Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mwambo wa Chikumbutso Umene Ukukukhudzani

Mwambo wa Chikumbutso Umene Ukukukhudzani

Mwambo wa Chikumbutso Umene Ukukukhudzani

YESU KRISTU ali padziko lapansi anakhazikitsa mwambo wa chikumbutso umene umalemekeza Mulungu. Umenewu ndi mwambo wa chipembedzo umodzi wokha umene iye analamulira ophunzira ake mwachindunji kuti azikumbukira. Ndi mwambo wa Mgonero wa Ambuye, umene umatchedwanso Mgonero Womaliza.

Tayerekezani kuti mwafika pa mwambowo popanda aliyense kudziŵa ndipo mukuonerera zimene zikuchitika mpaka pamene mwambowu ukuyambika. Yesu ndi atumwi ake asonkhana pamodzi m’chipinda chapamwamba ku Yerusalemu kuti akondwerere Paskha Wachiyuda. Amaliza kudya chakudya chimene anthu amadya nthaŵi zonse pa Paskha, chomwe ndi nyama ya nkhosa yowotcha, masamba owawa, mkate wopanda chotupitsa, ndi vinyo wofiira. Yudasi Iskariote, mtumwi wosakhulupirika, watulutsidwa ndipo pasanapite nthaŵi yaitali adzapereka Mbuye wakeyo kwa adani. (Mateyu 26:17-25; Yohane 13:21, 26-30) M’chipindamo mwatsala Yesu ndi atumwi ake okhulupirika 11. M’modzi mwa iwo ndi Mateyu.

Malinga ndi nkhani ya Mateyu imene analemba monga mboni yoona ndi maso, Yesu anakhazikitsa Mgonero wa Ambuye motere: “Yesu anatenga mkate [wopanda chotupitsa], nadalitsa, naunyema; ndipo mmene anapatsa kwa ophunzira, anati, Tengani, idyani; ichi ndi thupi langa. Ndipo pamene anatenga chikho [mmene munali vinyo], anayamika, napatsa iwo, nanena, Mumwere ichi inu nonse, pakuti ichi ndicho mwazi wanga wa pangano, wothiridwa chifukwa cha anthu ambiri ku kuchotsa machimo.”​—Mateyu 26:26-28.

N’chifukwa chiyani Yesu anakhazikitsa Mgonero wa Ambuye? N’chifukwa chiyani pochita zimenezo anagwiritsa ntchito mkate wopanda chotupitsa ndi vinyo wofiira? Kodi otsatira onse a Kristu anafunika kudya nawo zizindikirozi? Kodi mgonerowu unafunika kuti ophunzirawo aziukumbukira kangati? Ndipo kodi ulidi ndi tanthauzo kwa inu?