Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Chipembedzo Ndicho Chikuchititsa Mavuto a Anthu?

Kodi Chipembedzo Ndicho Chikuchititsa Mavuto a Anthu?

Kodi Chipembedzo Ndicho Chikuchititsa Mavuto a Anthu?

“CHIPEMBEDZO chikakhala kuti sichikulimbikitsa kukangana chimakhala chikuchititsa dzanzi chikumbumtima cha anthu ndipo chimapangitsa anthu kuganiza zinthu zosachitika pofuna kudzisangalatsa akakhala pamavuto. . . . Chimapangitsanso anthu kuganiza moperewera, kukhulupirira malodza, kudana kwambiri ndi anzawo ndiponso kukhala mwamantha.” Munthu amene kale anali mmishonale watchalitchi cha Methodist amene analemba mawu ameneŵa anatinso: “Zimenezi n’zoona. Pali chipembedzo choipa ndi chabwino.”​—Start Your Own Religion.

Anthu ena anganene kuti, ‘zimenezo si zoona.’ Komabe, ndani sangavomereze zimenezi poona zimene zachitika m’mbiri? Mbali yaikulu, chipembedzo chomwe chimatanthauza “utumiki ndi kulambira Mulungu kapena mizimu,” chili ndi mbiri yoipa zedi. Chiyenera kutitsegula m’maso ndi kutilimbikitsa. Koma kaŵirikaŵiri zimene chimachita n’kuyambitsa mikangano, tsankho, ndi udani. N’chifukwa chiyani zili chonchi?

“Mngelo wa Kuunika” Wosokeretsa

Malinga ndi Baibulo, yankho lake n’losavuta zedi. Podzionetsa ngati “mngelo wa kuunika,” Satana Mdyerekezi wanyenga anthu ambiri kutsatira zimene iye amaphunzitsa m’malo motsatira zimene Mulungu amaphunzitsa. (2 Akorinto 11:14) Mtumwi Yohane anasonyeza kuti Satana ndi wamphamvu kwambiri moti ‘dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.’ (1 Yohane 5:19) Yohane ankadziŵa kuti Satana anali ‘kunyenga dziko lonse.’​—Chivumbulutso 12:9.

Kodi zotsatira za zimenezi n’zotani? Satana wabweretsa magulu achipembedzo amene amaoneka ngati oyera. Iwo ali ndi “maonekedwe achipembedzo,” koma mmene iwo alili zimadziŵika ndi zipatso zoipa zimene amatulutsa. (2 Timoteo 3:5; Mateyu 7:15-20) M’malo mothandiza kuthetsa mavuto a anthu, kwenikweni chipembedzo chakhala mbali ya vutolo.

Musafulumire kunena kuti mfundo imeneyi ndi yonama kapena n’kusaganiza bwino. Kumbukirani kuti vuto la chinyengo n’lakuti wonamizidwayo sadziŵa kuti akunamizidwa. Mtumwi Paulo anapereka chitsanzo cha zimenezi pamene analemba kuti: “Zimene amitundu apereka nsembe azipereka kwa ziwanda [osati kwa Mulungu, NW].” (1 Akorinto 10:20) Anthu amenewo mosakayikira anadabwa kumva kuti anali kulambira ziwanda. Anali kuganiza kuti akulambira mulungu kapena kuti milungu inayake yabwino. Komabe, kwenikweni anali atanamizidwa ndi ‘mizimu yoipa yakumwamba,’ imene imathandiza Satana pantchito yake yosokeretsa anthu.​—Aefeso 6:12.

Mwachitsanzo, tiyeni tione zimene Satana anachita kuti athe kunamiza ndi kusokeretsa anthu ambiri amene anali kudzitcha kuti Akristu amene ananyalanyaza zimene mtumwi Yohane anachenjeza ponena za mphamvu yoipa ya ziwanda.​—1 Akorinto 10:12.

Zimene Yesu Anaphunzitsa Zinali Zochokera kwa Mulungu

Yesu Kristu anati: “Chiphunzitso changa sichili changa, koma cha Iye amene anandituma Ine.” (Yohane 7:16) Inde, zimene anaphunzitsa zinali zochokera kwa Mulungu Wamphamvuyonse. Choncho, zimene Yesu anaphunzitsa zinali zolimbikitsa kwambiri komanso zothandiza kwa anthu amene anamvetsera iye akuphunzitsa. ‘Sizinkachititsa dzanzi chikumbumtima cha anthu kapena kupangitsa anthu kuganiza zinthu zosachitika pofuna kudzisangalatsa akakhala pamavuto.’ Komano, zimene Yesu anaphunzitsa zinawamasula anthu ku ziphunzitso zolakwika za chipembedzo ndi nzeru za anthu za dziko limene linali ‘lodetsedwa m’nzeru’ chifukwa cha chinyengo cha Mdyerekezi.​—Aefeso 4:18; Mateyu 15:14; Yohane 8:31, 32.

Akristu oona anali kudziŵika osati chifukwa chodzinenerera kuti anali opembedza kwambiri, koma mwa chikhulupiriro chimene chinasonyeza makhalidwe abwino amene amabwera ndi mzimu woyera wa Mulungu. (Agalatiya 5:22, 23; Yakobo 1:22; 2:26) Khalidwe lapadera kwambiri pa makhalidwe ameneŵa ndiponso chizindikiro cha Chikristu chenicheni ndi khalidwe lapamwamba la chikondi.​—Yohane 13:34, 35.

Komabe, onani mfundo yofunika kwambiri iyi: Yesu ndi atumwi ake sanayembekezere kuti mpingo wachikristu ukakhalabe ngati mmene unalili pamene unali kukhazikitsidwa. Iwo anadziŵa kuti padzabwera mpatuko ndipo chipembedzo choona chikabisika kwa kanthaŵi.

Chipembedzo Choona Chinabisika kwa Kanthaŵi

Mu fanizo la tirigu ndi namsongole, Yesu ananeneratu kuti padzakhala kanthaŵi kena pamene chipembedzo choona chidzangotsala pang’onong’ono kubisikiratu. Ŵerengani nokha nkhaniyi pa Mateyu 13:24-30, 36-43. Yesu anafesa tirigu, “mbewu zabwino,” zimene zinaimira ophunzira ake okhulupirika amene anali kudzapanga mpingo wachikristu woyambirira. Iye anachenjeza kuti “mdani,” Satana Mdyerekezi, kenako adzafesa m’munda wa tirigu uja “namsongole”​—anthu odzinenera kuti amatsatira Yesu Kristu koma okana zimene iye anaphunzitsa.

Patapita nthaŵi pang’ono atumwi a Yesu atatha kufa, panapezeka anthu amene anasonyeza umboni wakuti anali “namsongole,” amene anali kukonda zinthu zopotoka zimene anthu anali kuphunzitsa kuposa “mawu a Yehova.” (Yeremiya 8:8, 9; Machitidwe 20:29, 30) Chotsatira chake chinali chakuti, padziko lapansi panakhala Chikristu chosiyana ndi choyambirira komanso chonyenga. Chinali kulamulidwa ndi amene Baibulo limatcha kuti ‘wosayeruzika,’​—gulu loipa la atsogoleri achipembedzo limene linali lodzaza ndi “chinyengo chonse cha chosalungama.” (2 Atesalonika 2:6-10) Yesu ananeneratu kuti zimenezi zikasintha “m’chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano.” Akristu onga tirigu adzasonkhanitsidwa pamodzi mogwirizana ndipo “namsongole” pamapeto pake adzawonongedwa.

Chikristu chonyenga chimenechi n’chimene chili ndi mlandu wa “zochitika za nkhanza kwambiri zimene zachitika kwa zaka mazana ambiri” ndiponso mdima wauzimu umene unakuta Matchalitchi Achikristu zaka mazana ambiri kuyambira panthaŵiyo. Pooneratu zimenezi ndiponso zinthu zoipa ndi zachiwawa zimene zachitika m’dzina la chipembedzo kuyambira pamene Chikristu chonyenga chinayamba, mtumwi Petro ananena zoona kuti “chifukwa cha iwo [odzitcha Akristu] njira ya choonadi idzanenedwa zamwano.”​—2 Petro 2:1, 2.

“Chipembedzo Chophunzitsa Ukali ndi Udani”

Ndithudi si Matchalitchi Achikristu okha amene apangitsa kuti chipembedzo chikhale ndi mbiri yoipa. Mwachitsanzo, taganizirani timagulu toumirira kwambiri miyambo yachipembedzo “ta anthu achiwawa odziona ngati opembedza kwambiri.” Karen Armstrong yemwe anali mviligo anati timagulu timeneti timayamba chifukwa cha “miyambo ikuluikulu yachipembedzo.” Malinga ndi Armstrong, chinthu chofunika kwambiri ku chipembedzo chilichonse n’chakuti chiyenera kuthandiza anthu “kusonyeza chifundo.” Kodi timagulu toumirira kwambiri miyambo yachipembedzo tili ndi mbiri yotani pambali imeneyi? Iye anati: “Timagulu toumirira miyambo, kaya ta Chiyuda, Chikristu, kapena Chisilamu, timalephera kukwaniritsa chinthu chofunika kwambiri chimenechi ngati tikhala chipembedzo chophunzitsa ukali ndi udani.” (The Battle for God​—Fundamentalism in Judaism, Christianity and Islam) Koma kodi ndi zipembedzo zokha za anthu “oumirira kwambiri miyambo yachipembedzo” zimene zalephera kuchita zimenezi ndi kukhala “chipembedzo chophunzitsa ukali ndi chidani”? Zochitika m’mbiri zikusonyeza kuti sichoncho ayi.

Kwenikweni, Satana wamanga ufumu wadziko lonse wa chipembedzo chonyenga, chodziŵika ndi ukali, udani, ndiponso pafupifupi kupha anthu kosalekeza. Baibulo limatcha ufumu umenewu ‘Babulo Wamkulu, amayi . . . wa zonyansitsa za dziko,’ ndipo umafotokozedwa ngati mkazi wachigololo wokwera pamsana pa dongosolo la ndale longa chilombo. N’zochititsa chidwi kuti akuimbidwa mlandu wa “mwazi wa . . . onse amene anaphedwa padziko.”​—Chivumbulutso 17:4-6; 18:24.

Si Onse Amene Anamizidwa

Komabe, mbiri ikusonyeza kuti si onse amene anamizidwa. Ngakhale m’nthaŵi yamdima wandiweyani, Melvyn Bragg anati, “anthu ambiri oyamikika anachita zinthu zabwino pamene ochuluka amene anali kukhala nawo pafupi anali kuchita zoipa.” Akristu enieni anapitiriza ‘kulambira [Mulungu] mumzimu ndi m’choonadi.’ (Yohane 4:21-24) Iwo anasiyana ndi dongosolo la chipembedzo la padziko lonse limene lachita uhule monga “loikira kumbuyo nkhondo.” Iwo anakana kuloŵa mu mgwirizano wa Tchalitchi ndi Boma umene malinga ndi mbiri zikusonyeza kuti “kwenikweni anayambitsa ndi Satana osati Yesu wa ku Nazareti.”​—Two Thousand Years​—The Second Millennium: From Medieval Christendom to Global Christianity.

Chaposachedwapa, Mboni za Yehova zadziŵika kuti zimalimbikitsa anthu kuchita zabwino. Kuti zisadetsedwe ndi chipembedzo chonyenga, zikhulupiriro ndiponso zochita zawo zonse n’zochokera kwambiri m’Mawu ouziridwa a Mulungu, Baibulo. (2 Timoteo 3:16, 17) Ndipo monga Akristu a m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino, atsatira lamulo la Yesu lakuti ‘asakhale a dziko lapansi.’ (Yohane 15:17-19; 17:14-16) Mwachitsanzo panthaŵi ya ulamuliro wa Anazi ku Germany, iwo anakana kuphwanya mfundo za makhalidwe abwino zachikristu ndipo pachifukwa chimenechi anali osavomerezedwa malinga ndi mfundo za Anazi. Hitler anali kuwada chifukwa cha zimenezi. Buku lina lophunziridwa kusukulu limati: “Mboni za Yehova . . . zinatsatira zimene Baibulo limaphunzitsa zoti siziyenera kutenga zida za nkhondo pa chifukwa chilichonse. Choncho zinakana kukhala asilikali kapena kuchita ntchito iliyonse yokhudzana ndi Anazi. Pobwezera, gulu la apolisi la SS linkamanga mabanja athunthu a Mboni za Yehova.” (Germany​—1918-45) Inde, Mboni za Yehova mazana ambiri ku Germany zinafa chifukwa chozunzidwa ndi Anazi.

N’zoona kuti anthu ena olimba mtima azipembedzo zosiyanasiyana anavutikanso chifukwa cha zimene anali kukhulupirira. Koma Mboni za Yehova zinachita zimenezi monga gulu lachipembedzo logwirizana. Ndithudi ambiri a Mboni za Yehova anagwiritsitsa mfundo yofunika ya m’Malemba yakuti: ‘Mverani Mulungu koposa anthu.’​—Machitidwe 5:29; Marko 12:17.

Chimene Chikuchititsa Mavuto a Anthu

Choncho si zoona kwenikweni kuti chipembedzo chikuchititsa mavuto onse a anthu. Chipembedzo chonyenga n’chimene chikuchititsa. Komabe, Mulungu akufuna kuti posachedwapa achotse zipembedzo zonse zonyenga. (Chivumbulutso 17:16, 17; 18:21) Aliyense amene amakonda chilungamo akumulamula kuti: “Tulukani m’menemo [kutanthauza, m’Babulo Wamkulu, ufumu wadziko lonse wa chipembedzo chonyenga], anthu anga; kuti mungayanjane ndi machimo ake, ndi kuti mungalandireko ya miliri yake; pakuti machimo ake anaunjikizana kufikira m’Mwamba, ndipo Mulungu anakumbuka zosalungama zake.” (Chivumbulutso 18:4, 5) Inde, Mulungu mwiniyo ndi wokhumudwa kwambiri ndi chipembedzo chimene ‘chimalimbikitsa kukangana, chimachititsa dzanzi chikumbumtima cha anthu, chimapangitsa anthu kuganiza zinthu zosachitika pofuna kudzisangalatsa akakhala pamavuto, ndipo chimapangitsa anthu kuganiza moperewera, kukhulupirira malodza, kudana kwambiri ndi anzawo ndiponso kukhala mwamantha.’

Pakalipano, Mulungu akusonkhanitsira anthu okonda choonadi m’chipembedzo choona. Ndi chipembedzo chimene chimatsatira mfundo za makhalidwe abwino ndiponso ziphunzitso za Mlengi wachikondi, wachilungamo, ndiponso wachifundo. (Mika 4:1, 2; Zefaniya 3:8, 9; Mateyu 13:30) Mukhoza kukhala nawo m’gululi. Ngati mukufuna kudziŵa zambiri pankhani ya mmene mungachidziŵire chipembedzo choona, masukani kulembera kalata amene amafalitsa magazini ino kapena funsani aliyense wa Mboni za Yehova kuti akuthandizeni.

[Chithunzi patsamba 7]

Anthu ochoka kosiyanasiyana apeza chimwemwe m’chipembedzo choona