kusonyeza kuti zimene ananena n’zoona. Kodi anthu ameneŵa adzakhala okhulupirikabe kwa Mulungu ngakhale atakumana ndi chitsutso ndi mavuto alionse? Limeneli ndi funso limene mtumiki wa Yehova aliyense ayenera kuyankha payekha.—Chivumbulutso 12:12, 17.
17. Kodi Yesu anatanthauzanji ponena kuti “kudzakhala kwa inu ngati umboni”?
17 Pouza ophunzira ake zinthu zimene zidzachitike pa “mathedwe a nthaŵi ya pansi pano,” Yesu anasonyeza chifukwa china chimene Yehova amalolera kuti atumiki ake akumane ndi chizunzo. Iye anawauza kuti: ‘Adzamuka nanu kwa mafumu ndi akazembe, chifukwa cha dzina langa. Kudzakhala kwa inu ngati umboni.’ (Mateyu 24:3, 9; Luka 21:12, 13) Yesu mwiniyo anachitira umboni kwa Herode ndi Pontiyo Pilato. Mtumwi Paulo nayenso ‘anamuka naye kwa mafumu ndi akazembe.’ Motsogozedwa ndi Ambuye Yesu Kristu, Paulo anafuna kuchitira umboni kwa wolamulira wamphamvu kwambiri mu nthaŵi yake pamene ananena kuti: “Nditulukira [“Ndikachita apilo,” NW] kwa Kaisara.” (Machitidwe 23:11; 25:8-12) Lerolinonso, nthaŵi ya ziyeso yachititsa kuti umboni wabwino uperekedwe kwa akuluakulu aboma ndi anthu wamba. *
18, 19. (a) Kodi kulimbana ndi ziyeso kungatithandize bwanji? (b) Kodi tikambirana mafunso ati mu nkhani yotsatira?
18 Pomaliza, kulimbana ndi ziyeso ndi masautso kungatithandize patokha. Motani? Wophunzira Yakobo anakumbutsa Akristu anzake kuti: “Muchiyese chimwemwe chokha, abale anga, m’mene mukugwa m’mayesero amitundumitundu; pozindikira kuti chiyesedwe cha chikhulupiriro chanu chichita chipiriro.” Inde, chizunzo chingalimbitse chikhulupiriro chathu ndi kupirira kwathu. Motero, sitiopa kukumana ndi chizunzo, ndiponso sitichizemba kapena kuchithetsa potsata njira zomwe si za m’malemba. M’malomwake, timatsatira malangizo a Yakobo akuti: “Chipiriro chikhale nayo ntchito yake yangwiro, kuti mukakhale angwiro ndi opanda chilema, osasoŵa kanthu konse.”—Yakobo 1:2-4.
19 Ngakhale kuti Mawu a Mulungu amatithandiza kumvetsa chifukwa chimene atumiki okhulupirika a Mulungu akuzunzidwira ndiponso chifukwa chimene Yehova walolera kuti azivutika, zimenezi kwenikweni sizichititsa chizunzo kukhala chosavuta kupirira. Kodi n’chiyani chingatilimbitse kuti tipirire? Kodi tingachite chiyani tikakumana ndi chizunzo? Mu nkhani yotsatira tikambirana mayankho a mafunso ofunika ameneŵa.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 15 Onani Nsanja ya Olonda ya December 15, 1995, masamba 27 mpaka 29; April 15, 1994, masamba 16 mpaka 17; ndi Galamukani! ya January 8, 1994, masamba 21 mpaka 28.
Kodi Mungafotokoze?
• Kodi Yesu anali wofera chikhulupiriro m’lingaliro liti?
• Kodi chizunzo chinawakhudza motani Akristu a m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino?
• Monga anafotokozera Petro, n’chifukwa chiyani Akristu ankazunzidwa?
• Kodi Yehova amalola kuti atumiki ake azikumana ndi chizunzo pa zifukwa ziti?
[Mafunso]
[Zithunzi pamasamba 10, 11]
Akristu a m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino anavutika chifukwa anali Akristu osati chifukwa chakuti anali atachita khalidwe linalake loipa
PAULO
YOHANE
ANTIPA
YAKOBO
STEFANO