Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumafunikira Lamulo la M’Baibulo Nthaŵi Zonse?

Kodi Mumafunikira Lamulo la M’Baibulo Nthaŵi Zonse?

Kodi Mumafunikira Lamulo la M’Baibulo Nthaŵi Zonse?

PAMENE munali wamng’ono, mosakayikira makolo anu anakupatsani malamulo ambiri. Pamene munali kukula, munazindikira kuti anali kukufunirani zabwino. Panopa pamene muli munthu wachikulire, mwina mumatsatirabe mfundo zina zimene anakuphunzitsani, ngakhale kuti panopa sakukulamuliraninso.

Atate wathu wakumwamba, Yehova, anatipatsa malamulo ena achindunji m’Mawu ake, Baibulo. Mwachitsanzo, amaletsa kupembedza mafano, dama, chigololo, ndi kuba. (Eksodo 20:1-17; Machitidwe 15:28, 29) ‘Tikamakula m’zinthu zonse’ mwauzimu, timazindikira kuti Yehova amatifunira zabwino ndiponso kuti malamulo ake siopondereza.​—Aefeso 4:15; Yesaya 48:17, 18; 54:13.

Komabe, pali zinthu zambiri zimene zilibe lamulo lachindunji. Chifukwa cha zimenezi, anthu ena amaganiza kuti ngati palibe lamulo lachindunji la m’Baibulo, ali ndi ufulu wochita chilichonse chimene akufuna. Amanena kuti Mulungu akanaona kuti n’kofunikira kutero, akananena zimene amafuna kudzera mu lamulo lachindunji.

Anthu amene amaganiza motere nthaŵi zambiri amachita zinthu zopanda nzeru zimene mapeto ake amadzadandaula nazo kwambiri. Amalephera kuona kuti m’Baibulo sikuti muli malamulo okha ayi, koma mulinso mfundo zosonyeza mmene Mulungu amaganizira. Tikamaphunzira Baibulo n’kuyamba kumvetsetsa mmene Yehova amaonera zinthu, timakhala ndi chikumbumtima chophunzitsidwa Baibulo ndipo zimenezi zimatithandiza kuchita zinthu m’njira imene imagwirizana ndi maganizo ake. Tikatero, timasangalatsa mtima wake ndipo timapindula chifukwa chochita zinthu mwanzeru.​—Aefeso 5:1.

Zitsanzo Zabwino Kwambiri za M’Baibulo

Tikaona nkhani za m’Baibulo zokhudza atumiki a Mulungu mu nthaŵi zakale, timapeza kuti nthaŵi zina anachita zinthu mogwirizana ndi mmene Yehova amaganizira ngakhale kuti panalibe lamulo lachindunji. Taganizirani chitsanzo cha Yosefe. Panthaŵi imene mkazi wa Potifara ankamuvutitsa kuti achita naye zachiwerewere, kunalibe lamulo louziridwa lolembedwa mwachindunji loletsa kuchita chigololo. Komabe, ngakhale popanda lamulo lachindunji, Yosefe anazindikira kuti kuchita chigololo kunali kuchimwira, osati chikumbumtima chake chokha, komanso “kuchimwira Mulungu.” (Genesis 39:9) Zikuoneka kuti Yosefe anazindikira kuti kuchita chigololo kunali kosemphana ndi maganizo ndi chifuniro cha Mulungu, monga mmene anafotokozera mu Edene.​—Genesis 2:24.

Taganizirani chitsanzo china. Pa Machitidwe 16:3 timaŵerenga kuti Paulo asanamutenge Timoteo kupita naye ku maulendo ake achikristu, anayamba wam’dula. Koma pa vesi 4 timaŵerenga kuti Paulo ndi Timoteo kenaka anayenda m’mizindayo kupereka “malamulo . . . amene analamulira atumwi ndi akulu a pa Yerusalemu.” Limodzi la malamulo amenewo linali loti Akristu safunika kutsatira lamulo loti ayenera kudulidwa! (Machitidwe 15:5, 6, 28, 29) N’chifukwa chiyani Paulo anaona kuti kunali kofunika kuti Timoteo adulidwe? “Chifukwa cha Ayuda amene anakhala m’maikomo; pakuti onse anadziŵa kuti atate ake [a Timoteo] anali Mhelene.” Paulo sanafune kukhumudwitsa munthu aliyense popanda chifukwa chomveka. Iye anafunitsitsa kuti Akristu ‘adzivomerezetse okha ku chikumbumtima cha anthu onse pamaso pa Mulungu.’​—2 Akorinto 4:2; 1 Akorinto 9:19-23.

Umu ndi mmene Paulo ndi Timoteo ankaganizira nthaŵi zonse. Ŵerengani malemba monga Aroma 14:15, 20, 21 ndi 1 Akorinto 8:9-13; 10:23-33, ndipo onani mmene Paulo anali wokhudzidwira kwambiri ndi moyo wauzimu wa ena, makamaka amene akanatha kukhumudwa ndi kanthu kena, kamene pakokha sikanali kolakwa. Ndipo Paulo ponena za Timoteo analemba kuti: “Ndilibe wina wa mtima womwewo, amene adzasamalira za kwa inu ndi mtima woona. Pakuti onseŵa atsata za iwo okha, si za Yesu Kristu. Koma muzindikira matsimikizidwe ake, kuti, monga mwana achitira atate wake, anatumikira pamodzi ndi ine Uthenga Wabwino.” (Afilipi 2:20-22) Amuna achikristu aŵiri ameneŵa akutipatsa chitsanzo chabwino kwambiri masiku ano. M’malo mochita zinthu zoti ziwasangalatse iwowo kapena zinthu zimene amakonda pakakhala kuti palibe lamulo lachindunji la Mulungu, anatsanzira chikondi cha Yehova ndi Mwana wake mwa kuganiza mmene zochita zawozo zingakhudzire anthu ena mwauzimu.

Taganizirani za Yesu Kristu, chitsanzo chathu chachikulu. Mu Ulaliki wake wa pa Phiri, iye anafotokoza momveka bwino kuti munthu amene wamvetsetsa mfundo ya malamulo a Mulungu amawamvera ngakhale kupitirira pa zimene akulamula kapena kuletsa mwachindunji. (Mateyu 5:21, 22, 27, 28) Anthu onseŵa, Yesu, Paulo, Timoteo, ndi Yosefe analibe maganizo oti ngati palibe lamulo la Mulungu lachindunji, munthu angachite chilichonse chimene akufuna. Pochita zinthu mogwirizana ndi mmene Mulungu amaganizira, amuna ameneŵa anatsatira malamulo amene Yesu anati ndiye malamulo aŵiri aakulu koposa onse, omwe ndi kukonda Mulungu ndi kukonda munthu mnzako.​—Mateyu 22:36-40.

Bwanji Akristu Masiku Ano?

Ndithudi sitiyenera kuliona Baibulo ngati mmene tingaonere chikalata chokamba za malamulo, n’kumayembekezera kuti chilichonse chofunika kuchita chilembedwe mwatsatanetsatane. Timasangalatsa kwambiri mtima wa Yehova ngati tichita zinthu zimene zimagwirizana ndi maganizo ake, ngakhale pamene palibe lamulo lachindunji loti lititsogolere. Zimenezi zikutanthauza kuti, m’malo moti nthaŵi zonse tizichita kuuzidwa zimene Mulungu akufuna kuti tichite, tingathe ‘kudziŵitsa chifuniro cha Ambuye n’chiyani.’ (Aefeso 5:17; Aroma 12:2) Kodi n’chifukwa chiyani kuchita zimenezi kumakondweretsa Yehova? Chifukwa kumasonyeza kuti cholinga chathu chachikulu si kuchita zimene timakonda kapena ufulu wathu, koma kum’sangalatsa iyeyo. Kumasonyezanso kuti timayamikira kwambiri chikondi chake, moti mpaka timafuna kutsanzira chikondi chimenecho kuti chikhale mphamvu imene imatitsogolera pochita zinthu. (Miyambo 23:15; 27:11) Kuonjezera apo, kuchita zinthu motsatira zimene zili m’Malemba kumatithandiza kukhala ndi moyo wauzimu wabwino ndiponso nthaŵi zambiri timakhala ndi thanzi labwino.

Tiyeni tione mmene tingagwiritsire ntchito mfundo imeneyi m’zinthu zokhudza munthu payekha.

Kusankha Zinthu Zodzisangalatsa Nazo

Taganizirani za mnyamata amene akufuna kugula tepi inayake ya nyimbo. Zimene wamva patepi imeneyo n’zosangalatsa kwambiri, koma akuda nkhaŵa chifukwa chikutiro chake chikusonyeza kuti mawu a nyimbozo ndi olaula ndiponso otukwana. Komanso akudziŵa kuti nyimbo zambiri za woimba ameneyo zimakhala zaukali ndiponso zachiwawa. Chifukwa chakuti mnyamata ameneyu amakonda Yehova, akufuna kudziŵa maganizo Ake ndi mmene akuionera nkhani imeneyi. Kodi angadziŵe bwanji zimene Mulungu akufuna pa nkhani imeneyi?

M’kalata imene Paulo analembera Agalatiya, anandandalika ntchito zathupi ndi chipatso cha mzimu wa Mulungu. Mosakayikira mukudziŵa zinthu zimene zili m’gulu la chipatso cha mzimu wa Mulungu, chimene ndi chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, ndi chiletso. Koma kodi ndi zinthu ziti zimene zili m’gulu la ntchito za thupi? Paulo analemba kuti: “Ndipo ntchito za thupi zionekera, ndizo dama, chodetsa, kukhumba zonyansa, kupembedza mafano, nyanga, madano, ndewu, kaduka, zopsa mtima, zotetana, magaŵano, mipatuko, njiru, kuledzera, mchezo, ndi zina zotere; zimene ndikuchenjezani nazo, monga ndachita, kuti iwo akuchitachita zotere sadzaloŵa Ufumu wa Mulungu.”​—Agalatiya 5:19-23.

Taonani mawu omaliza pa ndandanda imeneyi, oti “ndi zina zotere.” Paulo sanalembe ndandanda ya zinthu zonse zimene tingati zili m’gulu la ntchito za thupi. Sizikutanthauza kuti munthu angaganize kuti, ‘Malemba akundilola kuchita ntchito ina iliyonse imene siili pa ndandanda ya Paulo ya ntchito za thupi.’ M’malomwake, anthu oŵerenga ayenera kugwiritsa ntchito luso lawo lozindikira kuti adziŵe zinthu zimene mwina pa ndandandapo palibe koma ndi “zotere.” Anthu amene mosalapa amachita zinthu zimene sizinatchulidwepo koma ndi “zotere” sadzalandira nawo madalitso a Ufumu wa Mulungu.

Choncho tifunika kudziŵa, kapena kuti kuzindikira, zinthu zimene sizikondweretsa Yehova. Kodi kuchita zimenezo n’kovuta? Tiyerekezere kuti dokotala wanu wakuuzani kuti muzidya zipatso ndi ndiwo zamasamba zambiri koma musamadye maswiti, makeke, ndi zina zotere. Kodi kungakhale kovuta kudziŵa kuti mabisiketi ali m’gulu liti? Tsopano onaninso chipatso cha mzimu wa Mulungu ndi ntchito za thupi zija. Kodi tepi yanyimbo tinaitchula koyambirira ija ili m’gulu liti? Mosakayikira sikufanana m’pang’onong’ono pomwe ndi makhalidwe monga chikondi, kukoma mtima, chiletso, kapena makhalidwe ena amene ali m’gulu la chipatso cha mzimu wa Mulungu. Munthu sangachite kufunikira lamulo lachindunji kuti adziŵe kuti nyimbo ngati zimenezi n’zosemphana ndi mmene Mulungu amaganizira. Mfundo zomwezo zimagwiranso ntchito pa nkhani ya zimene timaŵerenga, mafilimu, mapulogalamu a pa TV, maseŵera a pakompyuta, kugwiritsa ntchito intaneti ndi zina zotero.

Kaonekedwe Kovomerezeka

Baibulo limatipatsanso mfundo zimene zimakhudza nkhani za kavalidwe ndi kaonekedwe. Mfundo zimenezi zimathandiza Mkristu aliyense kudziŵa chochita kuti azivala moyenera komanso mooneka bwino. Pamenepanso, munthu wokonda Yehova amaonapo mwayi woti achite zimene zidzasangalatsa Atate ake akumwamba, osati mwayi woti achite chilichonse chimene akufuna. Monga momwe taonera, Yehova akakhala kuti sanapereke malamulo achindunji pankhani inayake sizitanthauza kuti zimene anthu ake azichita alibe nazo ntchito. Masitayilo amasiyana m’malo osiyanasiyana, ndipo ngakhale m’dera lomwelo amasintha nthaŵi ndi nthaŵi. Komabe, Mulungu amapereka mfundo zoti anthu ake atsatire nthaŵi zonse komanso ku malo kulikonse.

Mwachitsanzo, lemba la 1 Timoteo 2:9, 10 limati: “Momwemonso, akazi adziveke okha ndi chovala choyenera, ndi manyazi, ndi chidziletso; osati ndi tsitsi lake loluka, ndi golidi kapena ngale, kapena malaya a mtengo wake wapatali; komatu (umo mokomera akazi akuvomereza kulemekeza Mulungu), mwa ntchito zabwino.” Choncho akazi, ngakhalenso amuna, achikristu ayenera kuganizira za kavalidwe kamene anthu m’dera lawolo amati n’koyenera anthu amene ‘amavomereza kulemekeza Mulungu.’ N’zofunika kwambiri makamaka kuti Mkristu alingalire zimene anthu angaganize za uthenga wa m’Baibulo umene akulengeza akaona mmene Mkristuyo akuonekera. (2 Akorinto 6:3) Mkristu wopereka chitsanzo chabwino saganiza kwambiri za zimene amakonda kapena ufulu wake, m’malomwake amaganiza zosafuna kudodometsa kapena kukhumudwitsa ena.​—Mateyu 18:6.

Mkristu akaona kuti sitayilo inayake ya kaonekedwe ikukhumudwitsa ena, angatsanzire mtumwi Paulo mwakuika moyo wauzimu wa ena patsogolo pa zimene iyeyo amakonda. Paulo anati: “Khalani onditsanza ine, monga inenso nditsanza Kristu.” (1 Akorinto 11:1) Ndipo ponena za Yesu, Paulo analemba kuti: “Kristunso sanadzikondweretsa yekha.” Mfundo imene Paulo amafuna kuuza Akristu onse ndi yachidziŵikire, yoti: “Ife amene tili olimba tiyenera kunyamula zofooka za opanda mphamvu, ndi kusadzikondweretsa tokha. Yense wa ife akondweretse mnzake, kum’chitira zabwino, zakum’limbikitsa.”​—Aroma 15:1-3.

Kunola Luso Lathu Lozindikira Zinthu

Kodi tinganole bwanji luso lathu lozindikira zinthu kuti tizikondweretsa Yehova ngakhale pamene sanatipatse lamulo lachindunji pankhani inayake? Ngati tiŵerenga Mawu ake tsiku lililonse, kuwaphunzira nthaŵi zonse, ndi kusinkhasinkha zimene taŵerengazo, tidzaona kuti luso lathu lozindikira zinthu likukula. Koma kukula kumeneko sikuchitika msangamsanga. Mofanana ndi mmene mwana amakulira, kukula mwauzimu kumachitika pang’onopang’ono ndipo sikuoneka nthaŵi yomweyo. Choncho m’pofunika kudekha, ndipo sitiyenera kukhumudwa ngati tikuona kuti sitikupita patsogolo nthaŵi yomweyo. Komabe, kupita kwa nthaŵi yaitali pakokha sikunganole luso lathu la kuzindikira zinthu. Mmalomweke, panthaŵi imeneyoyo tiyenera kukhala tikuganizira za Mawu a Mulungu monga momwe tafotokozera pamwambapa, ndipo tiyenera kutsatira Mawu amenewo pa moyo wathu monga momwe tingathere.​—Ahebri 5:14.

Tinganene kuti pamene malamulo a Mulungu amayesa kumvera kwathu, mfundo zake zimayesa kuya kwa moyo wathu wauzimu ndi chifuno chathu chomusangalatsa. Tikamakula mwauzimu, tidzayamba kufuna kwambiri kutsanzira Yehova ndi Mwana wake. Tidzakhala ofunitsitsa kuchita zinthu mogwirizana ndi mmene Mulungu amaganizira, monga momwe Malemba amasonyezera. Pamene tikukondweretsa Atate wathu wakumwamba m’zonse zimene timachita, tidzaona kuti chimwemwe chathu chidzaonjezekanso.

[Zithunzi patsamba 23]

Masitayilo a zovala amasiyana m’madera osiyanasiyana, koma mfundo za m’Baibulo zizititsogolera posankha zovala