Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Omaliza Maphunziro a Gileadi Analimbikitsidwa Kulankhula “Zazikulu”

Omaliza Maphunziro a Gileadi Analimbikitsidwa Kulankhula “Zazikulu”

Omaliza Maphunziro a Gileadi Analimbikitsidwa Kulankhula “Zazikulu”

PA SEPTEMBER 13, 2003, anthu okwana 6,635 ochokera ku mayiko 52 anapezeka pa mwambo wokondwerera kumaliza maphunziro a kalasi ya 115 ya Sukulu ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo.

Iwo anamvetsera chilimbikitso chochokera m’Baibulo choperekedwa kwa ophunzira 48 a m’kalasiyo choti akafotokoze “zazikulu za Mulungu” kwa anthu a mayiko 17. (Machitidwe 2:11) Ku mayiko ameneŵa n’kumene tsopano omaliza maphunzirowo azikachitira ntchito yawo yaumishonale.

M’mawu ake oyamba, Stephen Lett, yemwe ndi wa m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova ndipo anali tcheyamani wa mwambowo, anakumbutsa ophunzirawo kuti: “Mukapita kumene mudzatumikira, zilibe kanthu kumene mudzapita kapena zimene mudzakumana nazo, okhala pamodzi ndi inu achuluka koposa aja okhala pamodzi ndi iwo.” Mwa kugwiritsa ntchito 2 Mafumu chaputala 6, Mbale Lett anakumbutsa ophunzirawo kuti adzafunika kudalira thandizo la Yehova Mulungu ndiponso miyandamiyanda ya angelo pamene akudziŵikitsa “zazikulu za Mulungu.” (2 Mafumu 6:15, 16) Akristu a m’zaka 100 zoyambirira anakumana ndi chitsutso ndi mphwayi m’ntchito yawo ya kulalikira ndi kuphunzitsa ndipo Akristu omwe ndi amishonale iwonso amakumana ndi zinthu zofananazo masiku ano. Koma, amadalira thandizo lochokera kumwamba ndiponso ku gulu lapadziko lapansi la Yehova.​—Salmo 34:7; Mateyu 24:45.

Lankhulani “Zazikulu za Mulungu”

Mawu oyamba a tcheyamani ataperekedwa, Harold Corkern wa m’Komiti ya Nthambi ya ku United States, anakamba nkhani ya mutu wakuti: “Kuyembekezera Zotheka Ndiko Chinsinsi cha Utumiki Wachimwemwe Ndiponso Wopambana.” Mbale Corkern ananena kuti ziyembekezo zosakwaniritsidwa zingatigwiritse fuwa lamoto monga momwe Miyambo 13:12 imasonyezera. Komabe, nthaŵi zambiri kugwira fuwa lamoto kumachitika chifukwa choyembekezera zinthu zomwe sizingatheke. Omaliza maphunzirowo afunika kukhala ndi maganizo abwino komanso oyenera ponena za iwo eni ndi anthu ena. Afunika kuyembekeza kuti angalakwitse zinthu zina, koma zimenezi siziyenera kuwakhumudwitsa kwambiri pamene akuyesetsa kuthandiza ena kumvetsa “zazikulu za Mulungu.” Mbale Corkern analimbikitsa amishonale atsopanowo kudalira Yehova “wobwezera mphoto iwo akum’funa Iye.”​—Ahebri 11:6.

Mbale Daniel Sydlik wa m’Bungwe Lolamulira anali wotsatira papulogalamuyo ndipo anakamba nkhani ya mutu wakuti: “Kodi Chiyembekezo cha Akristu N’chotani?” Iye anati: “Chiyembekezo ndi khalidwe labwino limene Mkristu ayenera kukhala nalo. Ndi muyezo wachilungamo umene umapangitsa munthu kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu. N’zosatheka kuti munthu yemwe sali Mkristu akhale ndi chiyembekezo ngati chomwe ife tili nacho.” Mbale Sydlik anapitiriza kufotokoza mbali zosiyanasiyana za chiyembekezo cha Akristu zimene zimathandiza munthu kusataya mtima ngakhale akukumana ndi mavuto. “Tikakhala ndi chiyembekezo timatha kuwonjezera khama lathu ndiponso kukhala ndi mzimu wopambana pamoyo.” Chiyembekezo chimene Mkristu amakhala nacho chimam’thandiza kuona Yehova monga Mulungu wa chifuno ndiponso kusangalala pom’tumikira.​—Aroma 12:12.

Wallace Liverance, wosunga kaundula wa Sukulu ya Gileadi, analimbikitsa ophunzirawo ‘Kuyendabe ndi Mzimu.’ (Agalatiya 5:16) Iye anasonyeza mmene Baruki, mlembi wa Yeremiya anatsalira pang’ono kusiya kuyenda ndi mzimu. Panthaŵi ina, Baruki anatopa ndipo anayamba kudzifunira zinthu zazikulu. (Yeremiya 45:3, 5) Ndiyeno Mbale Liverance ananena kuti ena anasiya kutsatira Yesu ndipo anakana choonadi chauzimu chimene chili chofunika kuti munthu apulumuke. Zimenezi zinachitika chifukwa chakuti sanamvetse zimene iye anali kuphunzitsa ndipo anakhumudwa chifukwa choti zimene iwo ankayembekezera sizinakwaniritsidwe panthaŵiyo. (Yohane 6:26, 27, 51, 66) Kodi n’chiyani chimene amishonale, amene ntchito yawo ndi yophunzitsa anthu za Mlengi ndi chifuno chake angaphunzire pankhani zimenezi? Ophunzirawo anauzidwa kusaganizira kwambiri za kukhala ndi udindo, kutchuka kapena kugwiritsa ntchito utumiki umene Mulungu wawapatsa kudzipindulitsa iwo eni.

“Kodi Mudzakhala Wopatsa Kapena Wolandira?” linali funso limene Mark Noumir, mlangizi wa Gileadi anafunsa. Ndemanga zake zinachokera pa Oweruza 5:2, pamene Mwisrayeli aliyense anatamandidwa chifukwa cha kudzipereka mopanda dyera kutumikira m’gulu lankhondo la Baraki. Ophunzira a Gileadiwo anayamikiridwa chifukwa cha kuyankha chiitano cha Baraki Wamkulu, Yesu Kristu, cha kumenya nawo mokulira nkhondo yauzimu. Asilikali a Kristu afunika kukhala ndi chidwi chokondweretsa amene anawalemba ntchito. Mbale Noumair anakumbutsa ophunzirawo kuti: “Tikayamba kuganizira kwambiri zodzikondweretsa, timasiya kumenyana ndi mdani. . . . Utumiki waumishonale si wanu koma ndi wokhudza Yehova, Ufumu wake ndiponso kukwaniritsidwa kwa chifuniro chake. Sititumikira monga amishonale chifukwa chofuna kuti Yehova atikondweretse koma timam’tumikira chifukwa choti timam’konda.”​—2 Timoteo 2:4.

Lawrence Bowen, mlangizi wa sukulu ya Gileadi anatsogolera chigawo cha kukambirana kwa kagulu chimene chinali ndi mutu wakuti “Patulani Iwo M’choonadi.” (Yohane 17:17) Iye anati ophunzira a kalasi ya 115 ndi atumiki opatulidwa a Mulungu. Pamene anali kuphunzira analinso kutenga nawo mbali mu utumiki wakumunda, kufunafuna anthu oona mtima okonda choonadi. Mofanana ndi Yesu ndi ophunzira ake oyambirira, ophunzirawa sanalankhule ‘mwa iwo okha.’ (Yohane 12:49, 50) Iwo analalikira mwachangu mawu ouziridwa ndi opatsa moyo a choonadi. Zitsanzo ndi zokumana nazo za ophunzira zinasonyeza mmene Baibulo linakhudzira kwambiri anthu amene analankhula nawo.

Analimbikitsidwa ndi Malangizo Ndiponso Zimene Odziŵa Ntchitoyo Ananena

Anthony Pérez ndi Anthony Griffin, a mu Dipatimenti ya Utumiki ya Nthambi ya ku United States anafunsa a m’Komiti ya Nthambi ochokera m’mayiko osiyanasiyana. Amuna ameneŵa anafotokoza mavuto amene amishonale atsopano amakumana nawo ndipo anapereka malangizo othandiza mogwirizana ndi zimene iwo akumana nazo. Ena a mavuto ameneŵa ndi kusiyana kwa chikhalidwe, nyengo yotentha ya chaka chonse, kapena mmene nkhani za zipembedzo ndi ndale zilili zosiyana ndi zimene ophunzirawo akuzidziŵa. Kodi n’chiyani chimene chingathandize amishonale atsopano kuzoloŵera malo awo atsopano? Kukonda Yehova, kukonda anthu, osayang’ana m’mbuyo ndiponso osachita zinthu mopupuluma. Mbale wina wa m’Komiti ya Nthambi anati: “Anthu omwe ali komwe tikutumikira akhalako zaka mazana ambiri ife tisanapiteko. Mwachionekere ifenso tingakhaleko ndipo tingakuzoloŵere. Nthaŵi zonse pamene takumana ndi mavuto, tinkawaona kukhala mwayi woti tikonze umunthu wathu. Mukadalira pemphero ndi mzimu wa Yehova, mudzaona kukwaniritsidwa kwa mawu a Yesu akuti, ‘Ine ndili pamodzi ndi inu.’”​—Mateyu 28:20.

Samuel Herd wa m’Bungwe Lolamulira anachititsa pulogalamuyi kufika pakaindeinde ndi nkhani yake yakuti, “Pitirizani Kulankhula Zazikulu za Mulungu.” Kutsanulidwa kwa mzimu woyera pa ophunzira a Yesu pa Pentekoste mu 33 C.E., kunapatsa ophunzirawo mphamvu zolankhulira “zazikulu za Mulungu.” Kodi n’chiyani lerolino chimene chingathandize amishonale atsopano kulankhula mwachangu za Ufumu wa Mulungu mofanana ndi ophunzira a Yesu? Ndi mzimu woyera umodzimodziwo. Mbale Herd analimbikitsa omaliza maphunzirowo ‘kukhala achangu mu mzimu,’ kusangalala ndi ntchito yawo, osaiwala maphunziro amene awalandira. (Aroma 12:11) Mbale Herd anati: “Baibulo ndi buku lapadera kwambiri la Mulungu. Musamalione mopepuka. Uthenga wake ndi wamoyo ndipo umafika pamtima. Ligwiritseni ntchito kukonza zinthu pamoyo wanu. Liloleni kusintha maganizo anu. Tetezani luso lanu la kulingalira mwa kuphunzira, kuŵerenga ndi kusinkhasinkha Malemba . . . Motsimikiza mtima khalani ndi cholinga chogwiritsa ntchito maphunziro a Gileadi kulankhulabe ‘zazikulu za Mulungu.’”

Pambuyo poŵerenga moni wochoka m’mayiko osiyanasiyana ndiponso atapereka madipuloma, wophunzira mmodzi anaŵerenga kalata yochokera kwa ophunzirawo yoyamikira chifukwa cha maphunziro amene anawalandira. Ndiyeno Mbale Lett anamaliza mwambo wosangalatsawu mwa kufotokoza 2 Mbiri 32:7 ndi Deuteronomo 20:1, 4. Mwa kugwirizanitsa ndemanga zake zomaliza ndi mawu ake oyamba, anamaliza ndi mawu akuti: “Okondeka omaliza maphunzironu, pamene mukupita, kukaloŵa m’nkhondo yauzimu ku malo anu antchito atsopano, kumbukirani kuti Yehova adzakhala limodzi nanu. Osaiwala mfundo yakuti okhala pamodzi ndi inu achuluka koposa aja okhala pamodzi ndi iwo.”

[Bokosi patsamba 25]

ZIŴERENGERO ZAKALASI

Chiŵerengero cha mayiko kumene ophunzira anachokera: 7

Chiŵerengero cha mayiko kumene anawatumiza: 17

Chiŵerengero cha ophunzira: 48

Avareji ya zaka zakubadwa: 33.7

Avareji ya zaka zimene akhala m’choonadi: 17.8

Avareji ya zaka zimene akhala akuchita utumiki wa nthaŵi zonse: 13.5

[Chithunzi patsamba 26]

Kalasi la 115 la Omaliza Maphunziro a Sukulu ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo

M’ndandanda umene uli pansipa, mizera taiŵerenga kuyambira kutsogolo kumka kumbuyo, ndipo mayina tawandandalika kuyambira kumanzere kumka kumanja mumzera uliwonse.

(1) Brown, T.; Goller, C.; Hoffman, A.; Bruzzese, J.; Trahan, S. (2) Smart, N.; Cashman, F.; Garcia, K.; Lojan, M.; Seyfert, S.; Gray, K. (3) Beckett, M.; Nichols, S.; Smith, K.; Gugliara, A.; Rappenecker, A. (4) Gray, S.; Vacek, K.; Fleming, M.; Bethel, L.; Hermansson, T.; Hermansson, P. (5) Rappenecker, G.; Lojan, D.; Dickey, S.; Kim, C.; Trahan, A.; Washington, A.; Smart, S. (6) Goller, L.; Burghoffer, T.; Gugliara, D.; Nichols, R.; Washington, S.; Kim, J. (7) Beckett, M.; Dickey, J.; Smith, R.; Garcia, R.; Hoffman, A.; Seyfert, R.; Brown, H. (8) Fleming, S.; Bruzzese, P.; Burghoffer, W.; Bethel, T.; Cashman, J.; Vacek, K.