Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi Akristu ayenera kuiona bwanji nkhani yovala miyala ya miyezi yobadwira?

Kwa mitundu ina ya anthu, miyala ya miyezi yobadwira imakhudzana ndi mwezi umene munthu anabadwa. Mkristu aliyense payekha angasankhe kaya kuvala mphete ya miyala inayake yamtengo wapatali kapena ayi. (Agalatiya 6:5) Posankha zimenezo, pali mfundo zofunika kwambiri kuzilingalira.

Buku lakuti Encyclopaedia Britannica linanena kuti mwala wa mwezi wobadwira ndi “mwala wamtengo wapatali wokhudzana ndi tsiku limene munthu anabadwa, umene anthu nthaŵi zambiri amati munthu akavala amakhala wamwayi kapena wathanzi labwino.” Buku lomweli linatinso: “Kwanthaŵi yaitali okhulupirira nyenyezi akhala akunena kuti miyala ina yamtengo wapatali imakhala ndi mphamvu ya mizimu.”

Makamaka kale anthu ambiri ankakhulupirira kuti mwala wa mwezi wobadwira umam’patsa mwayi munthu amene wavalayo. Kodi Mkristu woona amakhulupirira zimenezi? Ayi, popeza amadziŵa kuti Yehova analanga anthu amene anamusiya Iye n’kumakhulupirira “mulungu wamwayi.”​—Yesaya 65:11.

M’zaka za m’ma 500 mpaka 1500, olosera za m’tsogolo anasankha mwala wa mwezi uliwonse pachaka. Ankalimbikitsa anthu kuvala mwala wa mwezi umene anabadwa, poganiza kuti umateteza wovalayo ku mavuto. Koma malinga ndi Malemba n’kulakwa kuti Mkristu atsatire zonena za openduza, chifukwa Baibulo limaletsa zimenezo.​—Deuteronomo 18:9-12.

Sikoyenera kwa Akristu kuona mphete ngati yofunika mwapadera chifukwa chakuti ili ndi mwala wa mwezi wobadwira. Mboni za Yehova sizikumbukira masiku akubadwa. Izi zili choncho chifukwa chakuti mapwando ameneŵa amaika maganizo kwambiri pa munthu ndipo masiku akubadwa amene amatchulidwa m’Baibulo ndi a olamulira amene sanali kutumikira Mulungu.​—Genesis 40:20; Mateyu 14:6-10.

Anthu ena amaganiza kuti kuvala mphete yokhala ndi mwala wa mwezi wobadwira kumathandiza wovalayo kukhala ndi makhalidwe abwino. Komabe, Akristu oona sakhulupirira zimenezi, chifukwa amadziŵa kuti munthu umavala ‘umunthu watsopano’ mwa mphamvu ya mzimu woyera wa Mulungu ndiponso mwa kutsatira mfundo zamakhalidwe abwino za m’Malemba.​—Aefeso 4:22-24.

Mfundo yaikulu yagona pa cholinga chovalira mpheteyo. Posankha kuvala mphete yokhala ndi mwala wa mwezi wobadwira, Mkristu angadzifunse kuti, ‘Kodi ndikufuna kuvala mphete imeneyi kokha chifukwa chakuti mwalawo umandisangalatsa, ngakhale kuti ndi wokhudzana ndi mwezi wobadwira? Kapena kodi ndatengera maganizo amene anthu okhulupirira mizimu amanena za miyala imeneyi?’

Mkristu ayenera kupenda mtima wake kuti aone cholinga chake pochita zinthu. Malemba amati: “Tchinjiriza mtima wako koposa zonse uzisunga; pakuti magwero a moyo atulukamo.” (Miyambo 4:23) Posankha zochita pankhani yokhudza miyala ya miyezi yobadwira, Mkristu aliyense angachite bwino kuona cholinga chake povala mphete yoteroyo ndiponso mmene zingam’khudzire iye ndi anthu ena ngati atachita zimenezo.​—Aroma 14:13.