Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Chitani Ntchito ya Mlaliki wa Uthenga Wabwino’

‘Chitani Ntchito ya Mlaliki wa Uthenga Wabwino’

‘Chitani Ntchito ya Mlaliki wa Uthenga Wabwino’

Khala maso m’zonse, . . . chita ntchito ya mlaliki wa Uthenga Wabwino.”​—2 TIMOTEO 4:5.

1. Kodi Yesu anapereka lamulo lotani kwa otsatira ake?

DZINA la Yehova ndiponso zofuna zake zikulengezedwa padziko lonse. Izi zili chonchi chifukwa chakuti athu odzipatulira a Mulungu alabadira lamulo limene Yesu Kristu anapereka kwa otsatira ake pamene ananena kuti: “Mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera: ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.”​—Mateyu 28:19, 20.

2. Kodi Timoteo yemwe anali woyang’anira analandira malangizo otani, ndipo njira imodzi yomwe oyang’anira achikristu angakwaniritsire utumiki wawo ndi iti?

2 Ophunzira a Yesu a m’zaka 100 zoyambirira sanalione mopepuka lamulo limenelo. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo analimbikitsa Timoteo, yemwenso anali woyang’anira wachikristu, kuti: “Chita ntchito ya mlaliki wa Uthenga Wabwino, kwaniritsa utumiki wako.” (2 Timoteo 4:5) Njira imodzi yomwe woyang’anira amakwaniritsira utumiki wake masiku ano ndiyo kukhala wolalikira Ufumu wachangu, kuchita nawo utumiki wa kumunda nthaŵi zonse. Mwachitsanzo, woyang’anira Phunziro la Buku la Mpingo ali ndi mwayi wotsogolera pantchito yolalikira ndi kuphunzitsa ena ntchitoyi. Paulo anakwaniritsa udindo wake wolalikira uthenga wabwino, ndipo anathandiza nawo pophunzitsa ena kuchita utumiki.​—Machitidwe 20:20; 1 Akorinto 9:16, 17.

Alaliki Achangu Akale

3, 4. Kodi Filipo anakumana ndi zotani monga mlaliki wa uthenga wabwino?

3 Akristu oyambirira ankadziŵika kuti anali alaliki achangu. Taganizirani za mlaliki Filipo. Anali mmodzi mwa “amuna asanu ndi aŵiri a mbiri yabwino, odzala ndi mzimu ndi nzeru” omwe anasankhidwa kugwira ntchito yogaŵa chakudya tsiku ndi tsiku mosakondera kwa akazi amasiye achikristu olankhula Chihelene ndiponso olankhula Chihebri ku Yerusalemu. (Machitidwe 6:1-6) Ntchito yapaderayi itatha, ndipo onse kusiyapo atumwi atabalalika chifukwa cha chizunzo, Filipo anapita ku Samariya. Ali kumeneko iye analalikira uthenga wabwino ndipo mzimu woyera unam’patsa mphamvu yochotsa ziwanda ndi kuchiritsa opunduka ndiponso amanjenje. Asamariya ambiri analabadira uthenga wa Ufumu ndipo anabatizidwa. Atumwi ku Yerusalemu atamva zimenezi, anatuma Petro ndi Yohane kupita ku Samariya n’cholinga choti okhulupirira amene anali atabatizidwa kumenewo akalandire mzimu woyera.​—Machitidwe 8:4-17.

4 Kenako mzimu wa Mulungu unatsogolera Filipo kuti akakumane ndi mdindo wa ku Aitiopiya panjira yopita ku Gaza. Filipo atafotokoza ulosi wa Yesaya momveka bwino, munthuyu yemwe anali “wamphamvu wa Kandake, mfumu yaikazi ya Aaitiopiya” anakhulupirira Yesu Kristu ndipo anabatizidwa. (Machitidwe 8:26-38) Kuchoka pamenepo, Filipo anapita ku Azotu ndipo kenako anakafika ku Kaisareya, ndipo m’njira ‘analalikira Uthenga Wabwino m’midzi yonse.’ (Machitidwe 8:39, 40) Kunena zoona iye anasonyeza chitsanzo chabwino kwambiri pantchito yolalikira uthenga wabwino.

5. Kodi ana aakazi anayi a Filipo ankadziŵika chifukwa cha chiyani makamaka?

5 Filipo anali kupitirizabe utumiki ku Kaisareya zaka pafupifupi 20 zimenezi zitachitika. Pamene Paulo ndi Luka anakhala kunyumba kwake, iye “anali nawo ana aakazi anayi, anamwali, amene ananenera.” (Machitidwe 21:8-10) Mosakayikira anaŵa anali ataphunzitsidwa bwino mwauzimu, anali achangu mu utumiki, ndipo analinso ndi mwayi wolosera zinthu. Changu chomwe makolo ali nacho mu utumiki chingawathandize kwambiri anyamata ndi atsikana masiku ano, zomwe zingawalimbikitse kukonza zoti ntchito yolalikira ikhale ya moyo wawo wonse.

Alaliki Achangu Masiku Ano

6. Kodi alaliki a m’zaka 100 zoyambirira zinawayendera bwino motani pantchito yawo?

6 Mu ulosi wake waukulu wonena za masiku athu ano ndiponso m’nthaŵi ya chimaliziro, Yesu Kristu anati: “Uthenga Wabwino uyenera uyambe kulalikidwa kwa anthu a mitundu yonse.” (Marko 13:10) Chimaliziro chidzafika uthenga wabwino utalalikidwa “padziko lonse lapansi.” (Mateyu 24:14) Pamene Paulo ndi alaliki ena a m’zaka 100 zoyambirira anali kulengeza uthenga wabwino, anthu ambiri anakhala okhulupirira, ndipo mipingo inakhazikitsidwa m’madera ambiri mu ufumu wonse wa Roma. Akulu omwe anali kuikidwa kuti azitumikira m’mipingo imeneyi anali kugwira ntchito yolalikira limodzi ndi abale ndi alongo awo, ndipo anagwira ntchito yolalikirayi m’madera osiyanasiyana. Mawu a Yehova anakula ndiponso kupambana m’masiku amenewo, monganso momwe akuchitira masiku ano chifukwa chakuti Mboni za Yehova mamiliyoni ambiri zikulalikira. (Machitidwe 19:20) Kodi ndinu mmodzi wa anthu achimwemwe ameneŵa omwe akutamanda Yehova?

7. Kodi olengeza Ufumu akuchitanji masiku ano?

7 Ambiri mwa anthu omwe akulengeza za Ufumu masiku ano akugwiritsa ntchito mipata yomwe apeza kuti awonjezere ntchito yawo yolalikira. Olengeza Ufumu zikwizikwi akuchita umishonale, ndipo ena miyandamiyanda akugwira ntchito yolalikira nthaŵi zonse monga apainiya okhazikika ndiponso othandiza. Ndipo amuna, akazi, ndi ana akugwira ntchito yotamandika kwambiri monga ofalitsa Ufumu achangu. Zoonadi, anthu onse a Yehova akupeza madalitso ochuluka pamene akum’tumikira ndi mtima umodzi monga alaliki achikristu.​—Zefaniya 3:9.

8. Kodi ndi ntchito yolemba chizindikiro iti yomwe ikuchitika panopo, ndipo ikuchitidwa ndi ndani?

8 Mulungu wapatsa otsatira odzozedwa a Yesu ntchito yolengeza uthenga wabwino padziko lonse. “Nkhosa zina” za Kristu, zomwe zikuchulukirachulukira zikuthandizana nawo pantchito yolalikirayi. (Yohane 10:16) Mwaulosi, ntchito yopulumutsa miyoyo imeneyi imayerekezedwa ndi kulemba chizindikiro pamphumi pa anthu omwe akuusa moyo ndi kulira chifukwa cha zonyansa zomwe zikuchitika masiku ano. Posachedwapa, anthu oipa awonongedwa. Pakalipano, ndi mwayi waukulu kuuza anthu a m’dzikoli choonadi chopulumutsa moyo.​—Ezekieli 9:4-6, 11.

9. Kodi atsopano angathandizidwe motani mu utumiki?

9 Ngati takhala tikugwira ntchito yolalikirayi kwa nthaŵi yaitali ndithu, n’zodziŵikiratu kuti tingachitepo kenakake pothandiza atsopano mu mpingo. Nthaŵi zina, tingathe kuwatenga kuti aloŵe nafe mu utumiki. Akulu akulimbikitsidwa kuchita zonse zomwe angathe kuti alimbitse mwauzimu okhulupirira anzawo. Khama la oyang’anira odzichepetsa lingachite zambiri pothandiza ena kukhala alaliki achangu ndiponso obala zipatso.​—2 Petro 1:5-8.

Kulalikira Kunyumba ndi Nyumba

10. Kodi Kristu ndi omutsatira ake oyambirira anasonyeza chitsanzo chotani mu utumiki?

10 Yesu Kristu anasonyeza omutsatira ake chitsanzo chabwino kwambiri monga mlaliki. Pankhani ya ulaliki wa Kristu ndi atumwi ake, Mawu a Mulungu amati: “Anayendayenda kumizinda ndi kumidzi, kulalikira ndi kuwauza Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu, ndi pamodzi naye khumi ndi aŵiriwo.” (Luka 8:1) Nanga bwanji za atumwiwo pawokha? Mzimu woyera utatsanulidwa pa Pentekoste wa mu 33 C.E., “masiku onse, m’Kachisi ndi m’nyumba, sanaleka kuphunzitsa ndi kulalikira Kristu Yesu.”​—Machitidwe 5:42.

11. Malinga ndi Machitidwe 20:20, 21, kodi mtumwi Paulo anachita chiyani mu utumiki wake?

11 Chifukwa cha ulaliki wake wachangu, mtumwi Paulo anauza akulu achikristu a ku Efeso kuti: “Sindinakubisirani zinthu zopindulira, osazilalikira kwa inu, ndi kukuphunzitsani inu pabwalo ndi m’nyumba m’nyumba.” Pamene Paulo anali ‘kuphunzitsa kunyumba ndi nyumba,’ kodi anali kuyendera nyumba za anzake omwe anali kulambira nawo Yehova, kupanga maulendo aubusa kwa okhulupirira? Ayi, chifukwa anapitiriza kunena kuti: ‘Ndachitira umboni Ayuda ndi Ahelene wa kutembenuza mtima kulinga kwa Mulungu, ndi chikhulupiriro cholinga kwa Ambuye wathu Yesu Kristu.’ (Machitidwe 20:20, 21) Kwakukulukulu, anthu omwe anali odzipatulira kale kwa Yehova sakanafunikira malangizo onena za “kutembenuza mtima kulinga kwa Mulungu, ndi chikhulupiriro cholinga kwa Ambuye wathu Yesu Kristu.” Paulo anaphunzitsa akulu achikristu a ku Efeso mu utumiki wa kunyumba ndi nyumba pamene anali kuphunzitsa anthu osakhulupirira za kutembenuka mtima ndi chikhulupiriro. Pochita zimenezi, Paulo anali kutsatira njira yomwe Yesu anakhazikitsa.

12, 13. Mogwirizana ndi Afilipi 1:7, kodi anthu a Yehova achita zotani pankhani ya ufulu wawo wolalikira?

12 Ulaliki wa kunyumba ndi nyumba ungakhale wovuta. Mwachitsanzo, ena amakwiya tikafika panyumba zawo ndi uthenga wa Baibulo. Sikuti ndi cholinga chathu kukwiyitsa anthu. Komabe, ulaliki wa kunyumba ndi nyumba ndi wa m’Malemba, ndipo timalalikira mwanjira imeneyi chifukwa chakuti timakonda Mulungu ndiponso anansi athu. (Marko 12:28-31) Pofuna ‘kuteteza ndi kukhazikitsa mwalamulo’ ufulu wathu wolalikira kunyumba ndi nyumba, tapititsa milandu ku makhoti, kuphatikizapo ku Khoti Lalikulu la ku United States. (Afilipi 1:7, NW) Pafupifupi nthaŵi zonse khoti limeneli lakhala likugamula milandu motikomera. Chitsanzo cha zimenezi ndi chigamulo ichi:

13 “Kugaŵa pamanja mathirakiti achipembedzo ndi njira yomwe inayamba kale kwambiri imene amishonale amagwiritsa ntchito polalikira, inayamba m’nthaŵi yomwe anayamba kupanga makina osindikizira mabuku. Nthaŵi yonseyi, magulu osiyanasiyana a zipembedzo akhala akuona njira imeneyi kukhala yamphamvu kwambiri. Kulalikira mwanjira imeneyi kukuchitikanso masiku ano, makamaka ndi magulu osiyanasiyana a zipembedzo omwe alaliki awo amayenda nyumba zikwizikwi ndi Uthenga Wabwino ndipo mwa kuyendera anthu iwo amafuna kupeza ena oloŵa chipembedzo chawo. . . . Mu lamulo lalikulu [m’malamulo a dziko la United States] ntchito yotereyi ya chipembedzo ndi yofunikanso mofanana ndi kupembedza m’matchalitchi ndiponso kulalikira pagome.”​—Mlandu wa Murdock ndi Boma la Pennsylvania, 1943.

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kupitiriza Kulalikira?

14. Kodi utumiki wathu ungakhale ndi zotsatirapo zotani m’kupita kwanthaŵi?

14 Pali zifukwa zambiri zolalikirira kunyumba ndi nyumba. Nthaŵi iliyonse yomwe tayendera mwininyumba, timayesetsa kuwoka mbewu ya choonadi cha m’Malemba. Mwa kupanga maulendo obwereza, timayesetsa kuithirira. Ndipo izi m’kupita kwanthaŵi zingakhale ndi zotsatirapo zabwino, chifukwa Paulo analemba kuti: “Ndinawoka ine, anathirira Apolo; koma Mulungu anakulitsa.” (1 Akorinto 3:6) Motero tiyeni tipitirize ‘kuwoka ndi kuthirira,’ tili ndi chikhulupiriro chakuti Yehova ‘adzakulitsa.’

15, 16. N’chifukwa chiyani timapita ku nyumba za anthu mobwerezabwereza?

15 Timalalikira chifukwa chakuti miyoyo ya anthu ili pangozi. Mwa kulalikira tingathe kudzipulumutsa ife eni ndiponso anthu omwe atimvetsera. (1 Timoteo 4:16) Ngati tadziŵa kuti moyo wa munthu winawake uli pangozi, kodi tingangom’thandiza ulendo umodzi wokha komanso mosaikirapo mtima? Ayi! Popeza kuti ndi nkhani yopulumutsa moyo wa munthu, timapita kunyumba za anthu mobwerezabwereza. Zinthu zikusintha nthaŵi zonse. Munthu amene watanganidwa kwambiri moti sangamvetsere nthaŵi ina, angathe kudzafuna kumva uthenga wa Baibulo panthaŵi ina. Mwina munthu wotilandira paulendo wina sangakhale amene tinam’peza poyamba, ndipo izi zingapangitse kuti tikambirane naye Malemba.

16 Kuwonjezera pa kusintha kwa zinthu pa moyo wa munthu, maganizonso a eninyumba amatha kusintha. Mwachitsanzo, imfa ya munthu wokondedwa yomwe ndi yopweteka kwambiri ingachititse munthu kumvetsera uthenga wa Ufumu. Timayembekezera kulimbikitsa munthu woteroyo, kum’dziŵitsa kusoŵa kwake kwauzimu, ndi kum’sonyeza mmene angathetsere vutolo.​—Mateyu 5:3, 4.

17. Kodi chifukwa chachikulu chimene timagwirira ntchito yathu yolalikira ndi chiti?

17 Chifukwa chachikulu chimene timagwirira ntchito yathu yolalikira kunyumba ndi nyumba kapena kuchita ntchito zina zachikristu n’chakuti timafunitsitsa titadziŵikitsa nawo dzina la Yehova. (Eksodo 9:16; Salmo 83:18) Zimapindulitsa kwambiri ntchito yathu yolalikira ikathandiza anthu okonda choonadi ndi chilungamo kukhala otamanda Yehova. Wamasalmo anaimba kuti: “Anyamata ndiponso anamwali; okalamba pamodzi ndi ana: Alemekeze dzina la Yehova; pakuti dzina lake lokha ndi lokwezeka; ulemerero wake uli pamwamba pa dziko lapansi ndi thambo.”​—Salmo 148:12, 13.

Kulalikira Kumatipindulitsa

18. Kodi timapindula motani tikamachita ntchito yolalikira?

18 Timapindula m’njira zosiyanasiyana chifukwa chogwira ntchito yolalikira. Kulalikira uthenga wabwino kunyumba ndi nyumba kumatithandiza kukhala odzichepetsa, makamaka anthu akapanda kutilandira bwino. Kuti tikhale alaliki ogwira mtima, tifunika kukhala ngati Paulo, amene ‘anakhala zonse kwa anthu onse, kuti pali ponse akapulumutse ena.’ (1 Akorinto 9:19-23) Kudziŵa bwino ntchito yolalikira kumatithandiza kukhala osamala polankhula. Mwa kudalira Yehova ndiponso kusankha bwino mawu athu, tingathe kugwiritsa ntchito malangizo a Paulo akuti: “Mawu anu akhale m’chisomo, okoleretsa, kuti mukadziŵe inu mayankhidwe anu a kwa yense akatani.”​—Akolose 4:6.

19. Kodi mzimu woyera umawathandiza motani alaliki?

19 Ntchito yolalikira imatithandizanso kudalira mzimu woyera wa Mulungu. (Zekariya 4:6) Tikamadalira mzimuwo, pamene tili mu utumiki timaonetsa chipatso chake, chomwe ndi “chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso.” (Agalatiya 5:22, 23) Umakhudza momwe timachitira zinthu ndi anthu, chifukwa chakuti kugonjera malangizo a mzimu kumatithandiza kukhala achikondi, achimwemwe ndiponso amtendere, kukhala oleza mtima ndiponso achifundo, kusonyeza kukoma mtima ndi chikhulupiriro, ndiponso kusonyeza chifatso komanso kudziletsa pamene tikulalikira uthenga wabwino.

20, 21. Kodi ena mwa madalitso okhala kalikiliki monga alaliki ndi ati?

20 Dalitso lina lomwe timapeza pokhala alaliki ndi lakuti timamvera ena chisoni. Anthu akatiuza mavuto awo, monga matenda, ulova, mavuto apanyumba, sitikhala ngati alangizi, koma timakambirana nawo malemba opatsa chiyembekezo ndiponso olimbikitsa. Timawamvera chisoni anthu amene achititsidwa khungu mwauzimu koma ooneka kuti amakonda ndithu chilungamo. (2 Akorinto 4:4) Ndipo zimasangalatsa kwambiri kupereka thandizo lauzimu kwa anthu amene ‘maganizo awo ndi oyenera moyo wosatha.’​—Machitidwe 13:48, NW.

21 Kuchita ntchito yolalikira nthaŵi zonse kumatithandiza kuika maganizo athu onse pa zinthu zauzimu. (Luka 11:34) Kunena zoona zimenezi ndi zopindulitsa, chifukwa chakuti kupanda kutero tingathe kugonjera ziyeso zokondetsa chuma zomwe n’zofala m’dzikoli. Mtumwi Yohane analimbikitsa Akristu kuti: “Musakonde dziko lapansi, kapena za m’dziko lapansi. Ngati wina akonda dziko lapansi, chikondi cha Atate sichili mwa iye. Pakuti chilichonse cha m’dziko lapansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma ku dziko lapansi. Ndipo dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi zonse.” (1 Yohane 2:15-17) Kukhala kalikiliki monga alaliki omwe ali ndi zochita zochuluka pa ntchito ya Ambuye kumatithandiza kuti tisakonde dziko lapansi.​—1 Akorinto 15:58.

Kundikani Chuma cha M’mwamba

22, 23. (a) Kodi alaliki achikristu amakundika chuma chotani? (b) Kodi nkhani yotsatirayi idzatithandiza motani?

22 Kukhala achangu pantchito yolalikira za Ufumu kumatipatsa phindu losatha. Yesu anasonyeza zimenezi pamene ananena kuti: “Musadzikundikire nokha chuma padziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri ziwononga; ndi pamene mbala ziboola ndi kuba: koma mudzikundikire nokha chuma m’Mwamba, pamene njenjete kapena dzimbiri siziwononga, ndipo mbala siziboola ndi kuba; pakuti kumene kuli chuma chako, komwe udzakhala mtima wakonso.”​—Mateyu 6:19-21.

23 Tiyeni tipitirize kukundika chuma m’mwamba, podziŵa kuti sitingapezenso mwayi wina waukulu kwambiri kuposa kuimira Ambuye Mfumu Yehova monga Mboni zake. (Yesaya 43:10-12) Pamene tikugwira ntchito yomwe tapatsidwa yokhala atumiki a Mulungu, nafenso tingathe kumva ngati mmene anamvera mayi wina wachikristu amene ali ndi zaka za m’ma 90, yemwe ananena izi zokhudza moyo wake wautali wotumikira Mulungu: “Kudzera mu utumikiwu ndimayamikira Yehova chifukwa chondilola kum’tumikira zaka zonsezi ngakhale kuti ndili ndi zofooka, ndipo ndimayesetsa kupemphera kuti iye akhale Atate wanga wondikonda mpaka kalekale.” Ngati ifenso timauyamikira motere ubwenzi wathu ndi Mulungu, mosakayikira tidzafuna kuyesetsa kukwaniritsa ntchito ya mlaliki. Nkhani yotsatirayi idzatithandiza kuona mmene tingakwaniritsire utumiki wathu.

Kodi Mungayankhe Motani?

• N’chifukwa chiyani tiyenera kuchita ntchito ya mlaliki?

• Kodi munganenenji za ntchito ya alaliki akale ndiponso amasiku ano?

• N’chifukwa chiyani timalalikira kunyumba ndi nyumba?

• Kodi inu mumapindula motani pochita ntchito ya mlaliki?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 10]

Alaliki monga Filipo ndi ana ake aakazi akufanana ndi anthu ena masiku ano omwe ndi achimwemwe

[Chithunzi patsamba 14]

Kodi inuyo mumapindula motani pamene mukulalikira uthenga wabwino kwa anthu ena?