Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zitsime Zosasunga Madzi

Zitsime Zosasunga Madzi

Zitsime Zosasunga Madzi

MU NTHAŴI za m’Baibulo, ankakumba zitsime zinazake zimene ntchito yake yaikulu inali kusungiramo madzi a mvula kapena oyenda m’makwaŵa. Panthaŵi zina m’Dziko Lolonjezedwa, zitsime zimenezi zokha n’zimene zimakhala ndi madzi, amene amafunika kwambiri.

Polemba mawu ochokera kwa Mulungu, mneneri Yeremiya anatchulapo za zitsime mophiphiritsira pamene anati: “Pakuti anthu anga anachita zoipa ziŵiri; anandisiya Ine kasupe wa madzi amoyo, nadziboolera zitsime, zitsime zong’aluka, zosakhalamo madzi.”​—Yeremiya 2:13.

Aisrayeli atasiya Mulungu wawo, Yehova, amene anali “kasupe wa madzi amoyo,” anayamba kudalira maubwenzi andale osalimba amene anapanga ndi mitundu yachikunja ndiponso anayamba kulambira milungu yosathandiza ndiponso yonama. Zinthu zimene anali kuzidalirazi, malinga ndi kunena kwa Yeremiya, zinadzakhala zitsime zochucha, zopanda mphamvu iliyonse yoteteza kapena kupulumutsa munthu.​—Deuteronomo 28:20.

Kodi m’chitsanzo chakale chimenechi muli phunziro lililonse kwa ife masiku ano? Monga mmene zinalili mu nthaŵi ya Yeremiya, Mulungu wamuyaya, Yehova, akadali Magwero okhawo a madzi opatsa moyo. (Salmo 36:9; Chivumbulutso 4:11) Iye yekha, kudzera mwa Mwana wake, Yesu Kristu, ndi amene angapatse anthu moyo wosatha. (Yohane 4:14; 17:3) Komabe, mofanana ndi mmene anachitira anthu amene analipo pa nthaŵi ya Yeremiya, anthu ambiri masiku ano amakana ndiponso amanyoza mawu a Mulungu amene analembedwa m’Baibulo. M’malomwake amadalira njira zothetsera mavuto za anthu andale, maganizo osathandiza a anthu, ndi mfundo zopanda pake ndiponso nzeru za anthu zonyoza Mulungu. (1 Akorinto 3:18-20; Akolose 2:8) Pamenepa njira yabwino yoti munthu angatsatire ndi yodziŵikiratu. Kodi mudzadalira chiyani? Kodi mudzadalira “kasupe wa madzi amoyo,” Yehova, kapena “zitsime zong’aluka, zosakhalamo madzi”?

[Chithunzi patsamba 32]

Fano la mulungu wachikazi limene analipeza m’manda a ku Israyeli

[Mawu a Chithunzi]

Chithunzi chojambulidwa mwachilolezo cha British Museum