Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Inu Ndinu Wamkulu Kuposa Mapiri’

‘Inu Ndinu Wamkulu Kuposa Mapiri’

Kukongola kwa Chilengedwe cha Yehova

‘Inu Ndinu Wamkulu Kuposa Mapiri’

KUONA dzuŵa likutuluka uli pamwamba pa phiri la Fuji chingakhale chinthu chosaiŵalika. Dzuŵa looneka ngati malaŵi a moto limaonekera chapansipansi, n’kuunika chipale chofewa ndi miyala yotuŵa imene inapangika ndi chiphalaphala chouma. Posakhalitsa pamene tsiku lina likuyamba, mthunzi wa phirilo umafika pa mtunda wa makilomita angapo kukuta mapiri aang’ono ndi zigwa.

Mofanana ndi phiri la Fuji, limene nthaŵi ina dzina lake ankalilemba m’zizindikiro zotanthauza kuti “palibe lofanana nalo,” nthaŵi zonse timachita chidwi ndi mapiri akuluakulu. Ndipotu, tikhoza kuona kuti ndife ochepa kwambiri tikamaona kukula kwa mapiriwo. Mapiriŵa ndi aakulu kwambiri moti anthu ambiri akhala akukhulupirira kuti, nsonga zazitali kwambiri za mapiri ameneŵa, zimene nthaŵi zambiri zimakutidwa ndi nkhungu ndi mitambo, ndi malo amene milungu imakhala.

Mulungu mmodzi yekha amene amatamandidwa moonadi chifukwa cha mapiri aataliŵa ndi Mlengi waluso, Yehova. Ndi iye yekha ‘amene anaumba mapiri.’ (Amosi 4:13) Pafupifupi gawo limodzi mwa magawo anayi a dziko lapansi ndi mapiri, ndipo Mulungu polenga dziko lapansili anaika mphamvu zimene kenako zinapanga nsonga za mapiri zazitali zochititsa chidwi ndi mitandadza ya mapiri. (Salmo 95:4) Mwachitsanzo, anthu akukhulupirira kuti mitandadza ya mapiri a Himalaya ndi Andes inapangika chifukwa cha kutumphuka kumene kunachitika pansi pa dziko lapansi ndiponso kugwedezeka kwa nthaka.

Anthufe sitimvetsa mokwanira mmene mapiri anawapangira komanso chifukwa chake anawapanga. Inde, sitingathe kuyankha mafunso amene Yobu wolungama anafunsidwa, akuti: “Unali kuti muja [ine Yehova] ndinaika maziko a dziko lapansi? . . . Maziko ake anakumbidwa pa chiyani?”​—Yobu 38:4-6.

Koma chomwe tikudziŵa n’choti, moyo wathu umadalira mapiri. Mapiri akhala akutchedwa kuti ndi magwero a madzi, chifukwa mitsinje yonse yaikulu imayambira kumapiri ndipo theka la anthu padziko lapansi amadalira mapiri kuti apeze madzi. (Salmo 104:13) Malinga ndi magazini yakuti New Scientist, “mitundu isanu ndi umodzi mwa mitundu 20 yaikulu ya zakudya zimene anthu amachita kudzala, inachokera ku mapiri.” M’dziko latsopano limene Mulungu walonjeza mmene zinthu zachilengedwe zidzakhala bwino, “mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri.”​—Salmo 72:16; 2 Petro 3:13.

Kwa anthu ambiri, akamva za mapiri amaganizira za mapiri a European Alps. Mapiri ameneŵa, kuphatikizapo phiri la Civetta limene lili pachithunzipa, amapereka umboni woti kuli Mlengi. (Salmo 98:8) Amatamanda Yehova, amene ‘anakhazikitsa mapiri ndi mphamvu yake.’​—Salmo 65:6. *

Mapiri okongola mochititsa chidwi kwambiri ndi a Alps omwe ali ndi nsonga zokutidwa ndi madzi oundana, m’mbali mwake mokutidwa ndi chipale chofeŵa, ndiponso ali ndi zigwa ndi nyanja, komanso madambo. Mfumu Davide inamutcha Yehova kuti ndi “amene aphukitsa msipu pamapiri.”​—Salmo 147:8.

Mitandadza ya mapiri, monga mapiri aŵa ku Guilin, m’dziko la China, angaoneke ngati si ochititsa chidwi kwambiri monga mapiri a Alps, koma ndi okongola mwapadera. Alendo amachita chidwi kwambiri ndi kukongola kwa mizeremizere ya nsonga za miyala ya njereza yokwera ya mapiri ameneŵa amene ayala motsata mtsinje wa Li. Kuona madzi oyera akuyenda m’mapiri okutidwa ndi nkhungu ameneŵa, kungachititse munthu kukumbukira mawu a wamasalmo akuti: “[Yehova] atumiza akasupe aloŵe m’makwaŵa; ayenda pakati pa mapiri.”​—Salmo 104:10.

N’koyeneradi kuti timachita chidwi ndi mapiri chifukwa timawaona kuti ndi mbali yaikulu ya zinthu zimene Mlengi anapereka kuti zithandize anthu ndiponso kuti asangalale nazo. Komabe, ngakhale kuti mapiri amachititsa mantha, sangafanane m’pang’ono pomwe ndi ukulu wa Yehova. Iye alidi ‘womveka [“wamkulu,” NW] kuposa mapiri.’​—Salmo 76:4.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Onani Kalendala ya 2004 ya Mboni za Yehova miyezi ya March/​April.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 9]

Anthu khumi mwa anthu 100 alionse amakhala m’madera a mapiri. Koma chimenecho si chopinga chachikulu kwa anthu amene amalengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Atumiki achikristu ameneŵa ali kalikiliki m’madera ambiri okwera. Ndipo “akongolatu pamapiri mapazi a iye amene adza ndi uthenga wabwino, amene abukitsa mtendere, amene adza ndi uthenga wabwino wa zinthu zabwino, amene abukitsa chipulumutso.”​—Yesaya 52:7.

Wamasalmo anaimba kuti: “Mapiri atali ndiwo ayenera zinkhoma.” (Salmo 104:18) Zinkhoma, kapena kuti mbuzi za m’mapiri, monga yotchedwa Nubian ibex yomwe ili ndi nyanga zazikulu, ndi imodzi mwa nyama za m’mapiri zomwe sizigwa chisawawa. Zimayenda mu nsolomondo zazing’ono kwambiri zimene zimaoneka ngati n’zosatheka kuti chinthu chingayendepo. Nyamayi inalengedwa mwa njira yoti ingathe kukhala m’malo omwe nyama zina kapena anthu sangafikeko. Chifukwa china chimene nyamayi imatha kuchitira zimenezi ndi mmene mapazi ake anapangidwira. Mpata wa pa mapazi a nyamayi umakanuka ikaponda pansi ndipo zimenezi zimathandiza kuti igwiritse kwambiri osagwa ikaima kapena ikamayenda mu nsolomondo zazing’ono kwambiri. Kunena zoona, nyama imeneyi inalengedwa mwapadera.

[Chithunzi patsamba 9]

Phiri la Fuji, ku Honshu, Japan