Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Khalani Wodziletsa Kuti Mudzalandire Mphoto!

Khalani Wodziletsa Kuti Mudzalandire Mphoto!

Khalani Wodziletsa Kuti Mudzalandire Mphoto!

‘Yense wakuyesetsana adzikanizira [“adziletsa,” NW] m’zonse.’​—1 Akorinto 9:25.

1. Mogwirizana ndi Aefeso 4:22-24, kodi anthu ambiri avomera motani kuchita zofuna za Yehova?

NGATI munabatizidwa monga wa Mboni za Yehova, ndiye kuti munasonyeza poyera kuti mukufuna kuchita nawo mpikisano umene mphoto yake ndi moyo wosatha. Munavomera kuchita chifuniro cha Yehova. Tisanadzipatulire kwa Yehova, ambirife tinasintha kwambiri n’cholinga choti kudzipatulirako kukhale kwatanthauzo, kovomerezeka kwa Mulungu. Tinamvera malangizo a mtumwi Paulo kwa Akristu, akuti: “Muvule, kunena za makhalidwe anu oyamba, munthu wakale, wovunda potsata zilakolako za chinyengo . . . nimuvale munthu watsopano, amene analengedwa monga mwa Mulungu, m’chilungamo, ndi m’chiyero cha choonadi.” (Aefeso 4:22-24) M’mawu ena, tisanavomere kudzipatulira kwa Mulungu, tinafunika kusiya makhalidwe akale osavomerezeka.

2, 3. Kodi pa 1 Akorinto 6:9-12 pakusonyeza motani kuti m’pofunika kusintha kwa mitundu iŵiri kuti Mulungu atiyanje?

2 Mbali zina za umunthu wakale zimene anthu oyembekezeka kukhala Mboni za Yehova afunika kuvula zimatsutsidwa mwachindunji m’Mawu a Mulungu. Paulo anatchula zina mwa zimenezi m’kalata yake yomwe analembera Akorinto, kuti: “Adama, kapena opembedza mafano, kapena achigololo, kapena olobodoka ndi zoipa, kapena akudziipsa ndi amuna, kapena ambala, kapena osirira, kapena oledzera, kapena olalatira, kapena olanda, sadzaloŵa Ufumu wa Mulungu.” Kenaka anasonyeza kuti Akristu a m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino anasintha zimene amafunika kusintha pamoyo wawo, powonjezera kuti: “Ndipo ena a inu munali otere.” Onani kuti ananena kuti munali osati muli.​1 Akorinto 6:9-11.

3 Paulo anasonyeza kuti pangafunike kusinthanso zinthu zina, chifukwa anapitiriza ndi kuti: “Zinthu zonse ziloledwa kwa ine; koma si zonse zipindula.” (1 Akorinto 6:12) Motero anthu ambiri amene lerolino akufuna kukhala Mboni za Yehova amaona kuti m’pofunikanso kukana zinthu zimene zilibe phindu kapena zaphindu losakhalitsa, ngakhale kuti n’zololedwa. Zinthu zimenezi zingawatayitse nthaŵi ndi kuwadodometsa kuchita zinthu zofunika kwambiri.

4. Kodi Akristu odzipatulira amavomerezana ndi Paulo pamfundo iti?

4 Munthu amadzipatulira kwa Mulungu mwa kufuna kwake, osati mokakamizidwa, ngati kuti kudzipatulirako kumalira kudzimana kwambiri. Akristu odzipatulira amavomerezana ndi Paulo, amene atayamba kutsatira Kristu ananena izi: “Chifukwa cha [Yesu] ndinatayikitsa zinthu zonse, ndipo ndiziyesa zapadzala, kuti ndikadziwonjezere Kristu.” (Afilipi 3:8) Paulo anakana mosangalala zinthu zosapindulitsa kwenikweni n’cholinga choti apitirize kuvomereza zofuna za Mulungu.

5. Kodi Paulo anapambana pa mpikisano wotani, ndipo ife tingatani kuti tichite mofananamo?

5 Pothamanga mpikisano wake wauzimu, Paulo anali wodziletsa ndipo pomaliza pake iye anatha kunena kuti: “Ndalimbana nako kulimbana kwabwino, ndatsiriza njirayo, ndasunga chikhulupiriro: chotsalira wandiikira ine korona wa chilungamo, amene Ambuye, woweruza wolungama, adzandipatsa ine tsiku lijalo: ndipo si kwa ine ndekha, komatunso kwa onse amene anakonda maonekedwe ake.” (2 Timoteo 4:7, 8) Kodi ifeyo tsiku lina tidzatha kunena mawu ofananawo? Tidzatero ngati tikhala odziletsa m’chikhulupiriro pamene tikuthamanga mpikisano wathu wachikristu, popanda kufooka ndiponso tikathamanga mpaka kumapeto.

N’kofunika Kudziletsa Kuti Tichite Zabwino

6. Kodi kudziletsa n’kutani, ndipo ndi mbali ziŵiri ziti zomwe tiyenera kusonyeza kudziletsa?

6 Mawu achihebri ndi achigiriki omwe m’Baibulo atembenuzidwa kuti “kudziletsa” kwenikweni amatanthauza kuti munthu akutha kudzilamulira. Nthaŵi zambiri mawuŵa amapereka lingaliro la kudzigwira kuti usachite choipa. Koma n’zoonekeratu kuti kudziletsa n’kofunikanso ndithu ngati tikufuna kugwiritsa ntchito matupi athu pantchito zabwino. Mwachibadwa anthu opanda ungwiro amakonda kuchita zoipa, motero nkhondo yathu ili paŵiri. (Mlaliki 7:29; 8:11) Pamene tikudzigwira kuti tisachite choipa, tifunikanso kudzikakamiza kuchita chabwino. Ndipotu kulamulira thupi lathu n’cholinga choti tichite zabwino ndi njira imodzi yabwino kwambiri yopeŵera kuchita choipa.

7. (a) Kodi tiyenera kupempherera chiyani, ngati mmene anachitira Davide? (b) Kodi tidzakhala odziletsa kwambiri ngati tisinkhasinkha za chiyani?

7 N’zoonekeratu kuti kudziletsa n’kofunika kwambiri kuti tisabwerere m’mbuyo pa kudzipatulira kwathu kwa Mulungu. Tifunika kupemphera ngati mmene Davide anachitira: “Mundilengere mtima woyera, Mulungu; mukonze mzimu wokhazikika m’kati mwanga.” (Salmo 51:10) Tingasinkhesinkhe phindu la kupeŵa zinthu zoipa kapena zowononga thupi. Ganizirani za vuto limene lingakhalepo chifukwa chosapeŵa zinthu zimenezo: kudwala matenda oopsa, kusokoneza maubale, mwinanso kufa msanga kumene. Ndiyeno, ganizirani zambiri zimene tidzapindula chifukwa choyendabe m’njira ya moyo yomwe Yehova amatiuza kuti tiyendemo. Komabe, kunena zoona, tisaiŵale kuti mtima wathu ndi wonyenga. (Yeremiya 17:9) Tifunika kutsimikiza kukana zimene mtima wathu ungachite zopeputsa kufunika kotsatira miyezo ya Yehova.

8. Kodi taphunzira mfundo yotani malinga ndi zomwe takumana nazo m’moyo wathu? Perekani chitsanzo.

8 Malinga ndi zimene takumana nazo m’moyo wathu, ambirife timadziŵa kuti nthaŵi zambiri thupi lathu likakhala kuti silikufuna kuchita zimene mzimu ukufuna, limalimbana nawo mzimuwo. Taganizirani kulalikira za Ufumu. Yehova amasangalala ndi kudzipereka kwa anthu kuchita nawo ntchito yopatsa moyo imeneyi. (Salmo 110:3; Mateyu 24:14) Kwa ambirife, siinali ntchito yamaseŵera kuti tiphunzire kulalikira poyera. Panafunika kuti tilamulire thupi lathu, ‘kulipumphuntha’ ndi ‘kuliyesa kapolo,’ m’malo molilola kutilamula kuchita zimene sizingativute ndipo izi mwina zikufunikabe mpaka pano.​—1 Akorinto 9:16, 27; 1 Atesalonika 2:2.

‘M’zonse’?

9, 10. Kodi ‘kudziletsa m’zonse’ kukuphatikizapo chiyani?

9 Langizo la m’Baibulo lakuti ‘tizidziletsa m’zonse’ likusonyeza kuti kudziletsa kumafuna zambiri osati kungobweza mkwiyo ndiponso kusachita khalidwe loipa. Mwina tikhoza kuona kuti tikutha kudziletsa pambali zimenezi, ndipo ngati ndi choncho, n’zosangalatsa kwambiri. Komano bwanji za mbali zina pamoyo wathu zomwe sizingachite kuoneka bwinobwino kuti n’zofunika kudziletsa? Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti tikukhala m’dziko lolemera, la moyo wapamwamba kwambiri. Kodi sichingakhale chanzeru kuphunzira kukana kuwonongera ndalama pa zinthu zosafunikira kwenikweni? Makolo angachite bwino kuphunzitsa ana awo kuti asamangogula chilichonse chomwe achiona, pachifukwa chabe choti chikupezeka, n’chosangalatsa, kapena ali ndi ndalama zokwanira kugulira chinthucho. Ndipotu kuti malangizowo agwire ntchito, makolo afunika kusonyeza chitsanzo chabwino.​—Luka 10:38-42.

10 Kuphunzira kukhala moyo wopanda zinthu zina kungalimbikitse kuti tikhale odziletsa. Kungatithandizenso kuyamikira kwambiri zinthu zomwe tili nazo komanso kungatithandize kuwachitira chifundo kwambiri anthu amene alibe zinthu zina, osati chifukwa choti sakuzifuna, koma chifukwa choti sangathe kukhala nazo. Inde, moyo wosalira zinthu zambiri umatsutsana ndi malingaliro ofala kwambiri monga akuti “dzikomereni mtima” kapena “mufunika zabwino zokhazokha.” Otsatsa malonda amalimbikitsa mtima wofuna kudzisangalatsa nthaŵi yomweyo, koma amatero n’cholinga chofuna kuti iwo alemere basi. Izi zingathe kusokoneza khama lathu lofuna kuti tikhale wodziletsa. Posachedwapa, magazini ya m’dziko lina lolemera kwambiri la ku Ulaya, inati: “Ngati anthu amene ali paumphaŵi wadzaoneni amafunika kumenya nkhondo zolimba kuti aletse zilakolako zoipa, ndiye kuli bwanji kwa anthu amene akukhala m’madera olemera oyenda mkaka ndi uchi masiku athu ano!”

11. N’chifukwa chiyani kuphunzira kukhala opanda zinthu zina kuli kopindulitsa, koma n’chiyani chimapangitsa kuti zimenezi zikhale zovuta?

11 Ngati zimativuta kusiyanitsa zinthu zimene timafuna ndi zinthu zomwe timafunikiradi, mwina ndi bwino kuchita zinthu zotithandiza kuti tisamachite zinthu mosaganiza bwino. Mwachitsanzo, ngati tikufuna kuthana ndi vuto la kumwaza ndalama mwachisawawa, mwina tingasankhe kuti tisamagule zinthu pangongole, kapena kuti popita kogula zinthu, tizitenga ndalama zochepa. Kumbukirani kuti Paulo ananena kuti “chipembedzo pamodzi ndi kudekha [“kukhala wokhutira,” NW] chipindulitsa kwakukulu.” Iye anafotokoza kuti: “Sitinatenga kanthu poloŵa m’dziko lapansi, ndiponso sitikhoza kupita nako kanthu pochoka pano; koma pokhala nazo zakudya ndi zofunda, zimenezi zitikwanire.” (1 Timoteo 6:6-8) Kodi ndi mmene timachitira? M’pofunika khama ndiponso kudziletsa kuti munthu uthe kukhala moyo wosalira zambiri, wosamangochita chinthu chilichonse chimene mtima ukufuna. Komabe ndi zinthu zofunika kwambiri kuti tiphunzire.

12, 13. (a) Kodi misonkhano yachikristu imafuna kudziletsa m’njira ziti? (b) Kodi ndi mbali zina ziti zomwe timafunika kukhala odziletsa?

12 Nakonso kukhala nawo pamisonkhano yampingo, yadera, ndiponso yachigawo kumafuna kudziletsa kwambiri. Mwachitsanzo, kudziletsa n’kofuna kuti maganizo athu asamayendeyende msonkhano uli mkati. (Miyambo 1:5) Pangafunikirenso kudziletsa kuti tisasokoneze anzathu mwa kunong’onezana ndi anthu omwe tayandikana nawo m’malo motchera khutu kwa wokamba nkhani. Kusintha zochita zathu n’cholinga choti tikafike nthaŵi yabwino pamsonkhano kungafune kudziletsa. Komanso, kudziletsa kungafunike kuti tipatule nthaŵi yokonzekera misonkhanoyo ndipo kenako n’kukalankhulapo nawo.

13 Kudziletsa pazinthu zazing’ono kumathandiza kukulitsa luso lathu lochita chimodzimodzi pa zinthu zazikulu. (Luka 16:10) Ndiyetu ndi bwino kuti tizidziletsa kuti tiziŵerenga nthaŵi zonse Mawu a Mulungu ndi mabuku ofotokoza Baibulo, kuwaphunzira ndi kusinkhasinkha zomwe tikuphunzirazo. N’chinthu chanzeru kudziletsa pankhani ya ntchito, mayanjano, maganizo, ndi zizoloŵezi zosayenera kapena kudziphunzitsa kunena kuti toto ku zochita zomwe zingatitengere nthaŵi yamtengo wapatali yochitira utumiki wa Mulungu. Kutanganidwa ndi kutumikira Yehova ndi chitetezo chabwino kwambiri ku zinthu zomwe zingatichotse m’paradaiso wauzimu wa mpingo wapadziko lonse wa Yehova.

Khalani Aakulu Misinkhu mwa Kudziletsa

14. (a) Kodi ana angaphunzire motani kudziletsa? (b) Kodi pali phindu lotani ngati ana aphunzira kudziletsa akali aang’ono?

14 Khanda longobadwa kumene silikhala lodziletsa. Chikalata china cha akatswiri a zochita za mwana chinafotokoza kuti: “Kudziletsa sikuyamba kokha kapena kuchitika mwadzidzidzi. Makanda ndiponso ana aang’ono amafunika kulangizidwa ndiponso kuthandizidwa ndi makolo kuti ayambe kuphunzira kudziletsa. . . . Pamene makolo akum’thandiza, kudziletsa kumakula m’zaka zonse zomwe mwanayo amakhala ali pasukulu.” Kafukufuku wina amene anachita pakati pa ana a zaka zinayi anasonyeza kuti ana omwe anali ataphunzirako kudziletsa “nthaŵi zambiri atakula anakhala achinyamata ophunzitsika bwino, okondedwa kwambiri, ochangamuka, odzidalira ndiponso odalirika.” Omwe anali asanayambe kuphunzira kudziletsa “zinali zotheka kwambiri kuti angakhale opanda anzawo ocheza nawo, osachedwa kukhumudwa ndiponso aliuma. Anali kutaya mtima akapanikizika kwambiri ndipo anali kupeŵa nkhani zikuluzikulu.” Mwachionekere, kuti mwana adzakhale wophunzitsika bwino akadzakula, afunika kuphunzira kudziletsa.

15. Kodi kulephera kudziletsa kumasonyezanji, zomwe n’zosiyana ndi cholinga chiti cha m’Baibulo?

15 N’chimodzimodzinso ndi ife, ngati tikufuna kukhala Akristu aakulu misinkhu, tifunika kuphunzira kukhala odziletsa. Kulephera kudziletsa kumasonyeza kuti tidakali makanda mwauzimu. Baibulo limatilimbikitsa kuti ‘tikhale aakulu misinkhu m’chidziŵitso.’ (1 Akorinto 14:20) Cholinga chathu ndicho ‘kufikira ku umodzi wa chikhulupiriro, ndi wa chizindikiritso cha Mwana wa Mulungu, kwa munthu wangwiro, ku muyeso wa msinkhu wa chidzalo cha Kristu.’ Chifukwa? “Kuti tisakhalenso makanda, ogwedezekagwedezeka, natengekatengeka ndi mphepo yonse ya chiphunzitso, ndi tsenga la anthu, ndi kuchenjerera kukatsata chinyengo cha kusokeretsa.” (Aefeso 4:13, 14) N’zoonekeratu kuti kuphunzira kudziletsa n’kofunika kwambiri pamoyo wathu wauzimu.

Kukulitsa Kudziletsa

16. Kodi Yehova amatithandiza motani?

16 Kuti tikulitse kudziletsa tifunikira thandizo la Mulungu, ndipo thandizolo lilipo. Mawu a Mulungu, monga kalilore wabwino kwambiri, amatisonyeza pamene tikufunika kusintha, ndipo amatipatsa malangizo a mmene tingachitire zimenezo. (Yakobo 1:22-25) Abale athu achikondi nawonso ndi okonzeka kutithandiza. Akulu achikristu amasonyeza kuti amamvetsa pamene akutithandiza. Yehova mwiniwakeyo amapereka kwaulere mzimu wake woyera ngati tipempha m’pemphero. (Luka 11:13; Aroma 8:26) Motero tiyeni tigwiritse ntchito zinthu zimenezi mosangalala. Mfundo zomwe zili patsamba 21 zingatithandize.

17. Kodi Miyambo 24:16 limatilimbikitsa chiyani?

17 N’zolimbikitsatu kwambiri kudziŵa kuti Yehova amayamikira zomwe timachita pofuna kuti tim’sangalatse. Izi ziyenera kutilimbikitsa kupitiriza kuyesetsa kuti tikhale odziletsa kwambiri. Zilibe kanthu kuti timalephera kangati kuchita zimenezi, koma tisagwe mphwayi. “Wolungama amagwa kasanu ndi kaŵiri, nanyamukanso.” (Miyambo 24:16) Nthaŵi iliyonse yomwe tachita bwino, m’pomveka kusangalala. Tingakhalenso ndi chikhulupiriro kuti Yehova akusangalala nafe. Mwamuna wina wa Mboni anati, asanapatulire moyo wake kwa Yehova, nthaŵi iliyonse yomwe wadziletsa kusuta kwa mlungu umodzi, ankadzipatsa mphoto mwa kutenga ndalama zomwe zapulumuka chifukwa cha kudziletsa, n’kugulira chinthu china chofunika.

18. (a) Kodi nkhondo yathu ya kukhala wodziletsa imaphatikizapo chiyani? (b) Kodi Yehova akutitsimikizira chiyani?

18 Koposa zonsezi, tiyeni tizikumbukira kuti kudziletsa kumaphatikizapo maganizo ndiponso mtima. Tingaone zimenezi m’mawu a Yesu akuti: “Yense wakuyang’ana mkazi kum’khumba, pamenepo watha kuchita naye chigololo mumtima mwake.” (Mateyu 5:28; Yakobo 1:14, 15) Iye amene waphunzira kulamulira maganizo sadzavutika kulamulira thupi lake lonse. Chotero tiyeni tilimbikitse kutsimikiza mtima kwathu osati kungopeŵa kuchita choipa koma kupeŵanso kuganizira choipa. Maganizo oipa akangofika, tiyeni tiwakane msangamsanga. Tingathaŵe chiyeso mwa kupempherera ndi kuyang’ana kwa Yesu nthaŵi zonse. (1 Timoteo 6:11; 2 Timoteo 2:22; Ahebri 4:15, 16) Pamene tikuyesetsa kuchita zonse zomwe tingathe, tidzakhala tikutsatira malangizo a pa Salmo 55:22, akuti: “Um’senze Yehova nkhaŵa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza: Nthaŵi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.”

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi ndi mbali ziŵiri ziti zomwe tiyenera kusonyeza kudziletsa?

• Kodi ‘kudziletsa m’zonse’ kumatanthauzanji?

• Kodi ndi malingaliro abwino ati okulitsira kudziletsa amene mwachita nawo chidwi m’phunziro lathuli?

• Kodi kudziletsa kumayambira kuti?

[Mafunso]

[Bokosi/​Zithunzi patsamba 21]

Mmene Tingakulitsire Kudziletsa

• Sonyezani kudziletsa ngakhale m’zinthu zazing’ono

• Sinkhasinkhani phindu lake la panopo ndi m’tsogolo

• Sinthanitsani zomwe Mulungu amaletsa ndi zomwe amalimbikitsa

• Kanani msangamsanga maganizo oipa

• Dzazani m’maganizo mwanu mfundo zauzimu zolimbikitsa

• Landirani thandizo lomwe Akristu achikulire angakupatseni

• Peŵani kukhala malo omwe angakuikeni pachiyeso

• Pemphani thandizo kwa Mulungu panthaŵi za chiyeso

[Zithunzi pamasamba 18, 19]

Kudziletsa kumatilimbikitsa kuchita zabwino