Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Imodzi Mwa Ntchito Zimene Panagona Luso Kwambiri”

“Imodzi Mwa Ntchito Zimene Panagona Luso Kwambiri”

“Imodzi Mwa Ntchito Zimene Panagona Luso Kwambiri”

KACHISI wa Yehova atamangidwa ku Yerusalemu mu ulamuliro wa Mfumu Solomo zaka pafupifupi 3,000 zapitazo, anapanga beseni lokongola kwambiri lamkuwa, n’kuliika panja pa khomo loloŵera m’kachisi. Linkalemera matani oposa 30 ndipo linkaloŵa malita pafupifupi 40,000 a madzi. Beseni lalikululi ankalitcha kuti thaŵale lamkuwa. (1 Mafumu 7:23-26) “N’zosakayikitsa kuti linali imodzi mwa ntchito zimene panagona luso kwambiri zomwe Ahebri anagwira,” anatero katswiri wa luso la ntchito zamanja yemwe ankagwira ntchito m’bungwe la zofufuzafufuza la National Research Council la ku Canada, Albert Zuidhof, m’magazini ya Biblical Archeologist.

Kodi thaŵaleli analikonza motani? Baibulo limati: ‘Mfumu inayenga [zipangizo zamkuwa] pa chidikha cha ku Yordano, m’dothi ladongo.’ (1 Mafumu 7:45, 46) ‘Kuyengako kuyenera kuti kunali kofanana ndi njira yomwe akuigwiritsabe ntchito panopa popanga mabelu akuluakulu amkuwa,’ anatero Zuidhof. Iye anafotokoza kuti: “Kwenikweni payenera kuti pankafunika kukhala ndi dongo lolimba kwambiri loumbidwa monga momwe chithaŵalecho chingaonekere chitagadabuka, ndiyeno n’kumata phula pamwamba pakepo. . . . Atatha kuchita izi, amisiriwo anafunika kuumba dongo pamwamba pa phulalo n’kuzisiya kuti ziume. Ntchito yomalizira inali kuchotsa phula lija mwa kulisungunula ndi kuthira chiphala chamkuwa mu mpata womwe munali phula muja.”

Poti thaŵale lamkuwali linali lalikulu ndiponso lolemera kwambiri polikonza panafunika luso loopsa. Dongo lomwe anaumba pansi ndiponso pamwamba pa phula linafunika kukhala lolimba kwambiri kuti lisagamuke ndi matani pafupifupi 30 a chiphala chamkuwa, ndipo ntchito yothira chiphalacho inali yoti akayamba mpaka amalize kuopera ming’alu kapena nthenya. Kuti zimenezi zitheke, mwachionekere panafunika ng’anjo zingapo zolumikizidwa pamodzi pothira chiphalacho. Panalidi ntchito osati yamaseŵera!

M’pemphero limene Mfumu Solomo inapereka potsekulira kachisiyo, mfumuyi inatama Yehova Mulungu chifukwa cha ntchito yonse yomanga kachisi, ndi mawu akuti: ‘Munalankhula m’kamwa mwanu ndi kukwaniritsa ndi dzanja lanu.’​—1 Mafumu 8:24.