Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Khalanibe Odzisunga mwa Kutchinjiriza Mtima Wanu

Khalanibe Odzisunga mwa Kutchinjiriza Mtima Wanu

Khalanibe Odzisunga mwa Kutchinjiriza Mtima Wanu

“Tchinjiriza mtima wako koposa zonse uzisunga; pakuti magwero a moyo atulukamo.”​—MIYAMBO 4:23.

1-3. (a) Nthaŵi zambiri anthu amasonyeza motani kuti saona kudzisunga kukhala kofunika? Perekani chitsanzo. (b) N’chifukwa chiyani kupenda phindu la kudzisunga kuli kofunika?

N’KUTHEKA kuti chithunzicho chinkaoneka chachikale. Mwina sichinkagwirizana ndi maonekedwe a m’nyumbamo. Mulimonsemo, n’zoonekeratu kuti mwini chithunzicho analibe nacho ntchito kwenikweni. Mapeto ake chinangogulitsidwa pamtengo wa madola 29 a ku United States, pofuna kupeza chithandizo cha osoŵa. Koma patatha zaka zingapo, chithunzichi chinapezeka kuti chingagulitsidwe madola pafupifupi wani miliyoni. Inde, chinali kuoneka kuti chinajambulidwa mwaluso kwambiri. Taganizirani mmene anamvera mwiniwake woyamba uja, yemwe anapeputsa chuma chimenechi!

2 Izi n’zofanana ndi zomwe zimachitikanso kaŵirikaŵiri pankhani ya kudzisunga, lomwe ndi khalidwe loyera la munthu. Anthu ambiri masiku ano amapeputsa kufunika kokhala wodzisunga. Ena amaganiza kuti khalidweli n’lachikale, losagwirizana ndi moyo wamasiku ano. Motero amalephera kudzisunga chifukwa cha zinthu zing’onong’ono. Ena amagulitsa kudzisunga kwawo pofuna kusangalala ndi chiwerewere kwa nthaŵi yochepa. Ena sadzisunga pofuna kudzikometsa kwa anzawo kapena kwa munthu wina amene si mwamuna kapena mkazi mnzawo.​—Miyambo 13:20.

3 Ambiri amadzazindikira mochedwa kuti kudzisunga n’kofunika kwambiri. Amakhala atataya chinthu chofunika ndipo nthaŵi zambiri izi zimakhala zoopsa kwambiri. Monga momwe Baibulo limanenera, zotsatira za chiwerewere zingafanane ndi ziphe, ‘zowawa ngati chivumulo.’ (Miyambo 5:3, 4) Malinga n’kuipa kwa makhalidwe masiku ano, kodi mungatani kuti muziona kudzisunga kukhala kofunika kwambiri komanso kuti mupitirize kukhala wodzisunga? Tiona njira zitatu zosasiyana kwenikweni zomwe tingachitire zimenezi.

Tchinjirizani Mtima Wanu

4. Kodi mtima wophiphiritsira n’chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani tiyenera kuutchinjiriza?

4 Chofunika kwambiri kuti mukhale wodzisunga ndicho kutchinjiriza mtima. Baibulo limati: “Tchinjiriza mtima wako koposa zonse uzisunga; pakuti magwero a moyo atulukamo.” (Miyambo 4:23) Kodi ‘mtima wanu,’ akuunenawu n’chiyani? Sikuti ndi mtima weniweni. Akunena za mtima wophiphiritsira. Ukuimira umunthu wanu wamkati, kuphatikizapo malingaliro ndiponso zochita zanu. Baibulo limati: ‘Muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, ndi mphamvu yanu yonse.’ (Deuteronomo 6:5) Yesu anatchula lamulo limeneli monga lalikulu pa onse. (Marko 12:29, 30) N’zoonekeratu kuti mtima wathu umenewu ndi wamtengo wapatali kwambiri. Ndi wofunikadi kuutchinjiriza.

5. Kodi mtima ungakhale motani chipangizo chofunika komanso choopsa nthaŵi imodzimodziyo?

5 Komabe, Baibulo limanenanso kuti “mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika.” (Yeremiya 17:9) Kodi mtima ungakhale bwanji wonyenga, yomwe ndi ngozi yaikulu kwa ife? Chabwino, galimoto mwachitsanzo, imathandiza kwambiri, mwinanso kupulumutsa moyo kumene pamavuto adzidzidzi. Koma ngati woyendetsa sakuiwongolera nthaŵi zonse, n’zosavuta kuti galimoto yomweyo iphe anthu. N’chimodzimodzinso ndi mtima. Ngati simuutchinjiriza, mungathe kumangotsatira chilichonse chimene mukulakalaka, ndipo mungagwe nazo m’mavuto aakulu. Mawu a Mulungu amati: “Wokhulupirira mtima wakewake ali wopusa; koma woyenda mwanzeru adzapulumuka.” (Miyambo 28:26) Zoonadi, mungayende mwanzeru ndi kupeŵa mavuto ngati mugwiritsa ntchito Mawu a Mulungu kukutsogolerani, monganso momwe mungaonere mapu a msewu musanayambe ulendo.​—Salmo 119:105.

6, 7. (a) Kodi chiyero n’chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani chili chofunika kwa atumiki a Yehova? (b) Kodi timadziŵa bwanji kuti anthu opanda ungwiro angathe kusonyeza chiyero cha Yehova?

6 Mtima wathu sudzatitsogolera wokha kuti tikhale wodzisunga. Ifeyo tiyenera kuutsogolera. Njira imodzi yochitira zimenezi ndiyo kusinkhasinkha phindu lenileni la kudzisunga. Khalidwe limeneli limagwirizana kwambiri ndi chiyero, khalidwe losonyeza kupanda litsiro, kupatuka pa uchimo. Chiyero ndi khalidwe lapadera kwambiri moti ndi khalidwe lalikulu la Yehova Mulungu. Mavesi mazanamazana a m’Baibulo amanena kuti Yehova ndi woyera. Ndipotu Baibulo limati “Chiyero n’cha Yehova.” (Eksodo 28:36, NW) Koma kodi khalidwe lapamwamba limeneli likutikhudza bwanji ifeyo anthu opanda ungwiro?

7 M’Mawu ake, Yehova akutiuza kuti: “Muzikhala oyera mtima, pakuti Ine ndine woyera mtima.” (1 Petro 1:16) Inde, tingathe kutsanzira chiyero cha Yehova; tingathe kukhala oyera pamaso pake, ndipo tingathe kukhalabe odzisunga. Motero tikamapeŵa kuchita zinthu zodetsa, ndiye kuti tikufunafuna mwayi wapadera kwambiri, mwayi wosonyeza khalidwe losangalatsa la Mulungu Wamkulukulu! (Aefeso 5:1) Tisaganize kuti sitingathe kuchita zimenezi, chifukwa chakuti Yehova ndi Mbuye wanzeru ndiponso amafuna kuti tichite zinthu zomwe tingathe kuchita, osati zinthu zomwe sitingazithe. (Salmo 103:13, 14; Yakobo 3:17) N’zoona kuti kukhala wodzisunga ndiponso woyera mwauzimu kumafuna khama. Komabe, mtumwi Paulo anati, ‘kuona mtima ndi kuyera mtima zili kwa Kristu.’ (2 Akorinto 11:3) Kodi sitiyenera kuyesetsa kukhala odzisunga chifukwa cha Kristu ndi Atate wake? Ndipotu iwo asonyeza kuti amatikonda kwambiri kuposa zomwe tingathe kuwabwezera. (Yohane 3:16; 15:13) Ndi mwayi wathu woti tisonyeze kuyamikira mwa kukhala amakhalidwe oyera ndi abwino. Tikakhala ndi malingaliro ameneŵa pankhani yodzisunga, tidzaona kuti khalidweli n’lofunika, ndipo tidzatchinjiriza mtima wathu.

8. (a) Kodi tingadyetse motani mtima wathu wophiphiritsira? (b) Kodi zolankhula zathu zingasonyeze chiyani za ifeyo?

8 Timatchinjirizanso mtima wathu ndi zimene timadya. Tifunika kuti nthaŵi zonse tizidyetsa maganizo ndiponso mtima wathu chakudya chabwino chauzimu, komanso tiziikira mtima kwambiri pa uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. (Akolose 3:2) Ngakhalenso zolankhula zathu zifunika kusonyeza zimenezo. Ngati timadziŵika monga okonda kulankhula nkhani za zinthu wamba, nkhani zoipa, timasonyeza kenakake ka mmene mtima wathu ulili. (Luka 6:45) M’malo mwake, tiyeni tidziŵike monga olankhula zinthu zauzimu ndiponso zolimbikitsa. (Aefeso 5:3) Kuti titchinjirize mtima wathu, pali ngozi zina zikuluzikulu zofunika kuti tipeŵe. Tiyeni tione ziŵiri mwa ngozi zimenezi.

Thaŵani Dama

9-11. (a) N’chifukwa chiyani n’zosavuta kuti anthu amene amanyalanyaza malangizo a pa 1 Akorinto 6:18 achite chiwerewere? Perekani chitsanzo. (b) Ngati tikuthaŵa dama, kodi timapeŵa chiyani? (c) Kodi munthu wokhulupirika Yobu anatiikira chitsanzo chabwino chiti?

9 Yehova anauzira mtumwi Paulo kulemba malangizo amene athandiza anthu ambiri kutchinjiriza mtima wawo ndiponso kukhala odzisunga. Paulo anati: “Thaŵani dama.” (1 Akorinto 6:18) Onani kuti iye sanangonena kuti, “Peŵani dama.” Akristu afunika kuchita zambiri. Afunika kuthaŵa khalidwe loipali, monga momwe angathaŵire pamene moyo wawo uli pangozi. Tikanyalanyaza malangizo ameneŵa, timakulitsa mpata wochita chiwerewere n’kusiya kuyanjidwa ndi Mulungu.

10 Taonani chitsanzo ichi: Mayi wasambitsa ndi kuveka mwana wake wamng’ono pokonzekera mwambo wofunika kwambiri. Mwanayo akupempha kuti abakaseŵera panja poyembekezera kuti banjalo linyamuke, ndipo mayiwo akumuuza kuti amulola ngati atsatira chinthu chimodzi. Mayiwo akuti: “Osakayandikira pachithaphwipo. Ukangoda, uona.” Koma patatha nthaŵi pang’ono, mayiwo akuona mwana uja ali m’mphepete mwenimweni mwa chithaphwi chija. Panthaŵiyi mwanayo sanade. Komabe akunyalanyaza chenjezo la mayiwo loti asayandikire pachithaphwipo, ndipo nthaŵi ina iliyonse mwanayo akhoza kuloŵa m’mavuto. (Miyambo 22:15) Ndi mmenenso achinyamata ndiponso achikulire ambiri anzeru zawo amalakwira. N’chifukwa chiyani tikutero?

11 Masiku ano pamene anthu ambiri akukonda kuchita “zilakolako zamanyazi,” kwadza bizinesi ya zinthu za makhalidwe oipa achiwerewere. (Aroma 1:26, 27) Mliri wa zithunzi zolaula wafalikira m’magazini, m’mabuku, m’mavidiyo, ndiponso pa Intaneti. N’zoonekeratu kuti amene akuika zithunzi zimenezo m’maganizo mwawo sakuthaŵa dama. Akuseŵera nalo, ali pangozi yaikulu, akunyalanyaza chenjezo la Baibulo. M’malo motchinjiriza mtima, akuuwononga ndi zithunzi zomwe zingatenge nthaŵi yaitali akuzikumbukira. (Miyambo 6:27) Tiyeni titengere phunziro kwa Yobu wokhulupirika amene anachita pangano ndi maso ake, kuti asaone zinthu zomwe zingam’kope kuti achite choipa. (Yobu 31:1) Chitsanzotu chofunika kuchitsatira chimenechi!

12. Kodi Akristu amene ali pachibwenzi ‘angathaŵe dama’ motani pa nthaŵi ya chibwenziyo?

12 ‘Kuthaŵa dama’ n’kofunika makamaka panthaŵi ya chibwenzi. Imeneyi iyenera kukhala nthaŵi yosangalatsa ndiponso yoyembekezera ndi chikhulupiriro chonse zinthu zosiyanasiyana zabwino, koma achinyamata ena amawononga nthaŵiyi mwa kuchita chiwerewere. Pochita zimenezi, iwo amalepheretsana kuika maziko enieni a ukwati wabwino, omwe ndi kugwirizana chifukwa cha chikondi chodzimana, kudziletsa, ndiponso kumvera Yehova Mulungu. Banja lina lachikristu linachita chiwerewere panthaŵi ya chibwenzi chawo. Atakwatirana, mkazi ananena kuti chikumbumtima chake chinkam’pweteka kwambiri, kufika mpaka pom’lepheretsa kusangalala patsiku la ukwati wake. Anati: “Ndakhala ndikupempha kambirimbiri kuti Yehova andikhululukire, koma ngakhale kuti patha zaka zisanu ndi ziŵiri kuchoka panthaŵiyo, chikumbumtima changa chikundivutabe.” N’zofunika kwambiri kuti amene achita machimo otereŵa apemphe thandizo kwa akulu achikristu. (Yakobo 5:14, 15) Komabe, Akristu ambiri amene ali pachibwenzi amakhala mosamala ndipo amapeŵa mavuto ngati ameneŵa panthaŵi ya chibwenziyo. (Miyambo 22:3) Amakhala ndi malire posonyezana chikondi. Pamene ali pamodzi, amakhala ndi wowaperekeza ndipo amaonetsetsa kuti asakhale aŵiriŵiri pamalo obisika.

13. N’chifukwa chiyani Akristu sayenera kuchita chibwenzi ndi munthu amene satumikira Yehova?

13 Akristu omwe amapanga zibwenzi ndi anthu amene satumikira Yehova mosakayikira amakumana ndi mavuto aakulu. Mwachitsanzo, kodi mungadziphatike bwanji kwa munthu amene sakonda Yehova Mulungu? Ndi bwino kuti Akristu aziloŵa m’goli ndi anthu okhawo okonda Yehova ndiponso olemekeza miyezo yake ya kudzisunga. Mawu a Mulungu amatiuza kuti: “Musakhale omangidwa m’goli ndi osakhulupira osiyana; pakuti chilungamo chigaŵana bwanji ndi chosalungama? Kapena kuunika kuyanjana bwanji ndi mdima?”​—2 Akorinto 6:14.

14, 15. (a) Kodi ndi malingaliro olakwika ati amene anthu ena ali nawo pankhani ya tanthauzo la “dama”? (b) Kodi “dama” limaphatikizapo zochitika ngati ziti, ndipo Akristu ‘angathaŵe dama’ motani?

14 Kudziŵa zinthu n’kofunikanso kwambiri. Sitingathaŵe dama bwinobwino ngati sitidziŵa kuti damalo n’chiyani kwenikweni. Ena masiku ano ali ndi malingaliro olakwika pankhani ya tanthauzo la “dama.” Amaganiza kuti angakhutiritse chilakolako chawo cha kugonana popanda kukwatira, malinga ngati akupeŵa kugonana. Ngakhalenso zipatala zina zodziŵika bwino zomwe zikulimbana ndi kuchepetsa chiŵerengero cha mimba zapathengo za ana aang’ono zimalimbikitsa achinyamata kugonana m’njira zina zimene sangatengere mimba. N’zomvetsa chisoni kuti malangizo ameneŵa ndi oipa kwambiri. Kupeŵa mimba zapathengo ndi kwina ndipo kukhala wodzisunga n’kwinanso. Ndipotu mawu oti “dama” samangotanthauza zokhazi.

15 Mawu achigiriki akuti por·neiʹa, omwe atembenuzidwa kuti “dama,” amatanthauza zinthu zambiri. Mawuŵa amanena za kugonana kwa anthu osakwatirana ndiponso amanena za kugwiritsa ntchito mpheto molakwika. Por·neiʹa amaphatikizapo zochita monga kugonana mkamwa, kugonana kumatako, komanso kuseŵeretsa mpheto za munthu wina, zomwe zimakonda kuchitika m’nyumba za mahule. Anthu amene amaganiza kuti kuchita zimenezi si “dama” akungodzinyenga ndipo akodwa mu umodzi wa misampha ya Satana. (2 Timoteo 2:26) Komanso, kukhala wodzisunga kumatanthauza zambiri osati kungopeŵa kalikonse kokhudza dama. Kuti ‘tithaŵe dama,’ tiyenera kupeŵa kugonana kulikonse kodetsedwa ndiponso khalidwe lotayirira lomwe lingatichititse tchimo la por·neiʹa. (Aefeso 4:19) Mwa kuchita zimenezi timakhala odzisunga.

Peŵani Mavuto a Kukopana

16. Kodi ndani ayenera kuchita zinthu zosonyezana chikondi, malinga ndi chitsanzo cha m’Malemba chiti?

16 Ngati tikufuna kukhalabe wodzisunga, vuto lina lomwe tifunika kuchenjera nalo ndilo kukopana. Ena anganene kuti kukopana ndi kungosangalala pakati pa mwamuna ndi mkazi ndipo kulibe vuto lililonse. N’zoona kuti pali nthaŵi ndiponso malo osonyezerana chikondi. Anthu anaona Isake ndi Rebeka ‘alin’kuseka’ kapena kuti atakumbatirana, ndipo kwa owaona zinali zodziŵikiratu kuti iwo sikuti anali mchimwene ndi mlongo wake ayi. (Genesis 26:7-9) Ili linali banja. Panali poyenera kuti achite zinthu zosonyezana chikondi. Kukopana ndi nkhani ina.

17. Kodi kukopana n’kutani, ndipo vutoli lingachepetsedwe motani?

17 Kukopana tingakufotokoze motere: kuonetsa chikondi chosonyeza kum’funa munthu popanda cholinga chenicheni chomanga naye banja. Anthu analengedwa modabwitsa kwambiri, motero n’zosakayikitsa kuti pali njira zambiri zokopera ena, ndipo zina n’zovuta kuzitulukira. (Miyambo 30:18, 19) Motero kuika malamulo okhwima sikungathandize kwenikweni. M’malo mwake, m’pofunika kuchita zinthu zina zoposa kutsatira malamulo, ndipo izi ndizo kudzipenda moona mtima ndiponso kuyesetsa kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo.

18. Kodi ena amakopa anzawo chifukwa chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani kukopana kuli koopsa?

18 Titadzipenda moona mtima, ambirife tingavomereze kuti munthu wina yemwe si mwamuna kapena mkazi mnzathu akakhala ndi malingaliro achikondi kwa ife timamva bwino. Umo ndi mmene anthufe anatilengera. Koma kodi timakopa ena n’cholinga choti timve kuti ndife ofunika kapena kupangitsa wina kumva choncho? Ngati ndi choncho, kodi talingalirapo mmene zochita zathuzo zimapwetekera? Mwachitsanzo, Miyambo 13:12 imati: “Chiyembekezo chozengereza chidwalitsa mtima.” Ngati tikopana mwadala ndi munthu wina, ndiye kuti sitikudziŵa mmene munthuyo akumvera. Iye angathe kuyamba kukhala ndi chiyembekezo choti pakhala chibwenzi ndipo kenako tidzamanga naye banja. Zingakhale zopweteka kwambiri kuti agwire fuwa lamoto. (Miyambo 18:14) Kuseŵeretsa malingaliro a wina ndi nkhanza yaikulu.

19. Kodi kukopana kungawononge motani mabanja achikristu?

19 M’pofunika kwambiri kuti tipeŵe kukopana ndi anthu a m’mabanja. Kuyambitsa maganizo achikondi mwa munthu wapabanja, kapena kuti munthu wapabanja achite zimenezi kwa munthu amene si mwamuna kapena mkazi wake, n’kulakwa. N’zomvetsa chisoni kuti Akristu ena akhala ndi maganizo opotoka akuti sikulakwa kuyambitsa maganizo achikondi mwa munthu wina amene si mwamuna kapena mkazi wawo. Ena amauza munthu amene amati ndi mnzawoyo nkhani zakukhosi kwawo, ndipo mwinanso kumuululira zinsinsi zomwe sauza mwamuna kapena mkazi wawo. Izi zimapangitsa kuti maganizo achikondi pakati pa aŵiriwo akule ndipo amayamba kukhala ndi maganizo odalirana moti zingapeputse banja ngakhalenso kuliwononga kumene. Akristu omwe ali pabanja afunika kukumbukira chenjezo la Yesu ponena za chigololo, kuti chigololo chimayambira mu mtima. (Mateyu 5:28) Motero, tiyeni titchinjirize mtima ndipo tipeŵe zinthu zomwe zingatichititse kugwa m’mavuto ngati ameneŵa.

20. Kodi tiyenera kutsimikiza mtima kukuona motani kudzisunga?

20 N’zoona kuti sichinthu chamaseŵera kukhala wodzisunga m’dziko lopanda khalidweli. Koma kumbukirani kuti kukhala wodzisunga n’kosavuta kusiyana ndi kuti munthu uchite kuyambiranso kudzisunga utaphonyetsa penapake. Inde, Yehova akhoza ‘kukhululukira koposa’ ndipo angathe kuyeretsa anthu amene alapadi machimo awo. (Yesaya 55:7) Komabe Yehova sateteza anthu ochita chiwerewere ku zotsatira za zochita zawozo. Zotsatira zake zingatenge zaka zambiri, mwinanso moyo wonse. (2 Samueli 12:9-12) Mwanjira iliyonseyo, khalani wodzisunga mwa kutchinjiriza mtima wanu. Onani kuyera ndi kudzisunga kwanu pamaso pa Yehova Mulungu monga chinthu chamtengo wapatali, ndipo musalolere kuchitaya!

Kodi Mungayankhe Motani?

• Kodi kudzisunga n’kutani, ndipo n’chifukwa chiyani kuli kofunika?

• Kodi mtima wathu tingautchinjirize motani?

• Kodi kuthaŵa dama kumaphatikizapo kuchitanji?

• N’chifukwa chiyani tiyenera kupeŵa kukopana?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 11]

Galimoto ingakhale yoopsa ngati sikuwongoleredwa bwino

[Zithunzi patsamba 12]

Kodi chingachitike n’chiyani ngati tinyalanyaza machenjezo?

[Chithunzi patsamba 13]

Kudzisunga pachibwenzi kumasangalatsa ndiponso kumalemekeza Mulungu