Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Musakhale Womangidwa m’Goli ndi Wosiyana’

‘Musakhale Womangidwa m’Goli ndi Wosiyana’

‘Musakhale Womangidwa m’Goli ndi Wosiyana’

MONGA mukuonera pachithunzipa, ngamila ndi ng’ombe zimene zikukokera limodzi pulawo zikuoneka kuti zikuvutika kwambiri. Goli limene azimangirira, limene anapangira nyama zofanana msinkhu ndiponso mphamvu, likupangitsa nyama zonsezi kuvutika. Posonyeza kuganizira moyo wa nyama zoterezi zokoka zinthu, Mulungu anauza Aisrayeli kuti: “Musamalima ndi bulu ndi ng’ombe zikoke pamodzi.” (Deuteronomo 22:10) Mfundo yomweyi inali kugwiranso ntchito pa ng’ombe ndi ngamila.

Nthaŵi zambiri, mlimi sanali kuchita zimenezi ndi nyama zake. Koma ngati alibe ng’ombe ziŵiri amatha kumangirira pamodzi nyama zimene ali nazo. Ziyenera kuti zimenezi n’zimene anachita mlimi wa m’ma 1800 amene ali pachithunzipa. Chifukwa chosiyana misinkhu ndiponso mphamvu, nyama yochepa mphamvu ingavutike kuti iziyenda mofanana ndi yamphamvu, ndipo nyama yamphamvuyo ingalemedwe kwambiri.

Mtumwi Paulo anagwiritsa ntchito chitsanzo chomangirira m’goli limodzi nyama zosiyana kutiphunzitsa mfundo yofunika kwambiri. Iye analemba kuti: “Musakhale omangidwa m’goli ndi osakhulupira osiyana; pakuti chilungamo chigaŵana bwanji ndi chosalungama? Kapena kuunika kuyanjana bwanji ndi mdima?” (2 Akorinto 6:14) Kodi Mkristu angamangidwe bwanji m’goli ndi wosiyana?

Njira imodzi ndiyo ngati Mkristu wasankha kukwatirana ndi munthu wosiyana naye zikhulupiriro. Ukwati wotere udzakhala wovuta kwa onsewo, okwatiranawo angasiyane maganizo pankhani zikuluzikulu.

Pamene Yehova amayambitsa ukwati, anaika mkazi kukhala ‘wothangatira.’ (Genesis 2:18) Mofananamo, mwa mneneri Malaki, Mulungu anatcha mkazi kuti “mnzako.” (Malaki 2:14) Mlengi wathu amafuna anthu okwatirana kuti azikokera mbali imodzi pankhani yauzimu, azithandizana mavuto ndiponso azipindula mofanana.

Mkristu akakwatira kapena kukwatiwa “mwa Ambuye,” amasonyeza kulemekeza malangizo a Atate wathu wakumwamba. (1 Akorinto 7:39) Izi zimayala maziko a ukwati wogwirizana, umene umapangitsa kuti Mulungu atamandidwe ndi kulemekezedwa pamene okwatiranawo akum’tumikira monga ‘anzake a m’goli oona’ mu njira yapadera.​—Afilipi 4:3.

[Mawu a Chithunzi patsamba 32]

Ngamila ndi ng’ombe: From the book La Tierra Santa, Volume 1, 1830