Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chikondi Chokhulupirika cha Yehova N’chachikulu

Chikondi Chokhulupirika cha Yehova N’chachikulu

Chikondi Chokhulupirika cha Yehova N’chachikulu

“Yehova . . . ndi wa chifundo chachikulu [“wokoma mtima mwachikondi kwambiri,” NW].”​—SALMO 145:8.

1. Kodi chikondi cha Mulungu n’chachikulu bwanji?

“MULUNGU ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:8) Mawu osangalatsa ameneŵa amatsimikizira kuti Yehova amalamulira mwachikondi. Inde, ngakhale anthu amene samumvera amapindula ndi dzuŵa ndiponso mvula zimene amapereka mwachikondi. (Mateyu 5:44, 45) Chifukwa choti Mulungu amakonda anthu, ngakhale adani ake angalape n’kubwerera kwa iye ndi kupeza moyo wosatha. (Yohane 3:16) Koma posachedwapa, Yehova adzawononga oipa omwe sangasinthe kuti anthu amene amam’konda asangalale ndi moyo wosatha m’dziko latsopano lolungama.​—Salmo 37:9-11, 29; 2 Petro 3:13.

2. Kodi ndi mbali iti yapadera ya chikondi imene Yehova amasonyeza kwa odzipatulira kwa iye?

2 Yehova amasonyeza chikondi kwa olambira ake mwa njira yamtengo wapatali ndiponso yokhalitsa. Mawu achihebri omasuliridwa kuti “kukoma mtima kwachikondi” kapena kuti “chikondi chokhulupirika” ndiwo amaimira chikondi chimenechi. Mfumu Davide ya Israyeli wakale inaona kukoma mtima kwachikondi kwa Mulungu kukhala kofunika kwambiri. Chifukwa cha zimene anakumana nazo ndiponso kusinkhasinkha mmene Mulungu anachitira zinthu ndi anthu ena, Davide anaimba motsimikiza kuti: ‘Yehova . . . ndi wokoma mtima mwachikondi kwambiri.’​—Salmo 145:8.

Kuzindikira Okhulupirika a Mulungu

3, 4. (a) Kodi Salmo 145 limatithandiza bwanji kuzindikira okhulupirika a Yehova? (b) Kodi okhulupirika a Mulungu ‘amam’dalitsa’ bwanji?

3 Ponena za Yehova Mulungu, mayi wa mneneri Samueli, Hana, anati: “Adzasunga mapazi a okondedwa [“okhulupirika,” NW] ake.” (1 Samueli 2:9) Kodi “okhulupirika” ameneŵa ndani? Mfumu Davide anapereka yankho. Atafotokoza makhalidwe apadera a Yehova, Iye anati: “Okhulupirika anu adzakudalitsani.” (Salmo 145:10, NW) Mungadabwe kuti, kodi anthu angadalitse bwanji Mulungu? Kwenikweni amachita zimenezi mwa kum’lemekeza kapena kuti kum’kweza.

4 Okhulupirika a Yehova tingawazindikire chifukwa amam’kweza. Pamene akucheza ndiponso ali pamisonkhano yachikristu, kodi amakambirana nkhani imodzi iti? Mwachionekere ndi ya Ufumu wa Yehova! Atumiki okhulupirika a Mulungu amamva mofanana ndi Davide amene anaimba kuti: “Adzanenera ulemerero wa ufumu wanu [Yehova], adzalankhulira mphamvu yanu.”​—Salmo 145:11.

5. Kodi timadziŵa bwanji kuti Yehova amamvetsera pamene okhulupirika ake am’kweza?

5 Kodi Yehova amamvetsera okhulupirika ake akamamulemekeza? Inde, amamvetsera zimene amalankhula. Mu ulosi wonena za kulambira koona masiku athu ano, Malaki analemba kuti: “Pamenepo iwo akuopa Yehova analankhulana wina ndi mnzake; ndipo Yehova anawatchera khutu namva, ndi buku la chikumbutso linalembedwa pamaso pake, la kwa iwo akuopa Yehova, nakumbukira dzina lake.” (Malaki 3:16) Zimam’sangalatsa kwambiri Yehova pamene okhulupirika ake am’kweza ndipo amawakumbukira.

6. Kodi ndi ntchito iti imene imatithandiza kuzindikira okhulupirika a Mulungu?

6 Atumiki okhulupirika a Yehova tingawazindikirenso chifukwa cha kulimba mtima kwawo akamagwiritsa ntchito mpata uliwonse kulankhula ndi anthu amene sali olambira Mulungu woona. Ndithudi, okhulupirika a Mulungu ‘amadziŵitsa ana a anthu zamphamvu zake, ndi ulemerero waukulu wa ufumu wake.’ (Salmo 145:12) Kodi mumafunafuna ndi kugwiritsa ntchito mokwanira mipata yoti mulankhule ndi anthu osakhulupirira za ufumu wa Yehova? Mosiyana ndi maboma a anthu amene adzatha posachedwapa, ufumu wake ndi wosatha. (1 Timoteo 1:17) N’kofunika kwambiri kuti anthu aphunzire za ufumu wosatha wa Yehova ndi kukhala ku mbali ya ufumuwo. Davide anaimba kuti: “Ufumu wanu ndiwo ufumu womka muyaya, ndi kuweruza kwanu kufikira mibadwo yonse yonse.”​—Salmo 145:13.

7, 8. Kodi n’chiyani chimene chinachitika mu 1914, ndipo pali umboni wotani woti Mulungu tsopano akulamulira mwa Ufumu wa Mwana wake?

7 Kuyambira mu 1914, pakhala chochititsa china kuti tilankhule za ufumu wa Yehova. Mu chaka chimenechi Mulungu anakhazikitsa Ufumu wakumwamba Waumesiya wokhala ndi Yesu Kristu, Mwana wa Davide, monga Mfumu. Motero, Yehova anakwaniritsa lonjezo lakuti ufumu wa Davide udzakhazikitsidwa ku nthaŵi zonse.​—2 Samueli 7:12, 13; Luka 1:32, 33.

8 Umboni wakuti Yehova tsopano akulamulira mwa Ufumu wa Mwana wake, Yesu Kristu, ukuoneka ndi chizindikiro cha kukhalapo kwa Yesu chimene ngakhale pakalipano chikukwaniritsidwa. Mbali yaikulu ya chizindikiro chimenechi ndi ntchito imene Yesu analosera kuti idzachitidwa ndi okhulupirika a Mulungu pamene anati: “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.” (Mateyu 24:3-14) Chifukwa choti okhulupirika a Mulungu akukwaniritsa mwachangu ulosi umenewu, anthu oposa 6 miliyoni amuna, akazi ndi ana akuchita nawo ntchito yaikulu imeneyi imene sidzabwerezedwanso. Posachedwapa chimaliziro chidzafika pa onse amene amatsutsa Ufumu wa Yehova.​—Chivumbulutso 11:15, 18.

Kupindula ndi Ufumu wa Yehova

9, 10. Kodi ndi kusiyana kotani kumene kulipo pakati pa Yehova ndi anthu olamulira?

9 Ngati ndife Akristu odzipatulira, tikupindula kwambiri ndi ubwenzi wathu ndi Yehova Ambuye Mfumu. (Salmo 71:5; 116:12) Mwachitsanzo, chifukwa choti timaopa Mulungu ndipo timachita chilungamo, iye amatiyanja ndipo tili oyandikana naye mwauzimu. (Machitidwe 10:34, 35; Yakobo 4:8) Mosiyana ndi zimenezi, anthu olamulira nthaŵi zambiri amagwirizana ndi anthu otchuka, monga atsogoleri a asilikali, amalonda achuma kapena anthu otchuka chifukwa cha maseŵera ndi zosangalatsa. Malinga ndi kunena kwa nyuzipepala ina ya mu Africa muno yotchedwa Sowetan, mwamuna wina wotchuka wogwira ntchito m’boma ananena zotsatirazi zokhudza madera osauka m’dziko lake: “Ndikumvetsa chifukwa chake ambirife sitifuna kupita ku madera ameneŵa. Ndi chifukwa choti timafuna kuiŵala kuti madera oterewa aliko. Zimativutitsa chikumbumtima ndipo timachita manyazi chifukwa cha galimoto zodula zimene timayendera.”

10 N’zoona kuti olamulira ena amaganizira moona mtima za moyo wa nzika zawo. Koma ngakhale olamulira abwino kwambiri sadziŵa nzika zawo bwinobwino. Ndithudi, tingafunse kuti: Kodi pali wolamulira amene amaganizira kwambiri nzika zake zonse moti amathandiza mwamsanga nzika iliyonse pamavuto? Inde, alipo. Davide analemba kuti: “Yehova agwiriziza onse akugwa, nawongoletsa onse owerama.”​—Salmo 145:14.

11. Kodi ndi mayesero otani amene amachitikira okhulupirika a Mulungu ndipo ali ndi thandizo lotani?

11 Mayesero ndiponso mavuto ambiri amachitikira okhulupirika a Yehova Mulungu chifukwa cha kupanda ungwiro ndiponso chifukwa choti akukhala m’dziko limene ligona m’mphamvu za Satana “woipayo.” (1 Yohane 5:19; Salmo 34:19) Akristu amakumana ndi chizunzo. Ena amavutika chifukwa cha matenda aakulu kapena kuferedwa. Nthaŵi zina, zolakwa za okhulupirika a Yehova zingawachititse ‘kuwerama’ chifukwa chokhumudwa. Komabe, mavuto alionse amene angawachitikire, Yehova nthaŵi zonse ali wokonzeka kuwatonthoza ndi kuwalimbitsa mwauzimu. Mfumu Yesu Kristu ali ndi chidwi chofanana ndi chimenechi, chokonda nzika zake zokhulupirika.​—Salmo 72:12-14.

Chakudya Chokwanira M’nyengo Yake

12, 13. Kodi Yehova amazimapatsa motani “zamoyo zonse” zosoŵa zawo?

12 Chifukwa cha kukoma mtima kwake kwachikondi kumene n’kwakukulu, Yehova amapatsa atumiki ake zosoŵa zonse. Zimenezi zimaphatikizapo kuwapatsa chakudya chabwino. Mfumu Davide inalemba kuti: “Maso a onse ayembekeza Inu [Yehova]; ndipo muwapatsa chakudya chawo m’nyengo zawo. Muwolowetsa dzanja lanu, nimukwaniritsira zamoyo zonse chokhumba chawo.” (Salmo 145:15, 16) Ngakhale m’nthaŵi yamavuto, Yehova angayendetse zinthu mwa njira yoti okhulupirika ake apeze “chakudya cha patsiku.”​—Luka 11:3; 12:29, 30.

13 Davide ananena kuti “zamoyo zonse” zimakwaniritsidwa. Zimenezi zikuphatikizapo nyama. Pakanapanda zomera zambiri za pamtunda ndi za m’nyanja, bwenzi zolengedwa za m’madzi, mbalame ndi nyama za pamtunda zilibe mpweya wopuma wa oxygen kapena chakudya. (Salmo 104:14) Koma Yehova amatsimikizira kuti zosoŵa zawo zonse zakwaniritsidwa.

14, 15. Kodi chakudya chauzimu chikuperekedwa bwanji masiku ano?

14 Mosiyana ndi nyama, anthu amafuna zinthu zauzimu. (Mateyu 5:3) Yehova amakwaniritsa bwino kwambiri zosoŵa zauzimu za okhulupirika ake. Yesu asanafe, analonjeza kuti “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” adzapatsa otsatira a Yesu ‘chakudya [chauzimu] panthaŵi yake.’ (Mateyu 24:45) Otsalira odzozedwa a 144,000 amapanga gulu la kapolo masiku ano. Kudzera mwa iwo, Yehova waperekadi chakudya chauzimu chambiri.

15 Mwachitsanzo, anthu a Yehova ambiri tsopano akupindula ndi Baibulo latsopano lomasuliridwa molondola m’chinenero chawo. Baibulo la New World Translation of the Holy Scriptures lakhalatu dalitso lalikulu kwambiri! Ndiponso, zothandizira kuphunzira Baibulo zambiri zikufalitsidwabe m’zinenero zoposa 300. Chakudya chauzimu chonsechi chakhala dalitso kwa olambira oona padziko lonse. Kodi ndani ayenera kutamandidwa chifukwa cha zonsezi? Yehova Mulungu. Mwa kukoma mtima kwake kwachikondi kumene n’kwakukulu, wachititsa kuti gulu la kapolo lipereke ‘chakudya panyengo yake.’ Kudzera m’makonzedwe ameneŵa ‘chokhumba cha zamoyo zonse’ m’paradaiso wauzimu wamakono chikukwaniritsidwa. Ndipo atumiki a Yehova akusangalala zedi kuyembekezera kuona dziko lapansi likukhala paradaiso!​—Luka 23:42, 43.

16, 17. (a) Kodi pali zitsanzo zotani za chakudya chauzimu chimene chinafika panthaŵi yake? (b) Kodi Salmo 145 limafotokoza bwanji maganizo a okhulupirika a Mulungu ponena za nkhani yaikulu imene Satana anayambitsa?

16 Taganizirani za chitsanzo chapadera cha chakudya chauzimu cholandiridwa panthaŵi yake. Mu 1939, nkhondo yachiŵiri yapadziko lonse inayamba ku Ulaya. Mu chaka chimenechi, Nsanja ya Olonda ya November 1 inali ndi nkhani yakuti “Kusaloŵerera M’zandale Komanso za M’dziko.” Chifukwa cha zinthu zomveka bwino zimene nkhaniyo inanena, Mboni za Yehova padziko lonse lapansi zinaona kufunika kosaloŵerera m’zochita za mayiko omwe anali kumenyana. Zimenezi zinachititsa kuti maboma a mbali zonse ziŵiri zomwe zinamenya nkhondo ya zaka zisanu ndi chimodziyo akwiyire Mbonizo. Ngakhale kuti analetsedwa kugwira ntchito zawo ndiponso anali kuzunzidwa, okhulupirika a Mulungu anapitirizabe kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu. Kuyambira mu 1939 mpaka 1946, anadalitsidwa ndi kuwonjezereka pafupifupi kuŵirikiza kaŵiri. Ndiponso, mbiri yochititsa chidwi ya kukhulupirika kwawo panthaŵi ya nkhondo imeneyi yapitirizabe kuthandiza anthu kuzindikira chipembedzo choona.​—Yesaya 2:2-4.

17 Chakudya chauzimu chimene Yehova amapereka ndi chapanthaŵi yake komanso chokhutiritsa kwambiri. Pamene mayiko anali kumenyana pankhondo yachiŵiri ya padziko lonse, anthu a Yehova anathandizidwa kuika mtima pa chinthu chofunika kwambiri kuposa kupulumutsa moyo wawo. Yehova anawathandiza kumvetsa kuti nkhani yaikulu, yomwe ikukhudza chilengedwe chonse, ndi yakuti Yehova ndiye woyenera kulamulira. N’zosangalatsa zedi kudziŵa kuti chifukwa cha kukhulupirika, aliyense wa Mboni za Yehova amathandiza nawo kutsimikizira kuti Yehova ndiye woyenera kulamulira ndiponso kuti Mdyerekezi ndi wabodza! (Miyambo 27:11) Mosiyana ndi Satana amene amanena mabodza ponena za Yehova ndi ulamuliro wake, okhulupirika a Yehova apitirizabe kulengeza poyera kuti: “Yehova ali wolungama m’njira zake zonse.”​—Salmo 145:17.

18. Kodi n’chiyani chomwe chili chitsanzo chaposachedwapa cha chakudya chauzimu chomwe chili chapanthaŵi yake ndiponso chokhutiritsa?

18 Chitsanzo china cha chakudya chauzimu cha panthaŵi yake ndiponso chokhutiritsa ndi buku lakuti Yandikirani kwa Yehova, limene linatulutsidwa pa Misonkhano Yachigawo yambirimbiri yakuti “Olengeza Ufumu Achangu” yomwe inachitika padziko lonse mu 2002 ndi 2003. Buku limeneli, lolembedwa ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” ndipo likufalitsidwa ndi Mboni za Yehova, limafotokoza kwambiri makhalidwe apadera a Yehova Mulungu, kuphatikizapo amene atchulidwa mu Salmo 145. Buku labwino kwambiri limeneli lidzachita mbali yofunika kwambiri pothandiza okhulupirika a Mulungu kuyandikira kwambiri kwa iye.

Nthaŵi Yoyandikira Kwambiri kwa Yehova

19. Kodi ndi nthaŵi yofunika iti imene yayandikira, ndipo tingachite chiyani panthaŵiyo?

19 Nthaŵi yofunika kwambiri yothetsa nkhani yakuti Yehova ndiye woyenera kulamulira yayandikira. Monga momwe ulosi wa mu Ezekieli chaputala 38 unanenera, posachedwapa Satana adzamaliza mbali yake monga “Gogi, wa ku dziko la Magogi.” Zimenezi zidzaphatikizapo kuukira anthu a Yehova padziko lonse. Satana adzayesetsa mwamphamvu kuwononga kukhulupirika kwa anthu a Mulungu. Koposa nthaŵi zonse, olambira a Yehova adzafunika kuitanira pa iye ndi mtima wonse, ngakhale kufuula kumene kuti awathandize. Kodi kuopa kwawo Mulungu ndiponso kum’konda kudzapita pachabe? Ndithudi, ayi, chifukwa chakuti Salmo 145 limati: “Yehova ali pafupi ndi onse akuitanira kwa Iye, onse akuitanira kwa Iye m’choonadi. Adzachita chokhumba iwo akumuopa; nadzamva kupfuula kwawo, nadzawapulumutsa. Yehova asunga onse akukondana naye; koma oipa onse adzawawononga.”​—Salmo 145:18-20.

20. Kodi mawu a pa Salmo 145:18-20 adzakhala bwanji oona posachedwapa?

20 Kudzakhalatu kosangalatsa kwambiri kuyandikana ndi Yehova ndiponso kuona mphamvu yake yopulumutsa pamene akuwononga oipa onse! Panthaŵi yofunika imeneyi yomwe yayandikira kwambiri, Yehova adzamvetsera kokha ‘oitanira kwa Iye m’choonadi.’ Iye sadzamvetsera achinyengo. Mawu a Mulungu amasonyeza bwino kwambiri kuti nthaŵi zonse anthu oipa akagwiritsa ntchito dzina lake nthaŵi itatha kale sizithandiza.​—Miyambo 1:28, 29; Mika 3:4; Luka 13:24, 25.

21. Kodi okhulupirika a Yehova amasonyeza bwanji kuti amasangalala kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu?

21 Tsopano kuposa ndi kale lonse ndiyo nthaŵi imene oopa Yehova ayenera ‘kuitanira kwa Iye m’choonadi.’ Okhulupirika ake amasangalala kugwiritsa ntchito dzina lake m’mapemphero awo ndiponso m’ndemanga zimene amapereka pamisonkhano yawo. Amagwiritsa ntchito dzina la Mulungu pamene akukambirana pawokha. Ndipo molimba mtima amalengeza dzina la Yehova m’utumiki wawo wapoyera.​—Aroma 10:10, 13-15.

22. Kodi n’chifukwa chiyani n’kofunika kupitiriza kukana makhalidwe ndiponso zolakalaka zadziko?

22 Kuti tipitirizebe kupindula ndi ubwenzi wathu wapamtima ndi Yehova Mulungu, n’kofunikanso kupitirizabe kukana zinthu zimene zimawononga mwauzimu monga kukondetsa chuma, zosangalatsa zoipa, mzimu wosakhululukira ena kapena kusaganizira anthu osoŵa. (1 Yohane 2:15-17; 3:15-17) Ngati sitisintha, zolakalaka ndiponso makhalidwe ameneŵa zingatichititse tchimo lalikulu ndiponso m’kupita kwanthaŵi Yehova sangatiyanje. (1 Yohane 2:1, 2; 3:6) Ndi nzeru kukumbukira kuti Yehova adzapitirizabe kusonyeza kukoma mtima kwachikondi kapena kuti chikondi chokhulupirika kwa ifeyo kokha ngati tikhalabe okhulupirika kwa iye.​—2 Samueli 22:26.

23. Kodi ndi tsogolo losangalatsa lotani limene okhulupirika onse a Mulungu akuyembekezera?

23 Chotero tiyeni tiike maganizo athu pa tsogolo losangalatsa kwambiri limene okhulupirika a Yehova onse akuyembekezera. Mwa kuchita zimenezi, tidzakhala ndi chiyembekezo chosangalatsa cha kukhala pakati pa anthu amene adzakweza, kudalitsa ndi kulemekeza Yehova ‘tsiku lonse’ ndiponso “ku nthaŵi za nthaŵi.” (Salmo 145:1, 2) Chotero, tiyeni ‘tidzisunge tokha m’chikondi cha Mulungu, kufikira moyo wosatha.’ (Yuda 20, 21) Pamene tipitirizabe kupindula ndi makhalidwe apadera a Atate wathu wakumwamba kuphatikizapo kukoma mtima kwachikondi kumene n’kwakukulu komwe amasonyeza kwa om’konda, tiyeni nthaŵi zonse maganizo athu akhale monga a Davide yemwe m’mawu omaliza a Salmo 145 anati: “Pakamwa panga padzanena chilemekezo cha Yehova; ndi zinthu zonse zilemekeze dzina lake loyera ku nthaŵi za nthaŵi.”

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi Salmo 145 likutithandiza bwanji kuzindikira okhulupirika a Mulungu?

• Kodi ndi motani mmene Yehova ‘amakwaniritsira zamoyo zonse chokhumba chawo’?

• Kodi n’chifukwa chiyani tifunika kuyandikira kwambiri kwa Yehova?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 16]

Okhulupirika a Mulungu amasangalala kukambirana ntchito zake zamphamvu

[Chithunzi patsamba 17]

Atumiki a Yehova molimba mtima amathandiza osakhulupirira kuphunzira za ulemerero wa ufumu wake

[Zithunzi patsamba 18]

Yehova amapatsa “zamoyo zonse” chakudya

[Mawu a Chithunzi]

Zinyama: Parque de la Naturaleza de Cabárceno

[Chithunzi patsamba 19]

Yehova amalimbitsa ndi kutsogolera okhulupirika ake amene amafuna thandizo lake mwa kupemphera