Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene Timasonyezera Kuti Timakonda Mulungu

Mmene Timasonyezera Kuti Timakonda Mulungu

Mmene Timasonyezera Kuti Timakonda Mulungu

KUKONDA Mulungu sikutanthauza kungophunzira za Mulungu. Atumiki a Mulungu padziko lonse angavomereze kuti chikondi chenicheni pa Mulungu chimakula pamene munthu adziŵa umunthu wa Mulungu, ndipo chimalimba pamene munthu adziŵa zimene Mulunguyo amakonda, amadana nazo, ndiponso zimene amafuna.

Chifukwa choti Yehova amatikonda watipatsa Mawu ake, Baibulo, limene limanena za iye. Mmenemo timaphunziramo zimene Yehova anachita pa zochitika zosiyanasiyana. Monga mmene timasangalalira ndi kalata yochokera kwa munthu amene timamukonda, timasangalala tikamaona m’Baibulo mfundo zatsopano za umunthu wa Yehova.

Komabe, monga timaonera nthaŵi zina polalikira, si nthaŵi zonse zimene kuphunzira za Mulungu kumapangitsa munthu kukonda Mulungu. Yesu ananena kwa Ayuda ena osayamikira a m’nthaŵi yake kuti: “Musanthula m’malembo, popeza muyesa kuti momwemo muli nawo moyo wosatha; . . . koma ndikudziŵani inu, kuti mulibe chikondi cha Mulungu mwa inu nokha.” (Yohane 5:39, 42) Anthu ena amaphunzira kwa zaka zambiri zimene Yehova wachita chifukwa chotikonda koma samukonda kwenikweni. Chifukwa chiyani? Amalephera kuganizira mfundo zogwirizana ndi zimene akuphunzira. Mosiyana ndi zimenezi, mamiliyoni a anthu oona mtima amene timaphunzira nawo Baibulo amaona kuti kukonda kwawo Mulungu kumakula nthaŵi zonse. Chifukwa chiyani? Chifukwa, monga mmene ifeyo tinachitira, amatsatira chitsanzo cha Asafu. Motani?

Kusinkhasinkha ndi Mtima Woyamikira

Asafu anatsimikiza mu mtima mwake kukhala wokonda Yehova. Iye analemba kuti: “Ndilingalira mumtima mwanga . . . Ndidzakumbukira zimene adazichita Ambuye; inde, ndidzakumbukira zodabwiza zanu zoyambira kale. Ndipo ndidzalingalira ntchito yanu yonse, ndi kulingalirabe zimene munazichita Inu.” (Salmo 77:6, 11, 12) Amene amasinkhasinkha njira za Yehova ngati mmene anachitira wamasalmo adzakulitsa kukonda Mulungu mu mtima mwake.

Ndiponso, kukumbukira zimene takumana nazo potumikira Yehova kumalimbitsa ubwenzi umene tili nawo ndi iye. Mtumwi Paulo ananena kuti tili “antchito anzake” a Mulungu, ndipo anthu ogwirira ntchito limodzi amakhala pa ubwenzi wapadera kwambiri. (1 Akorinto 3:9) Ngati tisonyeza kuti timakonda Yehova, iye amaona zimenezo kukhala zamtengo wapatali, ndipo zimasangalatsa mtima wake. (Miyambo 27:11) Ndiyeno, tikapempha Yehova kuti atithandize ndipo akatitsogolera pamavuto enaake, timadziŵa kuti ali nafe, ndipo chikondi chathu pa iye chimakula.

Ubwenzi wa anthu aŵiri umakula akamauzana maganizo awo. Mofananamo, tikamuuza Yehova chifukwa chake tinadzipereka kwa iye, timakulitsa chikondi chathu pa iye. Tikatero, mawu a Yesu akuti: “Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mphamvu yako yonse,” azingobwera okha m’maganizo mwathu. (Marko 12:30) Kodi tingatani kuti titsimikizire kuti tikupitiriza kukonda Yehova ndi mtima wathu wonse, moyo wathu wonse, nzeru zathu zonse, ndi mphamvu zathu zonse?

Kukonda Yehova ndi Mtima Wathu Wonse

Malemba amanena za mtima wophiphiritsira, umene ndi umunthu wam’kati​—zolinga zathu, mtima wathu, ndiponso maganizo athu. Choncho kukonda Yehova ndi mtima wathu wonse kumatanthauza kuti koposa zonse, timafuna kusangalatsa Mulungu. (Salmo 86:11) Timasonyeza kuti tili ndi chikondi chimenechi mwa kukhala ndi umunthu wovomerezeka kwa iye. Timayesetsa kutsanzira Mulungu mwa ‘kudana nacho choipa ndi kugwirizana nacho chabwino.’​—Aroma 12:9.

Kukonda kwathu Mulungu kumakhudza maganizo athu pachilichonse. Mwachitsanzo, ntchito yathu ingakhale yosangalatsa kapena yofuna kuikirapo maganizo kwambiri, koma kodi m’pamene pali mtima wathu? Ayi. Popeza timakonda Yehova ndi mtima wathu wonse, choyamba ndife atumiki a Mulungu. Mofananamo, timafuna kusangalatsa makolo athu, mwamuna kapena mkazi wathu, abwana athu, koma timasonyeza kuti timakonda Yehova ndi mtima wathu wonse mwa kusangalatsa iye choyamba. Ndipotu, amafunika kukhala pamalo oyamba mu mtima mwathu.​—Mateyu 6:24; 10:37.

Kukonda Yehova ndi Moyo Wathu Wonse

M’Malemba mawu akuti “moyo” kwenikweni amanena za munthu yense komanso moyo umene ali nawo. Choncho kukonda Yehova ndi moyo wathu wonse kumatanthauza kuti timagwiritsa ntchito moyo wathu kumutamanda ndiponso kusonyeza kuti timamukonda.

N’zoona kuti tingakhale ndi zochita zina pamoyo wathu, monga kuphunzira ntchito, kuchita malonda, kapena kulera ana. Koma panthaŵi yofananayo, timasonyeza kuti timakonda Yehova ndi moyo wathu wonse mwa kuchita zinthu momwe iye amafunira ndiponso mwa kuchita zinthu zina panthaŵi yoyenera, ‘tikumathanga tafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake.’ (Mateyu 6:33) Kulambira ndi moyo wonse kumatanthauzanso kukhala achangu. Timam’sonyeza Yehova kuti timamukonda mwa kulalikira mwachangu uthenga wa Ufumu, kupereka ndemanga zolimbikitsa pamisonkhano, kapenanso kuthandiza abale ndi alongo athu achikristu. Mu zonse, timapitiriza ‘kuchita chifuniro cha Mulungu mochokera mumtima [“ndi moyo wonse,” NW].’​—Aefeso 6:6.

Yesu anasonyeza kukonda Mulungu ndi moyo wonse mwa kudzikana yekha. Ankatsogoza kuchita chifuno cha Mulungu ndipo pambuyo pake anali kuchita zofuna zake. Yesu anatipempha kutsatira chitsanzo chake. Iye anati: “Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha, natenge mtanda wake, nanditsate Ine.” (Mateyu 16:24, 25) Kudzikana tokha kumatanthauza kudzipatulira. Kumatanthauza kuti timakonda Mulungu kwambiri moti timadzipereka kwa iye, monga Mwiisrayeli m’nthaŵi za m’Baibulo akakonda mbuye wake kwambiri ankadzipereka kukhala kapolo wake nthaŵi zonse. (Deuteronomo 15:16, 17) Kupatulira moyo wathu kwa Yehova ndi umboni wamphamvu wakuti timamukonda.

Kukonda Yehova ndi Nzeru Zathu Zonse

Kukonda Yehova ndi nzeru zathu zonse kumatanthauza kuti timachita zofunika kuti tizindikire umunthu wa Yehova, zolinga zake, ndiponso zimene iye amafuna. (Yohane 17:3; Machitidwe 17:11) Timasonyeza kuti timakonda Yehova mwa kugwiritsa ntchito nzeru zathu zonse kuthandiza ena kuti nawonso akonde Yehova ndiponso mwa kuwongolera luso lathu la kuphunzitsa. Mtumwi Petro analimbikitsa kuti: “Konzekeretsani maganizo anu kugwira ntchito.” (1 Petro 1:13, NW) Ndiponso timayesetsa kusonyeza kuganizira ena, makamaka anzathu amene tikutumikira nawo Mulungu. Timadziŵa mmene zinthu zilili pamoyo wawo ndipo timadziŵa pamene akufunika kuwayamikira kapena kuwalimbikitsa.

Timam’sonyeza Yehova kuti timamukonda ndi nzeru zathu zonse ngati maganizo athu agonjera iye. Timayesa kuona zinthu momwe iye amazionera, timalingalira za iye pamene tikusankha zochita, ndiponso kukhulupirira kuti njira yake ndiyo yabwino koposa. (Miyambo 3:5, 6; Yesaya 55:9; Afilipi 2:3-7) Koma pamene tikupitiriza kusonyeza kuti timakonda Mulungu, kodi mphamvu zathu tingazigwiritse ntchito bwanji?

Kukonda Yehova ndi Mphamvu Zathu Zonse

Achinyamata ambiri mu mpingo wachikristu amagwiritsa ntchito mphamvu zawo potamanda Yehova. (Miyambo 20:29; Mlaliki 12:1) Njira imodzi imene achinyamata achikristu ambiri amasonyezera kuti amakonda Yehova ndi mphamvu zawo zonse ndi yochita nawo utumiki wa upainiya womwe ndi utumiki wanthaŵi zonse. Amayi ambiri amachita nawo utumiki umenewu pamene ana awo ali kusukulu. Akulu okhulupirika amene amachita maulendo aubusa kuphatikiza pa kusamalira mabanja awo amasonyeza kuti amakonda Yehova ndi mphamvu zawo zonse. (2 Akorinto 12:15) Yehova amapereka mphamvu kwa amene amamukhulupirira n’cholinga chakuti asonyeze kuti amamukonda pom’tamanda mwa kugwiritsa ntchito mphamvu zonse zimene ali nazo.​—Yesaya 40:29; Ahebri 6:11, 12.

Chikondi chimakula ngati chisamalidwa bwino. Choncho, tipitirize kupeza nthaŵi yosinkhasinkha. Tizikumbukira zimene Yehova watichitira ndiponso chifukwa chake n’koyenera kudzipereka kwa iye. Monga anthu opanda ungwiro ochokera kwa Adamu, sitingayenere “zilizonse Mulungu anakonzereratu iwo akum’konda Iye,” koma tingasonyeze kuti timakonda Yehova ndi moyo wathu wonse. Tiyeni tipitirize kuchita zimenezi.​—1 Akorinto 2:9.

[Chithunzi patsamba 20]

Timasonyeza kuti timakonda Mulungu mwa zochita zathu