Kodi Banja la Yesu Linali Lotani?
Kodi Banja la Yesu Linali Lotani?
M’MADERA ambiri a padziko lapansili, mu December anthu amaona zithunzi za Yesu ali khanda akusamalidwa ndi amayi ake, Mariya, ndi atate ake omulera, Yosefe. Zithunzi za banja zimenezo, zingachititsenso chidwi anthu amene amati si Akristu. Popeza nkhani yaikulu m’zithunzizi imagona pa Yesu, kodi Malemba amatiuzanji zokhudza banja la Yesu lapadziko lapansi?
Yesu anachokera ku banja lochititsa chidwi kwambiri. Iye anabadwa kwa namwali wotchedwa Mariya, nakhala m’banja limenelo. Malinga n’kunena kwa Baibulo, moyo wa Yesu unasamutsidwa kuchokera kumwamba kudzakhala m’mimba mwa Mariya kudzera mwa mzimu woyera. (Luka 1:30-35) Asanadziŵe kuti adzakhala ndi mimba ya Yesu mozizwitsa, Mariya anatomerana ndi mwamuna wotchedwa Yosefe, yemwe anadzakhala tate wa Yesu womulera.
Yesu atabadwa, Yosefe ndi Mariya anabereka ana ena, omwe anali abale ndi alongo a Yesuyo. Tikupeza umboni wa zimenezi kuchoka pa funso lokhudza Yesu lomwe anthu a ku Nazarete anadzafunsa pambuyo pake, lakuti: “Kodi uyu si mwana wa mmisiri wa mitengo? Kodi dzina la amake si Mariya? ndi abale ake si Yakobo ndi Yosefe ndi Simoni ndi Yuda? Ndipo alongo ake sali ndife onseŵa?” (Mateyu 1:25; 13:55, 56; Marko 6:3) Chifukwa cha zimenezi tinganene kuti banja la Yesu linapangidwa ndi makolo ake, abale ake anayi, ndiponso alongo ake osachepera aŵiri.
Komabe, anthu ena masiku ano sakhulupirira kuti abale ndi alongo a Yesu anali ana a Yosefe ndi Mariya. Chifukwa chiyani? Buku lakuti New Catholic Encyclopedia limati: “kuyambira pachiyambi pomwe, Tchalitchi [cha Katolika] chinali kuphunzitsa kuti Mariya anakhalabe namwali. N’chifukwa chake, sitingakayikire kunena kuti Mariya analibe ana ena.” Buku lomwelo limanenanso kuti mawu akuti “mbale” kapena “mlongo” angaimire “anthu a m’chipembedzo chimodzi kapena kugwirizana kwinakwake” kapenanso kwa achibale, mwina ochokera kwa mbale wa bambo kapena mayi.
Kodi ndi mmene zinthu zililidi? Ngakhale akatswiri a zaumulungu Achikatolika, omwe sagwirizana ndi chiphunzitso chakale chimenechi, amagwirizana ndi mfundo yakuti Yesu anali ndi abale ndi alongo ake. John P. Meier, pulezidenti wakale wa Catholic Bible Association of America, analemba kuti: “M’chipangano Chatsopano mawu akuti adelphos [mbale], ngati sakugwiritsidwa ntchito monga chining’a kapena chifanifani koma posonyeza ubale weniweni kapena walamulo, amangotanthauza ubale wochokera kwa makolo onse aŵiri kapena kwa kholo limodzi basi.” * Malemba amasonyeza kuti Yesu anali ndi abale komanso alongo, omwe anabadwa kwa Yosefe ndi Mariya.
Mauthenga Abwino amatchula achibale ena a Yesu, koma tiyeni tione tsopano banja la Yesu ndi zimene tingaphunzire ku banjalo.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 6 Nkhani yakuti “Maganizo a Zipembedzo Zosiyanasiyana Pankhani ya Abale ndi Alongo a Yesu,” yolembedwa ndi J. P. Meier, m’magazini yotchedwa The Catholic Biblical Quarterly, January 1992, tsamba 21.”