Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Khalani ndi Mtima Wopatsa

Khalani ndi Mtima Wopatsa

Khalani ndi Mtima Wopatsa

PALIBE amene amabadwa ndi mtima wopatsa. Mwachibadwa mwana wakhanda amafuna kupeza zimene akufuna, mosaganizira ngakhale amene akumusamalira. Komabe, m’kupita kwa nthaŵi, mwanayo amaphunzira kuti si iye yekhayo amene amafuna zinthu. Ayenera kuganizira zofuna za ena, ndiponso kuphunzira kupatsa osati kulandira kokha. Mtima wopatsa umafunika kuchita kuuyambitsa kuti tikhale nawo.

Sikuti anthu onse amene amapatsa zinthu anzawo, ngakhale moolowa manja, amakhaladi ndi mtima wopatsa. Ena angapereke ku mabungwe kuti apititse patsogolo zolinga zawo. Ena angapereke kuti anthu awalemekeze. Komabe, kupatsa kumene Akristu oona amachita n’kosiyana ndi kumeneku. Motero, kodi ndi kupatsa kwamtundu wanji kumene kumalimbikitsidwa m’Mawu a Mulungu? Kukambirana mwachidule za kupatsa kumene Akristu a m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino anasonyeza kuyankha funso limeneli.

Zitsanzo za Kupatsa Kwachikristu

Kupatsa kwachikristu, monga mmene akufotokozera m’Baibulo, nthaŵi zambiri kunali “kugaŵira ena” amene anali osoŵadi. (Ahebri 13:16; Aroma 15:26) Sankafunika kupereka mokakamizidwa. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Yense achite monga anatsimikiza mtima, si mwa chisoni kapena mokakamiza, pakuti Mulungu akonda wopereka mokondwerera.” (2 Akorinto 9:7) Munthu sankafunikanso kupereka n’cholinga chongofuna kuti ena aone. Hananiya ndi Safira anachita zimenezo ndipo anapeza nazo mavuto aakulu.​—Machitidwe 5:1-10.

Kupatsa kunakhala kofunika kwambiri pamene Ayuda ochuluka ndi anthu amene anatembenukira ku Chiyuda ochokera kumadera akutali anasonkhana ku Yerusalemu kudzachita phwando la Pentekoste mu 33 C.E. Ndi panthaŵi imeneyi pamene otsatira a Yesu “anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula ndi malilime ena.” Anthu ambiri anasonkhana ndipo anamvetsera nkhani yolimbikitsa ya Petro yokamba za Yesu Kristu. Kenako, anthu anaona mmene Petro ndi Yohane anachiritsira munthu wolumala pakhomo la kachisi, ndipo anamvanso Petro akulankhula za Yesu ndi kufunika kolapa. Anthu zikwi zingapo analapa ndipo anabatizidwa n’kukhala otsatira a Kristu.​—Machitidwe, machaputala 2 ndi 3.

Anthu amene analowa Chikristu kumenewo anafuna kukhalabe ku Yerusalemu kuti alandire malangizo owonjezera kuchokera kwa atumwi a Yesu. Koma kodi atumwi akanawasamalira bwanji alendowo? Nkhani ya m’Baibulo imatiuza kuti: “Onse amene anali nayo minda, kapena nyumba, anazigulitsa nabwera nawo malonda ake a izo adazigulitsa, nawaika pa mapazi a atumwi; ndipo anagaŵira yense monga kusoŵa kwake.” (Machitidwe 4:33-35) Kunena zoona, mpingo umene unali utangopangidwa kumene mu Yerusalemuwo unalidi ndi mtima wopatsa!

Patapita nthaŵi, mipingo ina inasonyeza mtima womwewo wa kupatsa. Mwachitsanzo, Akristu a ku Makedoniya, ngakhale kuti anali osauka, anachita zoposa zomwe akanatha popereka kwa abale awo amene anali osoŵa ku Yudeya. (Aroma 15:26; 2 Akorinto 8:1-7) Mpingo wa ku Filipi unathandiza mwapadera Paulo pa utumiki wake. (Afilipi 4:15, 16) Nawonso mpingo wa mu Yerusalemu unkagaŵa chakudya kwa akazi amasiye tsiku lililonse, ndipo atumwi anasankha amuna asanu ndi aŵiri oyenerera kuti aonetsetse kuti akazi amasiye amene anali oyenera sananyalanyazidwe.​—Machitidwe 6:1-6.

Mipingo yachikristu yoyambirira inkachita changu pothandiza ngakhale pokonzekera nthaŵi ya mavuto. Mwachitsanzo, pamene mneneri Agabo analosera za njala yaikulu, ophunzira mu mpingo wa Antiokeya wa ku Suriya “yense monga anakhoza, anatsimikiza mtima kutumiza zothandiza abale akukhala m’Yudeya.” (Machitidwe 11:28, 29) Anasonyezadi mtima wabwino poganizira zimene abale awo angasoŵe m’tsogolo!

Kodi n’chiyani chinalimbikitsa Akristu oyambirira amenewo kuti akhale opatsa ndiponso achikondi choncho? Ndipo, kodi munthu amakhala nawo bwanji mtima wopatsa? Tingaphunzire zambiri poona mwachidule chitsanzo cha Mfumu Davide.

Davide Anathandiza Kulambira Koona Moolowa Manja

Kwa zaka pafupifupi 500, likasa lachipangano, lomwe linali bokosi lopatulika limene linkaimira kukhalapo kwa Yehova, linalibe malo okhalamo okhazikika. Linkasungidwa mu hema, amene ankamutengera ku malo osiyanasiyana nthaŵi imene Aisrayeli ankayenda m’chipululu mpaka kukalowa m’Dziko Lolonjezedwa. Mfumu Davide inafunitsitsa kuti ichotse likasa mu hema amene linkasungidwamo ndi kumangira Yehova nyumba yoyenera imene akanaikamo likasa lopatulikalo. Polankhula kwa mneneri Natani, Davide anati: “Taona, ndikhala ine m’nyumba yamikungudza, koma likasa la chipangano likhala m’nsalu zotchinga.”​—1 Mbiri 17:1.

Komabe, Davide anali munthu wankhondo. Motero Yehova ananena kuti mwana wake Solomo ndi amene anali woti adzamange kachisi kuti asungemo likasa la chipangano, panthaŵi ya ulamuliro wamtendere. (1 Mbiri 22:7-10) Komabe, zimenezi sizinalepheretse Davide kukhala ndi mtima wopatsa. Atasonkhanitsa anthu ambiri ogwira ntchito, anayamba kusonkhanitsa zipangizo zodzagwiritsa ntchito pomanga kachisi. Kenako anauza Solomo kuti: “Ndinakonzeratu nyumba ya Yehova matalente zikwi zana limodzi a golidi, ndi matalente zikwizikwi a siliva, ndi mkuwa, ndi chitsulo, osayesa kulemera kwake, pakuti zidachulukadi; mitengo yomwe ndi miyala ndakonzeratu.” (1 Mbiri 22:14) Posakhutitsidwa ndi zimene anachitazo, Davide anatenganso pa chuma chake golide ndi siliva amene masiku ano angakwane ndalama zopitirira $1,200,000,000. Kuwonjezera apo, akulu anaperekanso moolowa manja. (1 Mbiri 29:3-9) Davide anasonyezadi mtima wopatsa!

Kodi n’chiyani chinachititsa Davide kuti apereke moolowa manja chotero? Anadziŵa kuti zonse zimene anali nazo ndiponso zimene anatha kuchita anatero chifukwa chakuti Yehova anamudalitsa. Iye anavomereza m’pemphero kuti: “Yehova Mulungu wathu, zounjikika izi zonse tazikonzeratu kukumangirani inu nyumba ya dzina lanu loyera zifuma ku dzanja lanu, zonsezi ndi zanu. Ndidziŵanso, Mulungu wanga, kuti muyesa mtima, nimukondwera nako kuwongoka. Koma ine, ndi mtima wanga wowongoka ndapereka zonsezi mwaufulu; ndipo tsopano ndawona mokondwera anthu anu okhala pompano, napereka kwa inu mwaufulu.” (1 Mbiri 29:16, 17) Davide anaona ubale wake ndi Yehova kukhala wofunika kwambiri. Anadziŵanso kufunika kotumikira Mulungu “ndi mtima wangwiro ndi moyo waufulu,” ndipo anali wosangalala kuchita zimenezo. (1 Mbiri 28:9) Makhalidwe omwewo anachititsanso Akristu oyambirira kusonyeza mtima wopatsa.

Yehova Ndiye Wopatsa Kwambiri

Yehova ndiye chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani ya kupatsa. Iye ndi wachikondi ndipo amaganizira anthu moti “amakwezera dzuŵa lake pa oipa ndi pa abwino, namavumbitsira mvula pa olungama ndi pa osalungama.” (Mateyu 5:45) Amapatsa anthu onse “moyo ndi mpweya ndi zinthu zonse.” (Machitidwe 17:25) Inde, monga mmene wophunzira Yakobo anafotokozera, “mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro zichokera Kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko.”​—Yakobo 1:17.

Mphatso yaikulu kwambiri imene Yehova anatipatsa ndi kutumiza “Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Palibe amene anganene kuti akuyenerera mphatso imeneyo, “pakuti onse anachimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu.” (Aroma 3:23, 24; 1 Yohane 4:9, 10) Dipo la Kristu ndiwo maziko ndi njira ya Mulungu yoperekera “mphatso yakeyake yosatheka kuneneka” yomwe ndi “chisomo choposa cha Mulungu.” (2 Akorinto 9:14, 15) Pofuna kuyamikira mphatso ya Mulungu imeneyi, Paulo anaika pa malo oyamba m’moyo wake ntchito ‘yochitira umboni Uthenga Wabwino wa chisomo cha Mulungu.’ (Machitidwe 20:24) Iye anazindikiranso kuti chinali cholinga cha Mulungu kuti “anthu onse apulumuke, nafike pozindikira choonadi.”​—1 Timoteo 2:4.

Masiku ano, zimenezi zikukwaniritsidwa kudzera mu ntchito yaikulu yolalikira ndi kuphunzitsa imene tsopano ikuchitika m’mayiko okwana 234 padziko lonse lapansi. Yesu ananeneratu za kuwonjezeka kumeneku pamene anati: “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.” (Mateyu 24:14) Inde, “Uthenga Wabwino uyenera uyambe kulalikidwa kwa anthu a mitundu yonse.” (Marko 13:10) Chaka chatha anthu olengeza uthenga wabwino opitirira sikisi miliyoni anathera maola 1,202,381,302 pa ntchito imeneyi ndipo anachititsa maphunziro a Baibulo opitirira 5,300,000. Chifukwa chakuti miyoyo ili pangozi, kuphunzitsa uthenga wabwino n’kofunika kwambiri.​—Aroma 10:13-15; 1 Akorinto 1:21.

Zofalitsa mamiliyoni ambiri monga mabaibulo, mabuku, ndi mabulosha zikusindikizidwa chaka chilichonse kuti tithandize anthu amene akufuna choonadi cha m’Baibulo. Kuwonjezera apo, magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! oposa wani biliyoni akusindikizidwa chaka chilichonse. Pamene anthu akumvetsera uthenga wabwino, Nyumba za Ufumu ndi Malo a Misonkhano ambiri a Mboni za Yehova amene anthu amaphunzirirako Baibulo akumangidwa. Misonkhano ya dera ndi misonkhano yapadera ya tsiku limodzi, ndiponso misonkhano yachigawo imakonzedwa chaka chilichonse. Palinso ntchito yosalekeza yophunzitsa amishonale, oyang’anira oyendayenda, akulu, ndi atumiki otumikira. Tikuthokoza Yehova pokonza zonsezi kudzera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45-47) Timasangalala kwambiri tikamasonyeza kuyamikira kwathu kwa Iye!

Kusonyeza Kuyamikira Yehova

Monga momwe zinalili pomanga kachisi ndiponso pofuna kupeza zosoŵa za Akristu oyambirira mu mpingo wachikristu, ndalama zogwiritsira ntchito zimachokera pa zopereka za ufulu. Komabe, tiyenera kukumbukira kuti palibe amene angalemeretse Yehova, Mwini zinthu zonse. (1 Mbiri 29:14; Hagai 2:8) Choncho, zimene timapereka ndi umboni wa chikondi chathu kwa Yehova ndiponso kufunitsitsa kwathu kuti tipititse patsogolo kulambira koona. Paulo anati kupatsa kumeneku “kuchita mwa ife chiyamiko cha kwa Mulungu.” (2 Akorinto 9:8-13) Yehova amalimbikitsa kupatsa kumeneku chifukwa kumasonyeza kuti tili ndi mtima wopatsa ndiponso kuti timamukonda. Yehova adzadalitsa anthu amene ndi opatsa ndiponso amene amamudalira ndipo zinthu zidzawayendera bwino kwambiri mwauzimu. (Deuteronomo 11:13-15; Miyambo 3:9, 10; 11:25) Yesu anatitsimikizira kuti tidzapeza chimwemwe pamene ananena kuti: “Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.”​—Machitidwe 20:35.

Akristu amene ali ndi mtima wopatsa sadikira kuti anthu asoŵe kaye zinthu zinazake asanawathandize. Mmalomwake, amayesetsa kupeza mipata kuti ‘achitire onse chokoma, koma makamaka iwo a pa banja la chikhulupiriro.’ (Agalatiya 6:10) Pofuna kulimbikitsa kupatsa kovomerezeka ndi Mulungu, Paulo analemba kuti: “Musaiwale kuchitira chokoma ndi kugaŵira ena; pakuti nsembe zotere Mulungu akondwera nazo.” (Ahebri 13:16) Kugwiritsa ntchito zinthu zathu, nthaŵi yathu, mphamvu zathu, ndi chuma chathu kuti tithandize ena ndiponso kuti tipititse patsogolo kulambira koona kumakondweretsa kwambiri Yehova Mulungu. Ndithudi, iye amakonda mtima wopatsa.

[Bokosi/​Chithunzi pamasamba 28, 29]

Njira Zimene Ena Amasankha Popereka

ZOPEREKA ZA NTCHITO YA PADZIKO LONSE

Ambiri amapatula, kapena kulinganiza, ndalama zimene amaika m’mabokosi a zopereka olembedwa kuti: “Zopereka za Ntchito ya Padziko Lonse​—Mateyu 24:14.”

Mwezi uliwonse mipingo imatumiza ndalama zimenezi ku ofesi ya Mboni za Yehova imene imayang’anira ntchito ya m’dziko lawo. Mungatumizenso mwachindunji ndalama zopereka modzifunira ku Accounting Office, Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, P. O. Box 30749, Lilongwe 3, Malawi, kapena ku ofesi ya nthambi ya m’dziko lanu. Mukalemba macheke, musonyeze kuti alandire a “Watch Tower.” Mungaperekenso majuwelo kapena zinthu zina zamtengo wapatali. Tumizani pamodzi ndi kalata yachidule yofotokoza kuti zimenezo mwapereka monga mphatso yeniyeni.

MAKONZEDWE APADERA A ZOPEREKA

Ndalama zingaperekedwe pa makonzedwe apadera akuti, ngati woperekayo akuzifunanso, angam’bwezere zoperekazo. Kuti mudziŵe zambiri, lemberani ku Accounting Office pa adiresi imene tasonyeza pamwambapa.

KUPATSA KOLINGANIZA

Kuwonjezera pa mphatso zenizeni ndi ndalama zoperekedwa pa makonzedwe apadera, palinso njira zina zoperekera zinthu zopititsa patsogolo utumiki wa Ufumu padziko lonse. Zina mwa izo ndi izi:

Inshuwalansi: Watch Tower Society ingalembetsedwe kuti ndiyo idzapatsidwe phindu la inshuwalansi kapena penshoni.

Chuma ndi Ndalama Zoikizidwa: Chuma ndi ndalama zoikizidwa m’malonda ena zingaperekedwe kukhala za Watch Tower Society monga mphatso yeniyeni.

Malo: Malo oti angagulitsidwe angaperekedwe monga mphatso yeniyeni kapena, ngati ali malo oti mukhoza kumangapo nyumba, mwa kusunga malowo amene mwiniwake angapitirizebe kukhalapo pamene ali ndi moyo. Lankhulani ndi ofesi ya nthambi ya m’dziko lanu musanakonze pangano la malo alionse.

Chuma Chamasiye: Chuma kapena ndalama zingakhale choloŵa cha Watch Tower Society kudzera m’pangano la amene adzatenga chuma chamasiye lochitidwa mwalamulo.

Ngati mukufuna kudziŵa zambiri za alionse mwa makonzedwe a kupatsa kolinganiza ameneŵa, lankhulani ndi a ku Accounting Office patelefoni kapena lemberani ku adiresi imene ili pansipa kapena ku ofesi ya Mboni za Yehova ya m’dziko lanu.

Accounting Office

Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania

P. O. Box 30749 Lilongwe 3

Malawi

Telefoni: 01762111.

[Chithunzi patsamba 26]

Kodi n’chiyani chinalimbikitsa Akristu oyambirira kukhala opatsa?