Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Asanaphunzire ndi Ataphunzira Mfundo za m’Baibulo Zinamusintha

Asanaphunzire ndi Ataphunzira Mfundo za m’Baibulo Zinamusintha

“Yandikirani kwa Mulungu, Ndipo Adzayandikira kwa Inu”

Asanaphunzire ndi Ataphunzira Mfundo za m’Baibulo Zinamusintha

ALI mnyamata, Adrian anali waukali kwambiri ndiponso wokwiyakwiya. Mtima wake wapachala unkamupangitsa kukhala waukali kwambiri. Ankamwa moŵa, kusuta ndiponso anali wamakhalidwe oipa kwambiri. Adrian ankadziŵika monga munthu wa gulu linalake lamakhalidwe oipa ndipo anadzilemba chizindikiro chosonyeza kuti ndi munthu wachiwawa kwambiri. Pofotokoza za zaka zimenezo, iye anati: “Ndinkameta panke yeniyeni, n’kuthira mankhwala kuti tsitsi liimirire, ndipo nthaŵi zina ndinkalisintha kukhala lofiira kapena lamtundu winawake.” Adrian anaboolanso mphuno yake.

Adrian anakaloŵa nyumba ina yowonongeka, n’kumakhalamo ndi anyamata anzake angapo opanduka. Kumeneko ankamwa moŵa ndiponso kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. “Ndinkagwiritsa ntchito mankhwala oletsedwa komanso ndinkadzibaya jekeseni wa mankhwala a Valium ndiponso china chilichonse chomwe ndapeza,” anatero Adrian. “Ndikasoŵa mankhwala kapenanso gluu woti ndingafwenkhe, ndinkapopa mafuta m’galimoto za anthu pogwiritsa ntchito paipi, n’kuledzera nawo.” Adrian anali munthu woopsa kwambiri komanso wachiwawa koopsa chifukwa choti ankachitira anthu ziwawa m’misewu. Anthu ambiri sankamufuna. Panthaŵi imodzimodziyi, khalidwe lake linaitana anthu oipa.

Pang’ono ndi pang’ono, Adrian anazindikira kuti omwe ankati ndi anzakewo ankangofuna kum’dyera masuku pamutu. Komanso anaona kuti ‘palibe chomwe wapindulapo chifukwa cha ukali ndiponso kuchita zachiwawa.’ Poganiza kuti iye ndi wosafunika ndiponso chifukwa chokhumudwa, iye anasiyana ndi anzakewo. Atapeza magazini ya Nsanja ya Olonda pamalo ena a zomangamanga, anachita chidwi ndi uthenga wake wa m’Baibulo, ndipo izi zinapangitsa kuti ayambe kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Adrian anavomera ndi mtima wonse pempho lakuti: “Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu.” (Yakobo 4:8) Chotsatira chake chinali chakuti, posapita nthaŵi yaitali, Adrian anaona kufunika koyamba kugwiritsa ntchito mfundo za m’Malemba Opatulika.

Kulidziŵa bwino Baibulo kunakhudza kwambiri chikumbumtima cha Adrian ndipo kunam’sintha moyo wake. Anathandizidwa kukhala munthu wougwira mtima n’kuphunzira kukhala wodziletsa. Mothandizidwa ndi mphamvu ya Mawu a Mulungu, khalidwe la Adrian linasintha kwambiri.​—Ahebri 4:12.

Komano, kodi Baibulo lingakhale bwanji ndi mphamvu yotere? Kudziŵa Malemba kumatithandiza ‘kuvala umunthu watsopano.’ (Aefeso 4:24) Inde, khalidwe lathu limasintha mwa kugwiritsa ntchito zinthu zolondola za m’Baibulo. Koma kodi kudziŵa zinthu zimenezo kumawasintha bwanji anthu?

Choyamba, Baibulo limafotokoza makhalidwe osafunika omwe munthu ayenera kusiya. (Miyambo 6:16-19) Chachiŵiri, Malemba amatilimbikitsa kuonetsa makhalidwe abwino a mzimu woyera wa Mulungu. Makhalidweŵa ndi monga “chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso.”​—Agalatiya 5:22, 23.

Kumvetsa zinthu zimene Mulungu amafuna kunathandiza Adrian kuti adzipende ndi kuona makhalidwe omwe afunika kukhala nawo ndiponso omwe afunika kuwasiya. (Yakobo 1:22-25) Koma ichi chinali chiyambi chabe. Kuwonjezera pa kudziŵa zinthu zolondola, panafunika china chom’limbikitsa Adrian kuti asinthe.

Adrian anaphunzira kuti umunthu watsopano wabwino kwambiriwu umapangidwa ‘monga mwa chifaniziro cha Iye amene anaulenga.’ (Akolose 3:10) Anazindikira kuti khalidwe la Mkristu liyenera kufanana ndi la Mulungu. (Aefeso 5:1) Mwa kuphunzira Baibulo, Adrian anaona mmene Yehova amachitira zinthu ndi anthu ndipo anazindikira makhalidwe abwino kwambiri a Mulungu, monga chikondi, kukoma mtima, ubwino, chifundo, ndiponso chilungamo. Kudziŵa zimenezi kunalimbikitsa Adrian kuti azikonda Mulungu ndiponso kuyesetsa kuti Yehova amuyanje.​—Mateyu 22:37.

Patapita nthaŵi ndiponso ndi thandizo la mzimu woyera wa Mulungu, Adrian anachepetsa mkwiyo wake. Iye pamodzi ndi mkazi wake tsopano ali kalikiliki kuthandiza ena kusintha miyoyo yawo mothandizidwa ndi zimene zili m’Baibulo. “Mosiyana ndi ambiri mwa azinzanga omwe tsopano anamwalira, ine ndili moyo ndipo ndili ndi banja lachimwemwe,” anatero Adrian. Iye ndi umboni wooneka ndi maso wosonyeza kuti mphamvu ya Baibulo ingasinthe moyo wa munthu n’kukhala wabwino.

[Mawu Otsindika patsamba 25]

“Palibe chomwe ndinapindulapo chifukwa cha ukali ndiponso kuchita zachiwawa”

[Bokosi patsamba 25]

Mfundo za m’Baibulo Zikugwira Ntchito

Nazi zina mwa mfundo za m’Baibulo zomwe zathandiza anthu ambiri aukali komanso achiwawa kukhala anthu amtendere:

“Khalani ndi mtendere ndi anthu onse. Musabwezere choipa, okondedwa, koma patukani pamkwiyo.” (Aroma 12:18, 19) Lekerani Mulungu kugamula kuti ndi liti ndipo ndi ndani ayenera kulangidwa. Iye angachite zimenezo akudziŵa zonse zokhudza zomwe zachitikazo, ndipo chilango chilichonse chomwe angapereke chidzakhala chachilungamo.

“Kwiyani, koma musachimwe; dzuŵa lisaloŵe muli chikwiyire, ndiponso musam’patse malo Mdyerekezi.” (Aefeso 4:26, 27) Nthaŵi zina munthu angakhale ndi zifukwa zomveka zokwiyira. Zikatero, iye sayenera kukhala “chikwiyire.” Chifukwa? Chifukwa chakuti zimenezi zingam’pangitse kuchita chinthu china choipa, ndipo ‘angapatse malo Mdyerekezi,’ zomwe zingam’danitse ndi Yehova Mulungu.

“Leka kupsa mtima, nutaye mkwiyo: Usavutike mtima ungachite choipa.” (Salmo 37:8) Kulephera kulamulira mkwiyo kungapangitse munthu kumangochita zinthu mwachisawawa. Munthu akakwiya, kaŵirikaŵiri amatha kunena kapena kuchita zinthu zopweteka anthu ena okhudzidwa ndi nkhaniyo.