Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi pamene Ezekieli anakhala “chete” kapena kuti “wosalankhula” pamene mzinda wa Yerusalemu unazingidwa ndi kuwonongedwa zinatanthauza chiyani?

Mwachidule, zinatanthauza kuti panalibenso zina zimene akanawonjezera pa uthenga wa ulosi wa Yehova umene anali atauza kale anthu.

Mneneri Ezekieli anayamba kutumikira monga mlonda wokhulupirika wa Aisrayeli amene anali akapolo ku Babulo mu “chaka chachisanu cha kutengedwa ndende mfumu Yoyakini,” momwe munali mu 613 B.C.E. (Ezekieli 1:2, 3) Pa tsiku lakhumi la mwezi wakhumi mu 609 B.C.E., Mulungu anadziŵitsa Ezekieli za kuyambika kwa kuzinga mzinda wa Yerusalemu kumene Ababulo anachita. (Ezekieli 24:1, 2) Kodi n’chiyani chinali kudzachitika chifukwa cha kuzinga mzinda kumeneku? Kodi mzinda wa Yerusalemu ndi anthu amene anali kukhala mumzindawo omwe anali osakhulupirira akanapulumuka? Ezekieli monga mlonda, anali atanena kale uthenga wachiweruzo wosapita m’mbali wa Yehova, ndipo panalibe chifukwa choti Ezekieli awonjezere zina, ngati kuti akufuna kuchititsa uthengawo kukhala wogwira mtima kwambiri. Ezekieli anakhala chete pankhani yonena zinthu zina zokhudza kuzingidwa kwa Yerusalemu.​—Ezekieli 24:25-27.

Patapita miyezi pafupifupi isanu ndi umodzi mzinda wa Yerusalemu utawonongedwa mu 607 B.C.E., munthu wina amene anapulumuka anakauza Ezekieli ku Babulo za kuwonongedwa kwa mzinda wopatulikawo. Madzulo, munthu wopulumukayo asanafike, Yehova ‘anatsegula pakamwa [pa Ezekieli] ndipo sanakhalenso wosalankhula.’ (Ezekieli 33:22) Zimenezo zinachititsa kuti kukhala chete kwa Ezekieli kuthe.

Kodi panthaŵi imeneyo Ezekieli anakhala wosalankhula m’njira yakuti sankatha kutulutsa mawu pakamwa pake? Mwachionekere, sizinali choncho chifukwa ngakhale panthaŵi imeneyi, imene anali “chete,” analosera zokhudza makamaka mayiko amene anali pafupi ndi Yerusalemu amene anakondwera chifukwa cha kugwa kwake. (Ezekieli, machaputala 25-32) Kuchiyambi kwa ntchito ya Ezekieli monga mneneri ndi mlonda, Yehova anamuuza kuti: “Ndidzamamatiritsa lilime lako ku malakalaka ako, kuti ukhale wosanena, wosawakhalira wakuwadzudzula; pakuti iwo ndiwo nyumba yopanduka. Koma pamene ndilankhula nawe ndidzatsegula pakamwa pako.” (Ezekieli 3:26, 27) Nthaŵi imene Yehova analibe uthenga woti auze Aisrayeli, Ezekieli anafunika kukhala chete, osalankhula chilichonse chokhudza mtunduwo. Ezekieli anafunika kulankhula zimene Yehova anafuna kuti iye alankhule panthaŵi imene Yehova anafuna kuti atero. Kukhala chete kwa Ezekieli kunatanthauza kuti sanalankhule mawu alionse aulosi okhudza Aisrayeli.

Gulu la mlonda la masiku ano, Akristu odzozedwa, lakhala likuchenjeza za chiweruzo cha Matchalitchi Achikristu, omwe akuphiphiritsira Yerusalemu. ‘Chisautso chachikulu’ chikadzakantha ndi kuwononga ‘Babulo Wamkulu,’ ufumu wadziko lonse wa chipembedzo chonyenga, gulu la Ezekieli lodzozedwa silidzafunikira kulankhula zinthu zina zokhudza kutha kwa Matchalitchi Achikristu, omwe ndi mbali yaikulu ya ufumuwo.​—Mateyu 24:21; Chivumbulutso 17:1, 2, 5.

Inde, idzafika nthaŵi imene otsalira odzozedwa ndi anzawo adzakhala chete, sadzakhala ndi zinthu zina zowonjezera zoti auze Matchalitchi Achikristu. Imeneyo idzakhala nthaŵi imene “nyanga khumi” ndi “chilombo” zidzachititsa Babulo Wamkulu kukhala wabwinja ndi wamaliseche. (Chivumbulutso 17:16) Komabe, zimenezi sizikutanthauza kuti Akristu adzakhala osalankhula m’njira yakuti sadzatulutsa mawu pakamwa pawo. Monga mmene akuchitira pakadali pano, adzatamanda Yehova ndipo adzalankhula za iye tsiku ndi tsiku ndiponso “m’mibadwo mibadwo.”​—Salmo 45:17; 145:2.