Zifukwa Zimene Anthu Amapitira Kutchalitchi
Zifukwa Zimene Anthu Amapitira Kutchalitchi
“M’DZIKO la Republic of Korea tsopano muli anthu a mpingo wa Presbyterian oŵirikiza pafupifupi kanayi amene ali ku America.” Mawu amenewo, amene analembedwa mu nyuzipepala ya Newsweek, mwina anadabwitsa oŵerenga ambiri, chifukwa chakuti anthu ambiri amaganiza kuti ku Korea anthu ambiri ndi a chipembedzo cha Chikomfyushasi kapena Chibuda. Masiku ano, mlendo angaone matchalitchi “Achikristu” ambiri ku Korea, amene nthaŵi zambiri angawadziŵe chifukwa amakhala ndi mitanda yowalitsidwa ndi magetsi ofiira. Pa tsiku Lamlungu, sichachilendo kuona anthu ali aŵiriaŵiri kapena atatuatatu, atanyamula mabaibulo m’manja, akupita kutchalitchi. Malinga ndi kafukufuku amene anachitika mu 1998, pafupifupi anthu 30 mwa anthu 100 alionse a ku Korea amapemphera tchalitchi chachikatolika kapena chachipulotesitanti, kutanthauza kuti ndi ochuluka kuposa amene ali m’chipembedzo chachibuda.
Masiku ano, m’madera ena n’zachilendo kuona anthu ambiri choncho amene amapita kutchalitchi nthaŵi zonse. Koma zimenezi sikuti zikungochitika ku Korea kokha. Zikuchitikanso ku mayiko ena a ku Asia, ndiponso ku Africa ndi ku Latin America. Kodi n’chifukwa chiyani anthu ambiri choncho akukhulupirirabe Mulungu pamene chidwi cha anthu ambiri pankhani ya chipembedzo padziko lonse lapansi chikucheperachepera? Kodi amapita kutchalitchi chifukwa chiyani?
Pa kafukufuku amene anafunsa anthu maganizo awo, anapeza kuti pa anthu amene amapita kutchalitchi ku Korea, opitirira theka akufunafuna mtendere wa m’maganizo, pafupifupi munthu mmodzi mwa atatu alionse amafuna kudzakhala ndi moyo wosatha akadzamwalira, ndipo munthu mmodzi mwa anthu khumi amafuna thanzi labwino, chuma, ndi kuti zinthu ziwayendere bwino pamoyo wawo.
Anthu ambiri ku China amapita kutchalitchi pofuna kuti akapeze zinthu zimene amasoŵa mwauzimu zimene zikuchitika chifukwa cha kusintha kwa ulamuliro kuchoka mu Chikomyunizimu kuloŵa mu ulamuliro umene anthu ali ndi ufulu wokhala ndi zinthu zawozawo. Chaka chilichonse, mabaibulo mamiliyoni ambiri amasindikizidwa ndi kugaŵidwa ku China, ndipo zikuoneka kuti anthu akuŵerenga Baibulo mwakhama ngati mmene anali kuŵerengera kabuku kofiira ka Mao kamene analembamo nzeru zake.
Akatolika ena ku Brazil, makamaka achinyamata, sakukhutiritsidwa ndi lonjezo loti adzasangalala m’moyo umene ukubwerawo. Iwo akufuna kusangalala pakadali pano. Magazini yotchedwa Tudo inati: “Ngati chiphunzitso choti mpingo uyenera kubweretsa ufulu kwa anthu n’chimene chinakhudza mitima ya anthu m’zaka za m’ma 1970, masiku anu chimene chikukhudza mitima ya anthu ndi chiphunzitso choti mpingo umabweretsa chitukuko.” Mu kafukufuku wina ku Britain anafunsa anthu amene amapita kutchalitchi kuti atchule chinthu chimodzi chimene amakonda chokhudza tchalitchi chawo. Ambiri a iwo anati chimene amakonda kwambiri ndi kucheza ndi anzawo a kutchalitchiko.
Zonsezi zikusonyeza kuti ngakhale kuti anthu ambiri akukhulupirirabe Mulungu, ambiri amafuna zimene angapeze panopa osati zimene zikubwera m’tsogolo, ndipo ambiri saganizira kwenikweni za Mulungu weniweniyo. Kodi mukuganiza kuti chifukwa choyenera chokhulupirira Mulungu n’chiyani? Kodi Baibulo limati chiyani pankhani imeneyi? Mupeza mayankho mu nkhani yotsatira.