Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

N’chiyani chinachititsa Yuda kugona ndi mkazi amene iye ankamuyesa wadama, malinga ndi Genesis 38:15, 16?

Ngakhale kuti Yuda anagona ndi mkazi amene iye ankamuyesa wadama, sikuti mkaziyu analidi wadama. Malinga ndi Genesis chaputala 38, zinachitika ndi izi.

Mwana woyamba wa Yuda asanabereke mwana wamwamuna ndi mkazi wake, Tamara, iye anaphedwa chifukwa chakuti “anali woipa pamaso pa Yehova.” (Genesis 38:7) Nthaŵi imeneyo, kunali mwambo wa ukwati wapachilamu. Mwambowu unali woti mwamuna akamwalira wopanda mwana wodzaloŵa dzina lake, mchimwene wake ankakwatira mkazi wamasiyeyo kuti abereke mwana woti adzaloŵe dzinalo. Koma mwana wachiŵiri wa Yuda, Onani, anakana kuchita zimenezi. Motero anafa chifukwa cha chiweruzo chimene Mulungu anapereka. Zitatero, Yuda anatumiza mpongozi wake Tamara ku nyumba ya atate wake kuti akayembekezere mpaka mwana wa Yuda wachitatu, Sela, atafika pamsinkhu womukwatira. Komano m’kupita kwanthaŵi, Yuda analephera kupereka Sela kwa Tamara, kuti amange naye banja. Motero mkazi wa Yuda atamwalira, Tamara anakonza njira yoti aberekere mwana wodzaloŵa dzina kudzera mwa Yuda, Mwisrayeli amene anali mpongozi wake. Anachita izi mwa kudzibisa n’kukhala ngati mkazi wadama wa pakachisi n’kukakhala mphepete mwa msewu umene ankadziŵa kuti Yuda adutsamo.

Poti Yuda sanam’zindikire Tamara, iye anagona naye. Monga malipiro ake, Tamara mochenjera anatenga chikole kwa Yuda, ndipo anadzagwiritsa ntchito zinthu zachikolezo posonyeza kuti iye ndi amene anam’patsa pathupi. Choonadi cha nkhaniyi chitadziŵika, Yuda sanaimbe mlandu mkaziyu koma anadzichepetsa nati: “Akhale wolungama wopambana ine, chifukwa ine sindinam’patsa iye Sela mwana wanga wamwamuna.” Ndipo m’poyenera kuti, “iye sanam’dziŵanso mkaziyo.”​—Genesis 38:26.

Yuda analakwa chifukwa sanapereke Tamara kwa mwana wake wamwamuna, Sela, monga analonjezera. Komanso anagona ndi mkazi amene ankamuyesa wadama wa pakachisi. Izi zinali zosagwirizana m’pang’ono pomwe ndi cholinga cha Mulungu, chakuti kugonana kukhale kwa anthu okwatirana okha basi. (Genesis 2:24) Komabe, sikuti Yuda anagonadi ndi mkazi wadama. M’malo mwake, iye mosadziŵa anatenga malo a mwana wake Sela pa ukwati wapachilamu ndipo motero anakhala tate wa ana ovomerezeka mwa lamulo.

Kunena za Tamara, zomwe iye anachita sichinali chiwerewere. Mapasa ake aamuna sanaonedwe ngati ana achigololo. Boazi wa ku Betelehemu atakwatira mtsikana wachimoabu Rute pa ukwati wapachilamu, akuluakulu a ku Betelehemu anakamba zinthu zabwino kwambiri zokhudza mwana wa Tamara, Perezi, pouza Boazi kuti: “Nyumba yako inge nyumba ya Perezi, amene Tamara anam’balira Yuda, ndi mbewu imene Yehova adzakupatsa ya namwali uyu.” (Rute 4:12) Perezi akupezekanso pa mndandanda wa mayina a makolo a Yesu Kristu.​—Mateyu 1:1-3; Luka 3:23-33.