Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ehudi Anathyola Goli la Wopondereza

Ehudi Anathyola Goli la Wopondereza

Ehudi Anathyola Goli la Wopondereza

NKHANIYI, yomwe imasonyeza kulimba mtima ndiponso ukatswiri pochita zinthu, ndi yoona. Inachitika zaka pafupifupi 3,000 zapitazo. Nkhani ya m’Malembayi imayamba motere: “Ana a Israyeli anawonjezanso kuchita choipa pamaso pa Yehova; pamenepo Yehova analimbitsa Egiloni mfumu ya Moabu pa Israyeli, popeza anachita choipa pamaso pa Yehova. Ndipo anadzisonkhanitsira ana a Amoni ndi a Amaleki, namuka nakantha Israyeli, nalanda mudzi wa m’migwalangwa nakhalamo. Ndipo ana a Israyeli anatumikira Egiloni mfumu ya Moabu zaka khumi ndi zisanu ndi zitatu.”​—Oweruza 3:12-14.

Dziko la Amoabu linali kum’maŵa kwa mtsinje wa Yordano komanso kwa Nyanja Yakufa. Koma Amoabuwo anawoloka mtsinjewo ndi kulanda dera lozungulira Yeriko, “mudzi wa migwalangwa,” n’kuyamba kulamulira Aisrayeli. (Deuteronomo 34:3) Kwa zaka pafupifupi makumi aŵiri, mfumu ya Amoabu, Egiloni, yomwe inali “munthu wonenepa ndithu,” inakhala ikulandira kwa Israyeli mtulo womwe unalemetsa ndi kuwachotsera ulemu Aisrayeliwo. (Oweruza 3:17) Komabe, lamulo lake loti azim’patsa mtulo, linapatsa Aisrayeli mwayi woti athane ndi munthu woponderezayu.

Nkhaniyo imati: “Ana a Israyeli anafuula kwa Yehova, Yehova anawaukitsira mpulumutsi, Ehudi mwana wa Gera, Mbenjamini, munthu wamanzere, ndipo ana a Israyeli anatumiza mtulo m’dzanja lake kwa Egiloni mfumu ya Moabu.” (Oweruza 3:15) Yehova ayenera kuti anaonetsetsa kuti Ehudi wasankhidwa kukapereka mtulo. Kaya anali atachitapo ntchito imeneyi kale sizinatchulidwe. Koma, zomwe Ehudi anachita pokonzekera bwino kwambiri kukakumana ndi Egiloni ndiponso njira zaukatswiri zomwe anatsatira zikusonyeza kuti mwina ankadziŵako ndithu mmene nyumba yachifumu ya Egiloni inalili ndiponso zomwe zikanakam’chitikira kunyumbayo. Pazonsezi, chofunika kwambiri chinali chakuti iye anali wamanzere.

Kodi Anali Wolumala Kapena Msilikali?

Mu Chihebri, mawu akuti “wamanzere” kwenikweni amatanthauza ‘wolumala kapena womangika mkono wamanja.’ Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Ehudi anali ndi chilema, mwinamwake kuti mkono wake wamanja unali wolumala? Taonani zomwe Baibulo limanena zokhudza amuna “osankhika mazana asanu ndi aŵiri” amanzere a fuko la Benjamini. Oweruza 20:16 amati: “Yense wa iwo amaponya mwala mwa maluli osaphonya.” Mwachionekere amunaŵa ankawasankha chifukwa cha ukatswiri wawo pankhondo. Malinga ndi zimene ananena katswiri wina wamaphunziro a Baibulo, akamati “wamanzere” amatanthauza munthu wogwiritsa ntchito mikono yonse iŵiri, wamanzere ndi wamanja.​—Oweruza 3:15.

Ndipotu fuko la Benjamini linatchuka ndi amuna ogwiritsa ntchito mikono yamanzere. Pa 1 Mbiri 12:1, 2 pamafotokoza za Abenjamini ‘amphamvu othandiza kunkhondo amene ankakoka mauta; naponya miyala, naponya mivi ndi uta ndi dzanja lamanja ndi lamanzere lomwe.’ N’kutheka kuti ankafika pochita zimenezi, “mwa kumanga mikono yamanja ya ana aang’ono​—n’chifukwa chake liwulo limatanthauza kuti ‘womangidwa mkono wamanja’​—n’kumawaphunzitsa kugwiritsa ntchito mkono wamanzere,” limatero buku lina. Kaŵirikaŵiri adani a Israyeli ankaphunzitsidwa mmene angalimbanirane ndi msilikali wogwiritsa ntchito mkono wamanja. Motero zambiri zomwe mdani ankaphunzira zinkakhala zopanda ntchito ngati mosayembekezeka akumana ndi msilikali wogwiritsa ntchito dzanja lamanzere.

“Mawu Achinsinsi” kwa Mfumu

Chinthu choyamba chomwe Ehudi anachita chinali ‘kudzisulira lupanga,’ lomwe linali lakuthwa konsekonse ndiponso lalifupi bwino moti akanatha kulibisa m’zovala zake. N’kutheka kuti ankayembekezera kukasechedwa. Kaŵirikaŵiri malupanga ankawamangirira mbali ya kumanzere, komwe anthu ogwiritsa ntchito mkono wamanja sankavutika kulisolola. Popeza kuti Ehudi anali wamanzere, iye anabisa chida chakechi “pansi pa zovala zake pa ntchafu ya kulamanja,” komwe zinali zokayikitsa kuti alonda a mfumu angasecheko. Motero, iye anapita ‘kukapereka mtulo kwa Egiloni, mfumu ya Moabu’ popanda vuto lililonse.​—Oweruza 3:16, 17.

Sitikuuzidwa tsatanetsatane wa zimene zinachitika koyambirira m’nyumba ya Egiloni. Baibulo limangonena kuti: “[Ehudi] atatha kupereka mtulowo, anauza anthu onyamula mtulo achoke.” (Oweruza 3:18) Ehudi anapereka mtulo, naperekeza anthu onyamula mtulowo kuchoka panyumba ya Egiloni mpaka pamalo oti sangachitidwe choopsa, ndipo iye anabwerera atawauza anthuwo kuti azipita. N’chifukwa chiyani anachita zimenezi? Mwina anawatenga n’cholinga choti azimuteteza, kapena mwamwambo chabe, kapenanso monga anthu ongonyamula mtulo basi. Ndipo mwina Ehudi ankafuna kuti anthuwo ayambe achoka kaye n’cholinga choti iye akamachita zomwe anali atakonza iwo asavulazidwe. Kaya maganizo a Ehudi anali otani pamenepa, koma iye anabwerera yekha molimba mtima kunyumba ya Egiloni.

“[Ehudi] anabwerera pa mafano osema ali ku Giligala, nati, Ndiri nawo mawu achinsinsi kwa inu, mfumu.” Malemba safotokoza kuti zinatheka bwanji kuti amulolenso kukaonana ndi Egiloni. N’kutheka kuti alonda sanam’kayikire. Mwina alondawo ankaganiza kuti Mwisrayeli mmodzi sangachite choopsa chilichonse kwa mbuye wawo. N’kuthekanso kuti kubweranso yekha kwa Ehudi kunawapatsa maganizo oti akuwayenda pansi anthu a m’dziko lake. Mulimonsemo, Ehudi anafuna kuti alankhulane pa aŵiri ndi mfumu, ndipo anamulola.​—Oweruza 3:19.

Nkhani youziridwayi imapitiriza kuti: “Ehudi anam’dzera [Egiloni] alikukhala payekha m’chipinda chosanja chopitidwa mphepo. Nati Ehudi, Ndiri nawo mawu a Mulungu akukuuzani.” Sikuti Ehudi ankanena za uthenga wapakamwa wochoka kwa Mulungu. Zomwe Ehudi ankaganizira ndi zogwiritsa ntchito lupanga lake lija. Mwina poganizira kuti amva uthenga wochoka kwa mulungu wake Kemosi, mfumuyo ‘inauka pa mpando wake.’ Mwamsangamsanga, Ehudi anasolola chida chake chija n’kubaya nacho Egiloni pamimba. Mwachionekere lupangali linalibe chilichonse cholepheretsa chigumbu chake kuloŵa nawo m’mimbamo. N’chifukwa chake, “chigumbu chake chinaloŵa kutsata mpeni wake; ndi mafuta anaphimba mpeniwo, . . . [ndipo zonyansa zinayamba kutuluka, NW],” mwina kudzera pachilondapo kapena kudziwonongera kwa Egiloni.​—Oweruza 3:20-22.

Kuthaŵa Mosavutikira

Mosataya nthaŵi kuti asolole lupanga lake, ‘Ehudi anatulukira kukhonde [“pa bowo loloŵetsera mpweya,” NW] nam’tsekera pamakomo pa chipinda chosanja nafungulira [“nakhoma,” NW]. Ndipo atatuluka iye, anadza akapolo [a Egiloni]; napenya, ndipo taonani pamakomo pa chipinda chosanja [m’pokhoma]; nati iwo, Angophimba mapazi [“akudzithandiza,” NW] m’chipinda chake chosanja chopitidwa mphepo.’​—Oweruza 3:23, 24.

Kodi “bowo loloŵetsera mpweya” lomwe Ehudi anatulukirapo linali chiyani? “Tanthauzo lake lenileni [la mawu a Chihebri pamenepa] silikudziŵika,” limatero buku lina, koma “ena amaganiza kuti ndi njira kapena chipinda chapakati pa khomo lalikulu ndi m’kati mwa nyumba.” Mwina Ehudi anakhoma zitseko ali m’kati ndi kutulukira njira ina. Kapena n’kutheka kuti anakhoma zitseko ali kunja ndi makiyi amene anatenga kwa mfumu yakufayo. Mwina atachita zimenezi anayenda pang’onopang’ono kudutsa alonda aja ngati kuti sipanachitike chilichonse. Malemba sanenapo chilichonse. Kaya Ehudi anagwiritsa ntchito njira yotani, koma antchito a Egiloni sanakayikire chilichonse mwamsanga atapeza kuti zitseko zili zokhoma. Anangoganiza kuti mfumu ‘ikudzithandiza.’

Pamene antchito a mfumu anali kuchedwa, Ehudi anathaŵa. Kenako anauza Aisrayeli anzake kuti: “Nditsateni ine, pakuti Yehova wapereka adani anu Amoabu m’manja mwanu.” Mwa kulanda malo osavuta kuwoloka pamtsinje wa Yordano, omwe anali ofunika kwambiri, amuna a Ehudi anatseka njira yomwe Amoabu omwe analibe mtsogoleri akanadutsa pothaŵa kupita kwawo. Motero, “[Aisrayeli] anakantha Amoabu nyengo ija anthu zikwi khumi, onseŵa anthu amoyo, ndi ngwazi; ndipo sanapulumuka ndi mmodzi yense. Motero anagonjetsa Moabu tsiku lija pansi pa dzanja la Israyeli. Ndipo dziko linapumula zaka makumi asanu ndi atatu.”​—Oweruza 3:25-30.

Zimene Tingaphunzirepo

Zomwe zinachitika m’masiku a Ehudi zikutiphunzitsa kuti pamakhala zotsatirapo zoopsa tikachita chinthu chomwe Yehova amaona kuti ndi choipa. Komanso, Yehova amathandiza anthu omwe alapa ndi kubwerera kwa iye.

Zomwe Ehudi anakonza kuti achite zinayenda bwino, osati chifukwa cha kuchenjera kwake kapena chifukwa chakuti adani awo anali olephera penapake. Kukwaniritsidwa kwa cholinga cha Mulungu sikudalira zochita za anthu. Chinthu chachikulu chomwe chinachititsa kuti zinthu zimuyendere bwino Ehudi n’chakuti, Mulungu anali kum’thandiza pamene iye anali kuchita zinthu mogwirizana ndi cholinga cha Mulungu chopulumutsa anthu Ake chimene sichikanalepheretsedwa. Mulungu anautsa Ehudi, “ndipo pamene Yehova anawaukitsira oweruza [anthu ake], Yehova anakhala naye woweruzayo.”​—Oweruza 2:18; 3:15.