Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Akazi Amene Anakondweretsa Mtima wa Yehova

Akazi Amene Anakondweretsa Mtima wa Yehova

Akazi Amene Anakondweretsa Mtima wa Yehova

“Yehova akubwezere ntchito yako, nakupatse mphotho yokwanira Yehova.”​—RUTE 2:12.

1, 2. Kodi tingapindule bwanji mwa kusinkhasinkha zitsanzo za m’Baibulo za akazi amene anakondweretsa mtima wa Yehova?

KUOPA Mulungu kunachititsa akazi aŵiri kuti asamvere Farao. Chikhulupiriro chinachititsa mkazi wadama kuika moyo wake pangozi kuti ateteze azondi aŵiri achiisrayeli. Nzeru komanso kudzichepetsa pa nthaŵi ya mavuto kunathandiza mkazi wina kupulumutsa miyoyo yambiri ya anthu ndiponso kunachititsa kuti wodzozedwa wa Yehova asakhale ndi mlandu wakupha. Kukhulupirira Yehova Mulungu komanso kukhala ndi mtima wochereza alendo kunachititsa mkazi wamasiye amene analinso kholo kuti apereke chakudya chomaliza chimene anali nacho kwa mneneri wa Mulungu. Izi ndi zitsanzo zochepa chabe mwa zitsanzo zambiri zopezeka m’Malemba za akazi amene anakondweretsa mtima wa Yehova.

2 M’mene Yehova anawaonera akazi ameneŵa komanso madalitso amene anawapatsa zikusonyeza kuti makhalidwe auzimu ndi amene amakondweretsa Yehova koposa zonse, ndipo sayang’ana kuti kaya munthuyo ndi mwamuna kapena mkazi. M’dziko la masiku anoli, limene anthu amaganizira kwambiri zinthu zooneka ndi maso, n’zovuta kuti munthu aike zinthu zauzimu choyamba pa moyo wake. Komabe, munthu angakwanitse kuchita zimenezi, monga mmene asonyezera akazi oopa Mulungu ambirimbiri amene amapanga gawo lalikulu la anthu a Mulungu masiku ano. Akazi achikristu ameneŵa amatsanzira chikhulupiriro, nzeru, kuchereza alendo, ndi makhalidwe ena abwino amene akazi oopa Mulungu otchulidwa m’Baibulo anasonyeza. Inde, ngakhale amuna achikristu nawonso amafunika kutsanzira makhalidwe amene akazi akale opereka chitsanzo chabwino amenewo anasonyeza. Kuti tione mmene tingachitire zimenezi mokulirapo, tiyeni tipende mwatsatanetsatane nkhani za m’Baibulo za akazi amene tawatchula koyambirira aja.​—Aroma 15:4; Yakobo 4:8.

Akazi Amene Sanamvere Farao

3, 4. (a) N’chifukwa chiyani Sifra ndi Puwa anakana kumvera Farao atawauza kuti azipha khanda lililonse lalimuna lachiisrayeli? (b) Kodi Yehova anadalitsa motani anamwino aŵiriwo chifukwa cha kulimba mtima ndi kuopa kwawo Mulungu?

3 Pa milandu imene inachitikira ku Nuremberg, ku Germany nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse itatha, anthu ambiri amene anali kuimbidwa mlandu wopha anthu ambirimbiri anayesera kusonyeza kuti sanalakwe popha anthuwo mwa kunena kuti anali kungomvera chabe malamulo. Tsopano tayerekezani anthu ameneŵa ndi anamwino aŵiri achiisrayeli, Sifra ndi Puwa, amene anali kukhala ku Igupto wakale panthaŵi ya ulamuliro wankhanza wa Farao winawake amene dzina lake silinatchulidwe. Poopa kuti Ahebri angachulukane kwambiri, Farao ameneyo analamula anamwino aŵiriwo kuti azipha khanda lililonse lalimuna lachihebri. Kodi akaziŵa anachita chiyani atalamulidwa kuti achite zinthu zoipa kwambiri zimenezi? ‘Sanachita monga mfumu ya Aigupto inawauza, koma analeka ana aamuna akhale ndi moyo.’ N’chifukwa chiyani akazi ameneŵa sanaope munthu? Chifukwa chakuti “anaopa Mulungu.”​—Eksodo 1:15, 17; Genesis 9:6.

4 Inde, anamwinowo anadalira Yehova, ndipo iye anakhala “chikopa” chawo, n’kuwateteza ku mkwiyo wa Farao. (2 Samueli 22:31; Eksodo 1:18-20) Koma madalitso a Yehova sanathere pomwepo. Anadalitsa Sifra ndi Puwa mwa kuwapatsa mabanja awoawo. Ndipo analemekeza akazi ameneŵa mwa kuchititsa kuti mayina awo ndi zimene anachita zilembedwe m’Mawu ake ouziridwa kuti mibadwo yam’tsogolo idzaŵerenge, pamene dzina la Faraoyo linazimiririka.​—Eksodo 1:21; 1 Samueli 2:30b; Miyambo 10:7.

5. Kodi akazi achikristu ambiri masiku ano amasonyeza bwanji mtima wofanana ndi wa Sifra ndi Puwa, ndipo kodi Yehova adzawadalitsa motani?

5 Kodi masiku ano alipo akazi ofanana ndi Sifra ndi Puwa? Ndithudi alipo! Chaka chilichonse, akazi ambirimbiri ofanana ndi amenewo amalalikira mopanda mantha uthenga wopulumutsa moyo wa m’Baibulo m’mayiko amene “chilamuliro cha mfumu” chimaletsa kuchita zimenezi, kutanthauza kuti amaika ufulu wawo, ngakhale moyo wawo umene, pangozi. (Ahebri 11:23; Machitidwe 5:28, 29) Chifukwa cha kukonda kwawo Mulungu ndiponso anansi awo, akazi olimba mtima ameneŵa salola aliyense kuwaletsa kugaŵana uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndi anzawo. Chifukwa chochita zimenezi, akazi achikristu ambiri akuvutika ndi chitsutso komanso chizunzo. (Marko 12:30, 31; 13:9-13) Monga mmene zinalili ndi Sifra ndi Puwa, Yehova akudziŵa bwino ntchito za akazi abwino, olimba mtima ameneŵa ndipo adzasonyeza mmene amawakondera mwa kusunga mayina awo “m’buku la moyo,” ngati apitiriza kupirira mokhulupirika mpaka pamapeto.​—Afilipi 4:3; Mateyu 24:13.

Mkazi Amene Kale Anali Wadama Anakondweretsa Mtima wa Yehova

6, 7. (a) Kodi Rahabi ankadziŵa chiyani za Yehova ndi anthu ake, ndipo kodi kudziŵa zimenezi kunam’khudza bwanji? (b) Kodi Mawu a Mulungu amamulemekeza bwanji Rahabi?

6 M’chaka cha 1473 B.C.E., mu mzinda wachikanani wa Yeriko munali mkazi wa dama wotchedwa Rahabi. Zikuoneka kuti Rahabi anali mkazi wodziŵa zinthu zambiri. Pamene azondi achiisrayeli aŵiri anadzabisala kunyumba kwake, iye anatha kuwafotokozera mwatsatanetsatane za ulendo wodabwitsa wa Aisrayeli wochokera ku Igupto, ngakhale kuti zimenezi zinachitika zaka 40 m’mbuyomo! Anali kudziŵanso za kupambana kwa Aisrayeli kumene kunali kutangochitika kumene, pamene anagonjetsa Mafumu a Aamori, Sihoni ndi Ogi. Taonani mmene kudziŵa zimenezi kunam’khudzira Rahabi. Anauza azondiwo kuti: “Ndidziŵa kuti Yehova wakupatsani dzikoli, . . . pakuti Yehova Mulungu wanu, ndiye Mulungu wa m’mwamba umo, ndi pa dziko lapansi.” (Yoswa 2:1, 9-11) Inde, zimene Rahabi anamva za Yehova ndi zimene anachitira Aisrayeli zinakhudza kwambiri mtima wake ndipo zinam’chititsa kuti akhale ndi chikhulupiriro mwa Yehova.​—Aroma 10:10.

7 Chikhulupiriro cha Rahabi chinam’pangitsa kuchitapo kanthu. Iye analandira azondi achiisrayeli “ndi mtendere,” ndipo anamvera malangizo awo opulumukira pamene Aisrayeli anaukira Yeriko. (Ahebri 11:31; Yoswa 2:18-21) Palibe kukayikira zoti ntchito zosonyeza chikhulupiriro za Rahabi zinakondweretsa mtima wa Yehova, chifukwa anauzira wophunzira wachikristu Yakobo kuti alembe dzina lake pamodzi ndi dzina la Abrahamu, bwenzi la Mulungu, monga chitsanzo choti Akristu atsanzire. Yakobo analemba kuti: “Momwemonso sanayesedwa wolungama Rahabi mkazi wadamayo ndi ntchito kodi, popeza adalandira amithenga, nawatulutsa adzere njira ina?”​—Yakobo 2:25.

8. Kodi Yehova anadalitsa bwanji Rahabi chifukwa cha chikhulupiriro ndi kumvera kwake?

8 Yehova anadalitsa Rahabi m’njira zingapo. Njira imodzi inali yoti anateteza modabwitsa moyo wake ndi moyo wa onse amene anadzabisala m’nyumba mwake, limene linali “banja la atate wake, ndi onse anali nawo.” Kenaka analola kuti anthu ameneŵa akhale “pakati pa Israyeli,” ndipo aziwaona ngati mbadwa. (Yoswa 2:13; 6:22-25; Levitiko 19:33, 34) Koma sanalekere pomwepo. Yehova anam’patsanso Rahabi mwayi wapadera wokhala kholo la Yesu Kristu. Yehova anasonyezadi kukoma mtima kwachikondi m’njira yochititsa chidwi kwambiri kwa mkazi amene kale anali Mkanani wolambira mafano. *​—Salmo 130:3, 4.

9. Kodi mmene Yehova anaonera Rahabi ndi akazi ena achikristu m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino zingalimbikitse bwanji akazi ena masiku ano?

9 Monga mmene anachitira Rahabi, akazi ena achikristu, kuyambira m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino mpaka kufika masiku athu ano, asiya moyo wachiwerewere kuti akondweretse Mulungu. (1 Akorinto 6:9-11) Mosakayikira ena a iwo anakulira m’malo ofanana ndi dziko la Kanani lakale, kumene moyo wachiwerewere unali wofala, ndiponso mwina kumene ankaona kuti umenewo ndiye moyowo. Komabe, anasintha njira zawo chifukwa cha chikhulupiriro chobwera chifukwa chodziŵa Malemba molondola. (Aroma 10:17) Choncho tinganenenso kuti akazi ameneŵa “Mulungu sachita manyazi nawo poitanidwa Mulungu wawo.” (Ahebri 11:16) Ndi mwayidi waukulu kwambiri!

Anadalitsidwa Chifukwa cha Nzeru Zake

10, 11. Kodi n’chiyani chimene chinachitika pakati pa Nabala ndi Davide chimene chinapangitsa Abigayeli kuchitapo kanthu?

10 Akazi okhulupirika ambiri akale anasonyeza khalidwe lochita zinthu mwanzeru m’njira yochititsa chidwi kwambiri, zimene zinawapangitsa kuti akhale amtengo wapatali kwa anthu a Yehova. Mkazi mmodzi woteroyo anali Abigayeli, mkazi wa Nabala, Mwisrayeli wolemera amene anali mwinimalo. Kuchita zinthu mwanzeru kwa Abigayeli kunapulumutsa miyoyo ya anthu ndipo kunaletsa Davide, amene anali kudzakhala mfumu ya Israyeli m’tsogolo, kuti asakhale ndi mlandu wakupha. Tingaŵerenge za Abigayeli mu nkhani imene ili pa 1 Samueli chaputala 25?

11 Nkhaniyo ikuyamba n’kuti, Davide ndi anthu ake anamanga msasa pafupi ndi ziweto za Nabala, ndipo anateteza ziwetozo kwaulere usana ndi usiku chifukwa chokomera mtima Mwisrayeli mnzawo, Nabala. Pamene zakudya za Davide zinayamba kutha, anatuma anyamata khumi kwa Nabala kuti akapemphe chakudya. Pamenepo Nabala anali ndi mwayi woti asonyeze kuyamikira kwake kwa Davide komanso amulemekeze monga wodzozedwa wa Yehova. Koma Nabala anachita zinthu zosemphana ndi zimenezi. Atakwiya kwambiri, ananyoza Davide ndi kubweza anyamatawo chimanjamanja. Davide atamva zimenezi, anasonkhanitsa amuna 400 okhala ndi zida za nkhondo ndipo ananyamuka kuti akabwezere. Abigayeli anamva za mmene mwamuna wake anawayankhira anthuwo mopanda chifundo ndipo anachita zinthu mwamsanga ndiponso mwanzeru kuti amukhazike mtima pansi Davide mwa kumutumizira zakudya zambiri. Kenako iye mwiniyo anapita kwa Davide.​—Mavesi 2-20.

12, 13. (a) Kodi Abigayeli anachita bwanji zinthu mwanzeru ndiponso mokhulupirika kwa Yehova ndi wodzozedwa wake? (b) Kodi Abigayeli anachita chiyani atabwerera kunyumba, ndipo kodi zinthu zinamuyendera bwanji?

12 Pamene Abigayeli anakumana ndi Davide, pempho lake lodzichepetsa loti amuchitire chifundo linasonyeza kuti ankalemekeza kwambiri wodzozedwa wa Yehova. Iye anati: “Yehova adzapatsadi mbuye wanga banja lokhazikika, pakuti mbuyanga amaponya nkhondo za Yehova.” Kenako anaonjezera kunena kuti Yehova adzasankha Davide kukhala m’tsogoleri wa Israyeli. (Mavesi 28-30) Panthaŵi yomweyo, Abigayeli anasonyeza kulimba mtima ndithu mwa kuuza Davide kuti kubwezera kumene anali kufuna kuchitako, ngati sakanakulamulira, kukanachititsa kuti akhale ndi mlandu wakupha. (Mavesi 26, 31) Davide anayamba kuonanso zinthu bwinobwino chifukwa cha kudzichepetsa, ulemu waukulu, ndi kuganiza bwino kwa Abigayeli. Iye anayankha kuti: “Alemekezedwe Yehova Mulungu wa Israyeli, amene anakutumiza lero kudzandichingamira ine; ndipo, kudalitsike kuchenjera [“kuganiza mwanzeru,” NW] kwako, nudalitsike iwe, pakuti unandiletsa kusakhetsa mwazi, ndi kusabwezera chilango ndi dzanja la ine ndekha.”​—Mavesi 32, 33.

13 Atabwerera kunyumba, Abigayeli molimba mtima anafuna kuti auze mwamuna wake za mphatso imene anali atapereka kwa Davide. Koma anam’peza ‘ataledzera kwambiri.’ Choncho anadikira kuti mowa um’there kaye, kenako anamuuza. Kodi Nabala anachita chiyani atamva zimenezi? Mtima wake unamyuka mkati mwake moti anakhala ngati wadwala matenda enaake oumitsa ziwalo. Patatha masiku khumi anaphedwa ndi Mulungu. Davide atamva zoti Nabala wamwalira, anafunsira Abigayeli, amene mwachionekere anali kumusirira ndi kumulemekeza kwambiri. Abigayeli anamuvomera Davide.​—Mavesi 34-42.

Kodi Mungakhale Ngati Abigayeli?

14. Kodi ndi makhalidwe ati a Abigayeli amene tingafune kukulitsa?

14 Kodi mukuona makhalidwe enaake mwa Abigayeli amene inuyo, kaya ndinu mwamuna kapena mkazi, mungafune kukulitsa? Mwina mukufuna kuti muzichita zinthu mwanzeru pakabuka mavuto. Kapena mwina mukufuna kuti muzilankhula mwachifatse ndiponso mwaulemu anthu amene muli nawo akapsa mtima. Ngati mukufuna kutero, bwanji osapemphera kwa Yehova n’kumufotokozera zimenezi? Iye akulonjeza kuti adzapereka nzeru, kuzindikira, ndi kuganiza bwino kwa onse amene ‘amapempha ndi chikhulupiriro.’​—Yakobo 1:5, 6; Miyambo 2:1-6, 10, 11.

15. Kodi akazi achikristu amafunika kusonyeza makhalidwe amene Abigayeli anasonyeza makamaka ngati banja lawo n’lotani?

15 Makhalidwe abwino ameneŵa ndi ofunika kwambiri makamaka kwa mkazi amene ali ndi mwamuna wosakhulupirira amene amangotsatira pang’ono kapena satsatira n’komwe mfundo za m’Baibulo. Mwina amamwa mwauchidakwa. Tili ndi chiyembekezo choti mwina amuna oterowo adzasintha. Amuna ambiri asintha, nthaŵi zambiri chifukwa choona kufatsa, ulemu waukulu, ndi mayendedwe abwino a akazi awo.​—1 Petro 3:1, 2, 4.

16. Kaya akukhala m’banja lotani, kodi mlongo wachikristu angasonyeze bwanji kuti amaona kuti ubwenzi wake ndi Yehova ndi wamtengo wapatali kuposa chinthu china chilichonse?

16 Kaya mukukumana ndi mavuto otani kunyumba, kumbukirani kuti Yehova nthaŵi zonse amakhala pomwepo kuti akuthandizeni. (1 Petro 3:12) Choncho, yesetsani kudzilimbitsa mwauzimu. Pempherani kuti mukhale ndi nzeru komanso kuti muzichita zinthu mwachifatse. Inde, yandikirani kwambiri kwa Yehova kudzera m’phunziro la Baibulo la nthaŵi zonse, pemphero, kusinkhasinkha, ndi kuyanjana ndi Akristu anzanu. Chikondi chimene Abigayeli anali nacho pa Mulungu ndi mmene anali kuonera mtumiki Wake wodzozedwa sizinakhudzidwe ndi kupanda maganizo auzimu kwa mwamuna wake. Iye anachita zinthu motsatira mfundo zolungama. Ngakhale m’banja limene mwamuna ali mtumiki wa Mulungu wopereka chitsanzo chabwino, mkazi wachikristu amadziŵa kuti afunika kupitiriza kuchita khama kuti alimbitse ndi kusamalira moyo wake wauzimu. N’zoona kuti mwamuna wake ali ndi udindo wa m’Malemba woti azimusamalira mwauzimu komanso azim’pezera zimene amafunikira pamoyo wake, komabe, mkaziyo ayenera kugwira ntchito ‘ya chipulumutso chake ndi mantha, ndi kunthunthumira.’​—Afilipi 2:12; 1 Timoteo 5:8.

Analandira “Mphotho ya Mneneri”

17, 18. (a) Kodi mkazi wamasiye wa ku Zarefati anapatsidwa chiyeso chachilendo chotani? (b) Kodi mkazi wamasiyeyo anachita chiyani atamva pempho la Eliya, ndipo kodi Yehova anamudalitsa bwanji chifukwa cha zimene anachitazo?

17 Zimene Yehova anachita posamalira mkazi wamasiye wosauka mu nthaŵi ya mneneri Eliya zimasonyeza kuti amayamikira kwambiri anthu amene amathandiza pa kulambira koona mwa kudzipereka iwo eni komanso kupereka zinthu zimene ali nazo. Chifukwa cha chilala chimene chinakhalapo kwa nthaŵi yaitali m’nthaŵi ya Eliya, anthu ambiri anakhudzidwa ndi njala, kuphatikizapo mkazi wamasiye ndi mwana wake wamwamuna wamng’ono amene anali kukhala ku Zarefati. Pamene anali atangotsala ndi chakudya choti aphike kamodzi kokha, kunabwera mlendo, mneneri Eliya. Anapempha chinthu chachilendo kwambiri. Ngakhale kuti Eliya amadziŵa vuto la mkaziyo, anamupempha kuti amuotchereko “kamkate,” zimene zikanachititsa kuti amalize mafuta ndi ufa zimene zinatsalazo. Koma anaonjezera kunena kuti: “Popeza atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Mbiya ya ufa siidzatha, ndipo nsupa ya mafuta siidzachepa, kufikira tsiku lakugwetsa mvula Yehova pa dziko lapansi.”​—1 Mafumu 17:8-14.

18 Kodi inu mukanachita chiyani mukanamva pempho lachilendo limenelo? Mwachionekere mkazi wamasiye wa ku Zarefati, atazindikira kuti Eliya anali mneneri wa Yehova, ‘anachita monga mwa mawu a Eliya.’ Kodi Yehova anachita chiyani ataona khalidwe lake lochereza alendo? Anapereka chakudya modabwitsa kwa mkaziyo, mwana wake, ndi Eliya pa nthaŵi ya chilalayo. (1 Mafumu 17:15, 16) Inde, Yehova anam’patsa mkazi wa masiye wa ku Zarefatiyo “mphotho ya mneneri,” ngakhale sanali Mwisrayeli. (Mateyu 10:41) Mwana wa Mulungu analemekezanso mkazi wamasiye ameneyu pamene anamutchula ngati chitsanzo kwa anthu opanda chikhulupiriro a kumudzi kwawo ku Nazareti.​—Luka 4:24-26.

19. Kodi ndi njira ziti zimene akazi achikristu ambiri masiku ano amasonyezera mtima wofanana ndi wa mkazi wamasiye wa ku Zarefati, ndipo kodi Yehova amawaona bwanji akazi ameneŵa?

19 Masiku ano, akazi achikristu ambiri ali ndi mtima wofanana ndi wa mkazi wamasiye wa ku Zarefati. Mwachitsanzo, mlungu uliwonse alongo achikristu odzimana, ambiri a iwo osauka ndiponso okhala ndi mabanja oti asamalire, amachereza oyang’anira oyendayenda ndi akazi awo. Ena amagawana chakudya ndi anthu amene ali mu utumiki wa nthaŵi zonse kwawoko, amathandiza osoŵa, kapena m’njira inayake amadzipereka iwo eni kapena zinthu zimene ali nazo kuti zithandize pa ntchito ya Ufumu. (Luka 21:4) Kodi Yehova amaona zopereka zimenezo? Inde! “Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera ku dzina lake, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe.”​—Ahebri 6:10.

20. Kodi mu nkhani yotsatira tidzakambirana chiyani?

20 M’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino, akazi angapo oopa Mulungu anali ndi mwayi wotumikira Yesu ndi atumwi ake. M’nkhani yotsatira, tidzaona mmene akazi ameneŵa anakondweretsera mtima wa Yehova, ndiponso tidzakambirana zitsanzo za akazi a masiku ano amene amatumikira Yehova ndi mtima wonse, ngakhale ali pamavuto.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Mzera umene Yesu anadzabadwiramo umene unalembedwa ndi Mateyu umatchula mayina a akazi anayi omwe ndi Tamara, Rahabi, Rute, ndi Mariya. Akazi onseŵa amalemekezedwa kwambiri m’Mawu a Mulungu.​—Mateyu 1:3, 5, 16.

Kubwereza

• Kodi akazi otsatiraŵa anakondweretsa bwanji mtima wa Yehova?

• Sifra ndi Puwa

• Rahabi

• Abigayeli

• Mkazi wamasiye wa ku Zarefati

• Kodi kusinkhasinkha zitsanzo zimene akazi ameneŵa anasonyeza kungatithandize bwanji aliyense payekha? Perekani chitsanzo.

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 9]

Akazi ambiri okhulupirika atumikira Mulungu mosaopa “chilamulo cha mfumu”

[Chithunzi patsamba 10]

Kodi n’chifukwa chiyani Rahabi ali chitsanzo chabwino cha munthu wokhala ndi chikhulupiriro?

[Chithunzi patsamba 10]

Kodi ndi makhalidwe ati amene Abigayeli anasonyeza amene mukufuna kutsanzira?

[Chithunzi patsamba 12]

Akazi achikristu ambiri masiku ano amasonyeza mtima wofanana ndi wa mkazi wamasiye wa ku Zarefati