Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Pali Mafunso Ambiri Koma Mayankho Ogwira Mtima ndi Ochepa

Pali Mafunso Ambiri Koma Mayankho Ogwira Mtima ndi Ochepa

Pali Mafunso Ambiri Koma Mayankho Ogwira Mtima ndi Ochepa

PATSIKU la chikondwerero cha Tsiku la Oyera Mtima, pa November 1, 1755 nthaŵi ya m’maŵa, mu mzinda wa Lisbon munachitika chivomezi champhamvu kwambiri, anthu ambiri ali m’matchalitchi. Nyumba zambirimbiri zinagwa, ndipo anthu mazana mazana anafa.

Patangopita nthaŵi yochepa chivomezicho chitachitika, mlembi wachifalansa wotchedwa Voltaire anasindikiza ndakatulo yake yotchedwa Poème sur le désastre de Lisbonne (Ndakatulo Yonena za Ngozi ya ku Lisbon). M’ndakatuloyi, anatsutsa zoti ngoziyo inali chilango chochokera kwa Mulungu chifukwa cha machimo a anthuwo. Iye anati ngozi ngati zimenezo anthufe sitingazimvetse kapena kuzifotokoza bwino, ndipo analemba kuti:

Chilengedwe sichilankhula, sichitipatsa mayankho;

Tikufunikira Mulungu wolankhula ndi anthu.

Voltaire sanali woyamba kufunsa mafunso okhudza Mulungu. M’mbiri yonse ya anthu, zinthu zomvetsa chisoni ndi masoka zachititsa kuti anthu azikhala ndi mafunso m’maganizo mwawo. Zaka zikwi zingapo zapitazo, kholo lakale Yobu, amene ana ake onse anali atangofa kumene ndiponso amene anali kudwala matenda oipa kwambiri, anafunsa kuti: “[Mulungu] am’ninkhiranji kuunika wovutika, ndi moyo kwa iye wakuwawa mtima.” (Yobu 3:20) Masiku ano, anthu ambiri amadabwa kuti kodi n’chifukwa chiyani Mulungu wabwino komanso wachikondi amaoneka ngati sakuchitapo kanthu kalikonse pamene anthu akuvutika komanso akusoŵa kwambiri chilungamo chonchi.

Chifukwa chovutika ndi njala, nkhondo, matenda, ndi imfa, anthu ambiri amakaniratu zoti kunja kuno kuli Mlengi amene amaganiziradi anthu. Katswiri wina wa nzeru za anthu wosakhulupirira Mulungu anati: “Palibe chifukwa chilichonse chomuikira kumbuyo Mulungu polola ana kuti azivutika, . . . kupatulapo ngati Mulunguyo kulibeko.” Zochitika zambiri zomvetsa chisoni, monga kupulula anthu kumene kunachitika m’kati mwa nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse, kumachititsa anthu kuganiza zofanana ndi zimenezo. Taonani ndemanga iyi imene wolemba nkhani wina wachiyuda analemba mu nyuzipepala ina. Iye anati: “Chinthu chosavuta kufotokoza kuposa zonse chimene chinachititsa kuti anthu avutike ku Auschwitz n’chakuti kulibe Mulungu amene angathandize anthu.” Kafukufuku amene anachitika mu 1997 ku France, lomwe ndi dziko lachikatolika, anapeza kuti anthu 40 mwa anthu 100 alionse amakayikira zoti kunja kuno kuli Mulungu chifukwa cha kupulula anthu ngati kumene kunachitika ku Rwanda mu 1994.

Kodi N’cholepheretsa Kukhulupirira Mulungu?

Kodi n’chifukwa chiyani Mulungu sachitapo kanthu kuti zinthu zoipa zisamachitike? Wolemba nkhani wina wachikatolika anati funso limeneli ndi “cholepheretsa kukhulupirira Mulungu” chachikulu kwa anthu ambiri. Iye anafunsa kuti: “Kodi n’zothekadi kukhulupirira Mulungu amene amangokhala osachitapo kanthu pamene anthu mamiliyoni ambiri osalakwa akufa ndiponso mafuko a anthu akupululuka m’dzikoli iye osachitapo kanthu koletsa zimenezi?”

Nkhani ina imene anailemba mu nyuzipepala yachikatolika yotchedwa La Croix inanena ndemanga yofanana ndi imeneyo kuti: “Kaya ndi mavuto amene anachitika kale, mavuto obwera chifukwa cha kupita patsogolo kwa luso la zaumisiri, masoka achilengedwe, uchigawenga, kapena imfa ya munthu wokondedwa, pakachitika zinthu zimenezi anthu amakhala ndi mantha ndipo amayang’ana kwa Mulungu kuti awafotokozere chimene chikuchitika. Amafuna mayankho a mafunso akuti, Kodi Mulungu ali kuti? Kodi iye si Mulungu wosakhudzidwa ndi zimene zikuchitika ndiponso wosasamala za ena?”

Papa Yohane Paulo wachiŵiri anafotokozapo za nkhani imeneyi m’kalata yake yautumwi ya mu 1984 yotchedwa Salvifici Doloris. Iye analemba kuti: “Ngakhale kuti chilengedwe tingati chimatsegula maso a anthu kuzindikira kuti Mulungu alipo, kuti iye ndi wanzeru, wamphamvu ndiponso wamkulu, zinthu zoipa zimene zikuchitika ndi kuvutika kwa anthu zikuoneka ngati zikuphimba makhalidwe a Mulungu ameneŵa, ndipo nthaŵi zina zimatero mwamphamvu. Zimenezi zili choncho makamaka pamene tsiku ndi tsiku anthu ambiri akuchitiridwa zinthu mosalungama ndiponso pamene anthu akuchita zoipa zambiri koma osapatsidwa chilango choyenerera.”

Kodi zimene Baibulo limanena zoti kuli Mulungu wachikondi kwambiri komanso wamphamvu kwambiri n’zomveka poona kuvutika kwa anthu kumene kulipoku? Kodi iye amachitapo kanthu kuti pasachitike zinthu zomvetsa chisoni zogwera munthu payekha kapena anthu monga gulu? Kodi akutichitira kalikonse masiku ano? Mogwirizana ndi zimene ananena Voltaire, kodi kunja kuno kuli “Mulungu wolankhula ndi anthu” woti ayankhe mafunso ameneŵa? Chonde ŵerengani nkhani yotsatirayi kuti mupeze mayankho ake.

[Zithunzi patsamba 3]

Kuwonongeka kwa mzinda wa Lisbon mu 1755 kunachititsa Voltaire kunena kuti zinthu ngati zimenezo anthu sangazimvetse

[Mawu a Chithunzi]

Voltaire: Kuchokera m’buku lotchedwa Great Men and Famous Women; Lisbon: J.P. Le Bas, Praça da Patriarcal depois do terramoto de 1755. Foto: Museu da Cidade/​Lisboa

[Chithunzi patsamba 4]

Anthu ambiri amakayikira zoti kunja kuno kuli Mulungu chifukwa cha zinthu zomvetsa chisoni zimene zimabwera chifukwa cha kupulula mtundu wa anthu ngati kumene kunachitika ku Rwanda

[Mawu a Chithunzi]

AFP PHOTO

[Mawu a Chithunzi patsamba 2]

PA CHIKUTO, ana: USHMM, courtesy of Main Commission for the Prosecution of the Crimes against the Polish Nation