Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Patsani Mulungu Ulemerero Osati Anthu

Patsani Mulungu Ulemerero Osati Anthu

Patsani Mulungu Ulemerero Osati Anthu

M’MIYEZI yapitayi, anthu okonda chilungamo padziko lonse aphunzira mmene angapatsire Mulungu ulemerero pamene anali kusonkhana pa Misonkhano Yachigawo ya Mboni za Yehova yakuti “Patsani Mulungu Ulemerero.” Tiyeni tibwereze maphunziro amene anali kumeneko.

Pulogalamu yophunzira Baibuloyi inali ya masiku atatu kwa osonkhana ambiri ndipo inali ya masiku anayi kwa amene anakakhala nawo pamisonkhano yapadera yamayiko. Pamisonkhano yonseyi osonkhana anamvetsera zigawo zoposa 30 zofotokoza Malemba. Zigawozi zinaphatikizapo nkhani zomwe zinawathandiza kumvetsetsa ndi kuyamikira kwambiri zinthu zauzimu, zokumana nazo zomwe zinawalimbitsa chikhulupiriro, zitsanzo zomwe zinawathandiza kugwiritsa ntchito bwino mfundo za m’Baibulo, ndiponso seŵero la nthaŵi zakale lomwe linasonyeza mavuto omwe Akristu a m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino anakumana nawo. Ngati munali nawo pamsonkhano wina wa misonkhano imeneyi, bwanji osabwereza mfundo zomwe munalemba pamene mukuŵerenga nkhaniyi? Tikukhulupirira kuti nkhaniyi ikukumbutsani phwando lalikulu lauzimu limene tinali nalo ndiponso kuti ikupatsani malangizo.

Mutu wa Tsiku Loyamba: “Muyenera Inu Ambuye Wathu, . . . Kulandira Ulemerero”

Nyimbo ndi pemphero lotsekulira zitatha, wokamba nkhani woyamba analandira osonkhana onse ndi manja aŵiri m’nkhani yomwe inasonyeza cholinga chachikulu cha msonkhanowo yakuti: “Tasonkhana Kuti Tilemekeze Mulungu.” Pogwira mawu a pa Chivumbulutso 4:11, wokamba nkhaniyo anatsindika mfundo yaikulu ya msonkhano wonsewo. Mosachulutsa gaga m’diŵa, iye anafotokoza tanthauzo la kupatsa Mulungu ulemerero. Mwa kugwiritsa ntchito buku la Masalmo, iye anatsindika kuti kulemekeza Mulungu kumaphatikizapo kupembedza, kutamanda, ndiponso kuyamika.​—Salmo 95:6; 100:4, 5; 111:1, 2.

Nkhani yotsatira inali yakuti, “Odala Ndi Amene Akulemekeza Mulungu.” Wokamba nkhaniyi anatchula mfundo yochititsa chidwi kwambiri. Popeza kuti Mboni za Yehova zoposa sikisi miliyoni zili m’mayiko 234 padziko lonse, tinganene kuti kwa anthu amene akulemekeza Yehova dzuŵa sililoŵa. (Chivumbulutso 7:15) Anthu anayamikira ndi kusangalala kwambiri ndi mbali ya nkhaniyi yofunsa abale ndi alongo angapo Achikristu omwe akuchita utumiki wapadera wa nthaŵi zonse.

“Chilengedwe Chimalengeza Ulemerero wa Mulungu” ndiyo inali nkhani yotsatira. Ngakhale kuti miyamba yomwe timaionayi silankhula, komabe imasonyeza ukulu wa Mulungu ndipo imatithandiza kuti tizimuyamikira kwambiri popeza amatisamalira mwachikondi. Zimenezi zinafotokozedwa mwatsatanetsatane.​—Yesaya 40:26.

Umphumphu wa Akristu oona umayesedwa ndi chizunzo, chitsutso, zinthu zoipa zadzikoli, ndiponso zilakolako zauchimo. Motero, omvera anatchera khutu kwambiri ku nkhani yakuti “Yendani mu Umphumphu.” Wokamba nkhaniyi anafotokoza vesi limodzi ndi limodzi la Salmo 26 ndipo anafunsa Mboni yapasukulu imene inakana kuchita choipa ndiponso Mboni ina imene inali kuthera nthaŵi yambiri pa zosangalatsa zokayikitsa koma inathetsa vutolo.

Nkhani yaikulu yakuti, “Masomphenya Aulemerero Okhudza Maulosi Amatilimbikitsa!” ndiyo inamaliza chigawo cham’maŵachi. Wokamba nkhaniyi anatchula mneneri Danieli, mtumwi Yohane ndiponso mtumwi Petro monga zitsanzo za anthu omwe chikhulupiriro chawo chinalimba ndi masomphenya aulemerero okhudza maulosi a kukhazikitsidwa kwa Ufumu wa Mesiya wa Mulungu ndiponso mmene ukugwirira ntchito zake. Ponenapo za anthu amene mwina aiŵala umboni wosatsutsika wakuti tili m’nthaŵi ya mapeto, wokamba nkhaniyi anati: “Tikuyembekezera ndi mtima wonse kuti anthu oterowo adzayambanso kuika maganizo awo pa mfundo ya kukhalapo kwa Kristu mu ulemerero wa Ufumu ndipo adzathandizidwa kupezanso mphamvu zauzimu.”

Pulogalamu ya masana inayamba ndi nkhani yakuti, “Ulemerero wa Yehova Umavumbulidwa kwa Anthu Odzichepetsa.” Wokamba nkhaniyi anasonyeza mmene Yehova amasonyezera chitsanzo cha kudzichepetsa, ngakhale kuti iye ndiye Wamkulu kwambiri m’chilengedwe chonse. (Salmo 18:35) Yehova amakonda anthu amene amadzichepetsadi, koma amadana ndi anthu omwe amaoneka odzichepetsa akakhala ndi anzawo kapena anthu amene akuwayang’anira koma amasautsa anzawo akakhala kuti iwo ndiwo akuyang’anira ena.​—Salmo 138:6.

Kenako, ulosi wa m’Baibulo unafotokozedwa m’nkhani yosiyirana imene inagogomezera mbali zosiyanasiyana za mutu waukulu wakuti: “Ulosi wa Amosi​—Uthenga Wofunika M’nthaŵi Yathu.” Potchula chitsanzo cha Amosi, woyamba kukamba nkhani pamutuwu anafotokoza udindo umene tili nawo wochenjeza anthu za chiweruzo cha Yehova chimene chikubwera. Mutu wa nkhani yake unali wakuti “Lankhulani Mawu a Mulungu Molimba Mtima.” Wokamba nkhani wachiŵiri anafunsa kuti: “Kodi Yehova adzathetsa kuipa ndi kuvutika konse kumene kuli padziko lapansiku?” Nkhani yake yakuti, “Chiweruzo cha Mulungu pa Oipa,” inasonyeza kuti nthaŵi zonse chiweruzo cha Mulungu chimakhala choyenera, chosathaŵika, ndipo chimasankha. Wokamba mbali yomaliza pankhani yosiyiranayi anafotokoza mutu wakuti “Yehova Amayesa Mtima.” Anthu omwe akulakalaka kusangalatsa Yehova ayenera kutsatira mawu a pa Amosi 5:15, akuti: “Danani nacho choipa, nimukonde chokoma.”

Moŵa, monga vinyo amene amasangalatsa mtima, ungathe kumwedwa molakwika. M’nkhani yake yakuti “Peŵani Msampha wa Kumwa Moŵa Mopitirira Muyezo,” wokambayo anatchula mavuto akuthupi ndi auzimu amene amabwera chifukwa chomwa moŵa mopitirira muyeso, ngakhale ngati munthuyo saledzera. Anapereka mfundo iyi yofunika kuitsatira: Kuchuluka kwa moŵa umene munthu aliyense angamwe asanaledzere kumasiyanasiyana. Choncho, ngati mumwa moŵa wochuluka mulimonse woti n’kusokoneza “nzeru [yanu] yeniyeni ndi kulingalira,” ndiye kuti kwa inuyo kumeneko ndi kumwetsa moŵa.​—Miyambo 3:21, 22.

Popeza kuti tikukhala m’nthaŵi zovuta, nkhani yotsatira, yakuti “Yehova, Ndiye ‘Mphamvu Yathu M’nyengo ya Nsautso,’” inali yolimbikitsa kwambiri. Pemphero, mzimu woyera, ndiponso Akristu anzathu angatithandize kupirira.

Nkhani yomaliza patsikuli yakuti, “‘Dziko Lokoma’ Linali Chithunzi cha Paradaiso,” inatha ndi chinthu chosangalatsa kwambiri kwa onse, buku latsopano la mapu a m’Baibulo ambirimbiri! Lili ndi mutu wakuti Onani Dziko Lokoma.

Mutu wa Tsiku Lachiŵiri: “Fotokozerani Ulemerero Wake mwa Amitundu”

Atatha kukambirana lemba la tsikulo, pamsonkhanowu panakambidwa nkhani yosiyirana yachiŵiri, yamutu wakuti “Onetsani Ulemerero wa Yehova Monga Akalirole.” Mbali yoyamba inamveketsa bwino za kuonetsa ulemerero wa Yehova “Mwa kulalikira Uthenga Wabwino Kulikonse” ndipo inalinso ndi zitsanzo za zokumana nazo zenizeni mu utumiki wa kumunda. Nkhani yachiŵiri inali ndi chitsanzo cha ulendo wobwereza pamene wokamba anali kukamba nkhani yamutu wakuti “Mwa Kuwachotsa Chophimba Anthu Akhungu.” Mbali yomaliza, yakuti “Mwa Kuchita Utumiki Mokwanira,” inasangalatsa kwambiri chifukwa cha kufunsa anthu zokumana nazo m’munda.

Nkhani yotsatira pa pulogalamuyo inali ndi mutu wakuti “Odedwa Popanda Chifukwa.” Inali ndi mbali zolimbikitsa kwambiri zofunsa anthu okhulupirika amene mwa mphamvu ya Mulungu anakhalabe okhulupirika pamene anali kuzunzidwa.

Mbali imene anthu amaiyembekezera mwachidwi kwambiri pamisonkhano ikuluikulu ndi nkhani ya ubatizo ndipo ikatha pamakhala kumiza m’madzi anthu onse amene akuyenera kubatizidwa. Munthu akabatizidwa m’madzi amasonyeza kuti iye wadzipatulira ndi mtima wonse kwa Yehova. Motero mutu wa nkhaniyi unali woyenera kwambiri: “Kukwaniritsa Kudzipatulira Kwathu Kumalemekeza Mulungu.”

Pulogalamu yamasana inayamba ndi nkhani yomwe inalimbikitsa kudzipenda, yakuti “Khalani ndi Maganizo Onga a Kristu Pankhani ya Kukhala Wamkulu.” Wokamba nkhaniyi anatchula mfundo yosangalatsa iyi: Munthu amakhala wamkulu mwa kutsanzira kudzichepetsa kwa Kristu. Motero, Mkristu asamafune udindo n’cholinga chopeza zokhumba zake. Ayenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndimafuna kugwira ntchito zofunika zimene si zodzionetsera kwa anthu?’

Kodi mumatopa? Izo n’zosachita kufunsa. Onse anasangalala ndi nkhani yakuti “Otopa Koma Osalefuka.” Kufunsa anthu amene akhala Mboni nthaŵi yaitali kunasonyeza kuti Yehova angatipatse “mphamvu mwa Mzimu wake.”​—Aefeso 3:16.

Kupatsa ndi khalidwe limene sitibadwa nalo, timachita kuphunzira. Mfundo yofunikayi inatsindikidwa m’nkhani yakuti “Khalani Owoloŵa Manja, Okonzeka Kugaŵira Ena.” Ndipo panafunsidwa funso lopangitsa munthu kuganiza kwambiri lakuti: “Kodi ifeyo ndife okonzeka kupatula mphindi zingapo patsiku kuti ticheze ndi abale ndi alongo athu okalamba, odwala, opsinjika maganizo, kapena osungulumwa?”

Omvera anachita chidwi ndi nkhani yakuti “Chenjerani ndi ‘Mawu a Alendo.’” Nkhaniyi inayerekeza otsatira a Yesu ndi nkhosa zomwe zimamvera mawu ake okha basi monga “Mbusa Wabwino” ndipo sizimvera “mawu a alendo” omwe amachokera m’njira zosiyanasiyana zotsogoleredwa ndi Mdyerekezi.​—Yohane 10:5, 14, 27.

Gulu loimba lifunika kuimba mogwirizana kuti anthu amve zimene likuimba. Pofuna kulemekeza Mulungu, olambira oona padziko lonse lapansi ayenera kukhala ogwirizana. Motero, nkhani yakuti “Lemekezani Mulungu ndi ‘Pakamwa Pamodzi’” inapereka malangizo abwino kwambiri a mmene tonse tingalankhulire “chinenero choyera” (NW) chimodzi ndi kutumikira Yehova ndi “mtima umodzi.”​—Zefaniya 3:9.

Makolo, makamaka amene ali ndi ana ang’onoang’ono, anasangalala kwambiri ndi nkhani yomaliza patsikuli, yakuti “Ana Athu Ndi Choloŵa Chamtengo Wapatali.” Panatulutsidwa buku latsopano lamasamba 256, ndipo omvera anasangalala kwambiri. Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso ndi buku limene lithandize makolo kumakhala ndi nthaŵi yopindulitsa kwambiri mwauzimu yocheza ndi ana awo, mphatso zimene Mulungu wawapatsa.

Mutu wa Tsiku Lachitatu: “Chitani Zonse ku Ulemerero wa Mulungu”

Tsiku lomaliza la msonkhanowu linayamba ndi mfundo za lemba latsikulo zokhudza zinthu zauzimu. Gawo loyamba la pulogalamu ya tsikuli linakhudzanso kwambiri mabanja. Nkhani yoyamba, yakuti “Makolo, Pangitsani Banja Lanu Kukhala Lolimba,” inakonzekeretsa maganizo a omvera. Atapenda udindo wa makolo wopezera banja lawo zinthu zofunika pamoyo wawo, wokamba nkhaniyi anasonyeza kuti udindo waukulu wa makolo ndi kusamalira ana awo mwauzimu.

Wokamba nkhani yotsatira analankhula kwa ana ndipo anakamba nkhani yakuti “Mmene Achinyamata Akulemekezera Yehova.” Iye anati achinyamata ali ngati “mame” chifukwa chakuti ndi ambiri ndiponso kuchita kwawo zinthu mwachangu monga anyamata n’kosangalatsa kwambiri. Achikulire amasangalala kugwira nawo ntchito pamodzi potumikira Yehova. (Salmo 110:3) Nkhaniyi inalinso ndi mbali yosangalatsa kwambiri yofunsa achinyamata azitsanzo zabwino.

Nthaŵi zonse maseŵero a nthaŵi zakale a m’Baibulo amakhala mbali yochititsa chidwi kwambiri pamisonkhano yachigawo, ndipo pamsonkhano uwunso panali seŵero. Seŵero lakuti “Kulalikira Molimba Mtima Ngakhale Pali Otsutsa” linasonyeza otsatira a Yesu a m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino. Kuwonjezera pa kukhala losangalatsa, seŵeroli linalinso ndi malangizo, chomwe ndi chinthu chofunika kwambiri. Nkhani yomwe inatsatira seŵerolo, yakuti “Lengezani Uthenga Wabwino ‘Mosaleka,’” inamveketsa bwino mfundo zazikulu za seŵerolo.

Onse omwe anafika pamsonkhanowo anali ndi chidwi chomvera nkhani yaikulu m’pulogalamu ya Lamlungu, nkhani ya onse yakuti, “Ndani Amene Akupatsa Mulungu Ulemerero Masiku Ano?” Wokamba nkhaniyi anapereka umboni wokwanira wosonyeza mmene asayansi ndiponso azipembedzo sanalemekezere Mulungu. Ndi anthu okhawo odziŵika ndi dzina lake, amene akulalikira ndi kuphunzitsa choonadi ponena za Yehova, amene akulemekezadi dzina lake masiku ano.

Nkhani ya onse imeneyi itatha panali chidule cha phunziro la Nsanja ya Olonda la mlunguwo. Kenako inali nthaŵi ya nkhani yomaliza, yakuti “‘Pitirizani Kubala Zipatso Zambiri’ Kuti Yehova Alemekezeke.” Wokamba nkhaniyi anafotokoza chosankha cha mfundo khumi kuti onse omwe anali pamsonkhanowo avomereze. Mfundo zake zinali zokhudza njira zosiyanasiyana za momwe tingaperekere ulemerero kwa Yehova, yemwe ndi Mlengi. Pamisonkhano yonse padziko lonse pankamveka mawu ogwirizana akuti “Tikuvomereza.”

Motero pamapeto a msonkhanowo aliyense ankaganizira mfundo yaikulu yakuti “Patsani Mulungu Ulemerero.” Ndipo mothandizidwa ndi mzimu wa Yehova ndiponso mbali yooneka ndi maso ya gulu lake, tiyeni nthaŵi zonse tiyesetse kupatsa Mulungu ulemerero osati anthu.

[Bokosi/​Zithunzi patsamba 23]

Misonkhano Yamayiko

Misonkhano yamayiko ya masiku anayi inachitika ku Africa, Asia, Australia, Ulaya, ndi ku North ndi South America. Mboni zochoka m’mayiko a padziko lonse zinaitanidwa kukakhala nthumwi pamisonkhanoyi. Mwanjira imeneyi panali “kulimbikitsana” pakati pa alendowo ndi eni dziko. (Aroma 1:12, NW) Anthu amene anaonana kalekale anakumananso, ndipo enanso anapeza mabwenzi atsopano. Mbali yapadera papulogalamu ya misonkhano yamayiko inali mbali yakuti “Malipoti a ku Mayiko Ena.”

[Bokosi/​Zithunzi patsamba 25]

Mabuku Atsopano Amene Akupatsa Mulungu Ulemerero

Mabuku atsopano aŵiri anatulutsidwa pa Misonkhano Yachigawo yakuti “Patsani Mulungu Ulemerero.” Buku la mapu a m’Baibulo lakuti Onani Dziko Lokoma lili ndi chikuto cholimba ndiponso masamba 36 a mapu komanso zithunzi za malo otchulidwa m’Baibulo. Tsamba lililonse ndi la kalala ndipo bukuli lili ndi mapu a ufumu wa Asuri, Babulo, Mediya ndi Perisiya, Girisi, ndi Roma. Lili ndi mapu apadera okhudza utumiki wa Yesu ndiponso kufala kwa Chikristu.

Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso ndi buku lamasamba 256, lazithunzi pafupifupi 230. Nthaŵi zambiri makolo ndi ana angasangalale kwambiri kupeza nthaŵi yoti azingoona zithunzi ndi kuyankha mafunso othandiza kuganiza omwe ali m’bukuli. Buku latsopanoli lakonzedwa kuti lilimbane ndi zochita za Satana zolimbana ndi ana aang’ono, zomwe cholinga chake ndicho kuipitsa makhalidwe awo.

[Chithunzi patsamba 23]

Amishonale anafotokoza zokumana nazo zolimbitsa chikhulupiriro

[Zithunzi patsamba 24]

Ubatizo unali mbali yofunika kwambiri pa misonkhano yachigawo yakuti “Patsani Mulungu Ulemerero”

[Zithunzi patsamba 24]

Akulu ndi ana omwe amasangalala ndi maseŵero a m’Baibulo