Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Maonekedwe a Dzikoli Akusintha”

“Maonekedwe a Dzikoli Akusintha”

“Maonekedwe a Dzikoli Akusintha”

“Ichi nditi, abale, yafupika nthaŵi.”​—1 AKORINTO 7:29.

1, 2. Kodi ndi zinthu ziti m’dzikoli zimene mwaona zikusintha pa moyo wanu?

KODI ndi zinthu ziti m’dzikoli zimene mwaona zikusintha pa moyo wanu? Kodi mungafotokoze zina mwa zimenezo? Mwachitsanzo, pakhala kupita patsogolo kwa sayansi ya zamankhwala. Chifukwa cha kafukufuku pa zamankhwala, zaka zimene anthu ambiri amakhala ndi moyo zawonjezeka m’mayiko ena. Kuchiyambi kwa zaka za m’ma 1900 anthu ambiri anali kukhala ndi moyo zaka zosakwana 50 koma masiku ano ambiri akufika zaka zoposa 70. Taganiziraninso za njira zimene tapindula pogwiritsa ntchito moyenera wailesi, TV, matelefoni a m’manja, ndi makina a fax. Zinthu zinanso zofunika kwambiri ndizo kupita patsogolo pa nkhani ya maphunziro, kayendedwe, komanso pa ufulu wa anthu, zimene zonse zachitititsa kuti miyoyo ya anthu ambiri ikhale yabwinopo.

2 Komabe, si kusintha konse kumene kwakhala kwabwino. Sitinganyalanyaze mavuto aakulu amene abwera chifukwa cha kuwonjezeka kwa upandu, kuloŵa pansi kwa makhalidwe abwino, kuchuluka kwa anthu ogwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, kukwera kwa chiŵerengero cha anthu amene akusudzulana, ndiponso kukwera kwa mitengo ya zinthu, ndi kuipiraipira kwa uchigaŵenga. Mulimonse mmene zingakhalire, mosakayikira mudzavomereza zimene mtumwi Paulo analemba kale kwambiri kuti: “Maonekedwe a dzikoli apita [“akusintha,” NW].”​—1 Akorinto 7:31.

3. Kodi Paulo anatanthauzanji pamene analemba kuti “maonekedwe a dzikoli akusintha”?

3 Pamene Paulo amanena mawu ameneŵa, ankayerekezera dzikoli ndi bwalo la seŵero. Ochita seŵero pabwalolo amene ndi andale, achipembedzo, ndi anthu otchuka amabwera n’kuchitapo mbali yawo, kenaka n’kusiyira ena bwalolo. Zimenezi zakhala zikuchitika kwa nthaŵi yaitali. M’zaka za m’mbuyomu, maufumu ankalamulira kwa zaka zambiri ndithu, ndipo kuti zisinthe zinkatenga nthaŵi yaitali. Zinthu sizili choncho masiku ano, pamene sizitenga nthaŵi yaitali kuti munthu aphe mtsogoleri. Inde, mu nthaŵi zovuta zino, sitidziŵa chimene chichitike maŵa.

4. (a) Kodi Akristu ayenera kuona motani zochitika za m’dzikoli? (b)  Kodi ndi maumboni aŵiri ati ogwira mtima amene tikambirane tsopano?

4 Ngati dzikoli ndi bwalo la seŵero ndipo atsogoleri a dziko ndi ochita seŵero, ndiye kuti Akristu ndi oonerera. * Komabe, chifukwa chakuti “siali a dziko lapansi,” Akristuwo sakhudzidwa kwambiri ndi zimene oseŵerawo akuchita kapena kuti oseŵerawo ndi ndani. (Yohane 17:16) Mmalo mwake, amayang’ana mwachidwi zizindikiro zosonyeza kuti seŵerolo latsala pang’ono kufika kumapeto, omwe ndi mapeto omvetsa chisoni. Zimenezi zili choncho chifukwa chakuti amadziŵa kuti dongosolo lino la zinthu liyenera kutha Yehova asanabweretse dziko latsopano lachilungamo limene anthu akhala akuliyembekezera kwa nthaŵi yaitali. * Tiyeni tsopano tipende maumboni aŵiri amene akusonyeza kuti tikukhala mu nthaŵi yamapeto ndiponso kuti dziko latsopano layandikira. Umboni umenewu ndi (1) nthaŵi ya zochitika za m’Baibulo ndi (2) kuipiraipira kwa zochitika za m’dzikoli.​—Mateyu 24:21; 2 Petro 3:13.

Zovuta Kuzimvetsa Zadziŵika

5. Kodi “nthaŵi zawo za anthu akunja” n’chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani zikutichititsa chidwi ifeyo?

5 Yesu analankhula za nthaŵi imene atsogoleri a dzikoli adzakhala m’bwalo la seŵero popanda kusokonezedwa ndi Ufumu wa Mulungu. Anatcha nthaŵi imeneyo “nthaŵi zawo za anthu akunja.” (Luka 21:24) Kumapeto kwa “nthaŵi zawo” zimenezo, Ufumu wakumwamba wa Mulungu udzayamba kugwira ntchito, ndipo Yesu adzakhala Wolamulira woyenera. Poyamba, Yesu adzalamulira “pakati pa adani [ake].” (Salmo 110:2) Kenako, malinga ndi kunena kwa Danieli 2:44, Ufumuwo “udzaphwanya ndi kutha” maboma onse a anthu, ndipo udzakhalapo mpaka kalekale.

6. Kodi “nthaŵi zawo za akunja” zinayamba liti, zinatenga nthaŵi yaitali bwanji, ndipo zinatha liti?

6 Kodi “nthaŵi zawo za anthu akunja” zidzatha liti, nanga Ufumu wa Mulungu udzayamba liti kulamulira? Yankho lake, limene ‘linakhomeredwa chizindikiro mpaka nthaŵi ya chitsiriziro,’ limakhudza nthaŵi ya zochitika za m’Baibulo. (Danieli 12:9) Pamene “nthaŵi” imeneyo imayandikira, Yehova anachitapo kanthu kuti aulule mayankho kwa kagulu kodzichepetsa ka ophunzira Baibulo. Mothandizidwa ndi mzimu wa Mulungu, anazindikira kuti “nthaŵi zawo za anthu akunja” zinayamba pamene Yerusalemu anawonongedwa mu 607 B.C.E. ndiponso kuti “nthaŵi” zimenezo zinali zaka 2,520. Kuchokera pa zimenezi anaŵerengera anapeza kuti chaka cha 1914 chinali mapeto a “nthaŵi zawo za anthu akunja.” Ndiponso anazindikira kuti 1914 ndi pamene panayambira kutha kwa dongosolo lino la zinthu. Monga wophunzira Baibulo, kodi mungafotokoze kuchokera m’Malemba mmene mungawerengetsere kuti mupeze kuti chaka cha 1914 ndi pamene zimenezi zinachitika? *

7. Kodi ndi malemba ati amene akutithandiza kuzindikira chiyambi, kutalika, ndi mapeto a nthaŵi zisanu ndi ziŵiri zotchulidwa m’buku la Danieli?

7 Njira imodzi yodziŵira zimenezi ili m’buku la Danieli. Chifukwa chakuti Yehova anagwiritsa ntchito Mfumu Nebukadinezara ya Babulo kuti awononge Yerusalemu kumayambiriro kwa “nthaŵi zawo za anthu akunja,” mu 607 B.C.E., Iye anaulula kwa wolamulira ameneyo kuti mitundu idzapitiriza kulamulira mosasokonezedwa ndi Mulungu kwa nthaŵi zisanu ndi ziŵiri zophiphiritsira. (Ezekieli 21:26, 27; Danieli 4:16, 23-25) Kodi nthaŵi zisanu ndi ziŵiri zimenezo ndi zazitali bwanji? Malinga ndi Chivumbulutso 11:2, 3, ndi 12:614, nthaŵi zitatu ndi theka ndi masiku 1,260. Motero, nthaŵi zisanu ndi ziŵiri ziyenera kukhala kuŵirikiza kaŵiri masiku amenewo, kapena kuti masiku 2,520. Kodi zathera pomwepo? Ayi, chifukwa chakuti Yehova anapereka kwa mneneri Ezekieli, amene anakhalapo nthaŵi yofanana ndi Danieli, njira yomasulira nthaŵi yophiphiritsirayi kuti: “Ndakuikira . . . tsiku limodzi ngati chaka chimodzi.” (Ezekieli 4:6) Motero, nthaŵi zisanu ndi ziŵiri kwenikweni ndi zaka 2,520. Pogwiritsa ntchito chaka cha 607 B.C.E. monga poyambira ndipo zaka 2,520 monga kutalika kwake, tinganene kuti nthaŵi za akunja zinatha mu 1914.

Kutsimikizira Kuti Ndi “Nthaŵi ya Chitsiriziro”

8. Kodi mungasonyeze umboni uti kuti zochitika m’dzikoli zaipiraipira kuyambira 1914?

8 Zochitika m’dzikoli kuyambira mu 1914 kupita m’tsogolo zimatsimikizira kuti kumvetsa Baibulo kumene kwafotokozedwa pamwambapa pogwiritsa ntchito nthaŵi ya zochitika za m’Baibulo n’kolondola. Yesu ananena kuti “mathedwe a nthaŵi ya pansi pano” adzadziŵika ndi nkhondo, njala, ndi miliri. (Mateyu 24:3-8; Chivumbulutso 6:2-8) Zimenezi zakhala zikuchitikadi chiyambire 1914. Mtumwi Paulo anawonjezera kuti, anthu adzasintha mmene anali kuchitira zinthu ndi anthu anzawo. Kufotokoza kwake za kusintha kumeneku, kumene tonse takuona, kunali kolondola.​—2 Timoteo 3:1-5.

9. Kodi anthu ena anenanji zokhudza zochitika m’dzikoli kuyambira mu 1914?

9 Kodi “maonekedwe a dzikoli” asinthadi kuyambira mu 1914? M’buku la The Generation of 1914, pulofesa Robert Wohl anati: “Amene anapulumuka nkhondo anakhulupirira kuti dziko lina linatha ndipo lina linayamba mu August 1914.” Potsimikizira zimenezi, Dr. Jorge A. Costa e Silva, yemwe ndi katswiri wamatenda amaganizo wa bungwe la World Health Organization, analemba kuti: “Tikukhala mu nthaŵi imene zinthu zimasintha mofulumira kwambiri, zimene zimachititsa nkhaŵa ndi kuvutika maganizo kumene sikunachitikeponso m’mbiri yonse ya anthu.” Kodi zimenezo n’zimene inu mwaona?

10. Kodi Baibulo limatiunikira bwanji za kuipiraipira kwa zinthu m’dzikoli kuyambira mu 1914?

10 Kodi ndani akuchititsa kuti zinthu ziipe padziko lapansili? Lemba la Chivumbulutso 12:7-9 limatchula amene akuchititsa, ponena kuti: “Munali nkhondo m’mwamba. Mikayeli [Yesu Kristu] ndi angelo ake akuchita nkhondo ndi chinjoka [Satana Mdyerekezi], chinjokanso ndi angelo ake chinachita nkhondo; ndipo sichinalakika, ndipo sanapezekanso malo awo m’mwamba. Ndipo chinaponyedwa pansi chinjoka chachikulu, . . . wonyenga wa dziko lonse.” Choncho Satana Mdyerekezi ndi amene ali ndi mlandu woyambitsa mavuto, ndipo kuchotsedwa kwake kumwamba mu 1914 kwatanthauza “tsoka mtunda ndi nyanja, chifukwa mdyerekezi watsikira kwa [ife], wokhala nawo udani waukulu, podziŵa kuti kam’tsalira kanthaŵi.”​—Chivumbulutso 12:10, 12.

Mmene Zinthu Zidzathere

11. (a) Kodi Satana amagwiritsa ntchito njira zotani kuti asocheretse “dziko lonse”? (b) Kodi mtumwi Paulo anafotokoza kuti Satana akuchita khama lotani?

11 Podziŵa kuti nthaŵi yake yamuthera, kuyambira mu 1914, Satana wakhala akuyesetsa kusocheretsa “dziko lonse.” Nthaŵi zonse wonyenga wamkulu, Satana, amadzibisa, n’kumaonetsa atsogoleri adziko ndi anthu oyambitsa zinthu zatsopano ngati oseŵera. (2 Timoteo 3:13; 1 Yohane 5:19) Chimodzi mwa zolinga zake ndi kunyenga anthu kuti aziganiza kuti njira zake zolamulirira zikhoza kuwabweretsera mtendere weniweni. Kunena zoona, mabodza ake agwira ntchito, chifukwa anthu akukhulupirira kuti zinthu zidzayenda bwino ngakhale kuti pali umboni wochuluka kuti khalidwe la anthu likuipiraipira. Mtumwi Paulo analosera kuti dongosolo la zinthu lilipoli lisanawonongedwe, padzakhala zizindikiro zambiri zabodza la Satana. Iye analemba kuti: “Pamene angonena, Mtendere ndi mosatekeseka [“chitetezo,” NW], pamenepo chiwonongeko chobukapo chidzawagwera, monga zoŵaŵa mkazi wa pakati.”​—1 Atesalonika 5:3; Chivumbulutso 16:13.

12. Kodi pakhala zoyesayesa zotani zokhazikitsa mtendere masiku athu ano?

12 M’zaka zaposachedwapa, anthu andale nthaŵi zambiri akhala akunena kuti “mtendere ndi chitetezo” pofotokoza zolinga zawo zosiyanasiyana. Ndipo anatchula chaka cha 1986 kukhala Chaka cha Mtendere Padziko Lonse, ngakhale kuti chaka chimenecho sikunakhale mtendere. Kodi zoyesayesa zimenezo za atsogoleri adziko zikusonyeza kukwaniritsidwa kwakukulu kwa 1 Atesalonika 5:3, kapena kodi Paulo ankanena zinthu zimene zidzakhala zapadera kwambiri zimene zidzadziŵika kwambiri padziko lapansi?

13. Pamene Paulo analosera za “mtendere ndi chitetezo,” kodi anayerekezera chiwonongeko chimene chidzabwera ndi chiyani, ndipo tingaphunzire chiyani pa zimenezi?

13 Chifukwa chakuti maulosi a m’Baibulo nthaŵi zambiri timawamvetsa bwino atakwaniritsidwa kale kapena pamene akukwaniritsidwa, tifunika kungoyembekezera kuti tione. Komabe, n’zochititsa chidwi kuona kuti Paulo anayerekezera chiwonongeko chadzidzidzi, chimene chidzabwera atangonena kuti “Mtendere ndi chitetezo,” ndi zowawa za mkazi wa pakati. Pa nyengo ya miyezi pafupifupi isanu ndi inayi, mayi woyembekezera amadziŵa bwino kwambiri za mwana amene akukula m’mimba mwake. Akhoza kumva kugunda kwa mtima wa mwana wake kapena kumumva akutakataka m’mimba. Mwina angamumenye kumene ndi mapazi. Zizindikiro zimamveka kwambiri mpaka tsiku lina, mayiyo amamva kupweteka kwambiri, kusonyeza kuti nthaŵi imene wakhala akuyembekezera, yoti mwana abadwe, yafika. Motero, kaya ulosi wakuti “Mtendere ndi chitetezo” udzakwaniritsidwa motani, udzachititsa kuti pakhale kupweteka kwadzidzidzi. Kenako padzachitika zinthu zosangalatsa, kuipa konse kudzathetsedwa ndipo dziko latsopano lidzayambika.

14. Kodi zinthu zidzachitika mwadongosolo lotani, ndipo padzakhala zotsatira zotani?

14 Chiwonongeko chimene chikubweracho chidzakhala choopsa kwa Akristu okhulupirika pamene akungoonerera. Poyamba, mafumu a dziko lapansi (mbali za ndale za gulu la Satana) adzaukira Babulo Wamkulu (mbali yachipembedzo) ndipo adzaiwononga. (Chivumbulutso 17:1, 15-18) Choncho, modabwitsa kwambiri zinthu zidzatembenuka, ufumu wa Satana udzagaŵika pakati, pamene mbali ina idzaukira inzake, ndipo Satana sadzakhala ndi mphamvu zouteteza. (Mateyu 12:25, 26) Yehova adzaika mu mtima wa mafumu a dziko lapansi kuti ‘achite za mu mtima mwake,’ kuchotsa padziko lapansi mdani wake, chipembedzo chonyenga. Chipembedzo chonyenga chikadzawonongedwa, Yesu Kristu adzatsogolera magulu ake akumwamba kuchotsa kotheratu zinthu zotsala za gulu la Satana, zamalonda ndi zandale. Pomaliza, Satana weniweniyo adzamutsekera. Kenako, seŵero lalitalilo lidzatha.​—Chivumbulutso 16:14-16; 19:11-21; 20:1-3.

15, 16. Kodi mawu otikumbutsa akuti “yafupika nthaŵi” ayenera kutikhudza motani pa miyoyo yathu?

15 Kodi zinthu zonsezi zidzachitika liti? Sitikudziŵa tsiku kapena nthaŵi. (Mateyu 24:36) Komabe, tikudziŵa kuti “yafupika nthaŵi.” (1 Akorinto 7:29) Ndiyetu n’zofunika kuti tigwiritse ntchito mwanzeru nthaŵi imene yatsalayi. Motani? Monga mmene mtumwi Paulo anafotokozera, tiyenera ‘kuwombola nthaŵi’ kuti tichite zinthu zofunika kwambiri ndiponso kuchititsa kuti tsiku lililonse likhale laphindu. Chifukwa chiyani? “Popeza masiku ali oipa.” Ndipo ‘podziŵa chifuniro cha Ambuye n’chiyani’ kwa ife, sitidzawononga nthaŵi yochepa yamtengo wapatali imene yatsala.​—Aefeso 5:15-17, NW; 1 Petro 4:1-4.

16 Kodi aliyense wa ife ayenera kukhudzidwa motani podziŵa kuti dongosolo la zinthu lonseli latsala pang’ono kuwonongedwa? Mtumwi Petro analemba mawu otsatiraŵa n’cholinga choti atithandize: “Popeza izi zonse zidzakanganuka kotero, muyenera inu kukhala anthu otani nanga m’mayendedwe opatulika ndi m’chipembedzo.” (2 Petro 3:11) Inde, tiyeneradi kukhala anthu otero! Mogwirizana ndi mawu anzeru a Petro, tiyenera (1) kuonetsetsa kuti khalidwe lathu likhale loyera, ndiponso (2) kuonetsetsa kuti changu chathu mu utumiki wa Yehova nthaŵi zonse chikusonyeza kuti timamukonda kwambiri.

17. Kodi Akristu okhulupirika ayenera kupeŵa misampha iti ya Satana?

17 Kukonda kwathu Mulungu kudzatichititsa kupeŵa kutengeka ndi dzikoli chifukwa cha zinthu zake zokopa. Podziŵa zimene zichitikire dongosolo la zinthu limene lilipoli, tiyenera kupeŵa kukopeka ndi moyo wa m’dzikoli wokonda zosangalatsa umene umaoneka ngati ndi wabwino kwambiri. Ngakhale kuti tikugwira ntchito m’dzikoli ndiponso tikukhalamo, tiyenera kumvera langizo lanzeru losagwiritsa ntchito dziko kwambiri. (1 Akorinto 7:31) Mmalo mwake, tiyenera kuchita zonse zomwe tingathe kuti tisasocheretsedwe ndi mabodza a dzikoli. Dzikoli silidzatha kupeza njira zothetsera mavuto ake. Silidzapitiriza kudzikonza lokha. N’chifukwa chiyani tikunena motsimikiza choncho? Chifukwa chakuti Mawu a Mulungu ouziridwa amanena zimenezo kuti: “Dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi yonse.”​—1 Yohane 2:17.

M’tsogolomu Muli Zabwino

18, 19. Kodi ndi kusintha kotani kumene mukuyembekezera m’dziko lapansi latsopano, ndipo n’chifukwa chiyani mungadzanene kuti m’pake kuti munayembekezera?

18 Posachedwapa Yehova adzawononga Satana ndi omutsatira ake. Kenako, modalitsidwa ndi Mulungu, anthu amene adzapulumuke mapeto a dongosolo lino la zinthu adzayamba kusintha zinthu padziko zimene zidzakhala mpaka kalekale. Nkhondo sidzakhalakonso. Mulungu ‘adzaletsa nkhondo ku malekezero adziko lapansi.’ (Salmo 46:9) Mmalo mosoŵa chakudya, “m’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka . . . zidzati waa.” (Salmo 72:16) Sikudzakhalanso ndende, maofesi apolisi, matenda opatsirana pogonana, anthu ogulitsa mankhwala osokoneza bongo, makhoti kumene athu amasudzulana, milandu yokhudza anthu kapena makampani amene ndalama zawo zatha, ndiponso uchigaŵenga.​—Salmo 37:29; Yesaya 33:24; Chivumbulutso 21:3-5.

19 Anthu amene ali m’manda achikumbukiro adzauka, ndipo anthu oukitsidwa miyandamiyanda, oseŵera ambiri, adzakhala padziko lapansi. Zidzakhalatu zosangalatsa kwambiri pamene mibadwo idzagwirizana ndiponso pamene anthu okondana amene anasiyana kalekale adzakumbatirana mosangalala. Pamapeto pake, aliyense amene adzakhalapo adzalambira Yehova. (Chivumbulutso 5:13) Kusintha kumeneku kukadzatha, dziko lapansi lidzasanduka paradaiso. Kodi mudzamva bwanji kuona zochitika zimenezo? Mosakayikira mudzanena kuti, ‘Ndakhala ndikuyembekezera kwa nthaŵi yaitali zimenezi, koma m’pake kuti ndinayembekezera!’

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Mu nkhani ina, Paulo analankhula za Akristu odzozedwa kukhala “choonetsedwa ku dziko lapansi, ndi kwa angelo, ndi kwa anthu.”​—1 Akorinto 4:9.

^ ndime 4 Mwachitsanzo, kuti muidziŵe “mfumu ya kumpoto,” yotchulidwa pa Danieli 11:40, 44, 45, onani buku la Samalani Ulosi wa Danieli!, masamba 280 mpaka 281.

^ ndime 6 Baibulo limasonyeza kuti Yerusalemu anagwa zaka 70 Ayuda amene anagwidwa ukapolo asanabwerere kwawo mu 537 B.C.E. (Yeremiya 25:11, 12; Danieli 9:1-3) Kuti muone nkhani yatsatanetsatane ya “nthaŵi zawo za anthu akunja,” onani masamba 231 mpaka 233 a buku la Kukambitsirana za m’Malemba, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi mawu a mtumwi Paulo akuti “maonekedwe a dzikoli akusintha” akwaniritsidwa bwanji m’nthaŵi yathu ino?

• Kodi nthaŵi ya zochitika za m’Baibulo imatithandiza bwanji kudziŵa mapeto a “nthaŵi zawo za anthu akunja”?

• Kodi kusintha kwa zinthu m’dzikoli kwatsimikizira bwanji kuti chaka cha 1914 ndi pamene panayambira “nthaŵi yamapeto”?

• Kodi mfundo yakuti “yafupika nthaŵi” iyenera kutikhudza motani?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 20]

Zovuta kuzimvetsa zadziŵika!