Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukuyang’ana pa Mphoto?

Kodi Mukuyang’ana pa Mphoto?

Kodi Mukuyang’ana pa Mphoto?

MATENDA a maso amene amachititsa khungu amayamba pang’onopang’ono. Poyamba, matendaŵa amachititsa munthu kusaona bwinobwino. Ngati wodwalayo sanalandire mankhwala, matendaŵa angafalikire kufika m’katikati mwa diso. Mapeto ake, matendaŵa angachititse munthu kukhala wakhungu.

Monga mmene zilili kuti maso athu enieni angasiye kuona pang’onopang’ono, maso athu auzimu omwe ndi ofunika kwambiri, angasiyenso kuona. Motero, n’kofunika kwambiri kuti tiziona zinthu zauzimu kukhala zofunika kwambiri.

Kuyang’ana pa Mphoto

Chimodzi mwa “zinthu zosaoneka” ndi maso athu enieni ndi mphoto yamtengo wapatali ya moyo wosatha, umene Yehova adzapereka kwa anthu ake okhulupirika. (2 Akorinto 4:18) N’zoona kuti chifukwa chachikulu chimene Akristu amatumikira Mulungu n’chakuti amamukonda. (Mateyu 22:37) Komabe, Yehova amafuna kuti tiziyembekezera kudzalandira mphoto. Amafuna kuti tizimuona monga Atate wooloŵa manja yemwe ndi “wobwezera mphoto iwo akumfuna Iye.” (Ahebri 11:6) Motero, amene amam’dziŵadi Mulungu ndi kumukonda amaona kuti madalitso amene walonjeza ndi amtengo wapatali ndipo amayembekezera kukwaniritsidwa kwa malonjezowo.​—Aroma 8:19, 24, 25.

Anthu ambiri amene amaŵerenga magazini ino ndiponso magazini inzake ya Galamukani!, amasangalala ndi zinthunzi zosonyeza dziko la Paradaiso limene likubwera. Komabe, sitikudziŵa zonse zokhudza mmene dziko la Paradaiso lidzaonekera, ndipo zithunzi zimene timafalitsa zangokhala zithunzi zimene akatswiri ojambula amajambula poyerekezera mmene lidzaonekera pogwiritsa ntchito ndime za m’Baibulo monga Yesaya 11:6-9. Komabe, mkazi wina wachikristu anati: “Ndikaona zithunzi za Paradaiso amene akubwera mu Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, ndimaziyang’anitsitsa monga mmene munthu angachitire ndi kabuku kosonyeza malo osiyanasiyana amene alendo oona malo angapiteko. Ndimadziyerekezera ndili m’dzikolo chifukwa ndi mmene ndikuyembekezera kudzakhalamo nthaŵi ya Mulungu ikadzafika.”

Mtumwi Paulo anamva chimodzimodzi za “maitanidwe [ake] akumwamba.” Iye sanadzione ngati wapeza kale zimenezo, chifukwa anafunika kukhalabe wokhulupirika mpaka mapeto. Koma anapitiriza “kutambalitsira zam’tsogolo.” (Afilipi 3:13, 14) Mofanana ndi zimenezi, Yesu anapirira imfa pa mtengo wozunzirapo “chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake.”​—Ahebri 12:2.

Kodi munakayikirapo ngati mungadzaloŵe m’dziko latsopano? Inde, ndi bwino kusadzidalira mopambanitsa, popeza mphoto ya moyoyo tidzailandira pokhapokha ngati tikhalabe okhulupirika mpaka mapeto. (Mateyu 24:13) Komabe, ngati tiyesetsa kuchita zonse zimene tingathe pochita zimene Mulungu akufuna, tili ndi zifukwa zokwanira zokhulupirira kuti tidzapeza mphotoyo. Kumbukirani kuti Yehova “safuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.” (2 Petro 3:9) Ngati tidalira Yehova, adzatithandiza kuti tidzapeze zimene tikufuna. Inde, zingasemphane ndi chikhalidwe chake ngati atati azifufuza zifukwa zoti alepheretse anthu amene akuyesetsa kum’sangalatsa kuti asadzapeze mphotoyo.​—Salmo 103:8-11; 130:3, 4; Ezekieli 18:32.

Kudziŵa mmene Yehova amaonera anthu ake zimatipatsa chiyembekezo, khalidwe limene ndi lofunika mofanana ndi chikhulupiriro. (1 Akorinto 13:13) Liwu la Chigiriki limene analimasulira m’Baibulo kuti “chiyembekezo” limatanthauza “kuyembekezera chinthu chabwino” mwatcheru. Paulo, ali ndi chiyembekezo chimenecho m’maganizo mwake, analemba kuti: “Tikhumba kuti yense wa inu aonetsere changu chomwechi cholinga ku chiyembekezo chokwanira [“chotsimikizika,” NW] kufikira chitsiriziro; kuti musakhale aulesi, koma akuwatsanza iwo amene alikuloŵa malonjezano mwa chikhulupiriro ndi kuleza mtima.” (Ahebri 6:11, 12) Onani kuti ngati tipitirizabe kutumikira Yehova mokhulupirika, tingakhale otsimikizira kuti chiyembekezo chathucho chidzakwaniritsidwa. Mosiyana ndi zimene anthu m’dzikoli amayembekezera, chiyembekezo chimenechi “n’chosakhumudwitsa.” (Aroma 5:5, NW) Motero kodi tingatani kuti tiziona bwinobwino chiyembekezo chimenechi?

Zimene Tingachite Kuti Tiziona Bwino Mwauzimu

Maso athu enieni sangaone bwinobwino zinthu ziŵiri panthaŵi imodzi. N’chimodzimodzinso ndi maso athu auzimu. Mosakayikira, kuyang’ana zinthu za m’dongosolo lino kudzatichititsa kusaona bwinobwino m’maganizo mwathu lonjezo la Mulungu la dziko latsopano. M’kupita kwa nthaŵi sitingachitenso chidwi ndi chithunzi chosaoneka bwinocho ndipo kenako chingazimiririke mosavuta. Imeneyo ingakhale ngozi yaikulu kwabasi! (Luka 21:34) Ndiyetu m’pofunika kuti tikhale ndi ‘diso lakumodzi,’ diso limene likungoyang’ana pa Ufumu wa Mulungu ndi mphoto ya moyo wosatha.​—Mateyu 6:22.

Kukhala ndi diso la kumodzi si kophweka nthaŵi zonse. Pali mavuto a tsiku ndi tsiku amene amafunika kuti tiwasamalire, ndiponso tingakumane ndi zododometsa, ngakhalenso zokopa. M’zochitika ngati zimenezi, kodi tingatani kuti tiyang’anebe pa Ufumu ndi malonjezo a Mulungu a dziko latsopano popanda kunyalanyaza zinthu zina zofunika kwambiri? Tiyeni tione njira zitatu zimene zingatithandize.

Phunzirani Mawu a Mulungu tsiku ndi tsiku. Kuŵerenga Baibulo nthaŵi zonse ndi kuphunzira mabuku ofotokoza Baibulo kumatithandiza kuti maganizo athu akhale pa zinthu zauzimu. N’zoona kuti mwina takhala tikuphunzira Mawu a Mulungu kwa zaka zambiri, koma tiyenera kupitiriza kuwaphunzira, monga mmene timafunikira kudya chakudya nthaŵi zonse kuti tikhalebe ndi moyo. Sitisiya kudya chifukwa chakuti tadya chakudya chambirimbiri m’mbuyomu. Motero, ngakhale kuti tikulidziŵa bwino kwambiri Baibulo, timafunikira kupitiriza kudya chakudya chauzimu cha m’Baibulo nthaŵi zonse kuti tizionabe bwinobwino chiyembekezo chathu ndiponso kuti chikhulupiriro ndi chikondi chathu chikhale cholimba.​—Salmo 1:1-3.

Sinkhasinkhani Mawu a Mulungu muli ndi mtima woyamikira. N’chifukwa chiyani kusinkhasinkha n’kofunika? Pali zifukwa ziŵiri. Choyamba, kusinkhasinkha kumatithandiza kumvetsa zimene taŵerenga ndi kukhala ndi mtima woyamikira zimene taŵerengazo. Chachiŵiri, kusinkhasinkha kumatithandiza kupeŵa kuiŵala Yehova, ntchito zake zodabwitsa, ndi chiyembekezo chimene watipatsa. Mwachitsanzo: Aisrayeli amene anachoka ku Igupto pamodzi ndi Mose anaona ndi maso awo mphamvu za Yehova zochititsa mantha. Ndiponso anaona akuwateteza mwachikondi pamene anali kuwatsogolera kukalandira choloŵa chawo. Komabe, Aisrayeli atangofika kumene m’chipululu paulendo wawo wopita ku Dziko Lolonjezedwa, anayamba kudandaula, zimene zinasonyeza kuti analibiretu chikhulupiriro. (Salmo 78:11-17) Kodi vuto lawo linali chiyani?

Anthuwo anasiya kuyang’ana pa Yehova ndi chiyembekezo chabwino kwambiri chimene anawapatsa n’kuyamba kumayang’ana pa zinthu zabwino za panthaŵi yomweyo ndi zofuna za moyo wawo wa tsiku ndi tsiku. Ngakhale kuti anadzionera okha zozizwitsa, Aisrayeli ambiri anakhala anthu opanda chikhulupiriro, odandaula. Salmo 106:13 limanena kuti: ‘Anaiwala ntchito zake [za Yehova] msanga.’ Kunyalanyaza zinthu mwadala kumeneko kunachititsa kuti mbadwo umenewo usakaloŵe m’Dziko Lolonjezedwa.

Motero, mukamaŵerenga Malemba kapena mabuku othandizira kuphunzira Baibulo, patulani nthaŵi yosinkhasinkha zimene mukuŵerenga. Kusinkhasinkha kumeneko n’kofunika kwambiri kuti moyo wanu wauzimu ukhale wabwino komanso kuti upite patsogolo. Mwachitsanzo, poŵerenga Salmo 106, limene mbali ina taigwira kale mawu pamwambapa, sinkhasinkha pa makhalidwe a Yehova. Onani mmene analezera mtima ndi kuchitira chifundo Aisrayeli. Onani mmene anachitira zonse zimene akanatha kuti awathandize kukafika ku Dziko Lolonjezedwa. Onaninso mmene anthu anapitirizira kumupandukira. Yerekezerani mkwiyo ndi kupwetekedwa mtima kwa Yehova pamene chifundo ndi kuleza mtima kwake kunafika pamapeto chifukwa cha anthu amene anali osayamika m’pang’ono pomwe. Ndiponso, mwa kusinkhasinkha mavesi 30 ndi 31, amene akufotokoza zimene Pinehasi anachita molimba mtima potsata chilungamo, zikutitsimikizira kuti Yehova saiŵala anthu ake okhulupirika ndi kuti amawapatsa mphoto yaikulu.

Tsatirani mfundo za makhalidwe abwino za m’Baibulo pamoyo wanu. Pamene tikutsatira mfundo za makhalidwe abwino za m’Baibulo, timadzionera tokha kuti malangizo a Yehova ndi opindulitsa. Pa Miyambo 3:5, 6 pamanena kuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; umulemekeze m’njira zako zonse, ndipo Iye adzawongola mayendedwe ako.” Ganizirani mmene makhalidwe oipa a anthu ambiri achititsira anthuwo kuvutika m’maganizo, m’mtima, ndiponso pathupi lawo. Mwa kuchita zinthu zosangalatsa za kanthaŵi chabe, anthu oterowo amatuta mavuto amene amakhala nawo kwa zaka zambiri, ngakhalenso kwa moyo wawo wonse. Mosiyana kwambiri ndi zimenezo, anthu amene amayenda ‘m’njira yochepetsetsa’ amalaŵa moyo wa m’dongosolo latsopano, ndipo zimenezi zimawalimbikitsa kupitiriza kuyenda pa njira ya ku moyo.​—Mateyu 7:13, 14; Salmo 34:8.

Kutsatira mfundo za makhalidwe abwino za m’Baibulo kungakhale kovuta kwambiri. Nthaŵi zina, njira yothetsera mavuto yosagwirizana ndi malemba ingaoneke ngati ndi yothandiza kuti tithane ndi mavuto mwamsanga. Mwachitsanzo, panthaŵi za mavuto a zachuma, pangakhale chiyeso choika zinthu za Ufumu pa malo achiŵiri. Komabe, anthu amene amachita zinthu mwachikhulupiriro ndi kuyang’anabe pa zinthu zauzimu amakhala otsimikiza kuti pamapeto pake “omwe aopa Mulungu naopa pamaso pake adzapeza bwino.” (Mlaliki 8:12) Nthaŵi zina Mkristu angafunike kugwira ovataimu kuntchito, koma sayenera kukhala ngati Esau, amene ananyalanyaza zinthu zauzimu, kuziona ngati zosafunika.​—Genesis 25:34; Ahebri 12:16.

Yesu anafotokoza bwino udindo wathu monga Akristu. Tifunika ‘kuthanga tafuna Ufumu ndi chilungamo cha Mulungu.’ (Mateyu 6:33) Ngati tichita zimenezo, Yehova adzatisonyeza chikondi chake monga tate poonetsetsa kuti tili ndi zimene tikufunikira pa moyo wathu wa tsiku ndi tsiku. Iye safuna kuti tizidzilemetsa ndi kudera nkhaŵa zinthu zimene iye akunena kuti tingazipeze kwa iye. Nkhaŵa yopambanitsa imeneyo ingakhale ngati matenda a maso auzimu. Ngati sitingapeze mankhwala, nkhaŵa yoteroyo ingatichititse kumangoyang’ana kwambiri pa zofunika za tsiku ndi tsiku ndipo mapeto ake ingatichititse kukhala akhungu mwauzimu. Ngati tikhalabe akhungu mwauzimu, tsiku la Yehova lidzatifikira ngati “msampha.” Lingakhale tsoka lalikulutu limenelo!​—Luka 21:34-36.

Khalani Wosasunthika Ngati Yoswa

Tiyeni tiziyang’anabe kwambiri pa chiyembekezo chathu chamtengo wapatali cha Ufumu, tiziika zinthu zina pa malo ake oyenerera. Mwa kupitirizabe chizoloŵezi cha kuphunzira, kusinkhasinkha, ndiponso kutsatira mfundo za makhalidwe abwino za m’Baibulo, tingakhulupirire kuti chiyembekezo chathu chidzakwaniritsidwa monga mmene anachitira Yoswa. Atatsogolera Aisrayeli kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa, iye anati: “Mudziŵa m’mitima yanu yonse, ndi m’moyo mwa inu nonse, kuti pa mawu okoma onse Yehova Mulungu wanu anawanena za inu sanagwa padera mawu amodzi; onse anachitikira inu, sanasoŵapo mawu amodzi.”​—Yoswa 23:14.

Ndiyetu chiyembekezo cha Ufumu chikulimbikitseni, ndipo chikuthandizeni kukhala achimwemwe pamene mukusonyeza zimenezi mwa zimene mumaganiza, mmene mumamvera mumtima mwanu, zosankha zanu, ndiponso pa zochita zanu.​—Miyambo 15:15; Aroma 12:12.

[Chithunzi patsamba 21]

Kodi munakayikirapo zoti mudzaloŵa m’dziko latsopano?

[Chithunzi patsamba 22]

Kusinkhasinkha n’kofunika kwambiri pophunzira Baibulo

[Zithunzi patsamba 23]

Pitirizani kuyang’ana pa zinthu za Ufumu