Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Amakokera Anthu Odzichepetsa ku Choonadi

Yehova Amakokera Anthu Odzichepetsa ku Choonadi

Mbiri ya Moyo Wanga

Yehova Amakokera Anthu Odzichepetsa ku Choonadi

YOSIMBIDWA NDI ASANO KOSHINO

M’chaka cha 1949, patangopita zaka zochepa kuyambira pamene nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse inatha, munthu wochokera ku dziko lina, wamtali, wochezeka, anafika ku banja limene ndinali kugwirako ntchito mu mzinda wa Kobe. Munthuyu anali mmishonale wa Mboni za Yehova woyamba kufika ku Japan. Kufika kwakeko kunandipatsa mwayi woti ndikokeredwe ku choonadi cha Baibulo. Koma ndilekeni ndifotokoze kaye za moyo wanga.

NDINABADWA m’chaka cha 1926 m’mudzi waung’ono m’chigawo cha Okayama. Ndinali mwana wachisanu mwa ana asanu ndi atatu. Bambo anga anali kukhulupirira kwambiri mulungu wa kachisi wa Ashinto amene anali m’dera lathu. Choncho, anafe tinali kusangalala pa zikondwerero ndiponso pamene anthu a m’banja lathu anali kukumana pamodzi pa mapwando a chipembedzo m’kati mwa chaka.

Pamene ndinali kukula, ndinali ndi mafunso ambiri okhudza moyo, koma chomwe ndinali kuda nacho nkhaŵa kwambiri chinali imfa. Malinga ndi mwambo wakwathu, munthu amafunika kumwalirira kunyumba ndipo munthu wina m’banja akamamwalira, ana amafunika kukhala pafupi ndi bedi limene munthuyo wagona. Ndinamva chisoni kwambiri pamene agogo anga aakazi anamwalira ndiponso pamene mlongo wanga anamwalira asanakwanitse ngakhale chaka chimodzi. Ndinali kuda nkhaŵa kwambiri ndikaganiza kuti makolo anga adzamwalira. Ndinkafuna kudziŵa kuti, ‘Kodi mapeto a zonse ndi imfa basi? Kodi moyo uli ndi cholinga chilichonse?’

Mu 1937, ndili mu giredi sikisi ku sukulu ya pulayimale, nkhondo ya pakati pa dziko la Japan ndi China inayambika. Amuna anali kuwalemba usilikali n’kumawapititsa kunkhondo ku China. Ana asukulu anali kutsanzikana ndi abambo awo kapena azichimwene awo, n’kumafuula kuti “banzai!” (ikhale ndi moyo wautali) uku akutchula mfumu ya Japan. Anthu anali kukhulupirira kuti dziko la Japan, lolamulidwa ndi mulungu, lidzapambana pa nkhondoyo pamodzinso ndi mfumu yake imene inali mulungu wamoyo.

Pasanapite nthaŵi yaitali, mabanja anayamba kumva zoti anthu amwalira kunkhondoko. Mabanja ofedwawo anali ndi chisoni chachikulu moti anali osatheka kuwatonthoza. Anayamba kudana kwambiri ndi amene anali kumenyana nawowo ndipo anali kusangalala adani ambiri akaphedwa kapena kuvulazidwa. Koma ngakhale zinali choncho, ndinaganiza kuti: ‘Anthu amene ali kumbali ya adaniwo ayenera kuti amamva chisoni anthu amene anali kuwakonda akamwalira monga mmene tikuchitira ife.’ Pamene ndinali kumaliza maphunziro a ku pulayimale, nkhondoyo inali ikukulirakulira ku China.

Kukumana Mosayembekezeka ndi Munthu Wochokera ku Dziko Lina

Popeza tinali alimi, banja lathu linali losauka, koma bambo anandilola kupitiriza kuphunzira maphunziro amene anali aulere. Motero, mu 1941, ndinaloŵa sukulu ya atsikana mu mzinda wa Okayama, womwe unali pa mtunda wa makilomita pafupifupi 100 kuchokera kwathuko. Sukuluyo anaikonza kuti iziphunzitsa atsikana kuti adzakhale akazi ndi amayi abwino, ndipo ankapititsa ophunzirawo ku mabanja olemera a mu mzindawo kuti akaphunzire ntchito yosamala m’nyumba. Nthaŵi ya kum’maŵa ana a sukulu anali kuphunzira mwa kugwira ntchito m’nyumba zimenezi ndipo masana ankapita kusukulu.

Mwambo wotilandira utatha, aphunzitsi anga omwe anavala chovala chotchedwa kimono ananditenga kupita nane ku nyumba ina yaikulu. Koma pa zifukwa zina, mayi wa m’nyumbayo sanavomere kuti ndigwire ntchito m’nyumba yakeyo. Aphunzitsi angawo anafunsa kuti: “Kodi tingapite kunyumba kwa a mayi Koda?” Anandipititsa ku nyumba yachizungu ndipo anaimba belu la pakhomo. Patapita kanthaŵi, m’nyumbamo munatuluka mzimayi wa tsitsi loyera. Ndinadabwa kwambiri. Mzimayiyo sanali Mjapani, ndipo chibadwire ndinali ndisanaonepo mzungu. Aphunzitsi angawo anawauza mayi Maud Koda za ine ndipo anandisiya mofulumira iwo n’kumapita. Ndinakwakwaza zikwama zanga pamene ndinali kuloŵa m’nyumbamo mwamantha. Patapita nthaŵi ndinadziŵa kuti mayi Maud Koda anali a ku America ndipo anakwatiwa ndi mwamuna wachijapani amene anapita kukaphunzira ku United States. Mayiwa anali kuphunzitsa Chingelezi m’masukulu ophunzitsa za ntchito.

Tsiku lotsatira m’maŵa ndinayamba kutanganidwa ndi ntchito. Amuna awo a mayi Koda anali kudwala khunyu, ndipo ndinkathandiza mayiwa kusamalira amuna awowo. Popeza sindinali kumva Chingelezi, ndinayamba kuda nkhaŵa. Ndinakhazika mtima pansi pamene mayi Koda anandilankhula m’Chijapani. Tsiku ndi tsiku ndinali kuwamva akulankhulana m’Chingelezi, ndipo pang’ono ndi pang’ono ndinayamba kuzoloŵera kumva chinenero chimenecho. Ndinali kusangala ndi mtendere umene unali panyumbapo.

Ndinachita chidwi ndi kudzipereka kwa a Maud kwa amuna awo amene anali kudwalawo. Aamunawo anali kukonda kuŵerenga Baibulo. Patapita nthaŵi ndinadzamva kuti banjali linapeza buku lakuti The Divine Plan of the Ages la m’Chijapani ku sitolo yogulitsa mabuku ogwiritsidwa ntchito kale ndipo anali akulandira magazini a Nsanja ya Olonda a m’Chingelezi amene analembetsa kuti azilandira mwezi ndi mwezi ndipo anatero kwa zaka zingapo.

Tsiku lina anandipatsa mphatso ya Baibulo. Ndinasangalala kwambiri chifukwa inali nthaŵi yoyamba m’moyo wanga kukhala ndi Baibulo langalanga. Ndinali kuliŵerenga popita ndiponso pobwerako kusukulu koma sindinathe kumvetsa zambiri. Popeza ndinakulira m’chipembedzo cha Chishinto cha ku Japan, Yesu Kristu sindinali kumudziŵa. Sindinadziŵe kuti chimenechi chinali chiyambi cha zochitika zimene zinandithandiza kuti ndidziŵe choonadi cha m’Baibulo, chimene chinadzandiyankha mafunso anga okhudza moyo ndi imfa.

Mauthenga Atatu Achisoni

Zaka ziŵiri zimene ndinakhala ndikuphunzira ntchitoyo zinatha mofulumira, ndipo ndinatsanzikana ndi banjalo. Nditamaliza sukulu, ndinaloŵa nawo gulu lapadera la atsikana ogwira ntchito yongodzipereka ndipo ndinali kugwira nawo ntchito yopanga mayunifolomu a asilikali. Ndege zoponya mabomba za ku Amereka za mtundu wa B-29 zinayamba kuwombera, ndipo pa August 6, 1945, anaphulitsa bomba la atomu mumzinda wa Hiroshima. Patangopita masiku ochepa ndinalandira uthenga wa pa telegalamu ndipo ndinamva kuti Mayi anga anali kudwala kwambiri. Ndinakwera sitima yoyambirira kunyamuka yopita kumudzi. Nditangotsika sitimayo, ndinakumana ndi wachibale wina ndipo anandidziŵitsa kuti Mayi amwalira. Anamwalira pa August 11. Zimene ndinali kuda nazo nkhaŵa kwa zaka zambiri zija zinachitikadi! Sakanathanso kulankhula nane kapena kundimwetulira.

Pa August 15, dziko la Japan linagonjetsedwa pankhondo. Choncho, ndinakumana ndi zochitika zomvetsa chisoni zitatu, zonsezo kuchitika m’nthaŵi yochepa chabe ya masiku khumi: choyamba, kuphulitsidwa kwa bomba la atomu, chachiŵiri, kumwalira kwa Mayi anga, ndipo chachitatu, kugonjetsedwa kosaiŵalika kwa dziko la Japan. Komabe zinandikhazika mtima pansi kuganizira kuti nkhondo yatha ndipo anthu sapitiriza kumwalira pa nkhondoyo. Ndinali ndi chisoni chachikulu ndipo ndinasiya ntchito yopanga mayunifolomuyo ndi kubwerera kumudzi.

Kukokeredwa ku Choonadi

Tsiku lina ndinalandira kalata yochokera kwa a Maud Koda ku Okayama, chinthu chomwe sindinali kuyembekezera. Anandipempha kuti ndipite ndizikawathandiza ntchito zapakhomo, chifukwa amafuna kutsegula sukulu yophunzitsa Chingelezi. Ndinaganiza zochita, komabe ndinavomereza pempho lawo. Patapita zaka zochepa tinasamuka ndi banja la a Koda kupita ku Kobe.

Kuchiyambi kwa chilimwe cha mu 1949, munthu wina wamtali, wochezeka anafika ku banja la a Koda. Dzina lake anali Donald Haslett, yemwe anachokera ku Tokyo ndipo anafika ku Kobe kuti adzafunefune nyumba yoti amishonale azidzakhalamo. Ameneyu anali m’mishonale wa Mboni za Yehova woyamba kufika ku Japan. Anapeza nyumbayo, ndipo mu November 1949, amishonale angapo anafika ku Kobe. Tsiku lina amishonale asanu anafika kudzacheza ndi banja la a Koda. Aŵiri mwa iwo, Lloyd Barry ndi Percy Iszlaub, analankhula m’Chingelezi kwa mphindi pafupifupi khumi aliyense kwa anthu amene anasonkhana panyumbapo. Amishonalewo ankawatcha a Maud kuti ndi mlongo wawo wachikristu ndipo mwachionekere a Maud analimbikitsidwa kwambiri pocheza ndi amishonalewo. Nthaŵi imeneyi m’pamene ndinatsimikiza zophunzira Chingelezi.

Pang’onopang’ono ndinayamba kumvetsa ziphunzitso zazikulu za choonadi cha m’Baibulo mothandizidwa ndi amishonale achanguwo. Ndinapeza mayankho a mafunso amene ndinali nawo kuyambira ndili mwana. Inde, Baibulo limapereka chiyembekezo chakuti anthu adzakhala ndi moyo kosatha m’paradaiso padziko lapansi ndiponso limalonjeza kuti “onse ali m’manda [a chikumbukiro, NW]” adzaukitsidwa. (Yohane 5:28, 29; Chivumbulutso 21:1, 4) Ndinathokoza kwambiri Yehova chifukwa chokonza zoti anthu athe kukhala ndi chiyembekezo choterocho kudzera mu nsembe ya dipo ya Mwana wake, Yesu Kristu.

Ntchito Zauzimu Zosangalatsa

Kuyambira pa December 30, 1949 kudzafika pa January 1, 1950, msonkhano waukulu woyamba ku Japan unachitika ndipo unachitikira ku nyumba ya amishonale ku Kobe. Ndinapitako ndi a Maud. Nyumba yaikulu imene tinachitiramo msonkhanoyo kale inali ya a Nazi ndipo munthu akakhala panyumbayo amatha kuona bwino nyanja ya Inland ndi chilumba cha Awaji. Popeza sindinkadziŵa zambiri za m’Baibulo, ndinatha kumvetsa zinthu zochepa zokha zimene zinakambidwa pa msonkhanopo. Komabe, ndinachita chidwi kwambiri ndi amishonalewo, chifukwa anali kucheza momasuka ndi anthu a ku Japan. Anthu amene anamvetsera nkhani ya anthu onse pa msonkhano umenewu anali okwana 101.

Zitangochitika kumene zimenezi, ndinaganiza zochita nawo utumiki wakumunda. Ndinafunika kulimba mtima kuti ndipite kunyumba ndi nyumba, chifukwa ndinali wamanyazi mwachibadwa. Tsiku lina m’maŵa, Mbale Lloyd Barry anafika kunyumba kwathu kudzanditenga kuti tipite kolalikira. Anayambira pa nyumba imene inali pafupi ndi ya Mlongo Koda. Kunena zoona, ndinatsala pang’ono kubisala kumbuyo kwa mbaleyo, uku ndikumvetsera ulaliki wake. Nditapitanso kolalikira ulendo wina, ndinayenda ndi amishonale ena aŵiri. Mayi ena achikulire achijapani anatipempha kuloŵa m’nyumba mwawo, anamvetsera, ndipo kenako anatipatsa aliyense kapu imodzi ya mkaka kuti timwe. Anavomera kuti aziphunzira Baibulo panyumba ndipo patapita nthaŵi anabatizidwa monga Mkristu. Zinandilimbikitsa kwambiri kuwaona akupita patsogolo.

Mu April 1951, Mbale Nathan H. Knorr, wochokera ku likulu ku Brooklyn, anadzafika koyamba ku Japan. Anthu pafupifupi 700 anafika kudzamvetsera nkhani ya anthu onse imene anakamba mu holo yaikulu ya Kyoritsu ku Kanda, Tokyo. Pa msonkhano umenewu, onse amene anapezekapo anasangalala ndi kutulutsidwa kwa Nsanja ya Olonda ya m’Chijapani. Mwezi wotsatira, Mbale Knorr anapita ku Kobe, ndipo pamsonkhano wapadera umene unachitika kumeneko, ndinabatizidwa posonyeza kudzipatulira kwanga kwa Yehova.

Patatha pafupifupi chaka, ndinalimbikitsidwa kuyamba utumiki wa nthaŵi zonse, wa upainiya. Panthaŵi imeneyi kunali apainiya ochepa chabe ku Japan, ndipo ndinali ndi nkhaŵa kuti ndizipeza bwanji zosoŵa pa moyo wanga. Ndinaganizanso za tsogolo langa pankhani yokwatiwa. Komabe ndinazindikira kuti kutumikira Yehova kuyenera kukhala pamalo oyamba m’moyo wanga, motero ndinayamba upainiya mu 1952. N’zosangalatsa kuti ndinkatha kugwira ganyu kwa mlongo Koda, uku ndikuchita upainiya.

Chapanthaŵi imeneyi, mchimwene wanga, amene ndinali kuganiza kuti anaphedwa pa nkhondo, anabwerera kumudzi ndi banja lake kuchokera ku Taiwan. Achibale anga analibe chidwi ndi Chikristu, koma chifukwa cha changu changa monga mpainiya, ndinayamba kuwatumizira magazini ndi timabuku tathu. Kenako, mchimwene wangayo anasamukira ku Kobe ndi banja lake chifukwa cha ntchito imene anali kugwira. Ndinafunsa mlamu wanga kuti: “Kodi mwaŵerenga magazini aja?” Ndinadabwa pamene anandiyankha kuti: “Ndi magazini osangalatsa kwambiri.” Anayamba kuphunzira Baibulo ndi mmishonale wina, ndipo mng’ono wanga amene amakhala nawo nayenso anayamba kuphunzira nawo. Patapita nthaŵi, aŵiri onsewo anabatizidwa n’kukhala Akristu.

Kuchita Chidwi ndi Ubale wa Padziko Lonse

Pasanapite nthaŵi yaitali, ndinadabwa kulandira kalata yondiitana kuti ndikaphunzire nawo ku Sukulu ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo ya nambala 22. Ine ndi mbale Tsutomu Fukase tinali anthu a ku Japan oyamba kuitanidwa kukaphunzira ku sukuluyi. Mu 1953, tisanayambe maphunziro, tinapezeka nawo pa msonkhano wakuti New World Society (Anthu a Dziko Latsopano) umene unachitikira ku Yankee Stadium ku New York. Ndinachita chidwi kwambiri ndi ubale wa padziko lonse wa anthu a Yehova.

Pa tsiku lachisanu la msonkhanowo, nthumwi za ku Japan, makamaka amishonale, zinafunika kuvala zovala zotchedwa kimono. Popeza chovala changa cha mtundu umenewu chimene ndinali nditatumiza sichinafike panthaŵi yake, ndinabwereka chovala cha mtunduwu cha Mlongo Knorr. Msonkhanowo uli mkati mvula inayamba kugwa, ndipo ndinada nkhaŵa kuti chovalacho chinyowa. Ndikuganiza zimenezo, munthu wina kumbuyo kwanga anandiveka lenikhoti. Mlongo wina amene anaima pafupi nane anandifunsa kuti: “Ukumudziŵa amene wakuveka lenikhotiyi?” Anadzandiuza kuti anali Mbale Frederick W. Franz wa m’ Bungwe Lolamulira. Ndinaonadi chikondi cha gulu la Yehova!

Kalasi la Gileadi la nambala 22 linalidi la anthu ochokera padziko lonse chifukwa linali ndi ophunzira 120 ochokera m’mayiko 37. Ngakhale kuti panali vuto la kusiyana zinenero, tinasangalala kwambiri ndi ubale wa padziko lonse. Ndinamaliza maphunziro tsiku lina mu February 1954, tsiku lomwe kunagwa chipale chofeŵa, ndipo ananditumiza kwathu ku Japan. Mlongo wina amene tinali limodzi m’kalasilo wa ku Sweden dzina lake Inger Brandt ndi amene anati ndizikatumikira naye limodzi mu mzinda wa Nagoya. Kumeneko tinakhala pamodzi ndi amishonale amene anawachotsa ku Korea chifukwa cha nkhondo. Zaka zochepa zimene ndinakhala ndikuchita umishonale zinali za mtengo wapatali kwa ine.

Kutumikira Mosangalala ndi Mwamuna Wanga

Mu September 1957, anandipempha kukatumikira pa Beteli ku Tokyo. Ofesi ya nthambi ya Japan inali nyumba ya matabwa ya nsanjika ziŵiri. Pa nthambiyo panali anthu anayi okha basi, ndipo m’modzi mwa iwo anali Mbale Barry, yemwe anali woyang’anira pa nthambipo. A m’banja la beteli onsewo anali amishonale. Anandipatsa ntchito yomasulira mabuku ndiponso kuŵerenga zimene tamasulirazo kuona ngati zikumveka bwino. Kuwonjezera pamenepo, ndinkagwiranso ntchito yoyeretsa, kuchapa, kuphika, ndi zina zotero.

Ntchito ya Mboni za Yehova ku Japan inali kukulirakulira, ndipo abale ambiri anali kuwaitana kubwera ku Beteli. M’modzi mwa abale ameneŵa anadzakhala woyang’anira mumpingo umene ndinkasonkhana. Mu 1966, ndinakwatiwa ndi mbale ameneyu, dzina lake Junji Koshino. Titakwatirana, Junji anapatsidwa ntchito yoyang’anira dera. Zinali zosangalatsa kudziŵana ndi abale ndi alongo ambiri pamene tinali kuyendera mipingo yosiyanasiyana. Popeza ndinapatsidwa ntchito yomasulira mabuku, ndinali kuchita zimenezo kunyumba imene tinali kukhala mlungu umenewo. Poyendera mipingo, tinali kunyamula mabuku olemera otanthauzira mawu, kuwonjezera pa sutikesi yathu ndi zikwama zina.

Tinagwira ntchito yoyendera dera kwa zaka zinayi, ndipo tinaona gulu likupitiriza kuwonjezeka. Nthambi anaisamutsira ku Numazu, ndipo patapita zaka anaisamutsira ku Ebina, kumene kuli nyumba za nthambi pakalipano. Ine ndi Junji takhala tikutumikira pa Beteli kwa nthaŵi yaitali, ndipo tsopano tikugwira ntchito ndi banja la anthu pafupifupi 600. Mu May 2002, anzathu pa Beteli anakondwerera kuti ndakwanitsa zaka 50 ndili mu utumiki wa nthaŵi zonse.

Kusangalala Poona Kuwonjezeka

Pamene ndinayamba kutumikira Yehova mu 1950, panali ofalitsa ochepa chabe m’dziko la Japan. Panopa tsopano pali ofalitsa Ufumu oposa 210,000. Inde, anthu onga nkhosa zikwizikwi, akokeredwa kwa Yehova monga mmene zinachitikira kwa ine.

Amishonale aamuna anayi ndi mmishonale wamkazi mmodzi amene anadzafika kunyumba kwa Mlongo Koda mu 1949, pamodzinso ndi Mlongo Maud Koda, onse anamwalira ali okhulupirika. Mchimwene wanganso anamwalira ali wokhulupirika ndipo panthaŵiyo anali mtumiki wotumikira. Mlamu wanganso anamwalira atatumikira monga mpainiya kwa zaka pafupifupi 15. Kodi tsogolo la makolo anga amene imfa yawo ndinali kuda nayo nkhaŵa kuyambira ndili mwana n’lotani? Lonjezo la m’Baibulo lakuti kudzakhala kuuka kwa akufa limandipatsa chiyembekezo ndi kunditonthoza.​—Machitidwe 24:15.

Ndikamaganiza zakale, ndimaona kuti kukumana kwanga ndi a Maud mu 1941 kunasintha moyo wanga. Ndikanakhala kuti sindinakumane nawo nthaŵi imeneyo ndiponso ndikanakhala kuti ndinakana atandipempha kuti ndizikagwira ntchito kunyumba kwawo nkhondo itatha, mwina bwenzi nditakhazikika ku famu yathu kumudzi ndipo sindikanakumana ndi amishonale m’zaka zoyambirira zimenezo. Ndikuthokoza Yehova chifukwa chondikokera ku choonadi kudzera mwa a Maud ndi amishonale oyambawo!

[Chithunzi patsamba 25]

Ndili ndi a Maud Koda ndi amuna awo. Ine ndili kutsogolo cha kumanzere

[Chithunzi patsamba 27]

Ndili ndi amishonale ochokera ku Japan pa bwalo la maseŵero la Yankee Stadium mu 1953. Ine ndi womaliza kumanzere

[Zithunzi patsamba 28]

Ndili pa Beteli pamodzi ndi mwamuna wanga, Junji