‘Lunjikani Nawo Bwino Mawu a Mulungu’
‘Lunjikani Nawo Bwino Mawu a Mulungu’
“Uchite changu kudzionetsera kwa Mulungu wovomerezeka, wantchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi, wolunjika nawo bwino mawu a choonadi.”—2 TIMOTEO 2:15.
1, 2. (a) N’chifukwa chiyani ogwira ntchito amafunika zida? (b) Kodi Akristu ali ndi ntchito yotani, ndipo kodi amasonyeza bwanji kuti amafuna Ufumu choyamba?
OGWIRA ntchito amafunika zida zowathandiza kugwira ntchito yawo. Koma, kungokhala ndi chida china chilichonse sikokwanira. Wogwira ntchito amafunika chida choyenera, ndipo ayenera kuchigwiritsa ntchito moyenera. Mwachitsanzo, ngati pokhoma nyumba mukufuna kulumikiza matabwa aŵiri, mufunika zinthu zambiri osati nyundo ndi misomali basi. Mufunika kudziŵa mmene mungakhomere msomali pathabwa popanda kupinda msomaliwo. Kukhoma msomali pathabwa usakudziŵa kugwiritsa ntchito nyundo kungakhale kovuta kwambiri, ngakhale kopweteketsa mtima. Koma zida tikazigwiritsa ntchito moyenera, zimathandiza ntchito kuyenda bwino.
2 Monga Akristu, tili ndi ntchito yoti tigwire. Ndi ntchito yofunika kwambiri. Yesu Kristu analimbikitsa otsatira ake ‘kuthanga afuna Ufumu.’ (Mateyu 6:33) Kodi tingachite bwanji zimenezi? Njira imodzi ndiyo kukhala achangu mu ntchito yolalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira. Njira ina ndiyo yotenga Mawu a Mulungu kukhala maziko a utumiki wathu. Njira yachitatu ndiyo kukhala ndi khalidwe labwino. (Mateyu 24:14; 28:19, 20; Machitidwe 8:25; 1 Petro 2:12) Kuti tikhale ogwira mtima ndiponso osangalala mu ntchito yachikristu imeneyi, tifunika zida zoyenera ndiponso kudziŵa kuzigwiritsa ntchito bwino. Pambali imeneyi, mtumwi Paulo anapereka chitsanzo chabwino kwambiri monga wantchito wachikristu, ndipo analimbikitsa okhulupirira anzake kuti am’tsanzire. (1 Akorinto 11:1; 15:10) Choncho, kodi tingaphunzire chiyani kwa Paulo, yemwe anali wantchito mnzathu?
Paulo Anali Wolengeza Ufumu Wachangu
3. N’chifukwa chiyani tinganene kuti mtumwi Paulo anali wachangu pogwira ntchito ya Ufumu?
3 Kodi Paulo anali wantchito wotani? Mosakayikira anali wachangu. Paulo anayesetsa kwambiri, kufalitsa uthenga wabwino m’gawo lalikulu, m’dera lozungulira nyanja ya Mediterranean. Pofotokoza chifukwa chake anali kulengeza Ufumu 1 Akorinto 9:16) Kodi Paulo ankangofuna kupulumutsa moyo wake wokha? Ayi. Iye sanali munthu wodzikonda. Koma, ankafuna kuti anthu enanso apindule ndi uthenga wabwino. Iye analemba kuti: “Ndichita zonse chifukwa cha Uthenga Wabwino, kuti ndikakhale woyanjana nawo [“ndikaugaŵire kwa ena,” NW].”—1 Akorinto 9:23.
mwachangu, mtumwi wosatopa ameneyu anati: “Pakuti ngati ndilalikira Uthenga Wabwino ndilibe kanthu kakudzitamandira; pakuti chondikakamiza ndigwidwa nacho; pakuti tsoka ine ngati sindilalikira Uthenga Wabwino.” (4. Kodi ndi chida chiti chimene antchito achikristu amachigwiritsa ntchito kwambiri?
4 Mtumwi Paulo anali wantchito wodzichepetsa amene anazindikira kuti sangadalire luso lake lokha. Monga momwe kalipentala amafunikira nyundo, Paulo anafunika chida choyenera kuti akhomereze choonadi cha Mulungu m’mitima ya omvera ake. Kodi ndi chida chiti chimene ankachigwiritsa ntchito kwambiri? Chinali Mawu a Mulungu, Malemba Opatulika. Mofananamo, Baibulo ndi chida chachikulu chimene timagwiritsa ntchito kuti chitithandize kupanga ophunzira.
5. Kuti tikhale atumiki ogwira mtima, kodi tiyenera kuchita chiyani kuwonjezera pa kugwira mawu m’malemba?
5 Paulo ankadziŵa kuti kulunjika nawo bwino Mawu a Mulungu kumafuna zambiri osati kungogwira mawu m’Baibulo. Iye ankagwiritsa ntchito mfundo ‘zokopa.’ (Machitidwe 28:23) Motani? Paulo anagwiritsa ntchito bwino zedi Mawu olembedwa a Mulungu pofuna kuwakhutiritsa maganizo anthu ambiri kuti alabadire choonadi cha Ufumu. Iye anali kukambirana nawo. Kwa miyezi itatu m’sunagoge ku Efeso, Paulo anali ‘kutsutsa [“kukamba nkhani,” NW] ndi kukopa ponena za Ufumu wa Mulungu.’ Ngakhale kuti “ena anaumitsa mtima ndi kusamvera,” ena anamvetsera. Chifukwa cha utumiki wa Paulo ku Efeso, “mawu a Ambuye anachuluka mwamphamvu nalakika.”—Machitidwe 19:8, 9, 20.
6, 7. Kodi Paulo analemekeza bwanji utumiki wake, ndipo kodi ife tingachite motani zimenezi?
6 Paulo monga wolengeza Ufumu wachangu, ‘analemekeza utumiki wake.’ (Aroma 11:13) Motani? Iye sankafuna kudzitchukitsa; komanso sankachita manyazi chifukwa chodziŵika monga mmodzi wa antchito anzake a Mulungu. M’malomwake, anaona utumiki wake kukhala mwayi wapamwamba zedi. Paulo anagwiritsa ntchito Mawu a Mulungu mwaluso ndiponso mogwira mtima. Ntchito yake yobala zipatso inalimbikitsa ena kuchita utumiki wawo mokwanira. Mwanjira imeneyinso, utumiki wake unalemekezedwa.
7 Mofanana ndi Paulo, tingalemekeze ntchito yathu monga atumiki pogwiritsa ntchito kwambiri Mawu a Mulungu ndiponso mogwira mtima. M’mbali zonse za utumiki wathu wakumunda, cholinga chathu chizikhala kuuza anthu ambiri mfundo inayake ya m’Malemba. Kodi tingachite bwanji zimenezi mokopa? Onani njira zitatu zofunika izi: (1) Kambiranani Mawu a Mulungu mwanjira yoti aziwalemekeza. (2) Fotokozani mosamala zimene Baibulo limanena ndiponso kugwirizana kwake ndi zimene mukukamba. (3) Kambiranani Malemba mogwira mtima.
8. Kodi ndi zida zotithandiza kulalikira Ufumu ziti zimene tili nazo masiku ano, ndipo kodi mwazigwiritsa ntchito bwanji?
8 Olengeza Ufumu amasiku ano ali ndi zida zimene Paulo analibe panthaŵi ya utumiki wake. Zimenezi ndi zida monga mabuku, magazini, mabulosha, timapepala toitanira anthu, mathirakiti, ndiponso makaseti a wailesi ndi matepi a vidiyo. Kumayambiriro a m’ma 1900, olengeza Ufumu anali kugwiritsanso ntchito makadi aumboni, magalamafoni, galimoto zokhala ndi zokuzira mawu, ndiponso kuulutsa mawu pawailesi. Komabe, chida chathu chachikulu ndi Baibulo, ndipo chida chofunika kwambiri chimenechi tiyenera kuchigwiritsa ntchito bwino ndiponso moyenera.
Mawu a Mulungu Ayenera Kukhala Maziko a Utumiki Wathu
9, 10. Pankhani yogwiritsa ntchito Mawu a Mulungu, kodi tingaphunzire chiyani pa zimene Paulo analangiza Timoteo?
9 Kodi tingagwiritse ntchito bwanji Mawu a Mulungu monga chida champhamvu? Mwa 2 Timoteo 2:15) Kodi ‘kulunjika nawo bwino mawu a choonadi’ kumaphatikizapo chiyani?
kumvera mawu amene Paulo anauza wantchito mnzake Timoteo, akuti: “Uchite changu kudzionetsera kwa Mulungu wovomerezeka, wantchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi, wolunjika nawo bwino mawu a choonadi.” (10 Mawu achigiriki omasulidwa kuti “kulunjika bwino” kwenikweni amatanthauza “kudula mosakhotetsa” kapena “kukonza njira mosakhotetsa.” Mawu ameneŵa m’Malemba Achigiriki Achikristu anangogwiritsidwa ntchito pa zimene Paulo analangiza Timoteo basi. Mawu omweŵa angagwiritsidwe ntchito pofotokoza kulima mzere wosakhota m’munda. Mwachionekere mzere wokhotakhota ungakhale wochititsa manyazi kwa mlimi wodziŵa bwino ntchito yake. Kuti akhale “wantchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi,” Timoteo anakumbutsidwa kuti sikololeka kuchoka pa ziphunzitso zoona za m’Mawu a Mulungu. Timoteo sanafunike kuloŵetsapo maganizo ake pa zimene anali kuphunzitsa. Anafunika kulalikira ndi kuphunzitsa za m’Malemba zokhazokha. (2 Timoteo 4:2-4) Mwanjira imeneyi, anthu oona mtima akanadziŵa momwe Yehova amaonera nkhani zosiyanasiyana, osati kutengera nzeru za dziko. (Akolose 2:4, 8) Zimenezi zikugwiranso ntchito masiku ano.
Khalidwe Lathu Liyenera Kukhala Labwino
11, 12. Kodi khalidwe lathu limakhudza bwanji nkhani ya kulunjika nawo bwino Mawu a Mulungu?
11 Tiyenera kuchita zambiri osati kungolunjika nawo bwino Mawu a Mulungu mwa kulengeza mfundo zake. Khalidwe lathu liyenera kugwirizana ndi mfundozo. “Ndife antchito anzake a Mulungu,” choncho tisakhale antchito achinyengo. (1 Akorinto 3:9) Mawu a Mulungu amati: “Ndiwe tsono wakuphunzitsa wina, kodi ulibe kudziphunzitsa mwini? Iwe wakulalikira kuti munthu asabe, kodi ulikuba mwini wekha? Iwe wakunena kuti munthu asachite chigololo, kodi umachita chigololo mwini wekha? Iwe wakudana nawo mafano, umafunkha za m’kachisi kodi?” (Aroma 2:21, 22) Chotero, monga antchito anzake a Mulungu amasiku ano, njira imodzi imene tingalunjikire nawo bwino Mawu a Mulungu ndi mwa kumvera langizo ili: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; um’lemekeze m’njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.”—Miyambo 3:5, 6.
12 Kodi tingayembekezere zotani ngati tilunjika nawo bwino Mawu a Mulungu? Taonani mphamvu yomwe Mawu olembedwa a Mulungu angakhale nayo pamoyo wa anthu oona mtima.
Mawu a Mulungu Ali ndi Mphamvu Yosintha Moyo wa Munthu
13. Kodi kugwiritsa ntchito Mawu a Mulungu kungam’chititse chiyani munthu?
13 Tikawagwiritsa ntchito monga umboni wodalirika, Mawu a Mulungu ali ndi mphamvu imene imathandiza anthu kusintha kwambiri moyo wawo. Paulo anaona mawu a Mulungu akugwira ntchito ndipo anaona mmene anathandizira anthu amene anakhala Akristu ku Tesalonika wakale. Chotero anawauza kuti: “Ife tiyamika Mulungu kosalekeza, kuti, pakulandira mawu a Uthenga wa Mulungu, simunawalandira monga mawu a anthu, komatu monga momwe ali ndithu, mawu a Mulungu, amenenso achita mwa inu okhulupirira.” (1 Atesalonika 2:13) Kwa Akristu amenewo—inde otsatira oona onse a Kristu—nzeru zochepa za anthu sizingafanane ndi nzeru zapamwamba za Mulungu. (Yesaya 55:9) Atesalonika ‘analandira mawuwo m’chisautso chambiri, ndi chimwemwe cha Mzimu Woyera’ ndipo anakhala zitsanzo kwa okhulupirira ena.—1 Atesalonika 1:5-7.
14, 15. Kodi uthenga wa m’Mawu a Mulungu ndi wamphamvu motani, ndipo n’chifukwa chiyani?
14 Mawu a Mulungu ndi amphamvu, monga alili Mwiniwake, Yehova. Amachokera kwa “Mulungu wamoyo,” amene mwa mawu ake “zakumwamba zinalengedwa,” ndipo mawu amenewo nthaŵi zonse ‘amakula mmene anawatumizira.’ (Ahebri 3:12; Salmo 33:6; Yesaya 55:11) Katswiri wina wa maphunziro a Baibulo anati: “Mulungu sadzilekanitsa ndi Mawu ake. Sawakana ngati kuti palibe kugwirizana pakati pa mawuwo ndi iye. . . . Choncho mawu akewo si akufa, sangokhala osachita chilichonse; chifukwa ndi ogwirizana kwambiri ndi Mulungu wamoyo.”
15 Kodi uthenga wa m’Mawu a Mulungu ndi wamphamvu motani? Ndi wamphamvu kwambiri. Moyenerera, Paulo analemba kuti: “Mawu a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita [“amphamvu,” NW], ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse, napyoza kufikira kugaŵira moyo ndi mzimu, ndi zimfundo ndi mafuta a m’mafupa, nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima.”—Ahebri 4:12.
16. Kodi Mawu a Mulungu angasinthe munthu mpaka pati?
16 Uthenga wa m’Mawu olembedwa a Mulungu ndi ‘wakuthwa kuposa lupanga lakuthwa konsekonse.’ Chotero, uli ndi mphamvu yaikulu kuposa chida chilichonse chopangidwa ndi anthu. Mawu a Mulungu amapyoza mbali zamkati mwa munthu ndipo angasinthe umunthu wake wamkati, zimene zingakhudze mmene amaganizira ndi zimene amakonda, kuti akhale wantchito wamakhalidwe amene Mulungu amawavomereza. Ndi chida champhamvu bwanji!
17. Fotokozani mphamvu yosintha anthu ya Mawu a Mulungu.
17 Mawu a Mulungu amavumbula mmene munthu alili mu mtima mosiyana ndi zimene iye amaganiza kuti ndi mmene alili kapena zimene amaonetsa kwa anthu ena. (1 Samueli 16:7) Ngakhale munthu woipa nthaŵi zina angabise umunthu wake wamkati ponamizira kukhala wabwino ndiponso wopembedza kwambiri. Anthu achinyengo amadzibisa pa zifukwa zoipa. Anthu odzikuza amanyengezera kudzichepetsa pofuna kuti anthu aziwapatsa ulemu. Komabe, mwa kuvumbula zimene zilidi mu mtima, Mawu a Mulungu angamulimbikitse kwambiri munthu wodzichepetsa kuvula umunthu wake wakale ndi ‘kuvala umunthu watsopano, umene unalengedwa monga mwa Mulungu, m’chilungamo, ndi m’chiyero cha choonadi.’ (Aefeso 4:22-24) Zimene Mawu a Mulungu amaphunzitsa zingasinthenso anthu amantha kukhala Mboni za Yehova zolimba mtima ndiponso olengeza Ufumu achangu.—Yeremiya 1:6-9.
18, 19. Kuchokera m’ndime zimenezi kapena zimene inuyo munakumana nazo mu utumiki wakumunda, fotokozani momwe mfundo za m’Malemba zingasinthire maganizo a munthu.
18 Mphamvu yosintha anthu ya Mawu a Mulungu imathandiza anthu kulikonse. Mwachitsanzo, olengeza Ufumu a ku Phnom Penh, m’dziko la Cambodia, anali kukalalikira kaŵiri pamwezi ku chigawo cha Kompong Cham. Mbusa wina wamkazi wachipembedzo chakumeneko atamva abusa anzake akutsutsa Mboni za Yehova, anakonza zokumana ndi Mbonizo zikadzabweranso m’chigawocho. Iye anawafunsa mafunso ambiri okhudza nkhani za mapwando a masiku atchuthi ndipo anamvetsera mwatcheru pamene anali kukambirana naye kuchokera m’Malemba. Ndiyeno anati: “Tsopano ndadziŵa kuti n’zabodza zimene abusa anzanga anali kunena za inu. Ankati inu simugwiritsa ntchito Baibulo, koma m’maŵa uno mwagwiritsa ntchito Baibulo lokha basi.”
19 Mayi ameneyu anapitiriza kukambirana Baibulo ndi Mbonizo ndipo sanasiye ngakhale kuti anali kumuopseza kuti amuchotsa pa udindo wake waubusa. Anauza mnzake zinthu za m’Malemba zimene anali kukambirana ndi Mboni, amene kenako anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mbonizo. Mnzakeyo zinamufikadi pamtima kwambiri zimene anali kuphunzira moti pa mapemphero ena a tchalitchi chomwe amapita, anafika ponena kuti, “Tiziphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova.” Patangopita nthaŵi pang’ono, amene kale anali mbusa uja, ndi anthu enanso anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova.
20. Kodi chitsanzo cha mayi wa ku Ghana chikusonyeza bwanji mphamvu ya Mawu a Mulungu?
20 Mphamvu ya Mawu a Mulungu ikuonekanso pankhani ya Paulina, mayi wa ku Ghana. Wolengeza Ufumu wanthaŵi zonse anali kuphunzira naye Baibulo pogwiritsa ntchito buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. * Paulina anali paukwati wamitala ndipo anazindikira kuti anafunika kusintha, koma mwamuna wake ndi achibale ake onse anam’tsutsa mwaukali. Agogo ake, woweruza milandu m’khoti lalikulu omwenso ndi mkulu wampingo, anayesa kum’gwetsa mphwayi pogwiritsa ntchito molakwika Mateyu 19:4-6. Woweruza milanduyu anali kuoneka kuti akunena zoona, koma Paulina anazindikira msanga kuti zimenezi zinali kufanana ndi zimene Satana anachita popotoza Malemba pamene anali kuyesa Yesu Kristu. (Mateyu 4:5-7) Anakumbukira mawu omveka bwino amene Yesu ananena pankhani yaukwati, kuti Mulungu analenga anthu mwamuna ndi mkazi, osati mwamuna ndi akazi, ndiponso kuti aŵiri osati atatu, adzakhala thupi limodzi. Anatsimikiza mtima kuchita zofuna zake ndipo mapeto ake anasudzulidwa ukwati wamitalawo. Posapita nthaŵi, anali wolengeza Ufumu wobatizidwa ndi wosangalala.
Pitirizani Kulunjika Nawo Bwino Mawu a Mulungu
21, 22. (a) Kodi cholinga chathu chiyenera kukhala chotani monga olengeza Ufumu? (b) Kodi tikambirana zotani mu nkhani yotsatira?
21 Mawu olembedwa a Mulungu ndi chida champhamvudi choti tizigwiritsa ntchito pothandiza anthu ena kusintha moyo wawo kuti ayandikire kwa Yehova. (Yakobo 4:8) Monga momwe antchito aluso amagwiritsa ntchito zida kuti ntchito iyende bwino, chikhaletu cholinga chathu kuyesetsa kugwiritsa ntchito mwaluso Mawu a Mulungu, Baibulo, mu ntchito imene Mulungu watipatsa monga olengeza Ufumu.
22 Kodi tingagwiritse ntchito bwanji Malemba mogwira mtima kwambiri mu ntchito yathu yopanga ophunzira? Njira imodzi ndi mwa kukulitsa luso lathu monga aphunzitsi ogwira mtima. Ikani maganizo pankhani yotsatira, chifukwa ikutchula njira zophunzitsira ndi kuthandizira ena kulabadira uthenga wa Ufumu.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 20 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
Kodi Mukukumbukira?
• Kodi olengeza Ufumu ali ndi zida ziti?
• Kodi Paulo anali chitsanzo chabwino motani monga wogwira ntchito ya Ufumu?
• Kodi n’chiyani chimafunikanso kuti tilunjike nawo bwino Mawu a Mulungu?
• Kodi Mawu olembedwa a Yehova ndi amphamvu motani?
[Mafunso]
[Zithunzi patsamba 10]
Zina mwa zida zimene Akristu amagwiritsa ntchito polengeza Ufumu