Mfundo Zazikulu za M’buku la Genesis—Chigawo Chachiŵiri
Mawu a Yehova ndi Amoyo
Mfundo Zazikulu za M’buku la Genesis—Chigawo Chachiŵiri
KUYAMBIRA pamene munthu woyamba, Adamu, analengedwa kufika pamene Yosefe mwana wa Yakobo anamwalira, buku la Genesis likufotokoza mbiri ya anthu ya zaka 2,369. M’nkhani ya mu Nsanja ya Olonda yapita, tinakambirana machaputala 10 oyambirira ndiponso mavesi 9 a chaputala 11, amene akufotokoza nkhani yoyambira pa kulengedwa kwa zinthu kukafika pa nthaŵi ya nsanja ya Babele. * Nkhani ino ikufotokoza mfundo zazikulu za mbali yotsala ya Genesis, yomwe ikufotokoza zimene Mulungu anachita kwa Abrahamu, Isake, Yakobo, ndi Yosefe.
ABRAHAMU ANALI BWENZI LA MULUNGU
Patapita zaka pafupifupi 350 Chigumula chitachitika, mu mzera wa Semu, mwana wa Nowa, munabadwa munthu amene anakhala wapadera kwa Mulungu. Dzina lake anali Abramu, amene kenako anamutcha Abrahamu. Atauzidwa ndi Mulungu, Abramu anachoka mu mzinda wa Akasidi wa Uri ndipo anayamba kukhala m’mahema m’dziko limene Yehova anamulonjeza kuti adzam’patsa iye ndi mbadwa zake. Chifukwa cha chikhulupiriro chake ndi kumvera kwake, Abrahamu anatchedwa “bwenzi la Mulungu.”—Yakobo 2:23.
Yehova anawononga anthu oipa a ku Sodomu ndi a m’midzi ina yoyandikana nawo, koma anapulumutsa Loti ndi ana ake aakazi. Lonjezo la Mulungu linakwaniritsidwa pamene Isake, mwana wa Abrahamu, anabadwa. Patapita zaka, chikhulupiriro cha Abrahamu chinayesedwa pamene Yehova anamuuza kuti apereke nsembe mwana wake. Abrahamu anakonzeka kumvera koma pamene ankati azichita zimenezo, mngelo anam’letsa. N’zosachita kufunsa kuti Abrahamu anali ndi chikhulupiriro, ndipo anamutsimikizira kuti mitundu yonse idzadalitsidwa kudzera m’mbewu yake. Abrahamu anamva chisoni kwambiri mkazi wake wokondedwa Sara atamwalira.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
12:1-3—Kodi pangano la Abrahamu linayamba liti kugwira ntchito, ndipo linali loti ligwira ntchito kwa nthaŵi yaitali bwanji? Pangano la Yehova kwa Abramu lakuti “mwa [Abramu] adzadalitsidwa mabanja onse a dziko lapansi” mwachionekere linayamba kugwira ntchito pamene Abramu anaoloka mtsinje wa Firate popita ku Kanani. Zimenezi ziyenera kuti zinachitika pa Nisani 14, 1943 B.C.E., zaka 430 Aisrayeli asanawatulutse m’dziko la Igupto. (Eksodo 12:2, 6, 7, 40, 41) Pangano la Abrahamu ndilo “pangano la nthaŵi zonse.” Likupitiriza kugwira ntchito mpaka pamene mabanja a padziko lapansi adzadalitsidwa ndipo adani onse a Mulungu adzatha kuwonongedwa.—Genesis 17:7; 1 Akorinto 15:23-26.
15:13—Kodi kusautsidwa kwa zaka 400 kwa mbewu ya Abramu kumene ananeneratu kunakwaniritsidwa liti? Nthaŵi ya kusautsidwa imeneyi inayamba mu 1913 B.C.E. pamene mwana wa Abrahamu, Isake, anamusiyitsa kuyamwa ali ndi zaka pafupifupi zisanu ndipo Ismayeli, mbale wake wa mayi ena wa zaka 19, anali ‘kum’seka.’ (Genesis 21:8-14; Agalatiya 4:29) Kusautsidwa kumeneku kunatha pamene Aisrayeli anawamasula ku ukapolo ku Igupto mu 1513 B.C.E.
16:2—Kodi zinali zoyenera kuti Sarai apereke mdzakazi wake Hagara kwa Abramu kuti akhale mkazi wake? Zimene Sarai anachitazi zinali zogwirizana ndi mwambo wa panthaŵiyo. Panali mwambo wakuti mkazi wosabereka anayenera kupereka kwa mwamuna wake mkazi wamng’ono kuti abereke naye mwana wodzamuloŵa m’malo. Mitala inayamba ndi mbadwa za Kaini. Patapita nthaŵi, kuchita mitala kunasanduka mwambo ndipo olambira Yehova ena anatengera zimenezo. (Genesis 4:17-19; 16:1-3; 29:21-28) Komabe, Yehova sanasinthe mfundo yake yoyambirira yoti mwamuna azikwatira mkazi m’modzi yekha basi. (Genesis 2:21, 22) Mosakayika, Nowa ndi ana ake aamuna amene anawabwerezera lamulo lakuti ‘mubalane ndipo mudzaze dziko lapansi,’ anali ndi mkazi m’modzim’modzi. (Genesis 7:7; 9:1; 2 Petro 2:5) Ndipo Yesu Kristu anatsimikiziranso mfundo imeneyi yoti mwamuna azikhala ndi mkazi m’modzi yekha.—Mateyu 19:4-8; 1 Timoteo 3:2, 12.
19:8—Kodi Loti sanalakwitse pouza anthu a ku Sodomu kuti awapatsa ana ake aakazi? Malinga ndi chikhalidwe cha mayiko a Kum’maŵa, unali udindo wa munthu amene walandira alendo kuteteza alendowo panyumba pake, ngakhale kufika powafera ngati panafunikira kutero. Loti anali wokonzeka kuchita zimenezo. Anapita ku gulu la anthulo molimba mtima, anatseka chitseko, ndipo analankhula nawo ali yekha. Panthaŵi imene ankawauza anthuwo kuti awapatsa ana ake aakazi, Loti mosakayikira anali atazindikira kuti alendo akewo anali amithenga a Mulungu, ndipo mwina anaganiza kuti Mulungu akanatha kuteteza ana akewo monga mmene anatetezera Sara, mkazi wa bambo ake aakulu, ku Igupto. (Genesis 12:17-20) Inde, pamapeto pake Loti ndi ana ake aakazi anapulumutsidwa.
19:30-38—Kodi Yehova anagwirizana ndi kuledzera kwa Loti ndiponso kugona kwake ndi ana ake aakazi n’kuwaberekera ana aamuna? Yehova sagwirizana ndi kugonana kwa anthu apachibale ndiponso sagwirizana ndi kuledzera. (Levitiko 18:6, 7, 29; 1 Akorinto 6:9, 10) Ndipo Loti anatsutsa ‘ntchito zosayeruzika’ za anthu a ku Sodomu. (2 Petro 2:6-8) Mfundo yakuti ana aakazi a Loti anayamba aledzeretsa kaye bambo awowo ikusonyeza kuti anadziŵa kuti sakanavomereza kuti agone nawo akanakhala kuti sanaledzere. Koma popeza anali alendo m’dzikolo, ana akewo anaona kuti imeneyi inali njira yokhayo imene ikanathandiza kuti banja la Loti lisatheretu. Nkhaniyi anailemba m’Baibulo pofuna kuonetsa ubale wa Amoabu (kudzera mwa Moabu) ndi Aamoni (kudzera mwa Benammi) ndi Aisrayeli, mbadwa za Abrahamu.
Zimene Tikuphunzirapo:
13:8, 9. Abrahamu anapereka chitsanzo chabwino kwambiri pankhani yothetsa kusiyana maganizo. Tisalole kuti ubale wathu wamtendere usokonezeke chifukwa chofuna kupeza ndalama, kuumirira zimene timakonda, kapena kudzikuza.
15:5, 6. Pamene Abrahamu anali kukalamba koma asanakhalebe ndi mwana wamwamuna, anauza Mulungu wake nkhaniyo. Ndiyeno Yehova anamutsimikizira kuti am’patsa mbewu. Kodi zotsatira zake zinali zotani? Abrahamu “anakhulupirira Yehova.” Ngati timuuza Yehova zakukhosi kwathu m’pemphero, kuvomereza zimene amatitsimikizira m’Baibulo, ndi kumumvera, chikhulupiriro chathu chidzalimba.
15:16. Yehova sanaweruze msanga Aamori (kapena kuti Akanani) mpaka itadutsa mibadwo inayi. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti iye ndi Mulungu woleza mtima. Anadikira mpaka kufika poti panalibenso chiyembekezo choti anthuwo angasinthe. Ifenso tiyenera kukhala oleza mtima monga Yehova.
18:23-33. Yehova sawononga anthu mwachisawawa. Amateteza anthu olungama.
19:16. Loti “anachedwa,” ndipo angelo anachita kum’gwira dzanja pamodzi ndi banja lake kuti atuluke mumzinda wa Sodomu. Tingachite mwanzeru kupitiriza kukhala tcheru pamene tikudikira mapeto a dziko loipali.
19:26. N’kupusa kwambiri kudodometsedwa ndi zinthu zimene tazisiya m’dzikoli kapena kuzisiriranso.
YAKOBO ANALI NDI ANA AAMUNA 12
Abrahamu anakonza zoti Isake akwatire Rabeka, mkazi amene ankakhulupirira Yehova. Iye anabereka ana amapasa, Esau ndi Yakobo. Esau ananyoza ukulu wake ndipo anaugulitsa kwa Yakobo, amene kenako analandira madalitso a atate wake. Yakobo anathaŵira ku Padanaramu, kumene anakakwatira Leya ndi Rakele ndipo anasamalira ziweto za bambo a akazi akewo kwa zaka 20 asanachoke ndi banja lake. Yakobo anabereka ana aamuna 12 ndi mwana wamkazi m’modzi kudzera mwa Leya, Rakele, ndi adzakazi awo aŵiri. Yakobo analimbana ndi mngelo ndipo anadalitsidwa, komanso dzina lake analisintha n’kukhala Israyeli.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
28:12, 13—Kodi loto la Yakobo lokhudza “makwerero” linatanthauza chiyani? “Makwerero” ameneŵa omwe mwina ankaoneka ngati masitepe a miyala okwera m’mwamba, anasonyeza kuti pamakhala kulankhulana pakati pa okhala padziko lapansi ndi a kumwamba. Angelo a Mulungu amene anali kukwera ndi kutsika pa makwererowo anasonyeza kuti angelo amatumikira m’njira yofunika kwambiri pakati pa Yehova ndi anthu amene iye amawayanja.—Yohane 1:51.
30:14, 15—N’chifukwa chiyani Rakele anataya mwayi wake woti akanatha kutenga pakati posinthanitsa ndi zipatso za mankhwala a chikondi, kapena kuti, mankhwala osula? M’nthaŵi zakale, zipatso za mtengo wa mankhwala osula ankazigwiritsa ntchito monga mankhwala ogonetsa tulo ndiponso monga mankhwala othandiza munthu kuti asamve kupweteka minofu ikamakokana. Anthu ankakhulupiriranso kuti mankhwalawo anali ndi mphamvu yoyambitsa chilakolako chogonana ndiponso kuthandiza kusula munthu kapena kuthandiza kuti mkazi akhale ndi pakati. Ngakhale kuti Baibulo silifotokoza cholinga cha Rakele pochita zimenezi, iye ayenera kuti anaganiza kuti mankhwala osulawa akanamuthandiza kuti akhale ndi pakati ndi kuthetsa kunyozedwa chifukwa chakuti anali wosabereka. Komabe, panapita zaka zingapo kudzafika pamene Yehova “[a]natsegula m’mimba mwake.”—Genesis 30:22-24.
Zimene Tikuphunzirapo:
25:23. Yehova angazindikire chibadwa cha mwana yemwe sanabadwe ndipo angadziŵiretu za m’tsogolo ndi kusankhiratu munthu amene angamugwiritse ntchito kuti akwaniritse cholinga chake. Komabe, iye sakonzeratu zimene zidzachitikire munthu aliyense. (Hoseya 12:3; Aroma 9:10-12)
25:32, 33; 32:24-29. Kufuna kwa Yakobo kuti apeze ukulu ndiponso kulimbana kwake ndi mngelo usiku wonse kuti apeze madalitso kukusonyeza kuti ankaonadi zinthu zopatulika kukhala zofunika kwambiri. Yehova watiikiza zinthu zopatulika zambiri, monga ubale wathu ndi iye komanso ndi gulu lake, dipo, Baibulo, ndi chiyembekezo chathu cha Ufumu. Tiyenitu tikhale ngati Yakobo poona zinthu zimenezi kukhala zofunika kwambiri.
34:1, 30. Vuto limene ‘linasautsa’ Yakobo linayamba chifukwa chakuti Dina ankacheza ndi anthu amene sankakonda Yehova. Tiyenera kusankha mwanzeru anthu amene timacheza nawo.
YEHOVA ANADALITSA YOSEFE KU IGUPTO
Nsanje inachititsa ana aamuna a Yakobo kugulitsa mbale wawo Yosefe kuti akhale kapolo. Ali ku Igupto, Yosefe anaikidwa m’ndende chifukwa chakuti anatsatira mokhulupirika ndiponso molimba mtima mfundo za makhalidwe abwino za Mulungu. Patapita nthaŵi, anatulutsidwa Eksodo 13:19.
m’ndende kuti akamasulire maloto a Farao, amene analosera zaka zisanu ndi ziŵiri za chakudya chambiri ndi zaka zotsatira zisanu ndi ziŵiri za njala. Kenako Yosefe anamuika kukhala woyang’anira chakudya ku Igupto. Abale ake anafika ku Igupto kukafuna chakudya chifukwa cha njalayo. Banjalo linagwirizananso ndipo linakhala m’dera la chonde la Goseni. Ali pa bedi limene anamwalirira, Yakobo anadalitsa ana ake aamuna ndipo ananena ulosi umene unapereka chiyembekezo cha madalitso aakulu m’tsogolo. Mtembo wa Yakobo anaupititsa ku Kanani kukauika m’manda. Yosefe atamwalira ali ndi zaka 110, mtembo wake anaukonza ndi mankhwala, kuti pakapita nthaŵi adzaupititse ku Dziko Lolonjezedwa.—Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
43:32—N’chifukwa chiyani Aigupto ankaona kuti kudya pamodzi ndi Ahebri kunali konyansa? Ku mbali yaikulu, zimenezi zinali choncho mwina chifukwa cha kusankhana zipembedzo kapena mtundu. Aigupto ankanyansidwanso ndi abusa. (Genesis 46:34) Chifukwa chiyani? Abusa ayenera kuti anali anthu otsika kwambiri ku Igupto. Kapena mwina ankatero chifukwa chakuti Aigupto ankanyansidwa ndi anthu amene ankafunafuna malo odyetserako ziŵeto popeza malo olima anali ochepa kwambiri.
44:5—Kodi Yosefe ankagwiritsadi ntchito chikho chomwera poombeza? Chikho chomwera cha siliva ndiponso zimene ananena zokhudza chikhocho zinali zina mwa zochitika zongofuna kuwapusitsa. Yosefe ankalambira Yehova mokhulupirika. Sankagwiritsa ntchito chikhocho poombeza, monganso mmene zinalili kuti Benjamini sanabe chikhocho.
49:10—Kodi “ndodo yachifumu” ndi “[chibonga cha, NW] wolamulira” zikutanthauza chiyani? Ndodo yachifumu ndi ndodo imene wolamulira ankatenga monga chizindikiro cha ufumu. Chibonga cha wolamulira ndi chibonga chachitali chimene chimasonyeza kuti munthuyo ali ndi mphamvu yolamula. Pamene Yakobo anatchula zimenezi anasonyeza kuti fuko la Yuda lidzakhala ndi ulamuliro ndi mphamvu mpaka pamene Silo adzafika. Silo ameneyu, mbadwa ya Yuda, ndiye Yesu Kristu, amene Yehova wam’patsa ulamuliro wa kumwamba. Kristu ali ndi ulamuliro monga mfumu ndipo ali ndi mphamvu zolamulira.—Salmo 2:8, 9; Yesaya 55:4; Danieli 7:13, 14.
Zimene Tikuphunzirapo:
38:26. Yuda analakwitsa mmene anachitira zinthu ndi mpongozi wake wamasiye, Tamara. Komabe, atamuuza kuti iye ndi amene anam’patsa pakati, Yuda anavomereza kulakwa kwake modzichepetsa. Ifenso tizivomereza kulakwa kwathu mwamsanga.
39:9. Zimene Yosefe anayankha mkazi wa Potifara zinasonyeza kuti maganizo ake anali ogwirizana ndi a Mulungu pankhani ya makhalidwe ndipo mfundo za makhalidwe abwino za Mulungu zinkatsogolera chikumbumtima chake. Kodi ifenso sitiyenera kuyesetsa kuchita chimodzimodzi pamene tikupitiriza kudziŵa mfundo zambiri zolondola za choonadi?
41:14-16, 39, 40. Yehova angasinthe zinthu kwa anthu amene amamuopa kuti ziwayendere bwino. Tikakumana ndi mavuto, tingachite bwino kudalira Yehova ndi kukhalabe okhulupirika kwa iye.
Anali Ndi Chikhulupiriro Cholimba
Abrahamu, Isake, Yakobo, ndi Yosefe analidi anthu oopa Mulungu ndiponso anali ndi chikhulupiriro. Nkhani yofotokoza moyo wawo imene ili m’buku la Genesis ndi yolimbikitsadi chikhulupiriro ndipo ikutiphunzitsa zinthu zabwino zambiri.
Mungapindule ndi nkhani imeneyi pamene mukuŵerenga Baibulo mlungu ndi mlungu pokonzekera Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Kuganizira zimene takambiranazi kudzakuthandizani kuonadi kuti nkhaniyi ndi yeniyeni.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 1 Onani nkhani yakuti “Mawu a Yehova Ndi Amoyo—Mfundo Zazikulu za M’buku la Genesis—Chigawo Choyamba” mu Nsanja ya Olonda ya January 1, 2004.
[Chithunzi patsamba 26]
Abrahamu anali ndi chikhulupiriro
[Chithunzi patsamba 26]
Yehova anadalitsa Yosefe
[Chithunzi patsamba 26]
Loti wolungama ndi ana ake aakazi anapulumutsidwa
[Chithunzi patsamba 29]
Yakobo anaona zinthu zopatulika kukhala zofunika kwambiri. Kodi inunso mumatero?