Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kusonkhana pa “Mchombo wa Dziko Lapansi”

Kusonkhana pa “Mchombo wa Dziko Lapansi”

Kusonkhana pa “Mchombo wa Dziko Lapansi”

Kodi munamvapo mawu akuti “Te Pito o Te Henua”? Mawuŵa m’chinenero choyambirira chotchedwa Rapa Nui cha pa Chilumba cha Easter, amatanthauza “Mchombo wa Dziko Lapansi.” Kodi n’chiyani chinapangitsa msonkhano umene unachitika kumeneku kukhala wapadera?

CHILI kutali kwambiri ndi madera ena, chodabwitsa, chapadera kwambiri. Aŵa ndi ena mwa mawu amene amagwiritsidwa ntchito ponena za Chilumba cha Easter, kapena kuti Rapa Nui monga mmene anthu akumeneko amatchulira. Ndi dera lakutalidi kwambiri panyanja yamchere ya South Pacific, lopezeka pamtunda wa makilomita 3,790 kuchokera ku mzinda wa Santiago, ku Chile. Chilumbachi chinakhala chigawo cha Chile pa September 9, 1888.

Chilumba cha makona atatu chimenechi kwenikweni chinapangidwa ndi malo atatu omwe ankatuluka chiphalaphala ndipo chili ndi malo okwana masikweya kilomita 166. Ndipotu, monga momwe zilili zilumba zambiri za panyanja ya Pacific, chilumbachi ndi nsonga za mapiri akuluakulu apansi pamadzi. Chilumba chonsecho amati ndi malo a zachilengedwe ofunika kwambiri. Mosakayikira chilumbachi n’chodziŵika bwino chifukwa cha ziboliboli zake zodabwitsa kwambiri za miyala, zotchedwa moai. *

Kuwonjezera pa kukhala malo okongola ndiponso a zinthu zakale, Chilumba cha Easter chili ndi zakudya zokoma zosiyanasiyana. Amalimako zipatso monga nanazi, mapeyala, mapapaya, ndiponso mitundu isanu ndi inayi ya nthochi. Ndipo nyanja ili ndi nsomba zamitundu yambiri zedi ndiponso mumapezeka zakudya zina za m’madzi.

Ku Chilumba cha Easter si kotentha kwambiri komanso si kozizira kwambiri, kumagwa mvula ndiponso kumakhala utawaleza nthaŵi zonse, zimene zimapangitsa kuti alendo obwera pachilumbachi azipuma mpweya wabwino ndiponso kuona zinthu zochititsa chidwi. Pakalipano pachilumbachi pali anthu pafupifupi 3,800. Anthu ameneŵa ndi mbadwa za anthu oyambirira kudzakhala pachilumbachi, palinso azungu, anthu a ku Chile, ndi anthu ena. Anthu ambiri a ku Ulaya ndi ku Asia amabwera pachilumbachi, zimene zimapangitsa ntchito yokopa alendo kukhala njira yaikulu yopezera ndalama pachilumbachi.

Mbewu za Ufumu Zifesedwa Koyamba

Buku la 1982 Yearbook of Jehovah’s Witnesses linati: “Kwakanthaŵi ndithu tinali ndi wofalitsa mmodzi yekha pa Chilumba cha Easter. Mlongoyu anali kuthandizidwa mwauzimu polemberana makalata ndi mlongo wina amene anali mmishonale panthambi [ya ku Chile]. Ngakhale kuti tsopano anabwerera ku Chile, pachilumbachi tili ndi anthu amene analembetsa kuti azilandira Nsanja ya Olonda. Mosayembekezera, mu April 1980 tinalandira telefoni yochokera kutali kwambiri ya munthu amene ankafuna kudziŵa tsiku la Chikumbutso. Ndiyeno chaka chomwecho banja lina la ku Valparaiso linasamukira pachilumbachi, ndipo lakhala likuphunzira Baibulo ndi anthu achidwi. Mu April chaka cha 1981 anachita msonkhano wa Chikumbutso woyamba pachilumbachi ndipo panali anthu 13. Tili osangalala kwambiri kuti ‘uthenga wabwino’ ukufalikira kudera lakutali limeneli!”

Ndiyeno pa January 30, 1991, nthambi inatumiza pachilumbachi Dario ndi Winny Fernandez, banja limene linali kuchita upainiya wapadera. Mbale Fernandez anati: “Titayenda pandege kwa maola asanu tinafika padera limene lili kwalokha padziko lapansi, kwa anthu achikhalidwe chodabwitsa.” Nthaŵi yomweyo analinganiza misonkhano ndi ntchito yolalikira mothandizidwa ndi mbale wakomweko ndiponso mlongo amene anangofika kumene kuderalo ndi ana ake aŵiri. Ngakhale kuti pachilumbachi panali mavuto a m’banja, kukondetsa chipembedzo, ndiponso makhalidwe ena ofala kwa anthu a pazilumba zotchedwa Polynesia, anaona kuti Yehova anali kudalitsa khama lawo. Mbale ndi Mlongo Fernandez tsopano si apainiyanso apadera, koma akukhalabe pachilumbachi, kumene akulera mwana wawo, amene anabadwira komweku. Masiku ano, pali ofalitsa Ufumu osangalala okwana 32. Pa anthu ameneŵa pali nzika za ku Rapa Nui komweko, komanso anthu amene anadzakhala pachilumbachi kapena kusamukirako kuti adzatumikire kumene kunkafunika olengeza Ufumu ambiri.

Kukonzekera Msonkhano Wadera

Chifukwa cha kutalika kwa ulendo wa pakati pachilumbachi ndi South America, katatu pachaka mpingo unali kulandira matepi a vidiyo a pulogalamu ya tsiku la msonkhano wapadera, msonkhano wadera, ndi msonkhano wachigawo. Koma kumapeto kwa chaka cha 2000, Komiti ya Nthambi ya Chile inayamba kuganizira zoti pachilumbachi akhale ndi msonkhano wawo woyamba. Ndiyeno, anaganiza zochita msonkhano wadera mu November 2001, ndipo anthu amene anaitanidwa kudzakhala nawo pachochitika chapaderachi anali abale ndi alongo ochepa chabe a m’madera osiyanasiyana m’dziko la Chile. Chifukwa cha mmene maulendo a ndege analili, msonkhanowo unachitika Lamlungu ndi Lolemba.

Nthumwi 33 zimene zinaitanidwa zinasangalala kumva kuti zipita pachilumbachi kukachita nawo msonkhano wadera woyamba kudera lakutali limeneli. Zitayenda pandege mtunda wautali kudutsa nyanja yamchere ya Pacific, nthumwizo zinasangalala kulandiridwa ndi abale a pachilumbachi amene anali kuwadikira pabwalo landege. Abalewo analandira alendowo mwa kuwaveka mikanda yapakhosi yokongola (yopangidwa ndi maluŵa), yomwe ndi mphatso yofala pachilumbachi. Ndipo anapita nawo kumene akakhale, ndipo ataona malo kwanthaŵi yochepa, onse amene anali m’pulogalamu ya msonkhanowo anakumana mu Nyumba ya Ufumu.

Ufalitsidwa ndi Munthu Wosamuyembekezera

Nthumwi zina zili m’galimoto paulendo wa ku msonkhano, zinadabwa kumva pawailesi wansembe wa pachilumbacho akunena za kufika kwa alendowo m’deralo. Iye anatchula za alendo a ku South America amene aziyenda m’makomo kukambirana ndi anthu za kutha kwa dziko. Ngakhale kuti anauza anthu atchalitchi chake kuti asamvere zimene alendowo anene, zimene analengezazo zinathandiza kufalitsa kufika kwa Mboni za Yehova zambiri pachilumbapo. Izi zinadzutsa chidwi cha anthu pachilumbapo. Kwa masiku otsatira, nthumwizo mochenjera zinakambirana nawo mawu olimbikitsa a uthenga wabwino.

Msonkhano Uyamba

Lamlungu m’maŵa, abale a pachilumbachi anakadikirira pakhomo la Nyumba ya Ufumu kuti alandire nthumwi zikamafika patsiku loyamba lamsonkhano. “Iorana Koe! Iorana Koe!” “Takulandirani!” Alongo ena anavala mmene anthu a pachilumbachi amavalira ndipo anakongoletsa tsitsi lawo ndi maluŵa okongola mmene amachitiradi anthu a ku Polynesia.

Zitatha nyimbo zamalimba zoyambirira, anthu ambiri anaimbira pamodzi nyimbo yakuti “Khalani Okhazikika, Osasunthika!” zimene sizinachitikepo pachilumbachi. Abale akumeneko anafika pogwetsa misozi pamene tcheyamani analandira anthu mosangalala m’chinenero chawo, cha Rapa Nui. Panthaŵi yopuma yamasana, Mboni zitatu zatsopano zinasonyeza kudzipatulira kwawo kwa Mulungu mwa kubatizidwa m’madzi. Pulogalamu yatsiku loyamba itatha, aliyense anadzimva kuti ndi woyandikana ndi Yehova ndiponso abale onse.​—1 Petro 5:9.

Ulaliki wa M’maŵa

Chifukwa cha zochitika zapadera pachilumbachi, pulogalamu yatsiku lachiŵiri lamsonkhano waderawu inayamba masana. Choncho, nthumwi zinapezerapo mwayi pa zimenezi ndipo zinagwiritsa ntchito nthaŵi ya m’maŵa kuchita nawo utumiki wa kumunda. Kodi anakumana ndi zotani?

Mayi wina wachikulire wa ana asanu ndi atatu anauza Mboni kuti sakufuna kulankhula nazo chifukwa chakuti ndi Mkatolika. Atamuuza kuti anali kufuna kukambirana za mavuto amene akukhudza aliyense, monga mankhwala osokoneza bongo ndi mavuto a m’banja, analola kumvetsera.

Mayi wina wachikulire wa pachilumbachi sanasangalale banja lina la Mboni litam’fikira. Analiuza kuti likalankhule ndi anthu a ku South America amene anali kuzunza kwambiri anthu ena. Banjalo linauza mayiyo kuti mawu a ‘uthenga wabwino wa Ufumu’ akuuza munthu aliyense ndiponso kuti abwera pachilumbacho kudzachita nawo msonkhano umene uthandize onse kuwonjezera kukonda kwawo Mulungu. (Mateyu 24:14) Anamufunsa ngati angasangalale kukhala ndi moyo wautali m’malo abwino a paradaiso, ofanana ndi a pachilumbacho koma kopanda matenda ndi imfa. Atakambirana naye zaka zimene zibowo za pamapiri zomwe zinkatuluka chiphalaphala zakhala pachilumbapo, analingalira za kufupika kwa moyo ndipo anafunsa kuti: “Kodi n’chifukwa chiyani timakhala kwanthaŵi yochepa chonchi?” Anadabwa ataŵerenga Salmo 90:10.

Akukambirana zimenezi, Mbonizo mwadzidzidzi zinamva anthu m’chipinda china akukuwa. Ngakhale kuti sanamve zimene anali kunena, mayiyo anawauza kuti anzakewo anali kunyoza ndipo anali kunena kuti sakufuna kuti Mboni zifike kwawoko. Komabe, mayi ameneyu anali nua, kapena kuti mwana wamkulu pabanjalo. Popeza kuti bambo awo anamwalira, unali udindo wake wosankha zinthu zokomera banjalo. Pamaso pa abale akewo, analankhula m’chinenero chake zoikira kumbuyo Mbonizo ndipo anathokoza kulandira zofalitsa zimene anam’patsa. Kumapeto a mlunguwo, ali m’galimoto anaona Mboni zija, ndipo anauza mchimwene wake kuti aimitse galimotoyo. Ngakhale kuti mchimwene wakeyo anaoneka kuti sanasangalale nazo zimenezi, mayiyo anatsazikana ndi abalewo ndipo anawafunira zabwino mu utumiki wawo.

Ngakhale kuti poyamba anthu ena pachilumbachi ankaoneka kuti anali kukana uthenga umene Mboni za ku South America zinali kulalikira, zinali zoonekeratu kwa alendowo kuti a Rapa Nui mwachibadwa ndi anthu abwino ndiponso ochezeka. Ambiri a iwo anamvetsera mosangalala uthenga wabwino. Ndipotu, Mboni 6 pa Mboni 20 zobatizidwira pachilumbapo ndi nzika zakomweko. Mmodzi mwa iwo anayamba kuphunzira choonadi cha Baibulo mwa kumvetsera m’chipinda chapafupi mmene mkazi wake anali kuphunzirira Baibulo. Iye ndi mkazi wake tsopano ndi Mboni zobatizidwa, ndipo ndi mtumiki wotumikira mu mpingo.

Pulogalamu Yauzimu Ipitirira

Nthaŵi ya chakudya cha masana itatha, pulogalamu yatsiku lachiŵiri inayamba. Kachiŵirinso, abale ndi alongo 32 a pachilumbachi ndi nthumwi 33 anasonkhana pamodzi ndi anthu achidwi angapo. Pafupifupi anthu handiredi anamvera pulogalamuyo, ndiponso nkhani ya onse yakuti “Mmene Chikondi ndi Chikhulupiriro Zimagonjetsera Dziko.” Ndipotu, amene analipo pamsonkhanowu anaona chitsanzo chenicheni cha chikondi chimene chimapezeka pakati pa anthu a Yehova, ngakhale atakhala osiyana chikhalidwe.​—Yohane 13:35.

Panthaŵi yamsonkhano waderayo, oyang’anira dera ndi chigawo anakumana mwapadera ndi atumiki amene ndi apainiya. Apainiya okhazikika atatu a pachilumbachi anasonkhana ndi nthumwi zimene ndi apainiya okhazikika kapena apadera. Onse analimbikitsidwa kwambiri.

Tsiku lotsatira, abale ena akomweko ogwira ntchito yoonetsa anthu malo, anaonetsa nthumwi malo pachilumbacho. Anakaona ngwenya kumene anali kusemerako ziboliboli za moai, komanso mapiri a zibowo zimene munkatuluka chiphalaphala ndiponso komwe kale kunali kuchitikira mpikisano, ndiponso gombe la Anakena lomwe n’lokongola kwambiri, kumene anthu oyamba kudzakhala pachilumbachi anafikira. *

Nthaŵi yomaliza kukhala ndi abale akumeneku inali pa Phunziro la Buku la Mpingo. Atatha msonkhanowo, Mboni za kumeneko zinadabwitsa alendo awo powapatsa chakudya chimene anthu akumeneko amakonda kudya. Kenako, atavala zovala zimene amakonda kuvala pachilumbacho, anasonyeza bwino kwambiri mmene amavinira gule wachikhalidwe chamakolo awo. Nthumwizo, komanso abale ndi alongo a ku Rapa Nui, anaona kuti ntchito imene anagwira pokonzekera msonkhanowo sinapite pachabe.

Onse amene anabwera monga nthumwi pamsonkhanowo anaona kuti anali ogwirizana kwambiri ndi abale ndi alongo awo akutaliwo, amene anakhala nawo kwa mlungu umodzi wosangalatsa. Kunali kovuta kwambiri kuchoka pachilumbapo. Sadzaiŵala mabwenzi atsopano amene anapanga komanso chilimbikitso chauzimu chimene analandira. Kubwalo landege, abale akumeneko anakongoletsa makosi a nthumwi mwa kuwaveka mikanda ya zikamba za nkhono imene anapanga.

Nthumwizo zikuchoka, zinalonjeza kuti: “Iorana! Iau he hoki mai e Rapa Nui ee,” kutanthauza kuti: “Ndapita! Ndidzabweranso ku Rapa Nui.” Inde, amalakalaka atapitakonso kuti akayendere mabwenzi awo atsopano ndiponso a m’banja lauzimu pa Chilumba cha Easter chomwe n’chapadera, chakutali kwambiri ndi madera ena, chodabwitsa ndiponso cha anthu ochezeka.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Onani Galamukani! yachingelezi ya June 22, 2000, yofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 27 Pa chibowo cha Rano Raraku chimene chinkatuluka chiphalaphala pali ziboliboli zambiri. Mpikisano wa anthu ofuna kulamulira pachilumbachi unkayambira pa Rano Kau. Anali kuchita mpikisano wotsika pamalo okwera kwambiri, kusambira kupita pa zilumba zina zazing’ono, kukatenga dzira la mbalame ina yopezeka kumeneko, n’kusambiranso kubwerera pachilumba chija, n’kukweranso pamalo okwera kwambiri aja dzira lili losasweka.

[Bokosi patsamba 24]

Kulalikira pa Chilumba cha Easter

Pafupifupi zaka ziŵiri msonkhano wosaiwalika umenewu usanachitike, woyang’anira dera ndi mkazi wake anapita pachilumbachi ndipo anali ndi zokumana nazo zambiri zosangalatsa. Mwachitsanzo, tangolingalirani mmene anadabwira mlongo amene anawatenga kupita nawo kumene akakhale atawakumbutsa kuti anaphunzira naye Baibulo kumwera kwa dziko la Chile ali mtsikana pafupifupi zaka 16 m’mbuyomo. Kenako mbewu imeneyo inabala chipatso ku Rapa Nui.

Iwo analinso ndi chokumana nacho choseketsa ichi: Mwiniwake wa malo ena ogulitsira zinthu zopangidwa pachilumbapo zimene mlendo angagule kuti azikakumbukira zakumeneko analandira Baibulo la New World Translation of the Holy Scriptures ndiponso buku lothandiza anthu kuphunzira Baibulo la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, zonsezi n’zosindikizidwa ndi Mboni za Yehova. Atamuyenderanso, anawauza kuti sangathe kuŵerenga Baibulo lija. Anam’patsa Baibulo la Chifalansa, osati la Chisipanya! Anathetsa vutolo mwamsanga, ndipo mothandizidwa ndi Mboni za Yehova za pachilumbapo ndiponso Baibulo la m’chinenero chake anaona kuti Baibulo silinali lovuta kwambiri kulimvetsa.

[Mapu patsamba 22]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

CHILUMBA CHA EASTER

CHILE

[Zithunzi patsamba 23]

Aŵiri mwa anthu amene anabatizidwa pa msonkhano wadera

[Zithunzi patsamba 25]

Matsitso a phiri lomwe linkatuluka chiphalaphala la Rano Raraku; chithunzi chaching’ono: Chipatso cham’thengo chotchedwa “guayaba” chimene chimamera pachilumbachi