“Okonzeka pa Ntchito Iliyonse Yabwino”
“Okonzeka pa Ntchito Iliyonse Yabwino”
“UWAKUMBUTSE iwo agonje kwa akulu, ndi aulamuliro, akhale omvera, okonzeka pa ntchito iliyonse yabwino.” (Tito 3:1) Kodi mtumwi Paulo anali kuganizira za ntchito yabwino iti pamene analemba mawu amenewo kwa okhulupirira anzake? Katswiri wamaphunziro a Baibulo E. F. Scott anatchula mtundu umodzi wa ntchito yabwino pamene ananena kuti: “Sikuti Akristu anangofunika kumvera maulamuliro okha basi, koma anayeneranso kukhala okonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino. . . . Ngati panali pofunika kutero, Akristu anafunika kukhala oyambirira kusonyeza mtima wothandiza ena. Nthaŵi zonse pakanatheka kubuka moto, mliri wa matenda, masoka amitundumitundu, pamene anthu onse abwino akanafuna kuthandiza anzawo.”
Akristu amachita nawo ntchito zina zothandiza anthu ngati ntchitozo sizikusemphana ndi malamulo a Mulungu. (Machitidwe 5:29) Mwachitsanzo, pomvera malangizo a dipatimenti yakwawoko yoona za moto, ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Japan, imene ili mu mzinda wa Ebina, chaka chilichonse imakhala ndi maphunziro oyesezera kuzimitsa moto. Panthaŵi imeneyi, anthu onse a m’banja la Beteli amasonkhana pamodzi kudzamvera malangizo operekedwa ndi munthu wochokera ku dipatimenti yoona za moto kumeneko.
Kuonjezera apo, kwa zaka zopitirira khumi, ofesi yanthambiyo yakhala ikumvera akuluakulu aboma pochita nawo chionetsero chofuna kulimbikitsa anthu kudziŵa kapeŵedwe ka moto. Pachionetserocho, makampani ndi mabungwe a mumzindawu amasonyeza luso lawo lozimitsa ndi kupeŵa moto. Nthambiyi yakhala ikuyamikiridwa nthaŵi zambiri chifukwa cha luso ndi kumvera kwa anthu okhala panthambipo. Mu 2001 anapatsidwa mphoto yoyamba pa chionetserocho. Iwo ndi okonzeka kuchita ntchito yabwino imene ingapulumutse miyoyo patabuka moto.
Ntchito Yofunika Kwambiri
Komabe, Mboni za Yehova zimaika mtima kwambiri pa ntchito yofunika zedi imene ilinso yopulumutsa moyo. Nthaŵi zonse zimapita kwa anzawo kukagaŵana nawo uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. (Mateyu 24:14) Mbonizi zimalimbikitsa anthu kuphunzira ndi kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo m’moyo wawo kuti akhale ndi moyo wabwino pakadali pano ndiponso kuti akhale ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wosatha m’dziko limene mudzakhale mtendere ndi kutetezeka kwenikweni.
Ena mwina saona phindu la ntchito imene Mboni za Yehova zimagwira, ndipo mwina amaziona ngati anthu ovuta. Koma Jaji Jean Crepeau wa kukhoti lalikulu la ku Quebec, ku Canada anali ndi maganizo osiyana pa nkhani imeneyi. Mboni za Yehova kumeneko zinatsutsa lamulo limene mzinda wa Blainville, ku Quebec unapereka loti Mbonizo ziziyamba zatenga chilolezo zisanapite ku khomo ndi khomo. M’chigamulo chimene khotilo linapereka, Jaji Crepeau anati: “Ntchito imene Mboni za Yehova zimachita zikamayendera anthu ndintchito yachikristu yothandiza anthu ndipo . . . mabuku amene Mbonizo zimapereka kwa anthu achidwi ndi othandiza kwambiri. Mabukuŵa amakamba nkhani zokhudza chipembedzo, Baibulo, mankhwala osokoneza bongo, kumwa mowa mwauchidakwa, kuphunzitsa achinyamata, mavuto a m’banja ndi kutha kwa mabanja.” Chigamulocho chinapitiriza kunena kuti: “Khoti lino pomaliza likunena kuti kuyerekezera Mboni za Yehova ndi anthu ogulitsa malonda khomo ndi khomo ndi kunyoza, kulakwa, ndi kuonongerana mbiri.”
Mboni za Yehova zimachita ntchito yothandiza m’dera limene zimakhala mwa kuthandiza anthu kuthana ndi mavuto pa moyo wawo wa tsiku ndi tsiku ndiponso kuwapatsa chiyembekezo cha m’tsogolo. Baibulo limawathandiza kukwanitsa ntchito imeneyi. “Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo: kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.”—2 Timoteo 3:16, 17.
Kodi mungakonde kudziŵa mmene Mboni za Yehova zimakhalira ‘zokonzeka pa ntchito iliyonse yabwino’? Tikukupemphani kuti muzilole zikuthandizeni kuphunzira zambiri zokhudza Baibulo kuti mupindule ndi ntchito yofunika kwambiri yothandiza anthu imene zimagwira m’dera lanu komanso padziko lonse lapansi.
[Zithunzi pamasamba 30, 31]
Mboni za Yehova zimayesetsa kumvera akuluakulu aboma
[Chithunzi patsamba 31]
Mboni zimadziŵika ndi nkhani yothandiza anzawo