Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Achinyamata, Yendani Moyenera Yehova

Achinyamata, Yendani Moyenera Yehova

Achinyamata, Yendani Moyenera Yehova

ACHINYAMATA ena achikristu amakakhala kutali ndi banja lawo ndiponso mpingo wakwawo kwa nthaŵi yochepa. Ena achita zimenezi pofuna kuwonjezera zimene amachita mu utumiki. Ena amachoka kwawo chifukwa chokana kutenga mbali m’zochitika za dzikoli. (Yesaya 2:4; Yohane 17:16) M’mayiko ena, “Kaisara” walamula kuti achinyamata okhulupirika aikidwe m’ndende kapena agwire ntchito zachitukuko. *​—Marko 12:17; Tito 3:1, 2.

Achinyamata ameneŵa akapita kukakhala kundende chifukwa chosaloŵerera m’zochitika za dziko, angakhalire limodzi nthaŵi yaitali ndi achinyamata opulupudza. Kukhala kutali ndi kwawo pa zifukwa zina kwapangitsanso achinyamata kugwira ntchito m’malo oipa. Kodi achinyamata achikristu ameneŵa kapena ena amene ali m’malo otereŵa angathane bwanji ndi mavuto amene amakumana nawo pamene akuyesetsa ‘kuyenda moyenera Mulungu?’ (1 Atesalonika 2:12) Kodi makolo awo angawathandize bwanji kukonzekera mavuto ena alionse amene angawagwere?​—Miyambo 22:3.

Mavuto Apadera

Tákis wa zaka 21, amene anakakamizika kukhala kutali ndi kwawo kwa miyezi 37 anati: “Kunali kovuta ndiponso kochititsa mantha kukhala kutali ndi makolo anga amene anali kundisamala bwino ndiponso akulu ondidziŵa bwino amene anali kundiyang’anira mwachikondi.” * Iye anatinso: “Nthaŵi zina, ndinkadziona kuti ndinali wosatetezeka kwambiri.” Pétros wa zaka 20 anakhala kutali ndi kwawo kwa zaka zoposa ziŵiri. Iye anati: “Koyamba pamoyo wanga, ndinafunika kusankha ndekha zochita pankhani ya zosangalatsa ndiponso anzanga, ndipo nthaŵi zina sindinali kusankha bwino.” Ndiyeno anati: “Nthaŵi zina ndinkaopa chifukwa chakuti ndinkafunika kusamala kwambiri ndi ufulu umene ndinali nawo.” Tássos, mkulu wina wachikristu amene nthaŵi zambiri amalankhulana ndi achinyamata achikristu amene ali m’mavuto ameneŵa, anati: “Kulankhula koipa, kupanduka, ndiponso ziwawa zimene achinyamata osakhulupirira amachita zingakhudze achinyamata osadziŵa zambiri ndiponso osatetezeka ameneŵa.”

Pamene achinyamata achikristu ameneŵa akukhala ndiponso kugwira ntchito ndi anthu amene salemekeza mfundo za m’Baibulo, afunika kupeŵa chilakolako chofuna kutsanzira khalidwe loipa la anzawo ndiponso zochita zawo zimene Malemba amaletsa. (Salmo 1:1; 26:4; 119:9) Kungakhale kovuta kupitirizabe chizoloŵezi chabwino chochita phunziro laumwini, kupezeka pamisonkhano, ndiponso kuchita utumiki wakumunda. (Afilipi 3:16) Kungakhalenso kovuta kukhala ndi zolinga zauzimu ndiponso kuchita zinthu mogwirizana ndi zolinga zimenezo.

Ndithudi achinyamata okhulupirika achikristu amafuna kusangalatsa Yehova mwa zochita ndi zolankhula zawo. Amayesetsa ndi mtima wonse kumvera pempho labwino la Atate wawo wakumwamba lakuti: “Mwananga, khala wanzeru, nukondweretse mtima wanga; kuti ndimuyankhe yemwe anditonza.” (Miyambo 27:11) Amazindikira kuti zochita zawo ndiponso khalidwe lawo limakhudza mmene ena amaonera Yehova ndi anthu ake.​—1 Petro 2:12.

Zosangalatsa n’zakuti, ambiri mwa achinyamata ameneŵa amachita zonse zimene angathe kuti akhale ngati abale awo a m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino amene mtumwi Paulo anawapempherera kuti: ‘Yendani moyenera Ambuye kukam’kondweretsa monsemo, ndi kubala zipatso mu ntchito yonse yabwino, . . . kuchitira chipiriro chonse ndi kuleza mtima konse pamodzi ndi chimwemwe.’ (Akolose 1:9-11) Baibulo lili ndi zitsanzo zambiri za achinyamata oopa Mulungu amene anatha kuyenda moyenera Mulungu pakati pa anthu achilendo, oipa, ndiponso olambira mafano.​—Afilipi 2:15.

“Yehova Anali ndi Yosefe”

Ali wamng’ono, Yosefe, mwana wokondedwa wa Yakobo ndi Rakele, anakakhala kutali ndi kumene bambo ake oopa Mulungu omwe ankamuteteza anali kukhala. Anagulitsidwa ku ukapolo ku Igupto. Yosefe anapereka chitsanzo chabwino kwambiri, kuti anali mnyamata wolimbikira ntchito, wodalirika ndiponso wakhalidwe. Ngakhale kuti anali kapolo wa Potifara​—munthu amene sanali kulambira Yehova​—Yosefe anali wolimbikira ntchito ndiponso wakhama, mapeto ake mbuye wake anamuika kuti aziyang’anira zochitika zonse panyumbapo. (Genesis 39:2-6) Yosefe anakhalabe wokhulupirika kwa Yehova, ndipo ngakhale kuti zimenezi zinam’tengera kundende, iye sanaganize kuti: “Ndiye ndavutikiranji?” Ngakhale kundendeko anakasonyeza makhalidwe abwino, ndipo posapita nthaŵi anali kuyang’anira ntchito zambiri m’ndendemo. (Genesis 39:17-22) Mulungu anam’dalitsa, ndipo monga ananenera pa Genesis 39:23, “Yehova anali ndi [Yosefe].”

Sizikanam’vuta Yosefe kutengera khalidwe la anthu akunja amene anali kukhala nawo, kutsatira makhalidwe oipa a Aigupto popeza anali kutali ndi achibale ake oopa Mulungu. M’malo mwake, anasungabe mfundo za Mulungu ndiponso makhalidwe ake abwino ngakhale panali zokopa zamphamvu. Pamene mkazi wa Potifara anamulimbikitsa mobwerezabwereza kuti agone naye, anayankha motsimikiza kuti: “Ndikachita choipa chachikulu ichi bwanji ndi kuchimwira Mulungu?”​—Genesis 39:7-9.

Masiku ano, Mboni zachinyamata zifunika kumvera zimene Baibulo limachenjeza pankhani ya mayanjano oipa, zosangalatsa zoipa, zolaula, ndiponso nyimbo zoipa. Zimadziŵa kuti “maso a Yehova ali ponseponse, nayang’anira oipa ndi abwino.”​—Miyambo 15:3.

Mose Anakana “Zokondweretsa Zoipa”

Mose anakula ndi anthu amakhalidwe oipa ndiponso okonda zosangalatsa a kunyumba ya Farao. Za iye Baibulo limati: ‘Ndi chikhulupiriro Mose . . . anakana kutchedwa mwana wake wa mwana wamkazi wa Farao; nasankhula kuchitidwa zoipa pamodzi ndi anthu a Mulungu, kosati kukhala nazo zokondweretsa zoipa zakanthaŵi.’​—Ahebri 11:24, 25.

Ubwenzi ndi dziko ungabweretse phindu lina lake, koma la nthaŵi yochepa. Osapitirira nthaŵi yochepa imene yatsalira dziko lino. (1 Yohane 2:15-17) Kodi sizingakhale bwino kutsatira chitsanzo cha Mose? Baibulo limanena kuti “anapirira molimbika, monga ngati kuona wosaonekayo.” (Ahebri 11:27) Anaika maganizo ake pa choloŵa chauzimu cha makolo ake oopa Mulungu. Cholinga chake pamoyo wake chinali kuchita zimene Yehova amafuna, kukhala ndi cholinga chochita chifuno cha Mulungu.​—Eksodo 2:11; Machitidwe 7:23, 25.

Achinyamata oopa Mulungu akakhala ndi anthu osaopa Mulungu ndiponso oipa, angakulitse ubwenzi wawo ndi Yehova mwa kuchita phunziro la umwini, kumudziŵa bwino “wosaonekayo.” Pulogalamu yonse ya zochita zachikristu, kuphatikizapo kupezeka pamisonkhano ndiponso mu utumiki wakumunda nthaŵi zonse, idzathandiza achinyamata ameneŵa kuika maganizo awo pa zinthu zauzimu. (Salmo 63:6; 77:12) Ayenera kuyesetsa kukhala ndi chikhulupiriro ndiponso chiyembekezo chachikulu ngati cha Mose. Angachite bwino kuti zoganiza ndiponso zochita zawo zizikhala zokhudza Yehova, n’kumasangalala pokhala naye paubwenzi.

Anagwiritsa Ntchito Lilime Lake Kutamanda Mulungu

Wachinyamata wina amene anali wachitsanzo chabwino ali kutali ndi kwawo ndi mtsikana wachiisrayeli amene anatengedwa ukapolo ndi Aaramu m’masiku a mneneri wa Mulungu, Elisa. Anakhala mdzakazi wa mkazi wa kazembe wa khamu lankhondo la Aaramu amene anali wakhate, Namani. Mtsikana ameneyu anauza mbuyake wamkaziyo kuti: “Mbuye wanga akadakhala kwa mneneri ali m’Samariya, akadam’chiritsa khate lake.” Chifukwa cha ulaliki wake, Namani anapita kwa Elisa ku Israyeli ndipo anachiritsidwa khate lakelo. Ndiponso, Namani anakhala wolambira Yehova.​—2 Mafumu 5:1-3, 13-19.

Chitsanzo cha mtsikanayu chimagogomezera kufunika koti achinyamata azigwiritsa ntchito lilime lawo m’njira yolemekeza Mulungu, ngakhale akhale kutali ndi makolo awo. Ngati mtsikanayu akanakhala kuti ankakonda kulankhula “zopanda pake” kapena “zopusa,” kodi akanamasuka kugwiritsa ntchito lilime lake m’njira yabwino monga mmene anachitiramu pamene mpata unapezeka? (Aefeso 5:4; Miyambo 15:2) Níkos mnyamata amene ali m’zaka zoyambirira za m’ma 20, amene anaikidwa m’ndende chifukwa chosaloŵerera m’zochitika zadziko, anati: “Nthaŵi imene ndinali ndi abale achinyamata ku ndende ya zaulimi, kutali ndi makolo ndiponso mpingo, ndinaona kuti zolankhula zathu zinali kuipa pang’onopang’ono. Ndithudi sizinali zotamanda Yehova.” Ubwino wake, Níkos ndi ena anathandizidwa kumvera malangizo a Paulo pankhaniyi akuti: “Koma dama ndi chidetso chonse, kapena chisiriro, zisatchulidwe ndi kutchulidwa komwe mwa inu, monga kuyenera oyera mtima.”​—Aefeso 5:3.

Yehova Anali Weniweni kwa Iwo

Zimene anzake atatu a Danieli achihebri anakumana nazo ku Babulo wakale zikutsimikizira kuti mfundo imene Yesu ananena yakuti wokhulupirika m’zinthu zazing’ono amakhalanso wokhulupirira m’zinthu zazikulu ndi yoona. (Luka 16:10) Atapeza vuto pankhani ya kudya zakudya zimene Chilamulo cha Mose chinaletsa, akanatha kuganiza kuti iwo anali akapolo m’dziko lachilendo ndipo sakanachitira mwina. Koma si mmene anapezera madalitso posaona mwachibwana ngakhale nkhani imene inali kuoneka ngati yaing’ono. Iwo anakhala athanzi ndiponso anzeru kuposa akapolo ena onse amene anali kudya chakudya chokoma cha mfumu. Kukhulupirika m’zinthu zazing’ono zimenezi mosakayikira kunawalimbikitsa, moti atakumana ndi chiyeso chachikulu chogwadira fano, anakana kuchita zimenezo.​—Danieli 1:3-21; 3:1-30.

Yehova anali weniweni kwa anyamata atatu ameneŵa. Ngakhale kuti anali kutali ndi kwawo ndiponso kuchimake kolambira Mulungu, anatsimikiza mtima kusachitidwa mawanga ndi dziko. (2 Petro 3:14) Anaona ubwenzi wawo ndi Yehova kukhala wamtengo wapatali moti analolera kupereka moyo wawo kuti ateteze ubwenzi wawowo.

Yehova Sadzakusiyani

Achinyamata akakhala kutali ndi anthu amene amawakonda ndiponso kuwadalira, m’pomveka kudziona osatetezeka, osadziŵa chochita, ndiponso amantha. Komabe, angathane ndi mayesero awo ndi chidaliro chonse chakuti ‘Yehova sadzawasiya.’ (Salmo 94:14) Ngati achinyamata ameneŵa ‘amva zowawa chifukwa cha chilungamo,’ Yehova adzawathandiza kuti apitirize kuyenda “m’njira ya chilungamo.”​—1 Petro 3:14; Miyambo 8:20.

Yehova nthaŵi zonse analimbikitsa ndiponso anadalitsa kwambiri Yosefe, Mose, mdzakazi wachiisrayeli, ndiponso achinyamata atatu achihebri okhulupirika. Masiku ano, akugwiritsa ntchito mzimu wake woyera, Mawu ake, ndiponso gulu lake kulimbikitsa amene ‘akulimbana nayo nkhondo yabwino ya chikhulupiriro,’ kuti adzapeze mphoto ya “moyo wosatha.” (1 Timoteo 6:11, 12) Inde, kuyenda moyenera Yehova n’kotheka, ndipo ndi nzeru kuchita zimenezo.​—Miyambo 23:15, 19.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Onani Nsanja ya Olonda, ya May 1, 1996, masamba 18-20.

^ ndime 5 Tasintha mayina ena.

[Bokosi patsamba 25]

MAKOLO​—KONZEKERETSANI ANA ANU!

“Ana a ubwana wake wa munthu akunga mivi m’dzanja lake la chiphona.” (Salmo 127:4) Muvi sungalase mwangozi pamene mukufuna kulasa. M’pofunika kuuchetekera mwaluso. Mofananamo, ana sangakhale okonzeka kuthana ndi mavuto okhala kutali ndi kwawo popanda makolo kuwalangiza bwinobwino.​—Miyambo 22:6.

Ana amakonda kuchita zinthu mopupuluma kapena kugonjera “zilakolako za unyamata.” (2 Timoteo 2:22) Baibulo limachenjeza kuti: “Ntyole ndi chidzudzulo zipatsa nzeru; koma mwana wom’lekerera achititsa amake manyazi.” (Miyambo 29:15) Kulekerera zochita za mwana kumapangitsa mwanayo kusakonzekera mavuto a moyo wokhala kutali ndi kwawo.

Makolo achikristu ayenera kufotokozera ana awo momveka bwino ndiponso mosamala za mavuto, ndiponso zimene zimachitika pamoyo m’dongosolo la zinthu lino. Popanda kukayikira kuti zinthu zidzakhala bwino kapena kukhala ndi maganizo oipa, angafotokoze zinthu zoipa zimene mwanayo angakumane nazo ngati atachoka panyumba. Kumuuza zimenezi, pamodzi ndi nzeru za Mulungu, ‘kudzachenjeza achibwana, kuphunzitsa mnyamata kudziŵa ndi kulingalira.’​—Miyambo 1:4.

Makolo amene amakhomereza miyezo ya Mulungu ndiponso mfundo za makhalidwe abwino m’mitima ya ana awo, amawathandiza kuthana bwinobwino ndi mavuto amene angakumane nawo pamoyo wawo. Kuphunzira nthaŵi zonse Baibulo ndi banja, kulankhulana momasuka, kuchita chidwi ndi zochita za ana, n’zimene zingapangitse kuti anawo ziwayendere bwino. Makolo ayenera kuphunzitsa ana awo za Mulungu mosamala komanso molimbikitsa ndiponso mowaganizira, pokonzekeretsa ana awo kudzadziimira paokha nthaŵi ina pamoyo wawo. Mwa chitsanzo chawo, makolo angaphunzitse ana awo kuti n’kotheka kukhala m’dziko koma osakhala mbali yake.​—Yohane 17:15, 16.

[Chithunzi patsamba 23]

Achinyamata ena achikristu amachoka panyumba

[Zithunzi patsamba 24]

Mwa kukana zokopa, achinyamata angatsanzire Yosefe ndi kukhala odzisunga

[Zithunzi patsamba 26]

Tsanzirani mdzakazi wachiisrayeli amene anagwiritsa ntchito lilime lake kutamanda Yehova