Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Pulogalamu ya pa TV Inamuyambitsa Kulemekeza Mulungu

Pulogalamu ya pa TV Inamuyambitsa Kulemekeza Mulungu

Olengeza Ufumu Akusimba

Pulogalamu ya pa TV Inamuyambitsa Kulemekeza Mulungu

MTUMWI Paulo ananena kuti: “Enatu alalikiranso Kristu chifukwa cha [“kudzera mwa,” NW] kaduka ndi ndewu; koma enanso chifukwa cha kukoma mtima.” (Afilipi 1:15) Nthaŵi zina, ngakhale anthu amene amafuna kunyoza anthu a Yehova mosadziŵa achititsa anthu amtima wabwino kukopeka ndi choonadi.

Mu November 1998, pa pulogalamu ya pa TV m’dziko la France anaonetsa zithunzi za nyumba za Beteli ndi maofesi a Mboni za Yehova zimene zili ku Louviers m’dzikolo. Ngakhale kuti anthu anakhala ndi maganizo osiyanasiyana ataiona, pulogalamuyo inakhala ndi zotsatirapo zabwino mosayembekezera.

Mmodzi wa anthu amene anaonera pulogalamuyo anali Anna-Paula, amene ankakhala pa mtunda wa makilomita 60 kuchokera ku Beteli. Anna-Paula, mayi amene mwamuna wake anam’sudzula ndipo ali ndi ana aŵiri, anali kufunafuna ntchito. Motero tsiku lotsatira, anaimba telefoni ku Beteli kuti afunsire ntchito. Iye anati: “Pulogalamuyo inandichititsa kukhala ndi malingaliro akuti anali malo abwino kwambiri ndiponso kuti ntchito imene imachitika kumeneko ndi yofunika.” Anadabwa kwambiri kudziŵa kuti onse amene amagwira ntchito pa Beteli ndi atumiki ogwira ntchito mongodzipereka. Atakambirana mwachidule za ntchito ya Mboni za Yehova, anavomera kuti Wamboni akamuyendere.

Pamene Léna, mtumiki wa nthaŵi zonse wa mpingo wa kumeneko anapita kukamuyendera, anakambirana kwa nthaŵi yaitali, ndipo Anna-Paula analandira buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. * Léna atapita ulendo wachiŵiri, Anna-Paula anali atamaliza kuŵerenga bukulo ndipo anali ndi mafunso ambiri. Anavomera kuti aziphunzira Baibulo. Anna-Paula anati: “Kwa ine, unali mwayi kudziŵa Mawu a Mulungu. Ndinali ndisanagwirepo Baibulo m’manja mwanga.”

Mu January, Anna-Paula anapita kukacheza ku Beteli, ndipo mlungu wotsatira anakapezeka koyamba pa msonkhano wachikristu. Pasanapite nthaŵi yaitali, anayamba kuphunzira Baibulo ndi ana ake ndipo anayamba kulalikira kwa anzake. Iye anati: “Sindikanatha kungosunga zimene ndinali kuphunzira. Ndinafuna kugaŵanako choonadi cha m’Baibulo ndi anthu ndiponso kuwatonthoza.” Atayesetsa kugonjetsa mavuto osiyanasiyana amene anali nawo pa moyo wake, Anna-Paula anayamba kupezeka pa misonkhano nthaŵi zonse. Anapita patsogolo mofulumira kwambiri ndipo anabatizidwa pa May 5, 2002.

Kuwonjezera pamenepa, chifukwa cha chitsanzo chabwino cha Anna-Paula ndiponso chifukwa cholalikira mwachangu, mayi ake anayamba kuphunzira Baibulo ndipo anabatizidwa pasanapite nthaŵi yaitali. Anna-Paula anati: “Sindingathe kufotokoza chimwemwe chimene ndili nacho. Tsiku lililonse ndimathokoza Yehova chifukwa chondilola kuti ndim’dziŵe ndi kum’tumikira ndiponso chifukwa cha madalitso onse amene wandipatsa.”

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Zithunzi patsamba 8]

Pamwambapa: Anna-Paula

M’munsimu: Poloŵera ku ofesi ya nthambi ya ku France