Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Nkhani Imene Imalimbikitsa Chikhulupiriro Komanso Kulimba Mtima Mboni za Yehova ku Ukraine

Nkhani Imene Imalimbikitsa Chikhulupiriro Komanso Kulimba Mtima Mboni za Yehova ku Ukraine

Nkhani Imene Imalimbikitsa Chikhulupiriro Komanso Kulimba Mtima Mboni za Yehova ku Ukraine

MOFANANA ndi mmene Akristu anazunzidwira m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino, anthu a Mulungu masiku ano nawonso azunzidwa. (Mateyu 10:22; Yohane 15:20) Ndi m’madera ochepa okha mmene mwakhala chizunzo kwa nthaŵi yaitali kuposa ku Ukraine, kumene ntchito yolalikira za Ufumu inali yoletsedwa kwa zaka 52.

Buku la 2002 Yearbook of Jehovah’s Witnesses linafotokoza nkhani ya anthu a Mulungu m’dziko limenelo. Ndi nkhani yofotokoza za chikhulupiriro, kulimba mtima, ndi kupirira kwa anthu amene anali pamavuto oopsa. Zotsatirazi ndi ndemanga zosonyeza kuyamikira zimene ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Ukraine inalandira:

“Ndinalephera kupirira mpaka ndinalira pamene ndimaŵerenga za ntchito yanu ku Ukraine. Ndikufuna ndikudziŵitseni kuti ndalimbikitsidwa kwambiri chifukwa cha chitsanzo chanu cha changu ndi chikhulupiriro cholimba. Ndikuona kuti ndi mwayi wapadera kukhala m’banja limodzi lauzimu ndi inuyo. Ndikukuthokozani kwambiri kuchokera pansi pa mtima wanga.”​—Andrée, wa ku France.

“Ndikusowa mawu oti ndifotokoze m’mene ndikukuyamikirirani, inu ndiponso Yehova, chifukwa cha zinthu zosiyanasiyana zimene zinachitikira abale amene anathera nthaŵi ya moyo wawo imene anali ndi mphamvu m’ndende ndi m’misasa yachibalo. Ndachita chidwi kwambiri ndi kulimba mtima kwawo. Ngakhale kuti ndakhala Mboni kwa zaka 27, ndikhozabe kuphunzira kwa abale ndi alongo amenewo. Analimbitsa chikhulupiriro changa mwa Atate wathu wakumwamba, Yehova.”​—Vera, wa ku dziko limene kale linali Yugoslavia.

“Ndikulemba kalata ino mwachimwemwe chifukwa cha chitsanzo chanu chabwino cha kupirira ndi kukhulupirika kwa zaka zonse zimene munali kuzunzidwa. Kudalira kwanu Yehova ndi mtima wonse komanso kutsimikiza mtima kwanu kuti mukhalebe wokhulupirika kwatichititsa kuti tikulemekezeni. Kuonjezera apo, kudzichepetsa kwanu pokumana ndi mayesero kwalimbitsa chikhulupiriro changa choti Yehova sataya anthu ake. Chifukwa cha chitsanzo chanu chabwino cha kulimba mtima, kusasunthika, ndi kupirira, tikhoza kumalimbana ndi timavuto tathu tochepa mosavuta.”​—Tuteirihia, wa ku French Polynesia.

“Ndinakhudzidwa mtima kwambiri ndi zimene zinakuchitikirani, zomwe n’zolimbikitsa kwambiri. Ndinaona kuti ndi mwayi wapadera kukhala nawo m’gulu la anthu okhulupirika, ogwirizana oterowo, otsogozedwa ndi Atate achikondi ndiponso odziŵa kusamala, amene amatipatsa mphamvu pa nthaŵi yoyenera. Ndinamva chisoni kuti atumiki a Yehova olimba mtima ndi achangu ambiri anazunzika koopsa ndipo ena anataya ngakhale miyoyo yawo. Komabe ndinasangalala chifukwa kulimba mtima ndi changu chawocho zinathandiza kuti anthu ambiri aphunzire choonadi ndiponso am’dziŵe Atate wathu wachikondi.”​—Colette, wa ku Netherlands.

“Ine ndi mkazi wanga tinaona kuti tifunika kukulemberani kalata basi kuti tikudziŵitseni kuti mitima yathu inakhudzidwa pamene timaŵerenga nkhani ya ku Ukraine. Abale okhulupirikanu mwasonyeza chitsanzo chabwino kwambiri cha kupirira pamavuto oopsa kwa nthaŵi yaitali. Mogwirizana ndi mawu amene ali pa Miyambo 27:11, Yehova ayenera kukhala wokondwa kwambiri podziŵa kuti abale ambiri okhulupirika a ku Ukraine akhalabe osasunthika mosasamala kanthu za zinthu zonse zoipa zimene M’dyerekezi amachita.”​—Alan, wa ku Australia.

“M’maso mwanga munadzaza misozi pamene ndimaŵerenga za abale a ku Ukraine. Anapirira zinthu zambiri​—kukhala m’ndende zaka zambiri, kuzunzidwa, kuponderezedwa, ndi kulekanitsidwa ndi mabanja awo. Ndikufuna kuuza abale onse amene akutumikirabe m’mipingo mwanu kuti ndimawakonda ndi kuwalemekeza kwambiri. Ndine wosangalala kwambiri chifukwa cha kulimba mtima ndi kusasunthika kwawo. Ndikudziŵa kuti mzimu wa Yehova ndi umene unawapatsa mphamvu. Yehova ali nafe pafupi, ndipo amafuna kutithandiza.”​—Sergei, wa ku Russia.

“Abale ndi alongo ambiri mu mpingo wathu akhala akulankhula za inu. Ndinudi ofunika kwambiri. Ndine wosangalala kwambiri pokhala nawo m’banja lauzimu lalikulu chotero.”​—Yeunhee, wa ku South Korea.

“Ndakhudzidwa kwambiri ndi nkhani ya kukhulupirika kwanu, kupirira, ndi kukonda Yehova ndi Ufumu wake mosasunthika. Nthaŵi zina timaiwala kuyamikira ufulu umene tili nawo ndi chakudya chauzimu chochuluka chimene Yehova amatipatsa. Koma inu simunachite zimenezo. Chitsanzo chanu cha chikhulupiriro chikutithandiza kuzindikira kuti ngati tili ndi unansi wabwino ndi Mulungu wathu, adzatipatsa mphamvu zimene timafunikira kuti tithe kulimbana ndi mayesero osiyanasiyana.”​—Paulo, wa ku Brazil.

“Ndinali ndi mwayi woŵerenga zimene zinakuchitikirani. Zinandikhudza kwambiri, makamaka nkhani yokhudza mtima ya Mlongo Lydia Kurdas. Mlongo ameneyu anandikhudza mtima kwambiri.”​—Nidia, wa ku Costa Rica.

“Chikhulupiriro changa mwa Yehova chinalimba. Chinthu chimodzi chimene sindidzaiwala ndi nkhani yokhudza nthaŵi imene ena anayamba kukayikira anthu amene amatsogolera gulu. Zinandiphunzitsa kuti sindiyenera kukayikira abale amene akutsogolera gulu. Zikomo kwambiri! Chakudya chauzimu chimenechi n’chothandiza kwambiri mtima wa munthu ndipo chimatithandiza kukonzekereratu nthaŵi imene chikhulupiriro chathu chingayesedwe.”​—Leticia, wa ku United States.

“Kwa ofalitsa ambiri, aka kanali koyamba kuti aŵerenge za ntchito ya abale athu a ku Ukraine. Kwathu kuno abale analimbikitsidwa. Ambiri, makamaka achinyamata, awonjezera zimene amachita mu utumiki. Ena akutumikira monga apainiya okhazikika kapena othandiza. Onse analimbikitsidwa ndi nkhani za abale ndi alongo amene anatumikira Yehova panthaŵi ya chiletso.”​—Komiti ya utumiki ya mpingo wina ku Ukraine.

Kukhulupirika kwa abale athu a ku Ukraine kwalimbikitsadi anthu a Yehova padziko lonse. Zoonadi, kuŵerenga nkhani zokhudza mtima zoterozo ndi njira yabwino kwambiri yolimbitsira chikhulupiriro ndi kupirira kwathu m’masiku ovuta ano.​—Ahebri 12:1.