Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ukulu wa Yehova ndi Wosasanthulika

Ukulu wa Yehova ndi Wosasanthulika

Ukulu wa Yehova ndi Wosasanthulika

“Yehova ndi wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu; ndi ukulu wake ndi wosasanthulika.”​—SALMO 145:3.

1, 2. Kodi Davide anali munthu wotani, ndipo ankadziona motani pamaso pa Mulungu?

WOLEMBA Salmo 145 anali munthu wodziŵika kwambiri m’nthaŵi yakale. Ali mnyamata anamenyana ndi chimphona chokhala ndi zida ndipo anachipha. Ndipo monga mfumu yankhondo, wamasalmo ameneyu anagonjetsa adani ambiri. Dzina lake anali Davide ndipo anali mfumu yachiŵiri ya Israyeli wakale. Davide atamwalira anthu anakumbukirabe mbiri yake moti ngakhale masiku ano anthu ambiri amadziŵa kenakake ponena za iye.

2 Davide anali wodzichepetsa ngakhale kuti anachita zinthu zambiri. Poimba za Yehova, iye anati: “Pakuona ine thambo la kumwamba lanu, ntchito ya zala zanu, mwezi ndi nyenyezi, zimene munazikhazika, munthu ndani kuti mum’kumbukira? Ndi mwana wa munthu kuti mucheza naye?” (Salmo 8:3, 4) M’malo moganiza kuti iye anali wamkulu, Davide anaona kuti Yehova ndi amene anam’pulumutsa kwa adani ake onse ndipo ponena za Mulungu anati: “Munandipatsa chikopa cha chipulumutso chanu; ndi kufatsa [“kudzichepetsa,” NW] kwanu kunandikulitsa.” (2 Samueli 22:1, 2, 36) Yehova amasonyeza kudzichepetsa pochitira chifundo ochimwa ndipo Davide anayamikira kwambiri chisomo cha Mulungu.

‘Ndidzakweza Mulungu Mfumu’

3. (a) Kodi Davide anaona bwanji ufumu wa Israyeli? (b) Kodi Davide anafuna kulemekeza Yehova mpaka pati?

3 Ngakhale kuti Davide anali mfumu yoikidwa ndi Mulungu, iye anaona Yehova kukhala Mfumu yeniyeni ya Israyeli. Davide anati: “Ufumu ndi wanu, Yehova; ndipo mwakwezeka mutu wa pa zonse.” (1 Mbiri 29:11) Davide analemekezadi Mulungu monga Wolamulira! Iye anaimba kuti: “Ndidzakukwezani Mulungu wanga, Mfumu; ndipo ndidzalemekeza dzina lanu ku nthaŵi za nthaŵi. Masiku onse ndidzakuyamikani; ndi kulemekeza dzina lanu ku nthaŵi za nthaŵi.” (Salmo 145:1, 2) Davide anafuna kulemekeza Yehova Mulungu tsiku lonse ndiponso mpaka kalekale.

4. Kodi Salmo 145 limavumbula mabodza ati?

4 Salmo 145 ndi yankho lamphamvu ku zimene Satana ananena zoti Mulungu ndi wolamulira wodzikonda amene safuna kupatsa zolengedwa zake ufulu. (Genesis 3:1-5) Salmo limeneli limavumbulanso bodza la Satana loti amene amamvera Mulungu amachita zimenezo chabe chifukwa cha phindu ladyera limene angapeze osati chifukwa chokonda Mulungu. (Yobu 1:9-11; 2:4, 5) Mofanana ndi Davide, Akristu oona masiku ano akuyankha zonena zabodza za Mdyerekezi. Chiyembekezo chawo cha kukhala ndi moyo wosatha mu ulamuliro wa Ufumu amachiona kukhala chofunika kwambiri chifukwa amafuna kulemekeza Yehova mpaka kalekale. Anthu ambiri ayamba kale kuchita zimenezi mwa kusonyeza chikhulupiriro mu nsembe ya dipo ya Yesu ndiponso mwa kutumikira Yehova momvera chifukwa cha chikondi monga olambira ake odzipatulira ndi obatizidwa.​—Aroma 5:8; 1 Yohane 5:3.

5, 6. Kodi ndi mipata yotani imene ilipo yoyamikira ndi kulemekeza Yehova?

5 Taganizirani mipata yathu yambiri yoyamikira ndi kulemekeza Yehova monga atumiki ake. Tingachite zimenezi mwa kupemphera kwa iye pamene takhudzidwa kwambiri ndi chinachake chimene taŵerenga m’Mawu ake, Baibulo. Tingam’lemekeze ndi kum’yamikira mosangalala pamene takhudzidwa kwambiri ndi mmene Mulungu amachitira ndi anthu ake kapena pamene tasangalatsidwa ndi mbali inayake ya chilengedwe chake chodabwitsa. Timayamikiranso Yehova Mulungu pamene tikambirana zolinga zake ndi okhulupirira anzathu pamisonkhano yachikristu kapena pamene tikucheza patokha. Ndipotu, “ntchito zabwino” zonse zochitidwa chifukwa cha Ufumu wa Mulungu zimalemekeza Yehova.​—Mateyu 5:16.

6 Zitsanzo zaposachedwapa za ntchito zabwino zimenezi zikuphatikizapo malo ambiri olambiriramo amene anthu a Yehova amanga m’mayiko osauka. Ndipo nyumba zambiri zimenezi zamangidwa ndi thandizo la ndalama zimene okhulupirira anzathu a m’mayiko ena amapereka. Akristu ena athandiza mwa kupita modzifunira kumadera ameneŵa kuti akamange nawo Nyumba za Ufumu. Ndipo ntchito yofunika kwambiri pantchito zonse zabwino ndi yolemekeza Yehova mwa kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wake. (Mateyu 24:14) Monga mmene mavesi otsatira mu Salmo 145 akusonyezera, Davide anayamikira ulamuliro wa Mulungu ndipo analemekeza ufumu Wake. (Salmo 145:11, 12) Kodi mumayamikira mofananamo kuti Mulungu amalamulira mwachikondi? Ndipo kodi mumalankhula nthaŵi zonse ndi ena za Ufumu wake?

Zitsanzo za Ukulu wa Mulungu

7. Perekani chifukwa chachikulu cholemekezera Yehova.

7 Lemba la Salmo 145:3 limapereka chifukwa chachikulu cholemekezera Yehova. Davide anaimba kuti: “Yehova ndi wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu; ndi ukulu wake ndi wosasanthulika.” Ukulu wa Yehova ulibe malire. Anthu sangausanthule, kuumvetsa kapena kuuyesa. Koma tsopano tipindula kwambiri kupenda zitsanzo za ukulu wosasanthulika wa Yehova.

8. Kodi thambo limavumbula chiyani za ukulu ndi mphamvu za Yehova?

8 Takumbukirani nthaŵi imene munayang’ana m’mwamba usiku wopanda mitambo. Kodi simunadabwe ndi kuchuluka kwa nyenyezi zomwe munaona usiku umenewo? Kodi sizinakuchititseni kulemekeza Yehova chifukwa cha ukulu wake polenga zinthu za m’mwamba zonsezo? Koma zimene munaonazo zinali chabe mbali yochepa kwambiri ya chiŵerengero cha nyenyezi za m’mlalang’amba umene dziko lapansili lilimo. Ndiponso, zikuoneka kuti pali milalang’amba yoposa mabiliyoni zana limodzi ndipo ndi milalang’amba itatu yokha imene ingaoneke popanda kugwiritsa ntchito chipangizo choonera zinthu zakutali. Ndithudi, nyenyezi ndiponso milalang’amba yosaŵerengeka imene imapanga thambo lalikulu ili umboni wa mphamvu ya Yehova yakulenga ndiponso ukulu wake wosasanthulika.​—Yesaya 40:26.

9, 10. (a) Kodi ndi mbali ziti za ukulu wa Yehova zimene zasonyezedwa ndi zochitika zokhudza Yesu Kristu? (b) Kodi kuukitsidwa kwa Yesu kuyenera kukhudza bwanji chikhulupiriro chathu?

9 Taonani mbali zina za ukulu wa Yehova, zija zokhudza Yesu Kristu. Ukulu wa Mulungu unaonekera polenga Mwana wake ndiponso pom’gwiritsa ntchito monga “mmisiri” Wake kwa zaka zosaŵerengeka. (Miyambo 8:22-31) Ukulu wa chikondi cha Yehova unasonyezedwa nthaŵi imene anapereka Mwana wake wobadwa yekha monga nsembe ya dipo la anthu. (Mateyu 20:28; Yohane 3:16; 1 Yohane 2:1, 2) Ndipo chimene anthu sangachimvetse ndi thupi lauzimu, laulemerero ndiponso losafa limene Yehova anapangira Yesu pa kuukitsidwa kwake.​—1 Petro 3:18.

10 Kuukitsidwa kwa Yesu kunali ndi mbali zambiri zosangalatsa za ukulu wosasanthulika wa Yehova. Mwachionekere, Mulungu anapatsa Yesu mphamvu zokumbukira ntchito yomwe anachita polenga zinthu zosaoneka ndi zooneka. (Akolose 1:15, 16) Zinthu zimenezi zimaphatikizapo zolengedwa zina zauzimu, thambo, dziko ndi zomera zake ndiponso zamoyo zonse padziko lapansi lino. Kuwonjezera pa kupatsa Mwana wakeyo mphamvu zokumbukira mbiri yonse yakale ya zamoyo zakumwamba ndi zapadziko lapansi imene ankaidziŵa asanakhale munthu, Yehova anawonjezeranso zinthu zimene Yesu anakumana nazo monga munthu wangwiro. Inde, ukulu wosasanthulika wa Yehova unaoneka ndi kuukitsidwa kwa Yesu. Ndiponso, chochitika chachikulu chimenechi chikutitsimikizira kuti kuukitsidwa kwa ena kudzatheka. Ziyenera kulimbitsa chikhulupiriro chathu chakuti Mulungu angathe kuukitsa anthu mamiliyoni amene anafa omwe ali m’chikumbumtima chake changwiro.​—Yohane 5:28, 29; Machitidwe 17:31.

Ntchito Zodabwitsa Ndiponso Zamphamvu

11. Kodi ndi ntchito yaikulu iti ya Yehova yomwe inayamba pa Pentekoste wa mu 33 C.E.?

11 Kuyambira nthaŵi imene Yesu anaukitsidwa, Yehova wachita ntchito zina zazikulu ndiponso zodabwitsa. (Salmo 40:5) Pa Pentekoste wa mu 33 C.E., Yehova anayambitsa mtundu watsopano, “Israyeli wa Mulungu” wopangidwa ndi ophunzira a Kristu amene anadzozedwa ndi mzimu woyera. (Agalatiya 6:16) Mtundu wauzimu watsopano umenewu unakula mwamphamvu padziko lonse la nthaŵi imeneyo. Ngakhale kuti panali mpatuko womwe unachititsa kuti Matchalitchi Achikristu akhaleko atumwi a Yesu atamwalira, Yehova anapitirizabe kuchita ntchito zodabwitsa kuti chifuno chake chikwaniritsidwe.

12. Kodi kupezeka kwa Baibulo m’zinenero zonse zazikulu padziko lapansi ndi umboni wa chiyani?

12 Mwachitsanzo, Baibulo lonse linasungidwa ndipo m’kupita kwanthaŵi linamasuliridwa m’zinenero zonse zazikulu zomwe zili padziko lapansi lerolino. Nthaŵi zambiri pomasulira Baibulo zinthu zinali zovuta kwambiri ndipo oimira Satana anali kuopseza kupha omasulirawo. Kunena zoona, kumasulira Baibulo m’zinenero zoposa 2,000 kumeneku sikukanatheka ngati si chinali chifuno cha Yehova Mulungu, amene ukulu wake ndi wosasanthulika.

13. Kuyambira mu 1914, kodi ukulu wa Yehova waonekera bwanji pankhani yokhudza zifuno za Ufumu?

13 Ukulu wa Yehova waonekera pankhani yokhudza zifuno za Ufumu wake. Mwachitsanzo, m’chaka cha 1914, anaika Mwana wake, Yesu Kristu, monga Mfumu ya kumwamba. Patapita kanthaŵi zimenezi zitachitika, Yesu anachitapo kanthu motsutsa Satana ndi ziwanda zake. Anawathamangitsa kumwamba ndipo ali pafupi ndi dziko, kumene tsopano akudikira kuponyedwa kuphompho. (Chivumbulutso 12:9-12; 20:1-3) Kuyambira nthaŵi imeneyo otsatira odzozedwa a Yesu akumana ndi chizunzo chachikulu. Koma Yehova wawachirikiza panthaŵi imeneyi ya kukhalapo kosaoneka kwa Kristu.​—Mateyu 24:3; Chivumbulutso 12:17.

14. Kodi ndi ntchito yodabwitsa iti imene Yehova anachita mu 1919 ndipo zimenezi zinakwaniritsa chiyani?

14 M’chaka cha 1919, Yehova anachita ntchito ina yodabwitsa imene inasonyeza ukulu wake. Otsatira odzozedwa a Yesu, omwe anali atafooledwa mwauzimu anapatsidwanso mphamvu. (Chivumbulutso 11:3-11) Zaka zotsatira, kuchokera nthaŵi imeneyo, odzozedwa alalikira mwachangu uthenga wabwino wa Ufumu wokhazikitsidwa kumwamba. Odzozedwa ena asonkhanitsidwa kuti akwanitse chiŵerengero cha 144,000. (Chivumbulutso 14:1-3) Ndipo mwa kugwiritsa ntchito otsatira odzozedwa a Kristu, Yehova anayala maziko a “dziko latsopano,” gulu la anthu olungama. (Chivumbulutso 21:1) Kodi n’chiyani chidzachitikira “dziko latsopano,” odzozedwa onse okhulupirika akadzapita kumwamba?

15. Kodi ndi ntchito yotani imene Akristu odzozedwa akhala akutsogolera ndipo pakhala zotsatira zotani?

15 Mu 1935, magazini ino ya August 1 ndi August 15 inali ndi nkhani zazikulu zofotokoza “khamu lalikulu” lotchulidwa mu Chivumbulutso chaputala 7. Akristu odzozedwa anayamba kufunafuna ndi kubweretsa mwachangu m’gulu lawo olambira anzawo ameneŵa ochokera mwa mtundu uliwonse, fuko lililonse, anthu alionse, ndi manenedwe alionse. “Khamu lalikulu” limeneli lidzapulumuka “chisautso chachikulu” chimene chayandikira, lili ndi chiyembekezo cha moyo wosatha m’Paradaiso monga anthu okhaliratu a “dziko latsopano.” (Chivumbulutso 7:9-14) Chifukwa cha ntchito ya Ufumu ya kulalikira ndi kupanga ophunzira, yotsogoleredwa ndi Akristu odzozedwa, anthu oposa 6 miliyoni tsopano ali ndi chiyembekezo cha moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi. Kodi ndani ayenera kulemekezedwa chifukwa cha kuwonjezeka kumene kukuchitika ngakhale kuti Satana ndi dziko lake loipa akutsutsa? (1 Yohane 5:19) Ndi Yehova yekhayo amene angachite zonsezi, mwa kugwiritsa ntchito mzimu wake woyera.​—Yesaya 60:22; Zekariya 4:6.

Ulemerero ndi Ulemu Waukulu wa Yehova

16. Kodi n’chifukwa chiyani anthu sangaone ‘ulemerero waukulu wa ulemu wa Yehova’?

16 Mulimonse mmene zingakhalire, “ntchito zodabwitsa” ndiponso “zamphamvu” za Yehova sizidzaiŵalika. Davide analemba kuti: “Mbadwo wina udzalemekezera ntchito zanu mbadwo unzake, ndipo udzalalikira zamphamvu zanu. Ndidzalingalira ulemerero waukulu wa ulemu wanu, ndi ntchito zanu zodabwiza. Ndipo adzanenera mphamvu za ntchito zanu zoopsa; ndi ukulu wanu ndidzaufotokozera.” (Salmo 145:4-6) Komabe, kodi Davide akanadziŵa motani za ulemerero waukulu wa Yehova, popeza “Mulungu ndiye mzimu” ndipo motero sangaonedwe ndi maso a anthu?​—Yohane 1:18; 4:24.

17, 18. Kodi Davide anakulitsa bwanji kuyamikira ‘ulemerero waukulu wa ulemu wa Yehova’?

17 Ngakhale kuti sanathe kuona Mulungu, panali njira zina zimene Davide akanakulitsira kuyamikira ulemu wa Yehova. Mwachitsanzo, ankaŵerenga nkhani za m’Malemba za ntchito zamphamvu za Mulungu monga kuwonongedwa kwa dziko loipa mwa kugwiritsa ntchito chigumula cha dziko lonse. Zikuoneka kuti Davide anadziŵa mmene milungu yonyenga ya ku Igupto inachititsidwira manyazi pamene Mulungu anapulumutsa Aisrayeli ku ukapolo wa ku Igupto. Zochitika zimenezi zimachitira umboni ulemu ndi ukulu wa Yehova.

18 Mosakayikira Davide anakulitsa kuyamikira kwake ulemu wa Mulungu osati kokha mwa kuŵerenga Malemba komanso mwa kuwasinkhasinkha. Mwachitsanzo, ayenera kuti anasinkhasinkha zimene zinachitika nthaŵi imene Yehova anapatsa Israyeli Chilamulo. Panali mabingu, mphezi, mtambo wakuda bii ndi liwu lamphamvu la lipenga. Phiri la Sinai linagwedezeka ndipo linafuka utsi. Atasonkhana m’munsi mwa phirilo, Aisrayeli anamva ngakhale ‘mawu khumi’ akuchokera pakati pa moto ndi m’mtambo pamene Yehova analankhula kudzera mwa mngelo. (Deuteronomo 4:32-36; 5:22-24; 10:4; Eksodo 19:16-20; Machitidwe 7:38, 53) Zimenezitu zinali zochitika zosonyeza ukulu wa Yehova! Anthu okonda Mawu a Mulungu amene amasinkhasinkha nkhani zimenezi ayenera kuchita chidwi ndi ‘ulemerero waukulu wa ulemu wa Yehova.’ Ndipo masiku ano tili ndi Baibulo lonse, limene lili ndi masomphenya aulemerero osiyanasiyana amene amatisonyeza kwambiri ukulu wa Yehova.​—Ezekieli 1:26-28; Danieli 7:9, 10; Chivumbulutso, chaputala 4.

19. Kodi n’chiyani chimene chidzawonjezera kuyamikira kwathu ulemu wa Yehova?

19 Njira ina imene Davide akanaonera ulemu wa Mulungu ndi mwa kuphunzira malamulo amene Mulungu anapatsa Aisrayeli. (Deuteronomo 17:18-20; Salmo 19:7-11) Mtundu wa Israyeli unali wolemekezeka ndiponso wosiyana ndi anthu ena onse chifukwa chomvera malamulo a Yehova. (Deuteronomo 4:6-8) Monga mmene zinalili kwa Davide, kuŵerenga Malemba nthaŵi zonse, kuwasinkhasinkha mwakuya ndiponso kuwaphunzira ndi mtima wonse kudzawonjezera kuyamikira kwathu ulemu wa Yehova.

Makhalidwe a Mulungu Ndi Aakulu Koposa!

20, 21. (a) Lemba la Salmo 145:7-9 limasonyeza bwino kwambiri ukulu wa Yehova mwa kunena za makhalidwe ati? (b) Kodi makhalidwe a Mulungu otchulidwa pamenepa amawakhudza bwanji onse amene amam’konda?

20 Monga mmene taonera, mavesi oyambirira asanu ndi limodzi a Salmo 145 amatipatsa zifukwa zomveka zolemekezera Yehova chifukwa cha zinthu zokhudza ukulu wake wosasanthulika. Mavesi 7 mpaka 9 amasonyeza bwino kwambiri ukulu wa Mulungu mwa kunena za makhalidwe ake. Davide anaimba kuti: “Adzabukitsa chikumbukiro cha ubwino wanu waukulu, nadzaimbira chilungamo chanu. Yehova ndiye wachisomo, ndi wachifundo; wosakwiya msanga, ndi wa chifundo chachikulu [“wokoma mtima mwachikondi kwambiri,” NW]. Yehova achitira chokoma onse; ndi nsoni zokoma zake zigwera ntchito zake zonse.”

21 Pamenepa Davide choyamba anafotokoza ubwino ndi chilungamo cha Yehova, makhalidwe amene Satana Mdyerekezi anakayikira. Kodi makhalidwe ameneŵa amawakhudza bwanji onse amene amakonda Mulungu ndi kugonjera ulamuliro wake? Ndithudi, ubwino wa Yehova ndi kulamulira kwake kolungama zimasangalatsa olambira ake moti sangasiye kum’lemekeza. Ndipo ubwino wa Yehova umapita kwa “onse.” Tikukhulupirira kuti zimenezi zidzathandiza anthu ambiri kulapa ndi kukhala olambira Mulungu woona madzi asanafike m’khosi.​—Machitidwe 14:15-17.

22. Kodi Yehova amachita bwanji ndi atumiki ake?

22 Davide anayamikiranso kwambiri makhalidwe amene Mulungu anatchula pamene “anapita pamaso pa [Mose], nafuula, Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachoonadi.” (Eksodo 34:6) Motero, Davide anati: ‘Yehova ndiye wachisomo, ndi wachifundo; wosakwiya msanga, ndi wokoma mtima mwachikondi kwambiri.’ Ngakhale kuti ukulu wa Yehova ndi wosasanthulika, amalemekeza anthu omutumikira mwa kuwasonyeza chisomo. Iye ndi wachifundo kwambiri ndipo ali wofunitsitsa kukhululukira ochimwa olapa pamaziko a nsembe ya dipo ya Yesu. Yehova alinso wosakwiya msanga chifukwa amapatsa atumiki ake mpata wothetsa zofooka zimene zingawalepheretse kuloŵa m’dziko lake lolungama.​—2 Petro 3:9, 13, 14.

23. Kodi ndi khalidwe lofunika kwambiri liti limene tidzakambirana m’nkhani yotsatira?

23 Davide anafotokoza za kukoma mtima kwa chikondi kapena kuti chikondi chokhulupirika cha Mulungu. Ndipotu, mbali yotsala ya Salmo 145 imafotokoza mmene Yehova amasonyezera khalidwe limeneli ndiponso mmene atumiki ake okhulupirika amachitira ndi kukoma mtima kwake kwachikondi. Nkhani yotsatira ifotokoza zimenezi.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi pali mipata yotani yolemekezera Yehova ‘tsiku lonse’?

• Kodi ndi zitsanzo ziti zimene zimasonyeza kuti ukulu wa Yehova ndi wosasanthulika?

• Kodi tingakulitse bwanji kuyamikira ulemu waukulu wa Yehova?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 10]

Milalang’amba ya kuthambo imachitira umboni za ukulu wa Yehova

[Mawu a Chithunzi]

Courtesy of Anglo-Australian Observatory, photograph by David Malin

[Chithunzi patsamba 12]

Kodi ukulu wa Yehova wasonyezedwa bwanji ndi zochitika zokhudza Yesu Kristu?

[Chithunzi patsamba 13]

Pamene Aisrayeli analandira Chilamulo pa Phiri la Sinai, anaona ulemu waukulu wa Yehova