Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Kapolo Wokhulupirika” Wapambana Mayeso!

“Kapolo Wokhulupirika” Wapambana Mayeso!

“Kapolo Wokhulupirika” Wapambana Mayeso!

“Yafika nthaŵi kuti chiweruziro chiyambe pa nyumba ya Mulungu.”​—1 Petro 4:17.

1. Kodi Yesu anapeza zotani pamene anayendera “kapolo”?

PA Pentekoste mu 33 C.E., Yesu anakhazika “kapolo” woti azipatsa “banja” lake chakudya panthaŵi yake. Mu 1914, Yesu analongedwa Ufumu, ndipo posapita nthaŵi yaitali, nthaŵi yoyendera ‘kapoloyo’ inakwana. Anapeza kuti ‘kapoloyu’ kwakukulukulu anali “wokhulupirika ndi wanzeru.” Motero anam’khazika “woyang’anira zinthu zake zonse.” (Mateyu 24:45-47) Koma panalinso kapolo woipa, amene anali wosakhulupirika ndiponso wopanda nzeru.

“Kapolo Woipa Ameneyo”

2, 3. Kodi ‘kapolo woipa ameneyo’ anachokera kuti, ndipo zinakhala bwanji?

2 Yesu atangotha kufotokoza za “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” anafotokoza za kapolo woipa. Anati: “Kapolo woipa [ameneyo, NW] akanena mumtima mwake, Mbuye wanga wachedwa; nadzayamba kupanda akapolo anzake, nadya ndi kumwa pamodzi ndi oledzera; mbuye wa kapoloyo adzafika tsiku losamuyembekeza iye, ndi nthaŵi yosadziŵa iye, nadzam’dula, nadzaika pokhala pake ndi anthu onyenga; pomwepo padzakhala kulira ndi kukukuta mano.” (Mateyu 24:48-51) Mawu akuti ‘kapolo woipa ameneyo’ akutikumbutsa mawu okhudza kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amene Yesu ananena asanafike pamfundoyi. Inde, ‘kapolo woipayu’ anachokera pa kagulu ka kapolo wokhulupirika. * Motani?

3 Chaka cha 1914 chisanafike, ambiri a kagulu ka kapolo okhulupirika anali ndi chikhulupiriro chonse kuti chaka chimenecho akakumana ndi Mkwati kumwamba, koma zomwe ankayembekezerazo sizinachitike. Chifukwa cha zimenezi ndiponso zochitika zina, ambiri anakhumudwa ndipo ochepa anakwiya. Ena mwa anthu ameneŵa anayamba ‘kupanda’ ndi mawu abale awo akale ndiponso kugwirizana ndi “oledzera,” omwe ndi magulu a zipembedzo za Gawo la Matchalitchi Achikristu.​—Yesaya 28:1-3; 32:6.

4. Kodi Yesu anachitanji ndi “kapolo woipa” pamodzi ndi onse omwe asonyeza mtima wofanana ndi wake?

4 Anthuŵa, omwe kale anali Akristu, anayamba kudziŵika monga “kapolo woipa,” ndipo Yesu anawalanga ndi chilango ‘chowadula.’ Motani? Anawakana, ndipo sanayembekezerenso kupita kumwamba. Koma sikuti anawonongedwa nthaŵi yomweyo. Choyamba anafunika kukhala ndi nthaŵi yolira ndiponso kukukuta mano mu “mdima wakunja” kwa mpingo wachikristu. (Mateyu 8:12) Kuchokera masiku oyambirira amenewo, odzozedwa enanso ochepa asonyezanso mtima woipawu, ndi kugwirizana ndi “kapolo woipa.” Enanso a “nkhosa zina” atengera kusakhulupirika kwawo. (Yohane 10:16) Adani onse a Kristu ameneŵa alinso ‘ku mdima [wauzimu] kunja.’

5. Kodi kapolo wokhulupirika ndi wanzeru anachita motani, mosiyana ndi “kapolo woipa”?

5 Ngakhale kuti zili choncho, kapolo wokhulupirika ndi wanzeru anayesedwanso mofanana ndi ‘kapolo woipa ameneyo.’ Koma, m’malo mokwiya, iye anathandizidwa kukhala wangwiro. (2 Akorinto 13:11) Kukonda kwawo Yehova ndiponso abale awo kunalimbikitsidwa. Motero iwo akhala “mzati ndi mchirikizo wa choonadi” mu “masiku otsiriza” ovuta ano.​—1 Timoteo 3:15; 2 Timoteo 3:1.

Anamwali Ochenjera ndi Ena Opusa

6. (a) Kodi Yesu anapereka fanizo lotani pofuna kusonyeza kuchenjera kwa kagulu kake ka kapolo wokhulupirika? (b) Chaka cha 1914 chisanafike, kodi Akristu odzozedwa ankalengeza uthenga wotani?

6 Atatha kulankhula za ‘kapolo woipa ameneyo,’ Yesu anapereka mafanizo aŵiri pofuna kusonyeza chifukwa chomwe Akristu ena odzozedwa adzakhalire okhulupirika ndi anzeru pamene ena ayi. * Pofuna kusonyeza nzeru kapena kuti kuchenjera, iye anati: “Ufumu wa Kumwamba udzafanizidwa ndi anamwali khumi, amene anatenga nyali zawo, natuluka kukakomana ndi mkwati. Ndipo asanu a iwo anali opusa, ndi asanu anali ochenjera. Pakuti opusawo, mmene anatenga nyali zawo, sanadzitengeranso mafuta; koma anzeruwo anatenga mafuta m’nsupa zawo, pamodzi ndi nyali zawo.” (Mateyu 25:1-4) Anamwali khumiŵa akutikumbutsa za Akristu odzozedwa chaka cha 1914 chisanafike. Anali ataŵerengetsera kuti mkwati, Yesu Kristu, anali pafupi kuwonekera. Motero, ‘anatuluka’ kukakumana naye, akulalikira molimba mtima kuti “nthaŵi zawo za anthu akunja” zitha mu 1914.​—Luka 21:24.

7. Kodi ndi liti pamene Akristu odzozedwa tinganene mophiphiritsira kuti ‘anagona’ ndipo n’chifukwa chiyani?

7 Anali atalondola. Nthaŵi za akunja zinathadi mu 1914, ndipo Ufumu wa Mulungu wolamulidwa ndi Kristu Yesu unayamba kugwira ntchito. Koma izi zinkachitikira kumwamba kosaoneka. Padziko lapansi pano, anthu anayamba kukumana ndi “tsoka” lomwe linaloseredwa. (Chivumbulutso 12:10, 12) Ndiye panafika nthaŵi ya mayeso. Chifukwa chosamvetsa zinthu bwinobwino, Akristu odzozedwa anaganiza kuti ‘mkwati wachedwa.’ Popeza anali atasokonezeka maganizo ndiponso ankadedwa ndi dzikoli, iwo anabwerera m’mbuyo kwambiri, ndipo anatsala pang’onong’ono kusiyiratu ntchito yolalikira molinganizidwa bwino. Mofanana ndi anamwali a m’fanizo lija, tinganene kuti mwauzimu “anawodzera, nagona tulo,” monganso momwe anthu osakhulupirika odzitcha Akristu anachitira atumwi a Yesu atatha kufa.​—Mateyu 25:5; Chivumbulutso 11:7, 8; 12:17.

8. Kodi n’chiyani chinachititsa mfuu yakuti: “Onani, mkwati!” ndipo inali nthaŵi yoti Akristu odzozedwa achite chiyani?

8 Kenako, mu 1919 munachitika chinthu china chosayembekezeka. Timaŵerenga kuti: “Koma pakati pa usiku panali kufuula, Onani, mkwati! tulukani kukakumana naye. Pomwepo anauka anamwali onse amenewo, nakonza nyali zawo.” (Mateyu 25:6, 7) Panthaŵi yomwe anthu analibiretu chiyembekezo, m’pamene anthu anauzidwa kuti agalamuke! Mu 1918, Yesu, “mthenga wa chipangano,” anafika ku kachisi wauzimu wa Yehova kudzayendera ndi kuyeretsa mpingo wa Mulungu. (Malaki 3:1) Apa, Akristu odzozedwa anafunika kutuluka ndi kukumana naye m’mabwalo a padziko lapansi a kachisi ameneyo. Inali nthaŵi yoti iwo ‘aŵale.’​—Yesaya 60:1; Afilipi 2:14, 15.

9, 10. Mu 1919, n’chifukwa chiyani Akristu ena anali “ochenjera” ndipo ena anali “opusa”?

9 Koma tadikirani kaye! M’fanizo lija, ena mwa atsikana aja anali ndi vuto. Yesu anapitiriza kuti: “Ndipo opusa anati kwa ochenjera, Tipatseniko ena a mafuta anu; chifukwa nyali zathu zilikuzima.” (Mateyu 25:8) Popanda mafuta, nyali sizingayake. Motero mafuta a nyali akutikumbutsa za Mawu a Mulungu a choonadi ndi mzimu wake woyera, zomwe zimapatsa olambira oona mphamvu kuti akhale onyamula kuunika. (Salmo 119:130; Danieli 5:14) Chaka cha 1919 chisanafike, Akristu ochenjera odzozedwa anali ndi khama lofufuza kuti adziŵe kuti Mulungu ali nawo cholinga chanji, ngakhale kuti anali atafooka kwa nthaŵi yochepa. Motero, mfuu yoti aŵale itamveka, iwo anali okonzeka.​—2 Timoteo 4:2; Ahebri 10:24, 25.

10 Koma ena mwa odzozedwa sanali okonzeka kusiya zinthu zina kapena kuchita khama kwambiri, ngakhale kuti ankafunitsitsa kukakhala ndi Mkwati. Motero itakwana nthaŵi yoti akhale achangu pantchito yolalikira uthenga wabwino, iwo sanali okonzeka. (Mateyu 24:14) Ndipo anafika mpaka poyesa kubwezera m’mbuyo anzawo omwe anali achangu, tinganene kuti, mwa kuwapempha mafuta. M’fanizo la Yesu, kodi anamwali ochenjera aja anayankha motani? Iwo anati: “Kapena sangakwanire ife ndi inu; koma makamaka mukani kwa ogulitsa malonda, mukadzigulire inu nokha.” (Mateyu 25:9) Mofanana ndi zimenezi, Akristu odzozedwa okhulupirika mu 1919 anakana kuchita chilichonse chomwe chikanachepetsa mphamvu zawo zonyamulira kuunika. Motero anapambana mayeso.

11. N’chiyani chinachitikira anamwali opusa?

11 Yesu anamaliza ndi kuti: “Ndipo pamene [anamwali opusa] analikumuka kukagula, mkwati anafika; ndipo okonzekawo analoŵa naye pamodzi muukwati; ndipo anatseka pakhomo. Koma pambuyo pake anadzanso anamwali enawo, nati, Mbuye, Mbuye, mutitsegulire ife. Koma iye anayankha nati, Indetu ndinena kwa inu, sindikudziŵani.” (Mateyu 25:10-12) Inde, ena sanakonzekere kufika kwa Mkwati. Motero, analephera mayeso ndipo anataya mwayi wokakhala nawo pa phwando laukwati kumwamba. Zinalitu zomvetsa chisoni kwambiri!

Fanizo la Matalente

12. (a) Kodi Yesu anagwiritsa ntchito chiyani popereka fanizo losonyeza kukhulupirika? (b) Kodi munthu amene ‘anamuka ulendo’ ndani?

12 Atatha kupereka fanizo losonyeza kuchenjera, Yesu anaperekanso fanizo losonyeza kukhulupirika. Iye anati: “Monga munthu, wakum’ka ulendo, aitana akapolo ake, napereka kwa iwo chuma chake. Ndipo mmodzi anam’patsa ndalama za matalente zisanu, ndi wina ziŵiri, ndi wina imodzi; kwa iwo onse monga nzeru zawo; namuka iye.” (Mateyu 25:14, 15) Munthu wa m’fanizoli ndi Yesu mwiniyo, amene ‘anamuka ulendo’ pamene anakwera kum’ka kumwamba m’chaka cha 33 C.E. Koma asanam’ke kumwambako, Yesu anasiya “chuma chake” m’manja mwa ophunzira ake okhulupirika. Motani?

13. Kodi Yesu anachita chiyani pokonza munda waukulu wogwiramo ntchito ndi polamula “akapolo” ake kuchita malonda?

13 Panthaŵi ya utumiki wake padziko lapansi, Yesu anayamba kukonza munda waukulu wogwiramo ntchito mwa kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu m’dziko lonse la Israyeli. (Mateyu 9:35-38) ‘Asanamuke ulendo,’ iye anasiya mundawo m’manja mwa ophunzira ake okhulupirika, ndi kuwauza kuti: “Mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera: ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.” (Mateyu 28:18-20) Ndi mawu ameneŵa, Yesu analamula “akapolo” ake kuti achite malonda mpaka iye atabwera, “iwo onse monga nzeru zawo.”

14. N’chifukwa chiyani onse sankayembekezeredwa kuchita malonda mofanana?

14 Mawu amenewo akusonyeza kuti si Akristu onse a m’zaka 100 zoyambirira amene anali m’mikhalidwe yofanana kapenanso amene akanatha kuchita zofanana. Ena, monga Paulo ndi Timoteo, anali ndi mpata wochita zinthu zambiri pantchito yolalikira ndi kuphunzitsa. N’kutheka kuti ena ankalephera kuchita zambiri chifukwa chopanikizidwa ndi zochita zina. Mwachitsanzo, Akristu ena anali akapolo, ndipo ena anali kudwaladwala, okalamba, kapena anali ndi udindo wosamalira banja. Ndipotu n’zoona kuti si ophunzira onse amene anali ndi maudindo mu mpingo. Akazi odzozedwa limodzi ndi amuna ena odzozedwa sankaphunzitsa nawo mu mpingo. (1 Akorinto 14:34; 1 Timoteo 3:1; Yakobo 3:1) Komabe, mosasamala kanthu kuti zinthu zili motani kwa aliyense wa iwo, ophunzira onse odzozedwa a Kristu​—amuna ndi akazi​—anauzidwa kuti achite malonda, agwiritse ntchito bwino mipata yomwe anali nayo pochita utumiki wachikristu. Anzawo a masiku ano amachitanso chimodzimodzi.

Nthaŵi Yoyendera Iyamba!

15, 16. (a) Kodi nthaŵi yoŵerengerana inali liti? (b) Kodi akapolo okhulupirika anapatsidwa mwayi watsopano wotani wochita “malonda”?

15 Fanizoli limapitiriza kuti: “Ndipo itapita nthaŵi yaikulu, anabwera mbuye wa akapolo awo, naŵerengera nawo pamodzi.” (Mateyu 25:19) Mu 1914​—patathadi nthaŵi yaitali kuchokera mu 33 C.E.​—Kristu Yesu anayamba kukhalapo kwake monga Mfumu. Patatha zaka zitatu ndi theka, mu 1918, iye anabwera m’kachisi wauzimu wa Mulungu ndi kukwaniritsa mawu a Petro, akuti: “Yafika nthaŵi kuti chiweruziro chiyambe pa nyumba ya Mulungu.” (1 Petro 4:17; Malaki 3:1) Inali nthaŵi yoti aŵerengerane.

16 Kodi akapolo aja, abale odzozedwa a Yesu, anali atachita zotani ndi “matalente” a Mfumu? Kuchokera mu 33 C.E. kupita m’tsogolo, kuphatikizapo zaka zodzafika mu 1914, ambiri anali akhama pochita “malonda” a Yesu. (Mateyu 25:16) Ngakhalenso m’kati mwa nkhondo yoyamba yapadziko lonse, iwo anasonyeza mtima wofunitsitsa kutumikira Mbuyeyo. Ndiyeno panali poyenera kuti akapolo okhulupirika apatsidwe mwayi watsopano wochita “malonda.” Nthaŵi ya mapeto a dongosolo lino la zinthu inali itakwana. Uthenga wabwino unafunika kulalikidwa padziko lonse. “Dzinthu [“zokolola,” NW] za dziko” zinafunika kumwetedwa. (Chivumbulutso 14:6, 7, 14-16) Anthu omalizira a kagulu ka tirigu anafunika kupezedwa ndiponso a “khamu lalikulu” la nkhosa zina anafunika kusonkhanitsidwa.​—Chivumbulutso 7:9; Mateyu 13:24-30.

17. Kodi Akristu okhulupirika odzozedwa ‘analoŵa m’chikondwero cha mbuye wawo’ motani?

17 Nthaŵi yokolola imakhala nthaŵi yokondwera. (Salmo 126:6) Ndiye, zikugwirizana ndi mu 1919 kuti Yesu atawonjezera udindo wa abale ake odzozedwa omwe anali okhulupirika, anati: ‘Unali wokhulupirika pa zinthu zazing’ono, ndidzakhazika iwe pa zinthu zambiri; loŵa iwe m’chikondwero cha mbuye wako.’ (Mateyu 25:21, 23) Komanso, chimwemwe chomwe Mbuyeyo anali nacho monga Mfumu yongolongedwa kumene ya Ufumu wa Mulungu n’choposa mmene ifeyo tingaganizirire. (Salmo 45:1, 2, 6, 7) Kagulu ka kapolo wokhulupirika kamakondwera nawo mwa kuimira Mfumuyo ndiponso kuchulukitsa zinthu zake padziko lapansi. (2 Akorinto 5:20) Timaona kukondwa kwawo m’mawu aulosi a pa Yesaya 61:10, akuti: “Ndidzakondwa kwambiri mwa Yehova, moyo wanga udzakondwerera mwa Mulungu wanga; pakuti Iye wandiveka ine ndi zovala za chipulumutso.”

18. N’chifukwa chiyani ena sanapambane mayeso, ndipo zotsatira zake zinali zotani?

18 N’zomvetsa chisoni kuti ena analephera mayesowo. Timaŵerenga kuti: “Uyonso amene analandira ndalama imodzi, anadza, nati, Mbuye, ndinakudziŵani inu kuti ndinu munthu wouma mtima, wakututa kumene simunafesa, ndi wakusonkhanitsa kumene simunawaza; ndinawopa ine, ndinapita, ndinabisa pansi ndalama yanu: onani, siyi yanu.” (Mateyu 25:24, 25) Mofanana ndi zimenezi, Akristu ena odzozedwa sanachite “malonda.” Chaka cha 1914 chisanafike iwo sankalimbikira pantchito youza ena zomwe anali kuyembekezera, ndipo sanafune kuyamba zimenezo mu 1919. Kodi Yesu anachita chiyani ndi mwano wawowo? Anawalanda maudindo onse omwe anali nawo. ‘Anaponyedwa ku mdima kunja; kumene kunakhala kulira ndi kukukuta mano.’​—Mateyu 25:28, 30.

Ntchito Yoyendera Ikupitirira

19. Kodi ntchito yoyendera ikupitirira motani, ndipo kodi Akristu onse odzozedwa ngotsimikiza kuchita chiyani?

19 Ndi zoona kuti ambiri mwa anthu omwe anali kudzakhala akapolo odzozedwa a Kristu m’nthaŵi yachimaliziro anali asanayambe kutumikira Yehova pamene Yesu ankayamba kuyendera mu 1918. Kodi iwo anaphonya mwayi woyenderedwa? Ayi. Ntchito yoyenderayi inangoyamba mu 1918 kapena 1919 pamene kapolo wokhulupirika ndi wanzeru monga kagulu anapambana mayeso. Mkristu wodzozedwa aliyense payekha akupitiriza kuyenderedwa mpaka atatha kusindikizidwa chizindikiro. (Chivumbulutso 7:1-3) Pozindikira zimenezi, abale odzozedwa a Kristu ngotsimikiza mtima kupitiriza kuchita “malonda” mokhulupirika. Ngotsimikiza kuti akhala ochenjera, asunga mafuta ochuluka kotero kuti muuni uŵale kwambiri. Amadziŵa kuti aliyense akamaliza moyo wake ali wokhulupirika, Yesu adzam’landira m’malo okhala a kumwamba.​—Mateyu 24:13; Yohane 14:2-4; 1 Akorinto 15:50, 51.

20. (a) Kodi a nkhosa zina masiku ano ngotsimikiza kuchitanji? (b) Kodi Akristu odzozedwa amadziŵa za chiyani?

20 A khamu lalikulu la nkhosa zina atengera zochita za abale awo odzozedwa. Iwo akudziŵa kuti ali ndi udindo waukulu chifukwa chakuti adziŵa zolinga za Mulungu. (Ezekieli 3:17-21) Motero, mothandizidwa ndi Mawu a Yehova ndiponso mzimu woyera, nawonso amasunga mafuta ochuluka mwa kuphunzira ndi kufika pamisonkhano yachikristu. Ndipo amaŵalitsa kuunika kwawo, kugwira nawo ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa ndipo pochita zimenezi akuchita “malonda” limodzi ndi abale awo odzozedwa. Komabe, Akristu odzozedwa akudziŵa bwino lomwe kuti matalente anasiyidwa m’manja mwawo. Ayenera kudzafotokoza mmene chuma cha Mbuye cha padziko lapansi chakhala chikusamalidwira. Ngakhale kuti ndi ochepa panopa, sangatulire a khamu lalikulu udindo wawo. Poganizira zimenezi, kapolo wokhulupirika ndi wanzeru akupitiriza kutsogolera posamalira malonda a Mfumu, ndipo amayamikira thandizo lomwe amalandira kwa a khamu lalikulu odzipereka kwambiri. Iwo amazindikira udindo wa abale awo odzozedwa ndipo amaona kuti ndi mwayi waukulu kuyang’aniridwa ndi iwo.

21. Kodi ndi mawu ati amene akhala akugwira ntchito kwa Akristu onse kuyambira chaka cha 1919 chisanafike mpaka pano?

21 Motero, ngakhale kuti mafanizo aŵiriŵa amatizindikiritsa zomwe zinachitika mu 1919 kapena cha m’nthaŵi imeneyo, mfundo zake zikugwira ntchito kwa Akristu onse oona m’masiku onse otsiriza ano. Mwanjirayi, ngakhale kuti zomwe Yesu analimbikitsa kuchita pamapeto a fanizo la anamwali khumi zinagwira ntchito koyamba pa Akristu odzozedwa chaka cha 1919 chisanafike, mfundo zake zikugwirabe ntchito kwa Mkristu aliyense. Ndiyetu tiyeni tonse tilabadire mawu a Yesu akuti: “Chifukwa chake dikirani, pakuti simudziŵa tsiku lake, kapena nthaŵi yake.”​—Mateyu 25:13.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Mofanana ndi zimenezi, atumwi atatha kufa, “mimbulu yosautsa” inachokera pakati pa akulu odzozedwa achikristu.​—Machitidwe 20:29, 30.

^ ndime 6 Pofuna kuona kufotokoza kwinanso kwa fanizo la Yesuli, onani machaputala 5 ndi 6 m’buku lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova lakuti Chisungiko cha Padziko Lonse mu Ulamuliro wa “Kalonga wa Mtendere.”

Kodi Mungafotokoze?

• Ndi liti pamene Yesu anayendera otsatira ake, ndipo anapeza chiyani?

• N’chifukwa chiyani Akristu ena odzozedwa anayamba kukhala ndi mtima wa ‘kapolo woipa ameneyo’?

• Kodi tingasonyeze motani kuti ndife ochenjera mwauzimu?

• Motsanzira abale odzozedwa a Yesu omwe ndi okhulupirika, ndi njira iti yomwe tingapitirizire kuchita “malonda”?

[Mafunso]

[Bokosi patsamba 16]

KODI KUDZA KWA YESU KUKUCHITIKA LITI?

Mu Mateyu chaputala 24 ndi 25, Yesu ananena za ‘kudza’ ndi matanthauzo osiyanasiyana. Sakuchita kufunika kusintha malo kuti ‘adze.’ M’malomwake, iye ‘akudza’ m’lingaliro la kuika maganizo ake pa anthu kapena otsatira ake ndipo nthaŵi zambiri n’cholinga chopereka chiweruzo. Motero, mu 1914 ‘anadza’ kuti ayambe kukhalapo monga Mfumu yoikidwa. (Mateyu 16:28; 17:1; Machitidwe 1:11) Mu 1918 ‘anadza’ monga mthenga wa chipangano ndi kuyamba kuweruza anthu omwe ankanena kuti akutumikira Yehova. (Malaki 3:1-3; 1 Petro 4:17) Pa Armagedo, “adzadza” kudzaweruza adani a Yehova.​—Chivumbulutso 19:11-16.

Kudza (kapena kuti kufika) komwe akutchula maulendo angapo pa Mateyu 24:29-44 ndi 25:31-46 ndi kwa pa ‘chisautso chachikulu.’ (Chivumbulutso 7:14) Koma kudza kotchulidwa maulendo angapo pa Mateyu 24:45 mpaka 25:30 kukukhudza ntchito yake yoweruza anthu odzitcha ophunzira ake kuchokera mu 1918 mpaka m’tsogolo. Sizingakhale zomveka kunena kuti, mwachitsanzo, kufupa kapolo wokhulupirika, kuweruza anamwali opusa, ndi kuweruza kapolo waulesi, amene anabisa talente la Mbuye, kudzachitika Yesu ‘akadzadza’ pa chisautso chachikulu. Zimenezo zingasonyeze kuti ambiri mwa odzozedwa adzapezeka osakhulupirika panthaŵiyo motero padzafunika kuti ena awaloŵe m’malo. Koma Chivumbulutso 7:3 chimasonyeza kuti akapolo onse odzozedwa a Kristu adzakhala atatha ‘kusindikizidwa chizindikiro’ panthaŵi imeneyo.

[Chithunzi patsamba 14]

“Kapolo woipa” sanalandire madalitso mu 1919

[Chithunzi patsamba 15]

Anamwali ochenjera anali okonzeka pamene mkwati amafika

[Chithunzi patsamba 17]

Akapolo okhulupirika anali kuchita “malonda”

Kapolo waulesi sankatero

[Zithunzi patsamba 18]

Odzozedwa limodzi ndi a “khamu lalikulu” akupitiriza kuwalitsa kuunika kwawo