Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Muli ndi Mtima Wangwiro?

Kodi Muli ndi Mtima Wangwiro?

Kodi Muli ndi Mtima Wangwiro?

MFUMU Davide inalimbikitsa Solomo, yemwe anali mwana wake ndiponso amene anali kudzaloŵa m’malo mwake, kutumikira Yehova “ndi mtima wangwiro.” (1 Mbiri 28:9) Mawu amenewo ndi ofunikanso kwa anthu amene akufuna kutumikira Mulungu masiku ano. Kuti tizindikire bwinobwino kufunika kwake, tiyenera kumvetsa zimene olemba Baibulo amatanthauza akatchula mtima wa munthu.

Mtima unatchulidwa kwambiri m’Malemba, pafupifupi maulendo 1000 m’njira zosiyanasiyana. Olemba Baibulo anagwiritsa ntchito mawu achihebri (lev, le·vavʹ) ndi achigiriki (kar·diʹa) otanthauza “mtima” kunena mtima weniweni ndiponso wophiphiritsira. Ndi malo ochepa chabe amene amanena za mtima weniweni, umene ntchito yake yeniyeni ndi kupopa magazi ndi kupereka chakudya ku maselo a m’thupi. (2 Mafumu 9:24) Malo ambiri m’Malemba, pamene patchulidwa mawu akuti “mtima,” amanena wophiphiritsira.

Mtima Wophiphiritsira

Mtima wophiphiritsira wotchulidwa m’Baibulo sikuti umangotanthauza zimene zimapangitsa munthu kukonda ndiponso kuchita zinazake, komanso sikuti umangotanthauza nzeru. Buku lakuti The Metaphorical Use of the Names of Parts of the Body in Hebrew and in Akkadian linafotokoza kuti: “Kwa a Semite . . . mtima unkaimira chilichonse chokhudza munthu pankhani ya maganizo komanso nzeru ndi zofuna zake.” Bukuli linapitiriza kunena kuti mtima ndiwo “umunthu wonse wam’kati osati thupi looneka ndi kugwirikali.”

Chimene chili chofunika kwambiri kwa Mulungu amene amayesa mitima ndi mmene munthu alili m’kati osati maonekedwe akunja. (Miyambo 17:3; 24:12) Chotero Malemba amalangiza kuti: “Chinjiriza mtima wako [umunthu wonse wam’kati] koposa zonse uzisunga; pakuti magwero a moyo atulukamo.” (Miyambo 4:23) Ndipo akazi achikristu okwatiwa amalimbikitsidwa kusamalira kwambiri “munthu wobisika wamtima, m’chovala chosaola cha mzimu wofatsa ndi wachete, ndiwo wa mtengo wake wapatali pamaso pa Mulungu,” osati kudzikongoletsa kunja.​—1 Petro 3:​3, 4.

Malo angapo m’Baibulo pamene pali mawu akuti “mtima,” kwenikweni amanena za maganizo, koma sikuti amakhala akupatula maganizowo pa zina zonse zimene zimapanga umunthu wam’kati. Mose anapempha Aisrayeli kuti, ‘mukumbukire m’mtima mwanu [kapena kuti, kumbukirani m’maganizo mwanu], kuti Yehova ndiye Mulungu.’ Ndipo kenako anawauza kuti, “Yehova sanakupatsani mtima wakudziŵa [kapena kuti, maganizo odziŵa].”​—Deuteronomo 4:39; 29:4.

Mtima Ndiponso Chochititsa Munthu Kuchita Zinthu

Chimene chimachititsa kuti tikhale ndi khalidwe limene tili nalo ndi mbali ina yofunika kwambiri ya umunthu wam’kati, umene umaimiridwa ndi “mtima.” Chotero, amene anapereka zopereka zomangira chihema “anadza, aliyense wofulumidwa mtima.” (Eksodo 35:21) Pa Ahebri 4:12 pamafotokoza kuti Mawu a Mulungu alonjezo, amene ali monga lupanga lakuthwa, akhoza ‘kuzindikiritsa zolingalira ndi zitsimikizo za mtima.’ Yesu nayenso, anasonyeza kuti mtima ndi umene umatichititsa kuti tikhale ndi khalidwe limene tili nalo, kaya labwino kapena loipa.​—Mateyu 15:19.

Pofuna kutilimbikitsa kukhala ndi zolinga zabwino, Baibulo limatichenjeza kuti pochita zinthu ndi ena tizipeŵa kuchita zinthu chifukwa chofuna kupeza phindu kapena chifukwa chokonda ndalama komwe ndi kufuna chuma. (1 Timoteo 6:​9, 10; Yuda 16) M’malomwake, limatilimbikitsa kuti tizitumikira Mulungu chifukwa chakuti timamukondadi, ndiponso pochita zinthu ndi okhulupirira anzathu tizichita chifukwa cha chikondi chodzimana. (Yohane 15:​12, 13; 1 Yohane 5:3) Baibulo limatilimbikitsanso kuti tizoloŵere kukonda ena monga mmene timadzikondera tokha.​—Luka 10:​27-37.

Mmene mtima wathu wophiphiritsira ulili umaonekera mwa khalidwe lathu, zochita zathu, kaya ndife onyada kapena odzichepetsa. (Miyambo 16:5) Maganizo athu ndi mmene timamvera ndi mbalinso ya umunthu wam’kati umenewu. Zimenezi ndi monga chikondi, chimwemwe, kupweteka ndiponso chisoni, komanso udani.​—Levitiko 19:17; Deuteronomo 6:5; 28:47; Aroma 9:2.

Peŵani Mtima Wonyenga

Ngakhale kuti Adamu anali wangwiro, analekerera mtima wake kunyengedwa; anakana choonadi ndipo anapatuka kwa Mulungu. (Onani Yakobo 1:​14, 15.) Chotsatira chake chinali chakuti, anthu onse, ana a Adamu wochimwayo, anabadwira m’uchimo ndiponso m’zoipa. (Salmo 51:5) Ponena za anthu onse ochimwa Chigumula chitapita, Mulungu anati: “Ndingaliro ya mtima wa munthu ili yoipa kuyambira pa unyamata wake.”​—Genesis 8:21.

Mulungu anauza mtundu wopanduka wa Ayuda kuti: “Mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika.” (Yeremiya 17:9) Pamenepa pali chenjezo lalikulu lakuti amene akufuna kusangalatsa Mulungu ayenera kusamalira osati kokha zimene anthu ena angaone koma mmene iwo alilidi, umunthu wawo wam’kati. Munthu akhoza kukhala Mkristu kwa zaka zambiri, wodziŵa bwino Baibulo, ndiponso wodzidalira kuti angathane bwinobwino ndi vuto lililonse limene lingafike. Komabe, ngakhale akudziŵa bwino kuti kuchita chinachake n’kolakwika ndiponso kuti lamulo la Mulungu limaletseratu zimenezo, zimene amaganiza ndi zilakolako zomwe wakhala akuzibisa zingam’pangitse kuchita tchimo.

Pazifukwa zimenezi Mkristu, ngakhale akudziŵa choonadi ndiponso amadziona kuti ndi wokhwima mwauzimu, ayenera kukumbukira zinthu zonyenga zimene mtima wake ungasonyeze ndipo chotero ayenera kusamala kwambiri kuti asakhale pamalo amene angathe kuyesedwa.​—1 Akorinto 10:​8-12.

Kutumikira ndi “Mtima Wangwiro”

Mtima weniweni uyenera kukhala wathunthu kuti uzigwira ntchito bwino, koma mtima wophiphiritsira ukhoza kukhala wogaŵanika. Davide anapemphera kuti: “Muumbe mtima wanga ukhale umodzi kuti uliope dzina lanu,” kutanthauza kuti mtima wa munthu ukhoza kukhala wogaŵanika pa zimene umakonda ndiponso zimene umaopa. (Salmo 86:11) Munthu wotero angakhale ndi mtima wogaŵanika, wofunda polambira Mulungu. (Chivumbulutso 3:16) Munthu akhozanso kukhala ndi “mitima iŵiri,” kumatumikira ambuye aŵiri, kapena kumanena mwachinyengo chinthu chinachake pamene akuganiza zina.​—Salmo 12:2.

Munthu amene akufuna kusangalatsa Mulungu sayenera kukhala ndi mtima wogaŵanika kapena mitima iŵiri koma ayenera kumutumikira ndi mtima wangwiro. (1 Mbiri 28:9) Izi zimafuna khama chifukwa chakuti mtima ndi wosachiritsika ndiponso wokonda kuchita choipa. (Yeremiya 17:​9, 10) Zimene zingatithandize kukhala ndi mtima wangwiro ndi izi: kupemphera ndi mtima wonse, kuphunzira Mawu a Mulungu nthaŵi zonse, kulalikira mwachangu uthenga wabwino, ndiponso kucheza ndi amene mitima yawo ndi yangwiro kwa Yehova.​—Ezara 7:10; Salmo 119:145; yerekezani ndi 2 Mafumu 10:​15, 16; Yeremiya 20:9.