Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Pali Amene Tingamukhulupirire?

Kodi Pali Amene Tingamukhulupirire?

Kodi Pali Amene Tingamukhulupirire?

MPANDA waukulu umene unagaŵa mzinda wa Berlin ataugwetsa mu 1989, zinsinsi zina zimene zinali zobisika kwambiri zinaululika. Mwachitsanzo, Lydia * anatulukira kuti panthaŵi imene dziko la East Germany linali kulamulidwa ndi boma la chipani cha Socialist, Dipatimenti ya Boma Yoona za Chitetezo yomwe ankaitcha Stasi inasunga faelo imene analembamo zimene iye ankachita pamoyo wake zimene sizinafunike kuti ena azidziŵe. Ngakhale kuti Lydia anadabwa kwambiri kumva za faeloyo, anakhumudwa kwambiri kudziŵa kuti mwamuna wake ndi amene anali kuwauza a Stasi zimene iye anali kuchita. Munthu amene anayenera kumukhulupirira kwambiri ndi amenenso anamuika pamavuto.

Robert anali mwamuna wachikulire amene anali “kulemekeza ndi kukhulupirira kwambiri” dokotala wake, linatero lipoti la nyuzipepala ya The Times ya ku London. Dokotalayo akuti anali “wokoma mtima ndiponso wachifundo.” Ndiyeno Robert anamwalira mosayembekezeka. Kodi anadwala mtima kapena matenda a sitiroko? Ayi. Akuluakulu a boma anapeza kuti dokotalayo anapita kunyumba kwa Robert ndipo anamubaya jakisoni wa mankhwala akupha, Robert ndi banja lake osadziŵa. Mwachionekere, Robert anaphedwa ndi munthu amene anali kumukhulupirira kwambiri.

Lydia ndi Robert anagwiritsidwa fuwa lamoto ndi anthu amene anali kuwakhulupirira ndipo zotsatira zake zinali zomvetsa chisoni kwambiri. M’nkhani zina, zotsatira zake sizikhala zomvetsa chisoni moteremu. Komabe, sichachilendo kukhumudwitsidwa ndi munthu amene tinali kumukhulupirira. Lipoti limene bungwe lochita kafukufuku lalikulu ku Germany lotchedwa Allensbacher Jahrbuch der Demoskopie 1998-2002 linafalitsa, linati atachita kafukufuku, anthu 86 mwa anthu 100 alionse amene anayankha mafunso anati anakhumudwitsidwapo ndi munthu amene anali kumukhulupirira. Mwina inunso zinakuchitikiranipo zimenezi. Motero, sitingadabwe kuti nyuzipepala ya ku Switzerland ya Neue Zürcher Zeitung mu 2002 inanena kuti “m’mayiko olemera a azungu, maubwenzi oti anthu onse akukhulupirirana akhala akucheperachepera kwa zaka zambiri.”

Kumayamba Pang’onopang’ono Koma Kumawonongeka Mofulumira

Kodi kukhulupirira ena n’kutani? Buku lina lotanthauzira mawu limati kukhulupirira ena kumatanthauza kukhulupirira kuti munthuyo ndi woona mtima ndiponso kuti sadzachita dala zinthu zimene zingakukhumudwitseni. Kukhulupirira ena kumayamba pang’onopang’ono koma kungawonongedwe mofulumira. Popeza ambiri aona kuti agwiritsidwa mwala ndi munthu amene anali kumukhulupirira, kodi tingadabwe kuona kuti anthu zikuwavuta kukhulupirira anzawo? Malinga ndi zotsatira za kafukufuku zimene anazifalitsa ku Germany mu 2002, ananena kuti “achinyamata ochepa okha, osakwana pa wachinyamata m’modzi mwa atatu alionse, ndi amene amakhulupirira anthu ena.”

Tingadzifunse kuti: ‘Kodi tingakhulupiriredi winawake? Kodi ndi nzeru kukhulupirira munthu wina ngakhale kuti akhoza kutikhumudwitsa?’

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Tasintha mayina.

[Mawu Otsindika patsamba 3]

Kafukufuku wina anasonyeza kuti anthu 86 mwa anthu 100 alionse amene anayankha mafunso anati anakhumudwitsidwapo ndi munthu amene anali kumukhulupirira