Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tadalitsidwa Kwambiri Chifukwa Chopitiriza Kukhala ndi Mtima Waumishonale

Tadalitsidwa Kwambiri Chifukwa Chopitiriza Kukhala ndi Mtima Waumishonale

Mbiri ya Moyo Wanga

Tadalitsidwa Kwambiri Chifukwa Chopitiriza Kukhala ndi Mtima Waumishonale

YOSIMBIDWA NDI TOM COOKE

Madzulo a tsiku lina kunamveka kulira kwa mfuti ndipo mwadzidzidzi bata limene linalipo linasokonezeka. Zipolopolo zinkadutsa m’mitengo ya pabwalo pa nyumba yathu mothamanga kwambiri. Kodi n’chiyani chinkachitika? Pasanapite nthaŵi yaitali tinamva kuti asilikali alanda boma ndipo mkulu wankhondo, Idi Amin, ndi amene anali kulamulira dziko la Uganda. Mmenemu munali m’chaka cha 1971.

N’CHIFUKWA chiyani ine ndi mkazi wanga, Ann, tinachoka ku England, dziko la mtendere, n’kupita ku dziko la ku Africa kumene mtendere wake ukanatha kusokonezeka nthaŵi ina iliyonse? N’zoona kuti mwachibadwa, ndimafuna kuona zatsopano komanso zachilendo, koma chifukwa chachikulu chimene chinandichititsa kutero ndi chitsanzo cha makolo anga chochita utumiki wa Ufumu mwachangu chimene chinandilimbikitsa kukhala ndi mtima waumishonale.

Ndimakumbukira tsiku lina kukutentha mu August 1946 pamene makolo anga anakumana ndi Mboni za Yehova kwa nthaŵi yoyamba. Anaima pakhomo la kumaso kwa nyumba yathu n’kulankhula kwa nthaŵi yaitali ndi alendo aŵiri. Alendoŵa, Fraser Bradbury ndi Mamie Shreve, ankabwera kunyumbako nthaŵi zambiri ndipo m’miyezi yotsatira, moyo wa banja lathu unasintha kwambiri.

Chitsanzo cha Kulimba Mtima cha Makolo Anga

Makolo anga ankachita nawo ntchito zosiyanasiyana m’dera lathulo. Mwachitsanzo, patatsala nthaŵi yochepa kuti ayambe kuphunzira Baibulo, m’nyumba mwathu anakongoletsamo ndi zithunzi za Winston Churchill. Panthaŵi ya chisankho cha dzikolo, chimene chinachitika nkhondo itatha, nyumba yathu inali malo okumanira anthu a mu komiti ya chipani cha Conservative. Banja lathu linkadziŵananso ndi atsogoleri a tchalitchi ndiponso akuluakulu a m’deralo. Ngakhale kuti ndinali ndi zaka zisanu ndi zinayi zokha panthaŵiyo, ndinaona kuti achibale athu anakhumudwa kwambiri atamva kuti tikufuna kukhala Mboni za Yehova.

Chitsanzo cholalikira ndi mtima wonse ndiponso mopanda mantha cha Mboni zimene tinali kugwirizana nazo chinalimbikitsa makolo anga kukhala achangu pantchito yolalikira. Posakhalitsa, bambo anga anayamba kukamba nkhani za anthu onse pogwiritsa ntchito chokuzira mawu m’dera la masitolo ambiri ku Spondon, mudzi umene tinali kukhala, pamene anafe tinkaima pa malo oonekera bwino titatenga Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! m’manja. Kunena zoona, ana amene ndinali kuphunzira nawo limodzi kusukulu akamafika pamene panali ine, ndinkalakalaka nditaloŵa pansi kuti asandione.

Chitsanzo cha makolo anga chinalimbikitsa mlongo wanga wamkulu, Daphne, kuyamba upainiya. Mu 1955, iye anakaphunzira nawo ku Sukulu ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo ndipo anamutumiza kukachita umishonale ku Japan. * Koma mlongo wanga wamng’ono, Zoe, anasiya kutumikira Yehova.

Panthaŵiyi, ndinamaliza maphunziro a luso la zojambulajambula. Masiku amenewo, nkhani yofunika kwambiri kwa ophunzira anzanga inali yokhudza kuphunzira usilikali kaya munthu akufuna kapena ayi. Nditawauza kuti sindingaloŵe usilikali pa zifukwa za chipembedzo, anaona ngati njerengo. Nkhani imeneyi inandipatsa mpata wokambirana za m’Baibulo ndi ena mwa ophunzirawo. Posakhalitsa, ndinamangidwa ndi kuikidwa m’ndende kwa miyezi 12 chifukwa chokana kuloŵa usilikali. M’modzi mwa ophunzira ku koleji yophunzitsa luso la zojambulajambulayo amene anasonyeza chidwi ndi uthenga wa m’Baibulo, patapita nthaŵi anadzakhala mkazi wanga. Koma ndimulole Ann akufotokozereni yekha mmene anaphunzirira choonadi.

Mmene Ann Anayambira Choonadi

“Anthu a m’banja langa analibe chipembedzo, ndipo sindinabatizidwe m’chipembedzo chilichonse. Koma ndinkafuna kudziŵa nkhani za chipembedzo ndipo ndinkapita nawo kuchipembedzo chilichonse chimene anzanga ankapitako. Ndinayamba kuchita chidwi kwambiri ndi Baibulo pamene ndinamvetsera Tom ndi Mboni ina akukambirana mosangalatsa ndi ophunzira ena pakolejipo. Pamene Tom ndi Mboni inayo anawapititsa kundende chifukwa chokana kuloŵa usilikali, ndinakhumudwa kwambiri.

“Ndinapitiriza kulemberana makalata ndi Tom pamene anali kundende, ndipo chidwi changa pa nkhani ya Baibulo chinakula kwambiri. Nditapita ku London kukapitiriza maphunziro anga, ndinavomera kuphunzira Baibulo ndi Muriel Albrecht. Muriel anali atachitapo umishonale ku Estonia, ndipo iye ndi mayi ake anandilimbikitsa kwambiri. Patangopita milungu yochepa chabe, ndinayamba kupezeka pa misonkhano ndiponso kugaŵira Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! kunja kwa siteshoni ya Victoria.

“Ndinkasonkhana nawo mumpingo wa Southwark kum’mwera kwa mzinda wa London. Mpingowu unali ndi abale ndi alongo auzimu ochokera m’mayiko osiyanasiyana, omwe ambiri a iwo sanali opeza bwino. Ngakhale kuti ndinali mlendo, anandilandira ngati ndine m’modzi mwa iwo. Chikondi chimene anasonyeza mumpingowo n’chimene chinandichititsa kutsimikiza kuti ichi chinali choonadi, ndipo ndinabatizidwa mu 1960.”

Zolinga Zofanana Koma Zochitika Zosiyana

Ine ndi Ann tinakwatirana chakumapeto kwa chaka cha 1960, ndipo tinali ndi cholinga chodzakhala amishonale. Koma zinthu zinasintha pamene tinadziŵa kuti tinali kuyembekezera kukhala ndi mwana. Mwana wathu wamkazi Sara atabadwa, ine ndi Ann tinafunabe kukatumikira ku dziko limene kunkafunika olalikira Ufumu ambiri. Ndinafunsira ntchito m’mayiko ambiri, ndipo kenako mu May 1966, ndinalandira kalata kuchokera ku Unduna wa Zamaphunziro ku Uganda yondiuza kuti ndipite ndikagwire ntchito kumeneko. Komabe, panthaŵiyi n’kuti Ann ali ndi pakati pa mwana wathu wachiŵiri. Ena anakayikira ngati kunali kwanzeru kuganiza zosamuka. Tinafunsa dokotala wathu, amene anati: “Ngati mupite, muyenera kukwera ndege mkazi wanu asanakwanitse miyezi isanu ndi iŵiri ali ndi pakati.” Motero, tinanyamuka mwamsanga kupita ku Uganda. Chifukwa cha zimenezi, makolo athu sanathe kuona mwana wathu wamkazi wachiŵiri, Rachel, mpaka pamene anali ndi zaka ziŵiri. Popeza tsopano tili ndi zidzukulu, tikutha kumvetsa mtima wodzimana umene makolo athu okondedwa anasonyeza.

Zinali zosangalatsa pamene tinafika ku Uganda mu 1966 ngakhale kuti zinalinso zovutirapo. Titangotsika m’ndege, nthaŵi yomweyo tinachita chidwi kwambiri ndi mitundu yosiyanasiyana ya zinthu zimene tinaona. Mitundu ya zinthuyo inali yowala kwambiri. Malo athu oyamba kukhala anali tawuni yaing’ono ya Iganga, yomwe inali pa mtunda wa makilomita 50 kuchokera ku tawuni ya Jinja, imene inali kudera limene kunayambira mtsinje wa Nile. Mboni zimene tinali nazo pafupi zinali gulu lakutali limene linali ku Jinja. Gilbert ndi Joan Walters ndiponso Stephen ndi Barbara Hardy, anali amishonale amene anali kusamalira gululo. Ndinapempha a kuntchito kwanga kuti andisamutse ndizikagwirira ntchito ku Jinja n’cholinga choti tikathe kuthandiza bwino gulu limeneli. Rachel atangobadwa kumene, tinasamukira ku Jinja. Kumeneko tinasangalala kutumikira ndi gulu lochepa la Mboni zokhulupirika pamene linali kukula n’kudzakhala mpingo wachiŵiri ku Uganda.

Kutumikira Monga Banja M’dziko Lakunja

Ine ndi Ann timaona kuti malo amene tinasankha kulererako ana athu anali abwino kwambiri. Tinasangalala kugwira ntchito limodzi ndi amishonale ochokera m’mayiko osiyanasiyana ndiponso kuthandizira kuti mpingo umene unangoyambika kumenewo ukule. Tinkakonda kukhalira limodzi ndi abale ndi alongo athu a ku Uganda amene nthaŵi zambiri ankabwera kudzacheza kunyumba kwathu. Makamaka Stanley ndi Esinala Makumba anatilimbikitsa kwambiri.

Komabe, alendo amene ankafika kunyumba kwathu si abale okhaŵa, chifukwa nyama zosiyanasiyana zimene tinali nazo pafupi zinkafikanso pakhomo pathu. Mvuwu zinkatuluka mu mtsinje wa Nile usiku ndipo zinkafika pafupi kwambiri ndi nyumba yathu. Ndikukumbukira nthaŵi ina pamene tinaona nsato ya mamita asanu ndi imodzi pabwalo pa nyumba yathu. Nthaŵi zina tinkapita kukaona nyama ku nkhalango zosungirako nyama, kumene mikango ndi nyama zina zam’tchire zinkayenda momasuka.

Mu utumiki, zinali zachilendo kwa anthu a m’deralo akationa popeza anali asanaonepo chikuku chonyamulira mwana. Tikamayenda nyumba ndi nyumba, nthaŵi zambiri pankakhala gulu la ana limene linkatitsatira pambuyo. Anthu ankatiyang’anitsitsa mwaulemu ndiyeno n’kumasisita kamwana kachizunguko. Kulalikira kunali kosangalatsa chifukwa anthu ake anali aulemu kwambiri. Tinaganiza kuti anthu onse aloŵa m’choonadi, chifukwa zinali zosavuta kuyambitsa maphunziro a Baibulo. Komabe, ambiri zinawavuta kusiya miyambo yawo yosagwirizana ndi Malemba. Ngakhale zinali choncho, anthu ambiri anatsatira mfundo zapamwamba za m’Baibulo, ndipo mpingo unakula. Msonkhano wathu wadera woyamba ku Jinja mu 1968 unali wosaiŵalika. Timakumbukirabe tikuona ena mwa anthu amene tinaphunzira nawo Baibulo akubatizidwa mu mtsinje wa Nile. Koma mtendere wathu unadzasokonezeka pasanapite nthaŵi yaitali.

Chiletso Chinayesa Chikhulupiriro ndi Nzeru Zathu

Mu 1971, mkulu wa asilikali Idi Amin analanda boma. Panali chisokonezo chachikulu ku Jinja, ndipo zimene ndafotokoza kuchiyambi kwa nkhani ino zinachitika pamene tinali kumwa tiyi pabwalo pa nyumba yathu. M’zaka ziŵiri zotsatira, amwenye ambiri anawathamangitsa m’dzikolo. Anthu ena a mayiko akunja anaganiza zochoka, ndipo m’sukulu ndi m’zipatala zinthu sizinalinso kuyenda bwino. Ndiyeno panali chilengezo choipa kwambiri chakuti Mboni za Yehova zinaletsedwa. Podera nkhaŵa moyo wathu, Dipatimenti ya Zamaphunziro inatisamutsira ku likulu la dzikolo, ku Kampala. Kusamuka kumeneku kunali kopindulitsa m’njira ziŵiri. Anthu sanali kutidziŵa bwinobwino ku Kampala ndipo motero tinali ndi ufulu woyenda. Panalinso ntchito yambiri yoti tichite mu mpingo ndiponso mu utumiki wakumunda.

Mmene zinthu zinalili kwa ife ndi mmenenso zinalili kwa Brian ndi Marion Wallace ndi ana awo aŵiri, ndipo nawonso anaganiza zokhalabe ku Uganda. Tinkasangalala kwambiri kukhala nawo limodzi pamene tinali kutumikira mumpingo wa Kampala panthaŵi yovutayi. Nkhani zimene tinaŵerenga zokhudza abale athu amene anali kutumikira ali pa chiletso m’mayiko ena tsopano zinatilimbikitsa mwapadera. Tinkakumana m’magulu ang’onoang’ono ndipo tinkasonkhana gulu lalikulu kamodzi pamwezi pa malo otchedwa Entebbe Botanical Gardens, komwe tinkayerekezera ngati tinali pa phwando. Ana athu anaona kuti imeneyi inali nzeru yabwino kwambiri.

Tinafunika kukhala osamala kwambiri mmene tinali kuchitira ntchito yolalikira. Azungu akanaonekera kwambiri ngati akanati azipita ku nyumba za anthu a ku Uganda. Motero, magawo athu anali masitolo, nyumba zogundizana, ndi m’masukulu. Njira ina imene ndinkagwiritsa ntchito m’masitolo inali yofunsa ngati ali ndi chinthu chimene ndinkadziŵa kuti sichikupezeka, monga shuga kapena mpunga. Wogulitsa m’sitoloyo akadandaula chifukwa cha zimene zinkachitika m’dzikolo, ndinkamuuza uthenga wa Ufumu. Njira imeneyi inathandiza kwambiri. Nthaŵi zina ndinkachoka pa sitolo titapangana kuti ndidzabwerenso komanso ndinkapeza nawo zinthu zochepa zimene zinali zosoŵa kwambiri.

Komabe, chiwawa chinkachitika paliponse. Chifukwa chakuti ubale wa pakati pa dziko la Uganda ndi la Britain unaipiraipira, akuluakulu a boma sanavomereze kuti ndipitirize ntchito yanga nthaŵi imene tinapangana itatha. Motero, mu 1974, titakhala zaka zisanu ndi zitatu ku Uganda, tinawatsanzika mwachisoni abale athu. Komabe, mtima wathu wa umishonale sunathe.

Kupita ku New Guinea

Mu January 1975, tinapeza mwayi wokagwira ntchito ku Papua New Guinea. Chimenechi chinali chiyambi cha zaka zisanu ndi zitatu zosangalatsa zimene tinatumikira ku chigawo chimenechi cha ku nyanja ya Pacific. Kuchita zinthu limodzi ndi abale athu ndiponso utumiki zinachititsa moyo wathu kukhala watanthauzo ndiponso wopindulitsa.

Banja lathu likamakumbukira nthaŵi imene tinakhala ku Papua New Guinea limakumbukira kuti inali nthaŵi ya maseŵero a Baibulo. Chaka chilichonse, tinali kukonza nawo maseŵero a pa msonkhano wachigawo, ndipo tinkasangalala nazo kwambiri. Tinkasangalala kukhala limodzi ndi mabanja ambiri okonda zinthu zauzimu, ndipo mabanja ameneŵa analimbikitsa kwambiri ana athu. Mwana wathu wamkulu, Sara, anakwatiwa ndi mpainiya wapadera, Ray Smith, ndipo anatumikira limodzi monga apainiya apadera kufupi ndi malire a chigawo cha Irian Jaya (chimene tsopano ndi Papua, chigawo cha ku Indonesia). Ankakhala m’nyumba ya udzu kumidzi, ndipo Sara anati nthaŵi imene anakhala kumeneko anaphunzira zambiri.

Kusintha Moyo Wathu Kuti Tigwirizane ndi Kusintha kwa Zinthu

Panthaŵi imeneyi, makolo anga anafunika kuwasamalira mwapadera. M’malo moti tibwerere ku England, makolo anga anavomera zobwera kudzakhala nafe, ndipo tonse tinasamukira ku Australia mu 1983. Anakhalanso kwakanthaŵi ndi mlongo wanga Daphne, yemwe anali akadali ku Japan. Makolo anga atamwalira, ine ndi Ann tinaganiza zoyamba upainiya wokhazikika, ndipo zimenezi zinachititsa kuti tikhale ndi mwayi wochita utumiki umene ndinauona kuti unali wovuta kwambiri.

Titangoyamba kumene upainiya tinapemphedwa kuti titumikire m’ntchito yoyang’anira dera. Kuyambira ndili mwana, kuchezera kwa woyang’anira dera ndinkakuona kuti n’kwapadera kwambiri. Tsopano nthaŵi ino ineyo ndinali woyang’anira dera. Imeneyi inali ntchito yovuta kwambiri kuposa ntchito ina iliyonse imene tinachitapo kudzafika panthaŵi imeneyi, komabe nthaŵi zambiri Yehova anatithandiza m’njira zimene sitinaonepo n’kale lonse.

Mbale Theodore Jaracz’ atadzayendera nthambi ku Australia mu 1990, tinamufunsa maganizo ake ngati anaona kuti tinali achikulire kwambiri moti sitikanatha kukachita utumiki wa nthaŵi zonse ku mayiko ena. Iye anati: “Bwanji mutakatumikira ku zilumba za Solomon Islands?” Motero, pamene ine ndi Ann tinali ndi zaka za m’ma 50, tinanyamuka kupita ku dziko limene linadzakhala loyamba kukatumikirako monga amishonale ovomerezedwa.

Kutumikira ku “Zilumba Zachimwemwe”

Zilumba za Solomon Islands zimadziŵikanso kuti Zilumba Zachimwemwe, ndipo nthaŵi imene tatumikira ku zilumbazi m’zaka khumi zapitazi yakhaladi nthaŵi yachimwemwe. Ine ndi Ann tinkaona mtima wachifundo wa abale ndi alongo a ku Solomon Islands pamene ndinali kutumikira monga woyang’anira chigawo. Kutichereza kwawo kunakhudza mitima yathu, ndipo onse anali ololera pamene ndinali kuyesetsa kufotokoza zinthu m’mawu a chinenero cha Chipijini cha ku Solomon Islands chimene ndinaganiza kuti chinali chovomerezeka. Chinenerochi ndi chimodzi mwa zinenero zimene zili ndi mawu ochepa kwambiri pa dziko lonse.

Titangofika kumene ku Solomon Islands, anthu otsutsa anayesera kutisokoneza kuti tisagwiritse ntchito Nyumba yathu ya Misonkhano. A mpingo wa Anglican anasumira Mboni za Yehova, ponena kuti mbali ina ya Nyumba yathu ya Misonkhano yatsopano ku Honiara inali pa malo awo. Boma linawakhalira kumbuyo, motero tinachita apilo ku khoti lalikulu. Zotsatira za chigamulo cha apilo zikanachititsa kuti tiphwasule kapena tisaphwasule Nyumba ya Misonkhanoyo imene inakonzedwa kuti muzitha kuloŵa anthu 1,200.

Mlanduwo unakhala m’khoti kwa mlungu wathunthu. Loya wa anthu otiimba mlanduwo anasonyeza modzitukumula kuti apambana mlanduwo pamene anali kufotokoza mfundo zotitsutsa. Ndiyeno, pogwiritsa ntchito mfundo zamphamvu, imodzi ndi imodzi, loya wathu, Mbale Warren Cathcart wa ku New Zealand, anaonetsa poyera kuti mfundo zimene otitsutsawo anafotokoza zinali zabodza ndiponso zopanda pake. Pofika Lachisanu, nkhani ya zochitika zochititsa chidwi za m’khotimo inafalikira kutali, ndipo m’khotimo munadzaza atsogoleri a matchalitchi, akuluakulu a boma, ndi abale athu achikristu. Ndikukumbukira mmene analembera molakwitsa chidziŵitso cha pandandanda ya khotilo. Anati: “Boma la Solomon Islands ndi Tchalitchi cha ku Melanesia Akuimbana Mlandu ndi Yehova.” Tinapambana mlanduwo.

Komabe, bata limene tinali nalo ku Zilumba Zachimwemwe silinatenge nthaŵi yaitali. Ine ndi Ann tinapezekanso kuti tili m’chipwirikiti ndi m’chiwawa chimene chinayambika chifukwa cha zigaŵenga zimene zinafuna kulanda boma. Kulimbana kwa mafuko a m’dzikolo kunayambitsa nkhondo yapachiŵeniŵeni. Pa June 5, 2000, zigaŵengazo zinalanda boma ndipo likulu la dzikolo linali m’manja mwa zigaŵenga zimene zinali ndi mfuti. Kwa milingu ingapo, Nyumba yathu ya Misonkhano inali malo othaŵirako anthu amene anathamangitsidwa m’nyumba zawo. Akuluakulu a boma anadabwa kuti abale athu achikristu a m’mafuko amene anali kulimbanawo anali kukhalira limodzi monga banja la mtendere m’Nyumba ya Misonkhanoyo. Umenewu unali ulaliki wabwino kwambiri.

Ngakhalenso zigaŵengazo zinkalemekeza kusaloŵerera m’nkhani zandale kwa Mboni za Yehova. Zimenezi zinatithandiza kupempha m’modzi mwa akuluakulu a zigawengazo kuti alole galimoto imene inatenga mabuku ndi zinthu zina kukafika ku gulu laling’ono la abale. Abalewo anali kudera lina kumene kunali asilikali amene anali kulimbana nawowo. Titapeza mabanja amene tinali titasiyana nawo kwa miyezi ingapo, ndikukayika ngati panali amene sanagwetse msozi.

Pali Zambiri Zotichititsa Kuyamikira

Tikamaganizira za moyo wathu potumikira Yehova, pali zambiri zotichititsa kuyamikira. Monga makolo, tasangalala kwambiri kuona ana athu onse ndi amuna awo, Ray ndi John, akupitiriza kutumikira Yehova mokhulupirika. Atithandiza kwambiri pa ntchito yathu ya umishonale.

Pa zaka 12 zimene zapitazi, ine ndi Ann takhala ndi mwayi wotumikira pa ofesi ya nthambi ya ku Solomon Islands, ndipo panthaŵi imeneyi, taona chiŵerengero cha olengeza Ufumu chikuwonjezeka moŵirikiza n’kufika pa 1,800. Posachedwapa, ndinalandira mwayi wina wokaphunzira nawo m’Sukulu ya a m’Komiti ya Nthambi ku Patterson, New York. Kunena zoona, takhaladi ndi moyo wosangalatsa ndipo tapeza madalitso ambiri chifukwa chopitiriza kukhala ndi mtima waumishonale.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 10 Onani nkhani yakuti “We Did Not Procrastinate” (Sitinazengereze) mu Nsanja ya Olonda yachingelezi ya January 15, 1977.

[Chithunzi patsamba 23]

Pa tsiku la ukwati wathu, 1960

[Chithunzi patsamba 24]

Ku Uganda, Stanley ndi Esinala Makumba analimbikitsa kwambiri banja lathu

[Chithunzi patsamba 24]

Sara akuloŵa m’kanyumba ka anthu oyandikana nawo

[Chithunzi patsamba 25]

Ndinkajambula zithunzi kuti zindithandize kuphunzitsa anthu a ku Solomon Islands

[Chithunzi patsamba 25]

Kusonkhana ndi mpingo umene unali kutali ku Solomon Islands

[Chithunzi patsamba 26]

Banja lathu masiku ano