Kodi Chikhulupiriro Chingachiritse Wodwala?
Kodi Chikhulupiriro Chingachiritse Wodwala?
TIKADWALA, timafuna mpumulo ndiponso kuchiritsidwa. Mosakayikira, mukudziŵa kuchokera m’Baibulo kuti nthaŵi zambiri Yesu Kristu anachiritsa matenda a mitundu yonse, zimene zinapatsa mpumulo odwala ambiri. Kodi anali kuchiritsa bwanji? Baibulo limati mwa ‘ukulu wa Mulungu.’ (Luka 9:42, 43; Machitidwe 19:11, 12) Choncho, unali mzimu woyera wa Mulungu umene unali kuchiritsa anthu, osati chikhulupiriro cha munthu chokha. (Machitidwe 28:7-9) N’chifukwa chake Yesu sanafune kuti odwala asonyeze kaye kuti anali ndi chikhulupiriro mwa iye kuti achiritsidwe.
Mungafunse kuti: ‘Kodi kuchiritsa mozizwitsa kunatha, kapena kodi kuchiritsa kofanana ndi kumene Yesu anali kuchita kudzachitikanso? Kodi amene akudwala matenda opweteka kapena osachiritsika angayembekezere zotani?’
Baibulo limafotokoza kuti m’dziko latsopano la Mulungu lachilungamo, ukulu kapena kuti mphamvu ya Mulungu idzapangitsanso kuti kuchiritsa mozizwitsa kumene Yesu anachita nthaŵi imene anali padziko lapansi kuchitikenso. Mboni za Yehova za m’dera lanu zingasangalale kukusonyezani momwe Mulungu adzachitire zimene munthu wochiritsa mwachikhulupiriro sangachite—kuchotsa matenda onse ndi imfa yomwe, komanso nthaŵi imene Mulungu adzachite zimenezi. Inde, Mulungu ‘adzameza imfa ku nthaŵi yonse.’—Yesaya 25:8.