Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chikumbumtima Chokoma

Chikumbumtima Chokoma

Chikumbumtima Chokoma

TSIKU lina Charles, amene amagwira ntchito pa yunivesite inayake ku Kenya, anataya telefoni yake ya m’manja akupita kwawo kuchokera ku ntchito. Ku Kenya, matelefoni a m’manja akadali okwera mtengo kwambiri.

Charles anati: “Sindinayembekezere kuti munthu wina aliyense adzabweza telefoniyo.” Koma patangopita masiku ochepa, iye anadabwa a ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Kenya atamuimbira telefoni. Sanakhulupirire pamene anamuuza kuti apite akatenge telefoni yake ya m’manja! Anamuuza kuti mtumiki wa nthaŵi zonse wa Mboni za Yehova anakwera galimoto imenenso Charles anakwera ndipo anapeza foniyo. Pofuna kupeza mwiniwake wa foniyo, mtumikiyo anaibweretsa ku ofesi ya nthambi, ndipo anthu ongodzipereka ogwira ntchito kumeneko pamapeto pake anamupeza Charles atafufuza nambala imene inasonyezedwa pa fonipo.

M’kalata imene Charles analembera ofesi ya nthambiyo, anati: “Ndikuyamikira kwambiri khama lanu kuti mundipeze ngakhale kuti zinali zovuta kwambiri. Ndikuthokoza kwambiri anthu a m’gulu lanu amene anapeza foniyo, kufufuza kuti ndi yanga, ndi kundibwezera. N’chinthu chovuta kupeza munthu woona mtima masiku ano, koma n’zolimbikitsa kuti tili ndi anthu ochepa amene ali osiyana ndi ena onse chifukwa chokhala Mboni zoona za Yehova Mulungu.”

Mboni za Yehova zimadziŵika kulikonse chifukwa cha kuona mtima kwawo. Zimatsatira chitsanzo cha mtumwi Paulo, amene ananena kuti: “Takopeka mtima kuti tili nacho chikumbumtima chokoma m’zonse, pofuna kukhala nawo makhalidwe abwino.” (Ahebri 13:18; 1 Akorinto 11:1) Zimadziŵa kuti khalidwe loterolo limalemekeza Yehova Mulungu, monga mmene ananenera Yesu kuti: “Muŵalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.”​—Mateyu 5:16.