Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene Kukonda Zinthu Zauzimu Kumakhudzira Moyo Wanu

Mmene Kukonda Zinthu Zauzimu Kumakhudzira Moyo Wanu

Mmene Kukonda Zinthu Zauzimu Kumakhudzira Moyo Wanu

MOSAKAYIKA, mumatha nthaŵi yochuluka mukusamalira thanzi lanu. Tsiku lililonse mwina mumagona kwa maola asanu ndi atatu, mumatha maola angapo mukuphika ndi kudya, ndiponso mumagwira ntchito kwa maola asanu ndi atatu kapena kuposa pamenepo kuti mupeze ndalama zolipirira malo ogona ndiponso zogulira chakudya. Mukadwala muyenera kuti mumatha nthaŵi ndi ndalama zanu kupita kuchipatala kapena kukonza mankhwala a zitsamba. Mumayeretsa panyumba panu, mumasamba, ndiponso mwina mumachita maseŵero olimbitsa thupi nthaŵi ndi nthaŵi, ndipo zonsezi mumachita n’cholinga choti mukhale ndi thanzi labwino.

Komabe, kuti mupitirize kukhala ndi thanzi labwino pamafunika zambiri osati kungosamalira thupi lanu basi. Palinso chinthu china chimene chimakhudza kwambiri moyo wanu. Ofufuza zamankhwala apeza kuti thanzi la thupi lanu limayendera limodzi ndi thanzi lanu lauzimu, zimene zikutanthauza kuti kukonda kwanu zinthu zauzimu kapena kusazikonda kudzakhudza thanzi lanu.

Kugwirizana Kwake

Pulofesa Hedley G. Peach wa pa yunivesite ya Melbourne ku Australia, anati: “Pa kafukufuku amene anachitika pa nkhani imeneyi, tinapeza kuti munthu akamakonda kwambiri zinthu zauzimu, thanzi lakenso limakhala labwinopo.” Pothirirapo ndemanga pa zimene a kafukufukuŵa anapeza, magazini ya The Medical Journal of Australia (MJA) inati: “Kukonda kupembedza kwaoneka kuti kumathandiza . . . kuchepetsa vuto la kuthamanga kwambiri magazi, kumachepetsa mafuta a m’mitsempha. . . ndiponso kukhoza kuchepetsa kansa ya m’matumbo.”

Mofanana ndi zimenezi, pa kafukufuku amene a yunivesite ya California (UC), mumzinda wa Berkeley ku United States anachita mu 2002 pa anthu 6,545, anapeza kuti “anthu amene amapita kopembedza mlungu uliwonse amakhala ndi moyo wotalikirapo kusiyana ndi anthu amene sapitapita kapena sapita n’komwe kopembedza.” Doug Oman, amene anatsogolera kafukufukuyo komanso ndi mphunzitsi pa sukulu ya UC Berkeley’s School of Public Health, anati: “Tapeza kusiyana kumeneku ngakhale pamene tinaphatikizapo zinthu zina monga kucheza kwawo ndi anthu ena ndiponso zinthu zimene amakonda kuchita zimene zimakhudza thanzi lawo, monga kusuta ndi kuchita maseŵero olimbitsa thupi.”

Pofotokoza phindu lina limene anthu okonda zinthu zauzimu pamoyo wawo amakhala nalo, magazini ya MJA inati: “Kufufuza kumene anachita ku Australia anapeza kuti anthu amene amakonda kupembedza amakhala ndi mabanja olimbirapo, samwetsa kwambiri moŵa ndiponso sagwiritsa ntchito kwambiri mankhwala osokoneza bongo, si ambiri amene amadzipha ndipo ambiri saganizira n’komwe zodzipha, sada nkhaŵa kwambiri ndiponso savutika kwambiri maganizo, komanso ambiri si odzikonda.” Kuwonjezeranso pamenepo, magazini ya BMJ (imene kale ankaitcha The British Medical Journal) inati: “Anthu amene amati ali ndi zikhulupiriro zolimba zauzimu akuoneka kuti amathetsa chisoni chawo mofulumira ndiponso chimatheratu munthu amene ankagwirizana naye kwambiri akamwalira kusiyana ndi anthu amene sakhulupirira zinthu zauzimu.”

Pali maganizo osiyanasiyana pankhani yoti kukonda zinthu zauzimu kwenikweni n’kutani. Komabe, kukonda kapena kusakonda zinthu zauzimu kumakhudza thanzi lanu ndiponso maganizo anu. Umboni umenewu ukugwirizana ndi zimene Yesu Kristu ananena zaka pafupifupi 2,000 zapitazo. Iye anati: “Achimwemwe ndi anthu amene amazindikira kusoŵa kwawo kwauzimu.” (Mateyu 5:3, NW) Popeza kuti thanzi lanu ndiponso kuti mukhale wachimwemwe zimadaliranso mmene moyo wanu wauzimu ulili, mpake kufunsa kuti: ‘Kodi ndingapeze kuti malangizo auzimu odalirika? Ndipo kodi kukhala munthu wokonda zinthu zauzimu kumatanthauza chiyani?’

[Mawu a Chithunzi patsamba 2]

Kuyamikira zithunzi: Tsamba 18: Mao Tse-tung ndi Golda Meir: Hulton/Archive by Getty Images; Francis Ferdinand: Kuchokera m’buku la The War of the Nations; Hirohito, Lindbergh, & Einstein: chithunzi cha U.S. National Archives; Stalin: chithunzi cha U.S. Army; Roosevelt: Franklin D. Roosevelt Library; Churchill: The Trustees of the Imperial War Museum (MH 26392)