Chifukwa Choyenera Chokhulupirira Mulungu
Chifukwa Choyenera Chokhulupirira Mulungu
BUKU lina la ku Korea lotchedwa 31 Reasons Why Young People Leave the Church (Zifukwa 31 Zimene Zimachititsa Achinyamata Kusiya Kupita Kutchalitchi) linati anthu ambiri amasiya kupita kutchalitchi chifukwa chosapeza mayankho ogwira mtima a mafunso awo. Mwachitsanzo, ena amafunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani anthu okhulupirira Mulungu amavutika?’ ndiponso ‘N’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira zilizonse zimene matchalitchi amaphunzitsa pamene zinthu zambiri zimene amaphunzitsazo n’zosokoneza ndiponso zotsutsana?’
Chifukwa chokhumudwa ndi mayankho amene atsogoleri awo a tchalitchi anawapatsa, ambiri amangoganiza kuti m’Baibulo mulibe mayankho a mafunso awowo. Mtsogoleri wa tchalitchi akapereka yankho limene lili lochokera m’mutu mwake, zotsatirapo zake n’zoti munthu samvetsa ndipo mwina amapandukira Mulungu ndi Baibulo.
Zimenezo n’zimene zinachitikira Abel, amene anakulira mumpingo wa Lutheran, ku South Africa. Iye atakumbukira zimene anali kuphunzira anati: “Tchalitchi chimaphunzitsa kuti aliyense amene wamwalira ‘watengedwa’ ndi Mulungu. Koma sindinali kumvetsetsa chifukwa chimene Mulungu wachikondi ‘angatengere’ makolo kuwalekanitsa ndi ana awo. M’midzi ya ku Africa kuno, kumene ine ndinakulira, sitipha nkhuku ya anapiye mpaka anapiyewo atakula. Tikaona kuti n’gombe ili ndi bere, sitipha mpaka mwana wang’ombe uja abadwe ndiponso asiye kuyamwa. Sindinkamvetsa kuti n’chifukwa chiyani Mulungu wachikondi sachita chifundo ngati chimenecho kwa anthu.”
Aram, wa ku Canada, analinso ndi maganizo ofanana ndi amenewo. Iye anati: “Pamene ndinali ndi zaka 13, bambo anga anamwalira. Pamwambo wamaliro, mbusa wina wotchuka anafotokoza kuti Mulungu anafuna kuti bambo anga afe n’cholinga choti akayandikane ndi Mulungu kumwamba. Mbusayo anati: ‘Mulungu amatenga anthu abwino, chifukwa chakuti Mulunguyo amakonda anthu olungama.’ Sindinamvetse mmene Mulungu angakhalire wodzikonda choncho.”
Kenako Abel ndi Aram anakumana ndi Mboni za Yehova, anaphunzira nazo Baibulo, ndipo, pomalizira pake, anapeza mayankho a mafunso awo. Anayamba kumukonda Mulungu ndi kumukhulupirira kwambiri. Pomalizira pake anapatulira miyoyo yawo kwa Yehova n’kukhala atumiki ake okhulupirika.
Kudziŵa Zinthu Molondola N’kofunika Kwambiri Kuti Munthu Akhulupirire Mulungu
Kodi nkhani za anthu aŵiriŵa zikutiphunzitsa chiyani? Zikutiphunzitsa kuti, munthu amafunika kudziŵa Baibulo molondola kuti akhulupirire Mulungu. Mtumwi Paulo anauza Akristu a mu mzinda wakale wa Filipi kuti: “Ndipo ichi ndipempha, kuti chikondi chanu chisefukire chionjezere, m’chidziŵitso [cholondola, NW], ndi kuzindikira konse.” (Afilipi 1:9) Panopa Paulo anasonyeza kuti, munthu amafunika kudziŵa Mulungu molondola ndi kuzindikira zofuna zake kuti am’konde ndiponso kuti akonde okhulupirira anzake.
Zimenezi n’zomveka, chifukwa chakuti chinthu choyamba chofunika kuti munthu akhulupirire ndiponso adalire munthu wina ndicho kum’dziŵa bwino munthuyo. Ngati mwam’dziŵa bwino kwambiri ndiponso molondola, mumam’daliranso kwambiri. Mofanana ndi zimenezi, mumafunikanso kudziŵa zinthu molondola kuti muyambe kukhulupirira Mulungu. Paulo anati: “Chikhulupiriro ndicho chikhazikitso cha zinthu zoyembekezeka, chiyesero cha zinthu zosapenyeka.” (Ahebri 11:1) Kukhulupirira Mulungu popanda kudziŵa Baibulo molondola n’kofanana ndi nyumba yomanga ndi zitsononkho. Kungoikankha pang’ono imagwa.
Kuphunzira Baibulo kungakuthandizeni kupeza mayankho a mafunso ofanana ndi funso limene linathetsa nzeru Abel ndi Aram loti, N’chifukwa chiyani anthu amafa? Baibulo limafotokoza kuti “uchimo unaloŵa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.” (Aroma 5:12) Anthu amakalamba ndi kufa, osati chifukwa chakuti Mulungu amawatenga kuti akakhale naye, koma chifukwa chakuti Adamu anachimwa. (Genesis 2:16, 17; 3:6, 17-19) Kuonjezera apo, Baibulo limafotokoza za chiyembekezo chenicheni chimene Yehova Mulungu akutipatsa. Kudzera mwa Mwana wake, Yesu Kristu, Mulungu akutipatsa chiyembekezo choti adzaukitsa anthu ochimwa.—Yohane 5:28, 29; Machitidwe 24:15.
Kuti tithe kumvetsetsa zoona pankhani ya kuuka kwa akufa, m’Baibulo muli zitsanzo zingapo za anthu amene Yesu anawaukitsa kwa akufa. (Luka 7:11-17; 8:40-56; Yohane 11:17-45) Mukamaŵerenga nkhani za m’Baibulo zimenezi, onani mmene mabwenzi ndi achibale a anthu oukitsidwawo anasangalalira. Onaninso kuti zimenezi zinawapangitsa kulemekeza Mulungu ndi kukhulupirira Yesu.
Kum’dziŵa molondola Mulungu ndi zofuna zake kungakhudzenso anthu m’njira yofananayo masiku ano. Anthu ambiri m’mbuyomu anali osokonezeka, olemedwa, ndiponso ngakhale okhumudwa chifukwa cha mafunso ofunika amene sankatha kuwapezera mayankho ogwira mtima. Koma pamene anaphunzira Baibulo, anapeza mayankho amenewo, ndipo zimenezo zinasintha miyoyo yawo kwambiri.
Chikondi Ndicho Chifukwa Chachikulu Chotumikira Mulungu
Ngakhale kuti kudziŵa Mulungu molondola n’kofunika kuti munthu akhulupirire Mulungu, pamafunika zambiri kuti munthu akhale wofunitsitsa kumumvera ndi kumutumikira. Pamene Yesu anafunsidwa kuti lamulo lalikulu kwambiri la Mulungu ndi liti, anayankha kuti: “Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mphamvu yako yonse.” (Marko 12:30) Ngati munthu akonda Mulungu mofanana ndi mmene Yesu ananeneramu, adzakhala wofunitsitsa kumvera ndi kutumikira Mulungu. Kodi inu mumam’konda choncho Mulungu?
Rachel, amene watumikira monga m’mishonale ku Korea kwa zaka makumi angapo, anafotokoza zifukwa zotsatirazi zimene zimamuchititsa kukhala ndi chikhulupiriro: “Ndimaganizira mmene Yehova amaperekera zinthu mooloŵa manja kwa zolengedwa zake, kukhululuka kwake akamachita
zinthu ndi anthu ake, ndiponso kufunitsitsa kwake kuti ifeyo tipindule mwa kutiuza zimene amafuna kuti tizichita. Zonsezi zimachititsa kuti chikondi changa kwa Mulungu chikule. Ndipo chikondi chimenecho chimandichititsa kuti ndizifuna kumutumikira.”Martha, mkazi wamasiye wa ku Germany, watumikira Yehova kwa zaka 48. Iye anati: “N’chifukwa chiyani ndimatumikira Yehova? Chifukwa chakuti ndimamukonda. Madzulo alionse ndimapemphera kwa Yehova ndipo ndimamuuza mmene ndilili woyamikira chifukwa cha madalitso ake onse, makamaka nsembe ya dipo.”
Inde, kukonda Mulungu kumatichititsa kufuna kumutumikira kuchokera pansi pamtima. Koma kodi munthu amakhala bwanji ndi chikondi choterocho? Chinthu chachikulu kwambiri chimene chingatiyambitse kukonda Mulungu ndicho kuyamikira kwambiri chikondi chimene iyeyo watisonyeza. Taonani mawu abwino otsatiraŵa a m’Baibulo otikumbutsa zimenezi: “Iye wosakonda sazindikira Mulungu; chifukwa Mulungu ndiye chikondi. Umo chidaoneka chikondi cha Mulungu mwa ife, kuti Mulungu anam’tuma Mwana wake wobadwa yekha, alowe m’dziko lapansi, kuti tikhale ndi moyo mwa Iye. Umo muli chikondi, sikuti ife tinakonda Mulungu, koma kuti Iye anatikonda ife, ndipo anatuma Mwana wake akhale chiombolo chifukwa cha machimo athu.”—1 Yohane 4:8-10.
Kodi mumamvetsetsa kukula kwa chikondi chimenechi? Tangoyerekezerani kuti mukumira mumtsinje umene madzi ake akuthamanga kwambiri ndipo munthu wina waika moyo wake pangozi kuti akupulumutseni. Kodi mungamuiŵale munthu ameneyo, kapena mungakhale woyamikira kwambiri kwa iye? Kodi simungakhale wofunitsitsa kum’chitira chilichonse chomwe mungathe? Chikondi chimene Mulungu anasonyeza potipatsa Mwana wake, Yesu Kristu monga nsembe ya dipo n’chachikulu kwambiri kuposa pamenepo. (Yohane 3:16; Aroma 8:38, 39) Mtima wanu ukakhudzidwa ndi chikondi cha Mulungu, mudzakhala wofunitsitsa kumukonda ndi kumutumikira ndi mtima wanu wonse.
Madalitso Tsopano Lino ndi M’tsogolo
Ngakhale kuti kukonda kwathu Mulungu kuyenera kukhala chifukwa chachikulu kwambiri chochitira chifuniro chake, n’zokondweretsa kudziŵa Ahebri 11:6.
kuti Mulungu amadalitsa anthu amene amamutumikira. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Wopanda chikhulupiriro sikutheka kum’kondweretsa; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphotho iwo akum’funa Iye.”—Anthu amene amakonda ndi kumvera Mulungu amawadalitsadi kwambiri. Ambiri amakhala ndi thanzi labwino chifukwa chotsatira mfundo za m’Baibulo. (Miyambo 23:20, 21; 2 Akorinto 7:1) Anthu amene amagwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo kuti akhale oona mtima komanso olimbikira ntchito mabwana awo amawadalira, ndipo chifukwa cha zimenezi amakhalitsa pantchito. (Akolose 3:23) Chifukwa chokhulupirira Yehova, atumiki a Mulungu amakhala ndi mtendere wa mumtima ngakhale panthaŵi zovuta. (Miyambo 28:25; Afilipi 4:6, 7) Koposa zonse, akuyembekezera mosakayikira dalitso lodzakhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso akubwerayo wa padziko lapansi.—Salmo 37:11, 29.
Kodi anthu amene Yehova akuwadalitsa m’njira yoteroyo amamuona bwanji? Jacqueline, Mkristu wa ku Canada, anafotokoza kuyamikira kwake Mulungu motere: “Nthaŵi zonse amatipatsa mphatso zabwino kwambiri, ndipo amatipatsa chiyembekezo cha moyo wosatha. “ Abel, amene tamutchula koyambirira uja, anafotokoza maganizo ake motere: “Chiyembekezo chodzakhala ndi moyo kosatha m’paradaiso padziko lapansi chinali chatsopano kwa ine, ndipo ndikufuna kwambiri kudzakhalamo. Komabe, ngakhale kukanakhala kuti kulibe Paradaiso, ndikanakondabe kusonyeza chikondi changa kwa Mulungu mwa kumutumikira.”
Nanunso Mukhoza Kukhala ndi Chikhulupiriro Chenicheni
Baibulo limati: “Yehova wa makamu . . . aweruza molungama, . . . ayesa impso ndi mtima.” (Yeremiya 11:20) Zoonadi, Yehova amaona zobisika zamkati mwathu. Aliyense ayenera kudzifunsa zifukwa zimene amakhulupirira Mulungu. M’mbuyomu, zikhulupiriro ndi maganizo olakwika onena za Mulungu zingakhale zitachititsa munthu kuchita zinthu molakwika. Koma kudziŵa Baibulo molondola kungathandize munthu kukhala ndi unansi woyenera ndi Mlengi, Yehova Mulungu.—1 Timoteo 2:3, 4.
Mboni za Yehova zikuthandiza anthu kum’dziŵa Mulungu molondola mwa kuphunzira Baibulo ndi anthu pa nyumba pawo kwaulere. (Mateyu 28:20) Anthu ambiri amene alola kuti athandizidwe m’njira imeneyi tsopano anayamba kum’konda Mulungu ndi kum’khulupirira kuchokeradi pansi pa mtima. Mwa kuphunzira Baibulo, apeza “nzeru yeniyeni ndi kulingalira,” zimene zimawathandiza ‘kuyenda m’njira yawo osaopa’ m’masiku ovuta ano. (Miyambo 3:21-23) Koposa zonse, tsopano ali ndi chiyembekezo ‘chokhazikika ndi cholimba’ cham’tsogolo. (Ahebri 6:19) Nanunso mungathe kukhala ndi chikhulupiriro chenicheni ndiponso kusangalala ndi madalitso ameneŵa.
[Bokosi patsamba 6]
Mafunso Othetsa Nzeru Amene Ankafunika Mayankho
“Panthaŵi imene ndinali kuphunzira za chipatala kuti ndidzakhale dokotala, ndinaona anthu abwino akubuula ndi ululu chifukwa cha matenda ndi masoka. Ngati Mulungu aliko, n’chifukwa chiyani zinthu zimenezi zimachitika? Kodi chipembedzo changokhala njira yopezera mtendere wa mumtima?”—Anatero Munthu amene kale anali wa tchalitchi cha Presbyterian ku Korea.
“Nthaŵi zambiri ndinkadzifunsa kuti kodi bambo anga, amene anali chidakwa, anapita kumoto kapena kumwamba? Ndinkaopa kwambiri anthu akufa ndiponso moto wa helo. Sindinkatha kumvetsa kuti kodi Mulungu wachikondi angatumize bwanji munthu kuti akazunzike kosatha kumoto.”—Anatero munthu amene kale anali Mkatolika ku Brazil.
“Kodi tsogolo la dziko lapansi ndi anthu n’lotani? Kodi anthu adzatha bwanji kukhala ndi moyo kosatha? Kodi anthu adzapeza bwanji mtendere weniweni?”—Anatero munthu amene kale anali Mkatolika ku Germany.
“Chiphunzitso choti munthu akamwalira amabadwanso sichinali chomveka kwa ine. Nyama sizilambira, choncho ngati pa chifukwa chinachake munthu wabadwanso ngati nyama kuti ulipire machimo ako, kodi ungakonze bwanji zinthu kuti usadzabadwenso ngati nyama?”—Anatero munthu amene kale anali Mhindu ku South Africa.
“Ndinakulira m’banja lachipembedzo cha Chikomfyushasi, ndipo ndinkachita nawo mwambo wogoneka pansi mizimu yamakolo. Pamene ndinkaika nawo zinthu zansembe patebulo ndi kuwerama pansi, ndinkadzifunsa ngati makolo athu akufawo amabwera kudzadya chakudyacho ndiponso kudzationa tikuwaweramira.”—Anatero munthu amene kale anali m’chipembedzo cha Chikomfyushasi ku Korea.
Anthu onseŵa anapeza mayankho a mafunso awo ataphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova.