Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi n’chiyani chinachitika m’nkhani imene ili pa Eksodo 4:24-26, ndipo ndani amene akanaphedwayo?

Mose anali akupita ku Igupto pamodzi ndi mkazi wake, Zipora, ndi ana ake, Gerisomu ndi Eliezere, pamene izi zinachitika: “Kunali panjira, kuchigono, Yehova anakomana naye, nafuna kumupha. Koma Zipora anatenga mpeni wamwala, nadula khungu la mwana wake, naliponya pa mapazi ake; nati, Pakuti iwe ndiwe mkwati wanga wamwazi. Ndipo Iye anam’leka. Pamenepo anati mkaziyo, Mkwati wamwazi iwe, chifukwa cha mdulidwe.” (Eksodo 4:20, 24-26) Ngakhale kuti ndime imeneyi sinafotokoze momveka bwino ndipo n’zosatheka kukhala otsimikizira tanthauzo lake, Malemba amatithandizako kumvetsa mavesi ameneŵa.

Nkhaniyi sikunena mwachindunji kuti akanaphedwayo ndani. Komabe, n’zomveka kunena kuti si Mose amene akanaphedwayo, chifukwa Mulungu anali atangomulamula kumene kuti akatsogolere Aisrayeli kuchoka m’dziko la Igupto. (Eksodo 3:10) Zikuoneka kuti sizikanatheka kuti ali m’njira popita kukachita zimene anamuuzazo, mngelo wa Mulungu akanafuna kupha Moseyo. Motero, ziyenera kukhala kuti amene akanaphedwa ndi m’modzi mwa ana akewo. Lamulo limene Mulungu anapereka kwa Abrahamu m’mbuyomo pankhani ya mdulidwe linati: “Mwamuna wosadulidwa, wosadulidwa khungu lake, munthuyo am’sadze mwa anthu a mtundu wake; waphwanya pangano langa.” (Genesis 17:14) Mose ayenera kuti ananyalanyaza kudula mwana wake, ndipo chifukwa cha zimenezi, mngelo wa Yehova anafuna kupha mwanayo.

Kodi khungu limene Zipora anadula mwana wake pofuna kukonza zinthu analiponya pa mapazi a ndani? Mngelo wa Yehova ndi amene anali ndi mphamvu yopha mwana wosadulidwayo. Motero, m’pake kunena kuti Zipora ayenera kuti anaponya khungulo pa mapazi a mngeloyo, monga umboni wakuti watsatira panganolo.

Mawu a Zipora akuti “iwe ndiwe mkwati wanga wamwazi” ndi mawu achilendo. Kodi mawuŵa akusonyeza chiyani za iye? Mwa kutsatira zimene pangano la mdulidwe linafuna, Zipora anavomereza kuchita pangano ndi Yehova. Pangano la Chilamulo limene anapangana ndi Aisrayeli patapita nthaŵi, linasonyeza kuti m’panganolo, Yehova angakhale ngati mwamuna ndipo Aisrayeliwo ngati mkazi. (Yeremiya 31:32) Motero, pomunena Yehova (kudzera mwa mngelo amene anali kumuimira) kuti ‘mkwati wamwazi,’ Zipora akuoneka kuti anali kuvomereza kugonjera mfundo za m’panganolo. Zinali ngati kuti wavomereza kukhala monga mkazi m’pangano la mdulidwe, ndipo Yehova Mulungu ndiye mwamuna wake. Mulimonse mmene zinalili, chifukwa chochita zinthu mwamsanga pomvera zimene Mulungu anafuna, mwana wakeyo sanaphedwe.