Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Khalani Oyamikira’

‘Khalani Oyamikira’

‘Khalani Oyamikira’

“Mtendere wa Kristu uchite ufumu m’mitima yanu . . . ndipo khalani akuyamika.”​—AKOLOSE 3:15.

1. Kodi timaona kusiyana kotani pakati pa mpingo wachikristu ndi dzikoli limene Satana akulamulira?

M’MIPINGO ya Mboni za Yehova yokwana 94,600 padziko lonse, timapezamo anthu a mtima woyamikira. Msonkhano uliwonse umayamba ndiponso umatha ndi pemphero limene limakhala ndi mawu oyamikira Yehova. Nthaŵi zambiri timamva ana ndi achikulire ndiponso amene angokhala kumene Mboni komanso amene akhala Mboni kwa nthaŵi yaitali akunena kuti “zikomo kwambiri,” “zikomo,” kapena mawu ena ofanana ndi ameneŵa pamene akulambira pamodzi ndi kucheza mosangalala. (Salmo 133:1) Zimenezi n’zosiyana kwambiri ndi mtima wodzikonda umene uli ndi anthu ambiri omwe ‘sam’dziŵa Mulungu, ndipo samvera Uthenga Wabwino.’ (2 Atesalonika 1:8) Tikukhala m’dziko limene anthu sayamikira. Ndipo sitidabwa tikamaona zimenezi poganizira yemwe ali mulungu wa dziko lino, Satana Mdyerekezi, yemwe amalimbikitsa kwambiri kudzikonda kuposa wina aliyense, ndipo kunyada kwake ndi mtima wake wopanduka waloŵerera mwa anthu.​—Yohane 8:44; 2 Akorinto 4:4; 1 Yohane 5:19.

2. Kodi tifunika kumvera chenjezo liti, ndipo kodi tikambirana mafunso ati?

2 Popeza tili m’dziko la Satana, tifunika kusamala kwambiri kuti tisaipitsidwe ndi maganizo a dzikoli. M’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino, mtumwi Paulo anakumbutsa Akristu a ku Efeso kuti: “Munayendamo kale, monga mwa mayendedwe a dziko lapansi lino, monga mwa mkulu wa ulamuliro wa mlengalenga, wa mzimu wakuchita tsopano mwa ana a kusamvera; amene ife tonsenso tinagonera pakati pawo kale, m’zilakolako za thupi lathu, ndi kuchita zifuniro za thupi, ndi za maganizo, ndipo tinali ana a mkwiyo chibadwire, monganso otsalawo.” (Aefeso 2:2, 3) Zimenezi zilinso choncho kwa anthu ambiri masiku ano. Motero, kodi tingatani kuti tikhalebe ndi mtima woyamikira? Kodi Yehova amapereka thandizo lotani? Kodi tingasonyeze m’njira ziti kuti ndifedi oyamikira?

Zifukwa Zokhalira Oyamikira

3. Kodi tikuyamikira Yehova chifukwa cha zinthu ziti?

3 Tiyenera kuyamikira Yehova Mulungu, Mlengi ndi Wotipatsa Moyo, makamaka tikaganizira zina mwa mphatso zambirimbiri zimene watipatsa. (Yakobo 1:17) Tsiku ndi tsiku timayamikira Yehova kuti tili ndi moyo. (Salmo 36:9) Tikayang’ana uku ndi uku timaona umboni wochuluka wosonyeza ntchito za Yehova, monga dzuŵa, mwezi ndi nyenyezi. Dziko lathu lapansili lomwe lili ndi mchere wa pansi pa nthaka umene umathandiza zamoyo, m’mlengalenga momwe ndi mokonzedwa bwino kwambiri ndipo muli mipweya yofunika kwambiri, ndiponso kayendedwe ka zinthu za m’chilengedwe kogometsa kamene kamachitika mobwerezabwereza, zonsezi zimatsimikizira kuti tifunika kuyamikira Atate wathu wachikondi wakumwamba. Mfumu Davide inaimba kuti: “Inu, Yehova, Mulungu wanga, zodabwiza zanu mudazichita n’zambiri, ndipo zolingirira zanu za pa ife; palibe wina wozifotokozera Inu; ndikazisimba ndi kuzitchula, zindichulukira kuziŵerenga.”​—Salmo 40:5.

4. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyamikira Yehova chifukwa cha ubale wosangalatsa umene tili nawo m’mipingo yathu?

4 Ngakhale kuti atumiki a Yehova masiku ano sakukhala m’paradaiso weniweni, akusangalala kukhala m’paradaiso wauzimu. M’Nyumba za Ufumu zathu ndiponso pamisonkhano yaikulu, timaona okhulupirira anzathu akusonyeza chipatso cha mzimu wa Mulungu. Inde, polalikira kwa anthu amene akungodziŵa pang’ono chabe za chipembedzo kapena amene sadziŵa n’komwe, Mboni zina zimatchula zimene Paulo anafotokoza m’kalata yake kwa Agalatiya. Iwo amayamba kaye aŵerenga za “ntchito za thupi” n’kufunsa anthu amene akulankhula nawowo kuti anene zimene aona. (Agalatiya 5:19-23) Ambiri amavomereza kuti zimenezi n’zimene anthu ambiri akuchita masiku ano. Akawasonyeza mmene chipatso cha mzimu wa Mulungu achifotokozera ndiponso akawaitana kufika ku Nyumba ya Ufumu kuti akadzionere okha umboni wa chipatso cha mzimuwo, ambiri amavomereza mwamsanga kuti: “Mulungu ali ndithu mwa inu.” (1 Akorinto 14:25) Ndipo zimenezi sizingochitika ku Nyumba ya Ufumu ya m’dera lanu yokha. Kulikonse kumene mungapite, mukakumana ndi Mboni iliyonse mwa Mboni za Yehova zoposa 6,000,000, mudzaona mtima wosangalala ndi wachimwemwe woterowo. Inde, ubale wolimbikitsawu ukutipatsa chifukwa choyamikirira Yehova, amene amapereka mzimu wake kuti zimenezi zitheke.​—Zefaniya 3:9; Aefeso 3:20, 21.

5, 6. Kodi tingasonyeze bwanji kuyamikira Mulungu chifukwa cha mphatso yaikulu kwambiri ya dipo?

5 Mphatso yaikulu kwambiri ndiponso yangwiro imene Yehova wapereka ndiyo Mwana wake, Yesu, amene nsembe ya dipo inaperekedwa kudzera mwa iye. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Ngati Mulungu anatikonda ife kotero, ifenso tiyenera kukondana wina ndi mnzake.” (1 Yohane 4:11) Inde, timayamikira dipo mwa kukonda Yehova ndi kumuyamikira komanso mwa kuchita zinthu zimene zimasonyeza kuti timakonda anthu ena.​—Mateyu 22:37-39.

6 Tingaphunzire zambiri pankhani yoyamikira mwa kuona mmene Yehova anachitira zinthu ndi Aisrayeli akale. Yehova anaphunzitsa anthuwo zinthu zambiri pogwiritsa ntchito Chilamulo, chimene anapatsa mtunduwo kudzera mwa Mose. Kudzera mu “nzeru ndi choonadi cha m’Chilamulo,” tingaphunzire zambiri zimene zidzatithandiza kutsatira langizo la Paulo lakuti: “Khalani akuyamika.”​—Aroma 2:20, NW; Akolose 3:15.

Zinthu Zitatu Zimene Tikuphunzira M’Chilamulo cha Mose

7. Kodi chakhumi chinapereka bwanji mwayi kwa Aisrayeli woti asonyeze kuyamikira kwawo Yehova?

7 M’Chilamulo cha Mose, Yehova anapereka njira zitatu zimene Aisrayeli akanasonyezera kuyamikira kochokera pansi pa mtima chifukwa cha zabwino zimene anali kuwachitira. Choyamba, panali chakhumi. Gawo limodzi la magawo khumi a zinthu zimene anakolola, pamodzi ndi “limodzi la magawo khumi lonse la ng’ombe, kapena la nkhosa, kapena la mbuzi,” linayenera kukhala “lopatulikira Yehova.” (Levitiko 27:30-32) Aisrayeli ankati akamvera, Yehova anali kuwadalitsa kwambiri. “Mubwere nalo limodzi limodzi lonse la khumi, ku nyumba yosungiramo, kuti m’nyumba mwanga mukhale chakudya; ndipo mundiyese nako tsono, ati Yehova wa makamu, ngati sindikutsegulirani mazenera a kumwamba, ndi kukutsanulirani mdalitso wakuti adzasoŵeka malo akuulandira.”​—Malaki 3:10.

8. Kodi zopereka zaufulu zinasiyana bwanji ndi chakhumi?

8 Chachiŵiri, kuwonjezera pa kupereka chakhumi, Yehova anakonza zoti Aisrayeli azipereka zopereka zaufulu. Analangiza Mose kuuza Aisrayeli kuti: “Pamene muloŵa m’dziko limene ndilikukuloŵetsani, kudzali, pakudya inu mkate wa m’dzikolo, muzikwezera Yehova nsembe yokweza [“ya chopereka,” NW].” Zina mwa zipatso zoundukula za “kamtanda” kawo anayenera kuzipereka monga ‘chopereka kwa Yehova’ m’mibadwo yawo yonse. Onani kuti sanawauze kuti azipereka zochuluka mwakuti ayi. (Numeri 15:18-21) Koma pamene Aisrayeli anapereka zopereka posonyeza kuyamikira, anali otsimikizira kuti Yehova awadalitsa. Zofanana ndi zimenezi tikuziona m’nkhani ya kachisi wa m’masomphenya a Ezekieli. Timaŵerenga kuti: “Zoyamba za zipatso zoyamba za zinthu zili zonse, ndi nsembe zokweza [“zopereka,” NW] zilizonse za nsembe zanu zonse zokweza n’za ansembe; muperekenso ufa wanu woyamba kwa wansembe, kuti mdalitso ukhalebe pa nyumba yako.”​—Ezekieli 44:30.

9. Kodi Yehova anaphunzitsa chiyani kudzera pa nkhani ya khunkha?

9 Chachitatu, Yehova anakonza za khunkha. Mulungu analangiza kuti: “Pakukolola dzinthu za m’dziko mwanu, usamakololetsa m’mphepete mwa munda wako, nusamakunkha khunkha. Usamakunkha khunkha la m’munda wako wamphesa, usamazitola zidagwazi za m’munda wako wamphesa; uzisiyire wosauka ndi mlendo; ine ndine Yehova Mulungu wanu.” (Levitiko 19:9, 10) Apanso, sananene kuti munthu azisiya zochuluka bwanji. Mwiisrayeli aliyense anali ndi ufulu wosankha kuti asiya khunkha lochuluka bwanji kuti anthu osauka apeze. Moyenera, Mfumu yanzeru Solomo inati: “Wochitira waumphaŵi chifundo abwereka Yehova; adzam’bwezera chokoma chakecho.” (Miyambo 19:17) Motero, Yehova anaphunzitsa chifundo ndi kuganizira anthu ovutika.

10. Kodi n’chiyani chinachitikira Aisrayeli pamene analephera kusonyeza kuyamikira?

10 Yehova anadalitsa Aisrayeli pamene anali kumvera popereka chakhumi, zopereka zaufulu, ndiponso kusiyira osauka khunkha. Koma pamene Aisrayeli analephera kusonyeza kuyamikira, Yehova sanakondwere nawo. Zimenezi zinawabweretsera mavuto ndipo mapeto ake anatengedwa ukapolo. (2 Mbiri 36:17-21) Motero, kodi tikuphunzirapo chiyani?

Kusonyeza Kuyamikira Kwathu

11. Kodi njira yaikulu imene tingasonyezere kuyamikira Yehova ndi iti?

11 Njira yaikulu imene tingalemekezere Yehova ndiponso kusonyeza kuyamikira kwathu ndiyo kupereka “nsembe” monganso mmene zinalili kale. N’zoona kuti monga Akristu, sititsatira Chilamulo cha Mose, sitifunikira kupereka nsembe za nyama kapena zokolola. (Akolose 2:14) Komabe, mtumwi Paulo analangiza Akristu achihebri kuti: “Tipereke chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake.” (Ahebri 13:15) Mwa kugwiritsa ntchito luso lathu ndi zinthu zimene tili nazo kupereka nsembe yoyamika Yehova, kaya pochita utumiki kwa anthu onse kapena ‘posonkhana’ ndi Akristu anzathu, tingasonyeze kuyamikira ndi mtima wonse Atate wathu wakumwamba wachikondi, Yehova Mulungu. (Salmo 26:12) Pochita zimenezo, kodi tingaphunzire chiyani pa njira zimene Aisrayeli anali kutsatira posonyeza kuyamikira Yehova?

12. Malinga ndi udindo umene tili nawo monga Akristu, kodi tingaphunzire chiyani pankhani ya chakhumi?

12 Choyamba, monga mmene taonera, chakhumi sichinali choti munthu angasankhe kuchita kapena kusachita. Mwiisrayeli aliyense anayenera kupereka chakhumi. Ife monga Akristu, tili ndi udindo wochita nawo utumiki ndi kupezeka pa misonkhano yachikristu. Zimenezi munthu sachita kusankha kuti achita kapena ayi. Mu ulosi wake waukulu wonena za nthaŵi ya mapeto, Yesu ananena mwatchutchutchu kuti: “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.” (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Pankhani ya misonkhano yachikristu, mtumwi Paulo anauziridwa kulemba kuti: “Tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika.” (Ahebri 10:24, 25) Timasonyeza kuyamikira Yehova tikamachita mosangalala ntchito yathu yolalikira ndi kuphunzitsa komanso tikamasonkhana ndi abale athu nthaŵi zonse pa misonkhano ya mpingo, n’kumaona zimenezi monga mwayi ndiponso zinthu zopatsa ulemu.

13. Kodi tikuphunzira chiyani pa zopereka zaufulu ndi khunkha?

13 Ndiponso, tingapindule mwa kuona njira zina ziŵiri zija zimene Aisrayeli anali kusonyezera kuyamikira, zopereka zaufulu ndi khunkha. Mosiyana ndi chakhumi, chimene ananena kuti munthu afunika kupereka zochuluka mwakuti, zopereka zaufulu ndi khunkha sananene kuti munthu afunika kupereka zochuluka bwanji. M’malo mwake, zinapereka mpata woti kukula kwa kuyamikira kumene mtumiki wa Yehova anali nako mumtima mwake kumulimbikitse kuchitapo kanthu. Mofanana ndi zimenezi, ngakhale kuti timadziŵa kuti kuchita nawo utumiki ndiponso kupezeka pa misonkhano yachikristu ndi udindo wofunika kwambiri wa mtumiki wa Yehova aliyense, kodi timachita zimenezi ndi mtima wonse komanso mofunitsitsa? Kodi timaona zimenezi monga mwayi wosonyezera kuyamikira kwathu ndi mtima wonse chifukwa cha zonse zimene Yehova watichitira? Kodi timachita zimenezi ndi mtima wonse, mmene tingathere malinga ndi momwe zinthu zilili pa moyo wathu? Kapena kodi timangoziona monga udindo umene tifunika kuukwaniritsa basi? Ameneŵa ndi mafunso oti tiyenera kudziyankhira patokha. Mtumwi Paulo anafotokoza zimenezi motere: “Yense ayesere ntchito yake ya iye yekha, ndipo pamenepo adzakhala nako kudzitamandira chifukwa cha iye yekha, si chifukwa cha wina.”​—Agalatiya 6:4.

14. Kodi Yehova amafuna kuti tichite zotani pom’tumikira?

14 Yehova Mulungu amadziŵa bwinobwino mmene zinthu zilili pa moyo wathu. Amadziŵa zimene sitingathe kuchita. Iye amayamikira nsembe zimene atumiki ake amapereka ndi mtima wonse, kaya zikhale zambiri kapena zochepa. Sayembekezera kuti tonse tidzapereka mofanana, ndipo sitingathe kutero. Pofotokoza za kupereka zinthu, mtumwi Paulo anauza Akristu a ku Korinto kuti: “Ngati chivomerezocho chili pomwepo, munthu alandiridwa monga momwe ali nacho, si monga chim’soŵa.” (2 Akorinto 8:12) Mfundo imeneyi ikugwiranso ntchito chimodzimodzi pa kutumikira kwathu Mulungu. Chimene chimachititsa Yehova kusangalala ndi utumiki wathu si kuchuluka kwa zimene tikuchita koma mmene tikuchitira zimenezo, kuchita mosangalala ndiponso ndi mtima wonse.​—Salmo 100:1-5; Akolose 3:23.

Yambitsani Ndipo Pitirizani Kukhala ndi Mtima wa Upainiya

15, 16. (a) Kodi upainiya ukugwirizana bwanji ndi kuyamikira? (b) Kodi anthu amene sangathe kuchita upainiya angasonyeze bwanji mtima wa upainiya?

15 Njira yopindulitsa yomwe tingasonyezere kuyamikira kwathu Yehova ndiyo kuyamba utumiki wa nthaŵi zonse. Chifukwa cha kukonda Yehova ndiponso kuyamikira chifundo chake, atumiki odzipatulira ambiri asintha zinthu zambiri pamoyo wawo kuti apeze nthaŵi yochuluka yotumikira Yehova. Ena akukwanitsa kutumikira monga apainiya okhazikika ndipo amalalikira uthenga wabwino ndi kuphunzitsa anthu choonadi kwa maola 70 pa avareji mwezi uliwonse. Ena amene sangathe kufika pa maola ameneŵa chifukwa cha zovuta zina, amakonza zolalikira kwa maola 50 pamwezi nthaŵi ndi nthaŵi monga apainiya othandiza.

16 Koma bwanji nanga atumiki ambiri a Yehova amene sangakwanitse kuchita upainiya wokhazikika kapena wothandiza? Angasonyeze kuyamikira mwa kuyambitsa ndi kupitiriza kukhala ndi mtima wa upainiya. Motani? Mwa kulimbikitsa amene angathe kuchita upainiyawo, kulimbikitsa ana awo kuti akhale ndi mtima wofuna kuti ntchito yawo idzakhale utumiki wa nthaŵi zonse, ndiponso mwa kulalikira mwakhama monga mmene angathere. Zimene timachita muutumiki wathu zimadalira pa kukula kwa kuyamikira kumene kuli mumtima mwathu chifukwa cha zimene Yehova watichitira, zimene akutichitira, ndiponso zimene adzatichitira m’tsogolo.

Kusonyeza Kuyamikira ndi “Chuma” Chathu

17, 18. (a) Kodi tingasonyeze bwanji kuyamikira ndi “chuma” chathu? (b) Kodi Yesu ananena chiyani za chopereka cha mkazi wamasiye, ndipo chifukwa chiyani?

17 Lemba la Miyambo 3:9 limati: “Lemekeza Yehova ndi chuma chako, ndi zinthu zako zonse zoyambirira kucha.” Masiku ano atumiki a Yehova safunika kupereka chakhumi. M’malo mwake, Paulo analembera mpingo wa ku Korinto kuti: “Yense achite monga anatsimikiza mtima, si mwa chisoni mokakamiza, pakuti Mulungu akonda wopereka mokondwerera.” (2 Akorinto 9:7) Kupereka zopereka zaufulu zothandizira ntchito yolalikira Ufumu ya padziko lonse kumasonyezanso kuyamikira kwathu. Kuyamikira ndi mtima wonse kumatilimbikitsa kuchita zimenezi nthaŵi zonse, mwina kukonza zopereka kangachepe mlungu uliwonse, monga mmene anali kuchitira Akristu oyambirira.​—1 Akorinto 16:1, 2.

18 Chimene chimasonyeza kuyamikira kwathu Yehova si kuchuluka kwa zinthu zimene timapereka, koma mtima umene watichititsa kupereka zinthuzo. Zimenezi n’zimene Yesu ananena pamene anali kuona anthu akuponya zopereka zawo m’bokosi losungiramo ndalama la pakachisi. Yesu ataona mkazi wamasiye akuponya “timakobiri tiŵiri,” anati: “Zoonadi ndinena kwa inu, wamasiye uyu waumphaŵi anaikamo koposa onse; pakuti onse ameneŵa anaika mwa unyinji wawo pa zoperekazo; koma iye mwa kusoŵa kwake anaikamo za moyo wake, zonse anali nazo.”​—Luka 21:1-4.

19. N’chifukwa chiyani ndi bwino kuonanso njira zimene timasonyezera kuyamikira kwathu?

19 Zimene takambiranazi zofotokoza mmene tingasonyezere kuyamikira zitilimbikitsetu kuonanso njira zimene timasonyezera kuyamikira kwathu. Kodi mwina tingawonjezere nsembe zathu zoyamikira Yehova, pamodzinso ndi kuthandizira ntchito ya padziko lonse ndi chuma chathu? Pamene tichita zonse zimene tingathe pa mbali zimenezi, tingakhale ndi chikhulupiriro chonse kuti Atate wathu wachikondi ndiponso wooloŵa manja, Yehova, adzasangalala kwambiri kuti tikusonyeza kuyamikira.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi tiyenera kuyamikira Yehova pa zifukwa ziti?

• Kodi tikuphunzira chiyani pa chakhumi, zopereka zaufulu, ndi khunkha?

• Kodi timakhala bwanji ndi mtima wa upainiya?

• Kodi tingagwiritse ntchito bwanji “chuma” chathu kuyamikira Yehova?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 15]

“Mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro zichokera Kumwamba”

[Zithunzi patsamba 16]

Kodi ndi zinthu zitatu ziti zimene tikuphunzira m’Chilamulo zimene azisonyeza apa?

[Zithunzi patsamba 18]

Kodi ndi nsembe ziti zimene tingapereke?